Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumaona Kufunika Kopita Patsogolo Kuuzimu?

Kodi Mumaona Kufunika Kopita Patsogolo Kuuzimu?

“Pitiliza kukhala wodzipeleka poŵelenga pamaso pa anthu, powadandaulila, ndi powaphunzitsa.”—1 TIM. 4:13.

NYIMBO: 45, 70

1, 2. (a) Kodi lemba la Yesaya 60:22 lakwanilitsika bwanji masiku ano? (b) Kodi m’gulu la Yehova la padziko lapansi mufunika ciani?

“WAMNG’ONO adzasanduka anthu 1000, ndipo ocepa adzasanduka mtundu wamphamvu.” (Yes. 60:22) Ulosi umenewu ukukwanilitsika m’masiku ano otsiliza. Takamba izi cifukwa m’caka ca utumiki ca 2015, ofalitsa 8,220,105 analalikila uthenga wabwino mwakhama. Ndipo mau otsilizila a ulosi umenewu ayenela kukhudza Mkhiristu aliyense payekha. Atate wathu wakumwamba akutiuza kuti: “Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi panthawi yake.” Mwacitsanzo, tikakhala m’motoka, timadziŵa kuti ili pa liwilo lalikulu kapena ayi. Mofananamo, tidziŵa kuti nchito yopanga ophunzila yapita patsogolo kwambili. Conco, kodi aliyense wa ife akucitapo ciani? Kodi timalalikila mmene tingakwanitsile monga ofalitsa Ufumu acangu? Abale ndi alongo ambili ayamba upainiya wa nthawi zonse kapena wothandiza. Ndipo timasangalala tikaona ambili akudzipeleka kuti akatumikile kumalo osoŵa kapena kucitako utumiki winawake, si conco?

2 Panthawi imodzi-modzi, tiona kuti pafunikabe anchito ambili. Caka ciliconse, mipingo yatsopano yokwana 2,000 imakhadzikitsidwa. Ngati mpingo uliwonse watsopano wakhala ndi akulu 5, ndiye kuti atumiki othandiza 10,000 angafunike kuyamikilidwa caka ciliconse kuti akhale akulu. Izi zitanthauza kuti pafunika abale ambili amene ayenela kukwanilitsa ziyeneletso kuti ayamikilidwe kukhala atumiki othandiza. Kuwonjezela apo, kaya ndife abale kapena alongo, tifunikabe kukhala ndi “zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.

KODI KUPITA PATSOGOLO KUMATANTHAUZA CIANI?

3, 4. Kupita patsogolo kuuzimu kumatanthauza ciani?

3 Ŵelengani 1 Timoteyo 3:1. M’Cigiriki, liwu lakuti ‘kuyesetsa’ kapena kuti kukalamila, limatanthauza kunyenyemphela kuti utenge cinacake pa malo amene sufikilapo. Pamene Paulo anakamba mau amenewa, anaonetsa kuti kupita patsogolo kuuzimu kumafuna khama. Tiyelekeze kuti m’bale akuganizila mmene angapitile patsogolo mumpingo. Mwina si mtumiki wothandiza, koma adziŵa kuti afunika kukhala na makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa. Coyambilila, akuyesa-yesa kuti ayenelele kukhala mtumiki wothandiza. M’kupita kwa nthawi, akuganizilanso zimene angacite kuti ayenelele kukhala woyang’anila. Iye akucita khama kuti ayenelele kusenza maudindo mumpingo.

4 Mofananamo, abale na alongo amene amalakalaka kukhala apainiya, atumiki a pa Beteli, kapena kudzipeleka kumanga Nyumba za Ufumu, angacite bwino kupita patsogolo kuti akwanilitse zolinga zawo. Tiyeni tikambilane mmene Mau a Mulungu amatilimbikitsila kupita patsogolo kuuzimu.

YESETSANI KUPITA PATSOGOLO

5. Ni zinthu ziti zimene acicepele angacite kuti acilikize nchito ya Ufumu?

5 Acicepele ali ndi mphamvu yocita zambili mu utumiki wa Yehova. (Ŵelengani Miyambo 20:29.) Abale ena amene atumikila pa Beteli amagwila nchito yopulinta ndi kukonza Mabaibulo ndi zofalitsa zina. Abale ndi alongo ambili acicepele amagwila nchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu. Ngati pacitika ngozi ya cilengedwe, acicepele amadzipeleka kuti agwile nchito pamodzi ndi abale ena yothandiza amene akhudzidwa. Ndipo apainiya ambili acicepele amayenda kumalo osoŵa kapena kudela kumene akamba cinenelo cina kuti akalalikile uthenga wabwino.

6-8. (a) Kodi wacicepele wina anacita ciani kuti ayambe kuona zinthu zakuuzimu moyenelela? Nanga zotsatila zake ni zabwanji? (b) Tingacite ciani kuti ‘tilawe ndi kuona kuti Yehova ni wabwino?

6 Mwacionekele, mudziŵa kuti kutumikila Mulungu na mtima wonse n’kofunika kwambili. Koma bwanji ngati mumvela monga mmene m’bale wina dzina lake Aaron anali kumvelela? Olo kuti anakulila m’banja la Mboni, iye anakamba kuti: “Misonkhano ndi kulalikila zinali kunicititsa ulesi.” Anali kudabwa kuti n’cifukwa ciani sapeza cimwemwe potumikila Mulungu ngakhale kuti amafuna kutelo. Kodi anacitapo ciani?

7 Aaron anayamba kuŵelenga Baibulo mokhazikika, kukonzekela misonkhano na kuyankhapo. Iye anayambanso kupemphela nthawi zonse. Izi zinacititsa kuti akonde kwambili Yehova ndi kuyamba kupita patsogolo kuuzimu. Kucokela apo, Aaron anali kucita upainiya mokondwela ndi kugwila nchito pamodzi ndi ena amene amathandiza pakacitika ngozi. Anadzipelekanso kukatumikila ku malo osoŵa. Pano, Aaron ni mkulu ndipo atumikila pa Beteli. Kodi amamvela bwanji na zimene anasankha? Iye anati: “‘Nalaŵa ndipo naona kuti Yehova ni wabwino.’ Nikayang’ana madalitso amene napeza, nimayamikila kwambili Mulungu cakuti nimapitiliza kucita zambili mu utumiki wake. Izi zimacititsa kuti nilandile madalitso ena ambili.”

8 Wamasalimo anaimba kuti: “Ofunafuna Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.” (Ŵelengani Salimo 34:8-10.) N’zoona, Yehova sagwilitsa mwala anthu amene amamutumikila mwakhama. Pamene ticita zimene tingakwanitse kuti titumikile Mulungu, ‘timalaŵa ndi kuona kuti Yehova ni wabwino.’ Ndipo pamene tilambila Mulungu na mtima wonse, timakhala na cimwemwe codzaza tsaya.

LIMBIKILANI NDIPO MUSAFOOKE

9, 10. N’cifukwa ciani mufunika ‘kuyembekezela moleza mtima’?

9 Pamene muyesetsa kuti mukwanilitse zolinga zanu, ‘muziyembekezela moleza mtima.’ (Mika 7:7) Yehova amathandiza atumiki ake okhulupilika ngakhale kuti nthawi zina amawalola kuyembekezela kuti apatsidwe udindo wina wake, kapena kuti zinthu zisinthe. Iye analonjezapo Abulahamu kuti azamupatsa mwana, koma Abulahamu anafunika kuonetsa cikhulupililo na kuleza mtima. (Aheb. 6:12-15) Abulahamu anayembekezela kwa zaka zambili kuti Isaki abadwe, koma sanafooke, ndipo Yehova sanamugwilitse mwala.—Gen. 15:3, 4; 21:5.

10 Kuyembekezela cinthu n’kovuta nthawi zina. (Miy. 13:12) Ngati timaganizila kwambili pa zinthu zimene tinali kuyembekezela koma sizinacitike, tingafooke kwambili. Conco, cinthu canzelu cimene tingacite ni kupita patsogolo kuti tikwanilitse ziyeneletso. Tiyeni tikambilane njila zitatu za mmene tingacitile zimenezi.

11. Ni makhalidwe abwino ati amene tifunika kukhala nawo? Nanga n’cifukwa ciani ni ofunika?

11 Khalani na makhalidwe abwino. Ngati muŵelenga Mau a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha, mudzakhala anzelu, ozindikila, acidziŵitso, ndi oganiza bwino. Makhalidwe amenewa ni ofunika kwambili kwa anthu otsogolela pa kulambila koona. (Miy. 1:1-4; Tito 1:7-9) Ndipo pamene tiŵelenga zofalitsa zathu, timayamba kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Tsiku lililonse, timafunika kusankha pankhani ya zosangulutsa, kavalidwe na kudzikongeletsa, mmene tingaseŵenzetsele ndalama, ndi mmene tingakhalile ndi ena. Ngati titsatila zimene tiphunzila m’Baibulo, tingasankhe zinthu zimene zingakondweletse Yehova.

12. Kodi anthu mumpingo angaonetse bwanji kuti ni okhulupilika?

12 Onetsani kuti ndinu wokhulupilika. Kaya ndife abale kapena alongo, tonse tiyenela kucita zimene tingakwanitse kuti tizigwila nchito iliyonse imene tapatsidwa. Mwacitsanzo, Nehemiya anali bwanamkubwa, ndipo anafunika kusankha anthu ena a Mulungu kuti akhale oyang’anila. Anasankha ndani? Iye anasankha anthu amene anali kuopa Mulungu, okhulupilika, ndi odalilika. (Neh. 7:2; 13:12, 13) Olo masiku ano, “cofunika kwa woyang’anila ndico kukhala wokhulupilika.” (1 Akor. 4:2) Ngati munthu amacita bwino, amaonekela.—Ŵelengani 1 Timoteyo 5:25.

13. Mungatsatile bwanji citsanzo ca Yosefe ngati ena akucitilani zoipa?

13 Lolani kuti Yehova akuyengeni. Mumacita ciani ngati anthu ena akucitilani zinthu zoipa? Mwina mumacitapo kanthu mwamsanga kuti mukonze zinthu. Koma nthawi zina kucita zinthu mwamsanga kuti mudziteteze kumaonongelatu zinthu. Kumbukilani zimene Yosefe anacita abale ake atamucitila zinthu zoipa. Iye sanaŵasungile cakukhosi. Patapita nthawi, Yosefe anapatsidwa mlandu wabodza ndi kuikiwa m’ndende. Koma panthawi yovuta imeneyo analola kuti Yehova amutsogolele. Cinatsatilapo n’ciani? “Mawu a Yehova anamuyenga.” (Sal. 105:19) Pamene mayeselo amenewo anatha, Yosefe anayenelela kulandila udindo wapadela. (Gen. 41:37-44; 45:4-8) Ngati mukumana ndi mavuto, muzipemphela kuti Mulungu akupatseni nzelu, muzikamba ndi kucita zinthu modekha, ndipo muzidalila Mulungu kuti akulimbitseni. Kukamba zoona, Yehova adzakuthandizani.—Ŵelengani 1 Petulo 5:10.

PITANI PATSOGOLO PANKHANI YOLALIKILA

14, 15. (a) N’cifukwa ciani tifunika ‘kusamala nthawi zonse’ ndi kalalikidwe kathu? (b) N’cifukwa ciani nthawi zina mungafunikile kusintha njila yolalikilila? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino, ndi bokosi yakuti “ Kodi Mumayesako Kulalikila M’njila Zina?”)

14 Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Pitiliza kukhala wodzipeleka poŵelenga pamaso pa anthu, powadandaulila, ndi powaphunzitsa. Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:13, 16) Panthawiyo, Timoteyo anali kale mlaliki wa Ufumu wacangu. Koma anafunikabe ‘kusamala nthawi zonse’ ndi zimene anali kuphunzitsa kuti ulaliki wake ukhale wogwila mtima. Kungolalikila mwacizoloŵezi anthu samvetsela. Timoteyo anafunikila kudziŵa zimenezi. Conco, kuti apitilize kuwafika pamtima anafunika kusintha-sintha ulaliki wake malinga ndi zosoŵa za anthu. Ifenso tifunika kucita cimodzi-modzi polalikila uthenga wa Ufumu.

15 Nthawi zambili polalikila khomo ndi khomo, timapeza kuti anthu acokapo panyumba. M’madela ena, timalephela kulalikila m’manyumba ena a mafulati kapena a kumipanda. Ngati ndiye mmene zilili m’gawo lanu, bwanji osayesako njila zina zolalikilila?

16. Kodi tingalalikile bwanji mwaluso mu ulaliki wapoyela?

16 Ulaliki wapoyela ni njila imodzi yabwino kwambili yoyalikilila. Mboni zambili zikupindula ndi ulaliki umenewu. Iwo amapatula nthawi yolalikila anthu pa masitesheni a basi ndi a sitima, m’mamaketi, m’mapaki ndi pamene pamapitila anthu ambili. Mosamala, mboni ingayambe makambilano ndi munthu wina mwa kukambako za nyuzi, kuyamikila khalidwe la ana ake, kapena kum’funsako za nchito yake. Mkati mwa kuceza kwawo, wofalitsa angaloŵetsepo mfundo ya palemba, na kum’funsapo funso. Nthawi zambili zimene munthuyo angakambe zingacititse kuti akambilane zambili za m’Baibulo.

17, 18. (a) N’ciani cingakuthandizeni kukhala ndi cidalilo mu ulaliki wapoyela? (b) N’cifukwa ciani mzimu wa Davide wotamanda Yehova ni wothandiza pamene tili mu ulaliki?

17 Ngati mumaona kuti kucita ulaliki wapoyela n’kovuta, musabwelele m’mbuyo. Mwacitsanzo, mpainiya wina wa ku New York City, dzina lake Eddie, anali kucita mantha kukambilana ndi anthu. Koma m’kupita kwa nthawi, mantha anathelatu. N’ciani cinam’thandiza? Iye anati: “Pakulambila kwa pabanja, ndinali kufufuza ndi mkazi wanga m’zofalitsa zathu kuti tipeze mfundo zoyankhila anthu pa zimene amakhulupilila kapena amene amatsutsa. Timapemphanso malingalilo kwa Mboni zinzathu.” Masiku ano, Eddie amacita kulakalaka ulaliki wapoyela.

18 Pamene muwonjezela luso ndi kukhala na cidalilo polalikila, kupita kwanu patsogolo kudzaonekela. (Ŵelengani 1 Timoteyo 4:15.) Mwakutelo, mudzakhala mukutamanda Atate wathu wakumwamba monga mmene Davide anacitila: Iye anaimba kuti: “Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse. Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza. Ndidzadzitamandila mwa Yehova. Ofatsa adzamva ndi kukondwela.” (Sal. 34:1, 2) Conco, utumiki wanu ungathandize anthu ofatsa kuyamba kulambila Mulungu.

TAMANDANI MULUNGU MWA KUPITA PATSOGOLO KUUZIMU

19. N’cifukwa ciani mtumiki wa Yehova wokhulupilika ayenela kukhala wokondwela, ngakhale pamene zinthu si zili bwino mu umoyo wake?

19 Davide anaimbanso kuti: “Nchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova, Ndipo okhulupilika anu adzakutamandani. Iwo adzanena za ulemelelo wa ufumu wanu. Ndi kulankhula za mphamvu zanu, Kuti ana a anthu adziŵe za nchito zanu zamphamvu Ndi kukula kwa ulemelelo wa ufumu wanu.” (Sal. 145:10-12) Mau amenewa aonetsa mmene atumiki onse a Yehova okhulupilika amamvelela. Koma bwanji ngati simukwanitsa kucita ulaliki mmene mufunila cifukwa ca kudwala kapena ukalamba? Nthawi zonse pamene muuzako anthu amene amakusamalilani ndi ena uthenga wabwino, mumalemekeza Mulungu. Ngati muli m’ndende cifukwa ca cikhulupilio canu, n’zodziŵikilatu kuti mumauzako ena coonadi mukapeza mpata. Kucita zimenezo kumakondweletsa Yehova. (Miy. 27:11) Mwina enanu amuna anu kapena akazi anu si Mboni, koma mumapitiliza kucita zinthu za kuuzimu. Dziŵani kuti Yehova amakondwela nanu. (1 Pet. 3:1-4) Conco, ngakhale pamene zinthu si zili bwino, mungatamande Yehova ndi kupita patsogolo kuuzimu.

20, 21. Kodi anthu ena angapindule bwanji ngati mwapita patsogolo m’gulu la Yehova?

20 Ngati mupitiliza kupita patsogolo kuuzimu, mosakayikila Yehova adzakudalitsani. Mwina mukhoza kusintha zinthu zina ndi zina mu umoyo wanu kuti mukhale na nthawi yambili youzako ena coonadi ca mtengo wapatali. Ndipo kupita kwanu patsogolo ndi kudzipeleka kwanu kudzapindulitsa kwambili Akhiristu anzanu. Ngati mumayesetsa kutumikila modzicepetsa mumpingo, mudzadalitsidwa cifukwa anthu amene amakonda Yehova adzakukondani, kukuyamikilani, ndi kukuthandizani.

21 Kaya tatumikila Yehova kwa zaka zambili, kapena kwa miyezi ing’ono, tonse tingapite patsogolo pomulambila. Kodi Akhiristu ofikapo kuuzimu angathandize bwanji acatsopano kupita patsogolo? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.