Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

N’cifukwa ciani adani a Yesu anakhumudwa na nkhani yosamba m’manja?

Iyi inali imodzi mwa nkhani zimene adani a Yesu anakambapo pofuna kupeza cifukwa Yesu na ophunzila ake. Cilamulo ca Mose cinafotokoza zinthu zimene zingadetse munthu. Mwacitsanzo, zinthu monga nthenda ya kukha m’thupi, khate, kapena kugwila mtembo wa nyama kapena wa munthu. Cilamuloco cinapeleka malangizo a zimene munthu angacite kuti akhalenso woyela. Anafunika kupeleka nsembe, kusamba thupi lonse, kapena kuthilidwa madzi.—Lev., caputala 11 mpaka 15; Num., caputala 19.

Atsogoleli Aciyuda anawonjezela malamulo awo m’cilamulo ca Mose. Buku ina inakamba kuti iwo anapanga malamulo ena ndi kukhwimitsa zinthu pa nkhani ya zimene zingadetse munthu, ndi mmene angadetselenso anthu ena. Anapanganso malamulo okhudza mtundu wa ziwiya zimene zingacititse munthu kukhala wodetsedwa, komanso zimene sizingadetsedwe. Malamulo ena anali kukamba za miyambo imene anthu anafunika kutsatila kuti akhalenso oyela.

Adani amenewo anafunsa Yesu kuti: “N’cifukwa ciyani ophunzila anu satsatila miyambo ya makolo, koma amadya cakudya ndi manja oipitsidwa?” (Maliko 7:5) Apa adani amenewa sanali kutanthauza kusamba m’manja kumene tonse timacita tikafuna kudya. Iwo anali atapanga malamulo akuti munthu akalibe kudya, anali kufunika kusambitsidwa manja mpaka ca m’mapewa. Anali kucita izi potsatila miyambo yawo. Buku imeneyo inafotokozanso kuti: “Anapanganso malamulo okhudza mabeseni oikamo madzi amene anafunika kuseŵenzetsa, mtundu wa madzi ogwilitsila nchito, munthu amene anafunika kusambitsa wodetsedwa, ndi mbali ya manja imene inayenela kusambitsidwa.”

Yesu anakamba mosapita m’mbali pa malamulo onse a anthu amenewo. Iye anauza atsogoleli Aciyuda amenewa kuti: “Yesaya analosela moyenela za anthu onyenga inu, monga mmene Malemba amanenela kuti, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo ili kutali ndi ine [Yehova]. Amandipembedza pacabe, cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’ Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu, ndi kuumilila mwambo wa anthu.”—Maliko 7:6-8.