MBILI YANGA
Napeza Cimwemwe Cifukwa Copatsa
PAMENE n’nali ndi zaka 12, n’nazindikila kuti nili na cinthu camtengo wapatali cimene ningapatseko ena. Pa msonkhano wadela, m’bale wina ananifunsa ngati ningakonde kulalikila. Ninayankha kuti “Inde,” ngakhale kuti n’nali n’kalibe kulalikilapo. Titapita m’gawo, ananipatsa tumabuku tokamba za Ufumu wa Mulungu. Ndipo ananiuza kuti: “Ulalikile mbali ija ya mseu, ine nidzalalikila mbali iyi.” Mwamantha, n’nayamba kulalikila nyumba ndi nyumba. Koma n’nangoona kuti nasiliza kugaŵila tumabuku tonse. Zinaonekelatu kuti anthu ambili anali kufuna kumvela uthenga umene n’nali kuwalalikila.
N’nababwa mu 1923 mumzinda wa Chatham, Kent, ku England. N’nakulila ku malo amene anthu anali okhumudwa cifukwa cakuti Nkhondo Yaikulu imene inacitika m’delali sinacititse kuti dziko likhale labwino. Makolo anga analinso okhumudwa ndi abusa a chechi ca Baptist, amene anali kungofuna zawo zokha. Pamene n’nali ndi zaka pafupi-fupi 9, amayi anayamba kupita ku holo kumene Ophunzila Baibulo [dzina lakale la Mboni za Yehova] anali kucitila misonkhano yawo. Pamene n’nayendako, mlongo wina anayamba kuphunzitsa ife ana nkhani za m’Baibulo poseŵezetsa buku lakuti Zeze wa Mulungu. N’nayamba kukonda kwambili zimene n’nali kuphunzila.
N’NAPHUNZILA ZAMBILI KWA ABALE ACIKULILE
Kucokela nili mwana, napeza cimwemwe cifukwa copatsa mwa kuuzako ena ciyembekezo copezeka m’Mau a Mulungu. Ngakhale kuti nthawi zambili n’nali kupita nekha mu ulaliki, n’naphunzilanso zinthu zina cifukwa colalikila ndi ena. Tsiku lina pamene ine ndi m’bale wina wacikulile tinali kupita kukalalikila m’gawo na njinga, tinaona m’busa wacipembedzo. N’nauza m’baleyo kuti, “Mbuzi iyo.” M’baleyo anaimitsa njinga yake ndi kunipempha kuti tikhale pansi pamalo ena ake. Iye ananifunsa kuti: “Ndani anakupatsa mphamvu zoweluza anthu kuti ni mbuzi? Udziŵa, nchito yathu n’kuuza anthu uthenga wabwino koma kuweluza n’kwa Yehova.” M’masiku amenewo n’naphunzila kuti kupatsa kumabweletsa cimwemwe.—Mat. 25:31-33; Mac. 20:35.
M’bale wina wacikulile ananiphunzitsa kuti nthawi zina kupeza cimwemwe kumafuna kupilila. Mwacitsanzo, mkazi wawo anali kuzonda Mboni za Yehova. Tsiku lina m’baleyo ananiitana kunyumba kwawo kuti tikamwe tiyi. Mkazi wawo atadziwa kuti tinali mu ulaliki, anakwiya kwambili cakuti anayamba kutitema ndi mapaketi a masamba. M’malo momukalipila, m’baleyo anangotenga mapaketiwo n’kuwaika pamalo ake. Patapiza zaka, mkazi wa m’baleyo anabatizika
n’kukhala wa Mboni za Yehova. N’zoonekelatu kuti apa Mulungu anadalitsa m’baleyo cifukwa cokhala woleza mtima.Cifuno canga couzako ena za ciyembekezo ca kutsogolo cinakula. Conco, ine na amayi tinabatizika mu March 1940 mumzinda wa Dover. Pamene n’nali ndi zaka 16, dziko la Britain linayamba kumenya nkhondo ndi dziko la Germany mu September 1939. Mu June 1940, n’taima pakhomo n’naona mathilaki onyamula asilikali ambili akudutsa. Iwo anapulumuka pa nkhondo ya ku Dunkirk ndipo anali acisoni. Iwo analibe ciyembekezo ciliconse. Conco n’nali kulakalaka kuwauza za Ufumu wa Mulungu. Patangopita nthawi, dziko la Britain linayamba kuphulitsa mabomba. Usiku uliwonse, n’nali kuona ndeke za ku Germany zoponya mabomba zikuzungulila dela lathu. Mabomba anali kumveka akuphulitsidwa m’mwamba zimene zinali kuticititsa mantha kwambili. Tsiku lotsatila, pamene tinacoka m’nyumba tinapeza kuti manyumba ambili awonongeka. Zinthu zimenezi zinanicititsa kuzindikila kuti anthu ayenela kuyembekezela Ufumu wa Mulungu cabe.
KUYAMBA UMOYO WOPATSA
M’caka ca 1941, n’nayamba umoyo umene wanithandiza kukhala wacimwemwe. Panthawiyo n’nali n’tayamba kuphunzila nchito yokonza maboti pa kampani ina yochedwa Royal Dockyard mu mumzinda wa Chatham. Nchito imeneyi inali yosililika ndipo inali kunibweletsela mapindu ambili. Kucokela kale, atumiki a Yehova akhala akudziŵa kuti Akhiristu sayenela kumenya nkhondo. Ca m’ma 1941 tinazindikila kuti Akhiristu sayenela kugwila nchito pa kampani yokonza zida za nkhondo. (Yoh. 18:36) Popeza kuti pa kampaniyi tinali kukonza sitima za pamadzi zankhondo, n’nasankha zosiya nchitoyi ndi kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Coyamba, ananitumiza ku tawuni yokongola ya Cirencester mumzinda wa Cotswolds.
Nili ndi zaka 18, n’naikidwa m’ndende kwa miyezi 9 cifukwa cokana kuloŵa usilikali. Pamene ananitsekela m’maselo nekhanekha n’nacita mantha kwambili. Posapita nthawi, alonda andende ndi akaidi anayamba kunifunsa cifukwa cimene ninaloŵela m’ndende, ndipo ninali wokondwa kuwafotokozela cikhulupililo canga.
Pamene n’nacoka m’ndende, ananipempha kukalalikila m’matauni osiyanasiyana a m’dziko la kwathu mumzinda wa Kent ndi M’bale Leonard Smith. * Kuyambila mu 1944, ndeke zambili za nkhondo zinagwetsa mabomba mumzinda wa Kent. Panthawiyi ife tinali kukhala pakati pa Europe ndi dziko la London. Malo amenewa panali kudutsa ndeke za nkhondo. Mabomba amene ndeke zinali kuphulitsa anali kuchedwa doodlebugs. Tinali kulalikila mwamantha cifukwa ukangomvela kuti injini ya ndeke yazima, udziŵa kuti posacedwapa ndeke idzaphulitsa bomba. Tinali kuphunzila Baibulo ndi banja lina la anthu 5. Nthawi zina tinali kukhala munsi mwa thebulo ya nsimbi imene anaipanga n’colinga cakuti iziwateteza ngati nyumba yagwa. M’kupita kwa nthawi banja lonse linabatizika.
KULALIKILA UTHENGA WABWINO KU DZIKO LINA
Pambuyo pa nkhondo, n’napita kukacita upainiya kum’mwela kwa dziko la Ireland kwa zaka ziŵili. Sitinadziŵe kuti dziko la Ireland lisiyana bwanji ndi dziko la England. Conco, tinayamba kuyenda nyumba ndi nyumba kuuza anthu kuti ndife amishonale ndi kupempha malo ogona. Tinali kuwagaŵilanso magazini. Kucita zimenezi kunali “kusaganiza bwino” cifukwa dzikoli linali la Akatolika. Pamene munthu wina anatiwopseza, n’nafotokozela wapolisi. Iye ananiyankha kuti, “Ufuna nicite ciani?” Ife sitinadziŵe kuti abusa acipembedzo ndi amene anali ndi ulamulilo m’delalo. Abusawo anali kucititsa kuti anthu amene anali kulandila mabuku athu acotsedwe nchito. Iwo anacititsanso kuti ticotsedwe m’nyumba zimene tinali kukhala.
Zimenezi zinatiphunzitsa kuti tikafika kudela latsopano, ndi bwino kuti tisamalalikile m’delalo. M’malo mwake tinafunika kulalikila m’dela la kutali limene abusa acipembedzo satidziŵa. Potsilizila pake tinali kulalikila anthu a pafupi. M’dela la Kilkenny tinali kuphunzila Baibulo ndi m’nyamata wina katatu pa mlungu ngakhale kuti magulu a anthu aciwawa anali kutiwopseza. N’nali kukonda kwambili kuphunzitsa anthu Baibulo cakuti n’naganiza zofunsila Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo.
Pambuyo pophunzila Baibulo kwa miyezi 5 ku New York, ine ndi anzanga ena atatu anatitumiza ku zisumbu zing’ono-zing’ono za pa Nyanja ya Caribbean. Mu November 1948, tinacoka mumzinda wa New York kupita ku Bahamas. Tinakwela boti yaitali mamita 18 yochedwa Sibia. Popeza n’nali n’kalibe kukwelapo boti n’nakondwela kwambili. Mnzanga mmodzi, dzina lake Gust Maki anali kaswili woyendetsa boti. Iye anatiphunzitsa zinthu zina zocepa zothandiza poyendetsa boti. Anatiuza mokwezela ndi kutsitsa nsalu za boti, moseŵenzetsela kampasi, ndi motetezela boti kumphepo ya panyanja. Ngakhale kuti pa nyanja panali mphepo za mkuntho, Gust anayendetsa botiyo kwa masiku 30 mpaka kufika ku Bahamas.
KULENGEZA UTHENGA WABWINO PA ZISUMBU
Titalalikila kwa miyezi ingapo ku zisumbu za ku Bahamas, tinasamukila ku zisumbu za Leeward ndi Windward zimene zili pam’tunda wa makilomita 800 kucokela ku zisumbu za Virgin. Zisumbu zimenezi zili pafupi ndi Puerto Rico ndipo zimayandikila ku Trinidad. Kwa zaka 5 tinalalikila kwambili pa zisumbu za kutali kumene kunalibe Mboni. Nthawi zina tinali kukhala milungu ingapo osatuma kapena kulandila uthenga. Koma tinali okondwela polengeza mau a Yehova pa zisumbu zimenezi.—Yer. 31:10.
Tikafika pa cisumbu, anthu a kumidzi imeneyo anali kucita cidwi, ndipo anali kufika pafupi kuti adziŵe kuti ndife ndani. Ena anali asanaonepo boti kapena mzungu. Anthuwo anali aubwenzi, opembedza ndipo anali kuidziŵa bwino Baibulo. Nthawi zambili anali kutipatsa nsomba, makotapela, na nshawa. Kanyumba kathu kanali kang’ono, koma tinali kukwanitsa kugonamo, kuphikilamo, ndi kuchapa zovala.
Tinali kuyenda ndi boti kukaceza ndi anthu tsiku lonse, ndipo tinali kuwaitanila kunkhani ya Baibulo. Ndiyeno m’madzulo, tinali kuliza belu. Zinali zokondweletsa kuona kuti anthuwo abwela kudzamvela nkhani. Pobwela anali kunyamula nyale zimene zinali kuoneka bwino monga nyenyezi zowala. Nthawi zina kunali kubwela anthu ambili, ndipo anali kufunsa
mafunso ambili mpaka usiku. Iwo anali kukonda kuimba nyimbo. Conco, tinawapulintila nyimbo za Ufumu ndi kuwapatsa. Ine ndi anzanga atatu tikayamba kuimba nyimbo mokweza, iwo anali kutitsatila bwino-bwino. Eee! Inalidi nthawi yosangalatsa kwambili.Tikasiliza kuphunzila Baibulo, ophunzila ena, anali kutitsatila tikapita pa nyumba ina n’colinga cakuti akaphunzilenso. Tinali kufunika kucoka pamalo ena ake pambuyo pa milungu ingapo. Conco, tinali kupempha anthu acidwi kwambili kuti apitilize kuphunzitsa ena mpaka pamene tidzabwelelanso. Zinali zosangalatsa kwambili kuona mmene ena anakwanilitsila bwino udindo wawo.
Masiku ano, ku zisumbu zambili zimene tinapitako, kumapita anthu ambili oona malo. Koma panthawiyo anali cabe malo okhala ndi madzi, micenga, komanso mitengo ya kanjeza. Usiku tinali kucoka pa cisumbu cina kupita pa cina ndi boti. Tikakhala m’boti tinali kuona nsomba zochedwa madolofini zikuseŵela pamadzi. Ndipo tinali kungomva congo ca boti tikamayenda pa madzi. Tinali kuonanso kukongola kwa mwezi ukawala usiku makamaka ngati waunika pa nyanja.
Titalalikila ku zisumbu zimenezi kwa zaka 5, tinayamba ulendo wopita ku Puerto Rico kuti tikasinthitse boti yathu ndi boti ya injini. Titafika kumeneko n’nakumana ndi Maxine Boyd, mlongo wokongola amene anali m’mishonale. Kuyambila ali mwana, iye anali kulalikila uthenga wabwino mwacangu. Ndiyeno anatumikila monga mmishonale m’dziko la Dominican Republic mpaka pamene anacotsedwa m’dzikolo ndi boma la Akatolika mu 1950. Popeza n’nali mmodzi wa anthu oyendetsa boti, ananilola kukhala m’dzikolo mwezi umodzi cabe. Conco, n’nafunikanso kupita kukatumikila ku zisumbu zina kwa zaka zingapo. Motelo, n’naziuza kuti: ‘Ronald, ngati umufunadi mtsikanayu, ufunika kucitapo kanthu mwamsanga.’ Pambuyo pa milungu itatu ninam’funa, ndipo patapita milungu 6 tinamanga banja. Ndiyeno anatituma kukacita umishonale ku Puerto Rico. Conco, sin’nabwelele nawo anzangawo ndi boti yatsopano.
Mu 1956 tinayamba kuyendela mipingo monga oyang’anila dela. Abale ambili anali osauka koma tinali kusangalala kuŵayendela. Mwacitsanzo, m’mudzi wina wa Potela Pastillo munali mabanja aŵili a Mboni amene anali ndi ana ambili ndipo n’nali kukonda kuwalizila citolilo. N’nafunsa kamtsikana kena, dzina lake Hilda, ngati kangakonde kukalalikila nafe. Kanakamba kuti: “Nifuna, koma siningapite cifukwa nilibe nsapato.” Tinakagulila nsapato ndipo kanapita nafe mu ulaliki. Pambuyo pa zaka zingapo, mu 1972 ine ndi Maxine, tinapita ku Beteli ya ku Brooklyn. Tinangoona mlongo wina amene anasiliza maphunzilo a Sukulu ya Gileadi akubwela kwa ife. Mlongoyo anali pafupi kupita ku Ecuador kukatumikila monga m’mishonale. Anatifunsa kuti: “Kodi mwanikumbukila? Ndine uja mtsikana wa ku mudzi wa Pastillo amene munagulila nsapato.” Iye anali Hilda. Tinakondwela kwambili cakuti tinalila.
Mu 1960, anatipempha kukatumikila ku ofesi ya nthambi ya ku Puerto Rico. Ofesiyi inali nyumba ing’ono yasanjika mumzinda wa Santurce, San Juan. Poyamba, ine ndi Lennart ndife tinali kugwila nchito yambili mu ofesi imeneyi. Johnson ndi mkazi wake ndiwo anali Mboni zoyamba m’dziko la Dominican Republic. Mu 1957, iwo anabwela m’dziko la Puerto Rico. Ndiyeno Maxine anayamba kuyang’anila ndalama zimene anthu anali kulipila kuti alandile magazini. Pa mlungu, ndalamazo zinali kukhala zambili. Iye anali kusangalala kugwila nchito imeneyi cifukwa anali kudziŵa kuti ni anthu ambili amene anali kulandila cakudya ca kuuzimu.
Nimasangalala ndi utumiki wa pa Beteli cifukwa umapeleka mwayi wotumikila ena. Koma sikuti utumiki umenewu ulibe mavuto. Mwacitsanzo, mu 1967 pa msonkhano woyamba wa maiko ku Puerto Rico, ninavutika maganizo cifukwa ca udindo umene n’nali nawo. M’bale Nathan Knorr, amene anali kutsogolela gulu la Yehova panthawiyo, anabwela ku Puerto Rico. Iye anaona monga n’nanyalanyaza kupanga makonzedwe a thilansipoti ya a mishonale amene anali kubwela. Koma si mmene zinalili. Ngakhale conco, anakhumudwa ndi kunipatsa uphungu wamphamvu. Anakamba kuti sinicita zinthu mwadongosolo. Sininafune kukangana naye koma n’naona kuti sanacite bwino ndipo n’nakhumudwa kwa ka nthawi. Ngakhale n’telo, ine ndi Maxine titaonananso ndi M’bale Knorr, anatipempha kupita ku nyumba kwake ndipo anatikonzela cakudya.
Tili ku Puerto Rico, tinali kupita ku England kukaona makolo nthawi zambili. Pamene ine ndi Amayi tinali kuphunzila coonadi, atate anali kukana. Koma akambi a nkhani ocokela ku Beteli akabwela, amayi
anali kukonda kudzipeleka kuti awasunge kunyumba kwathu. Atate anali kuona kuti abale a pa Beteli amenewa anali odzicepetsa kusiyana ndi azibusa a chechi amene anali atawakhumudwitsa kwambili m’mbuyomo. Zokondweletsa n’zakuti mu 1962, atate anabatizika n’kukhala Mboni.Mu 2011, wokondedwa wanga Maxine anamwalila. Nikuyembekezela mwacidwi kudzamuonanso akadzaukitsidwa. N’kaganizila zimenezi nimakondwela kwambili. Kwa Zaka 58 zimene tinatumikila pamodzi ndi mkazi wanga, tinaona ciŵelengelo ca anthu a Yehova ku Puerto Rico cikukwela kucoka pa 650 kufika pa 26,000. Ndiyeno mu 2013, ofesi ya nthambi ya ku Puerto Rico anaiphatikiza ndi ya ku United States, ndipo ine ananitumiza ku ofesi ya nthambi ya ku Wallkill, ku New York. Zaka 60 zimene n’nakhala pa cisumbu, n’nayamba kudziona kuti ndine wa ku Puerto Rico monga kacule ka kumeneko kamene kamakhala m’mitengo kochedwa coqui. M’madzulo, kacule kameneka kamaimba kuti ko-kee, ko-kee. Koma n’nafunikabe kucoka.
“MULUNGU AMAKONDA MUNTHU WOPELEKA MOKONDWELA”
Nikali kusangalala ndi utumiki wa pa Beteli. Tsopano nili ndi zaka zoposa 90 ndipo nchito yanga ni kulimbikitsa atumiki a pa Beteli monga m’busa wakuuzimu. Kucokela pamene n’nabwela ku Wallkill, nauzidwa kuti nathandizapo anthu oposa 600. Ena amene amanifikila amafuna kuti niwathandize pamavuto aumwini kapena a m’banja. Ena amafunsa zimene angacite kuti acite bwino utumiki wawo pa Beteli. Ena amene anamanga banja posacedwapa amapempha malangizo a zimene angacite kuti banja lawo liyende bwino. Ndipo ena amene atumizidwa kukacita upainiya amabwela kupempha malangizo. Aliyense amene wabwela nimamumvetsela bwino-bwino, ndipo nthawi zina nimawauza kuti: “‘Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.’ Conco, uzikhala wokondwela ndi utumiki uliwonse, cifukwa utumikiwo ni wa Yehova.”—2 Akor. 9:7.
Utumiki wa pa Beteli umakhala ndi mavuto ena amene angakulande cimwemwe, mofanana ndi utumiki wina uliwonse. Koma cofunika ni kuganizila cifukwa cake zimene ucita n’zofunika kwambili. Nchito iliyonse imene timagwila pa Beteli ni yofunika cifukwa imathandiza “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kupeleka cakudya ca kuuzimu ku gulu lonse la abale. (Mat. 24:45) Tili ndi mwayi wotamanda Yehova kulikonse kumene tingakhale. Conco, tiyeni tizicita zimene watiuuza mokondwela cifukwa “Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”
^ par. 13 Mbili ya m’bale Leonard Smith ili mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012.