Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Eric na Amy

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Ghana

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Ghana

KODI mudziŵako m’bale kapena mlongo amene anayenda ku dziko lina kumene kufunikila ofalitsa Ufumu ambili? Nthawi zambili, ngati tikamba za abale ndi alongo amenewa timanena kuti akutumikila kumalo osoŵa. Koma kodi munadzifunsapo kuti: ‘N’cifukwa ciani anasankha kukatumikila ku dziko lina? Nanga amakonzekela bwanji kuti akwanitse utumiki umenewu? Kodi ine ningakwanitse kucitako utumiki umenewu?’ Kuti tipeze mayankho a zoona a mafunso awa, tiyenela kukamba nawo abale ndi alongo amenewa. Conco tiyeni tiwafunse.

N’CIFUKWA CIANI ANASANKHA UTUMIKI UMENEWU?

N’cifukwa ciani munasankha kukatumikila ku dziko lina kumene ni kosoŵa? Amy, wa ku United States, amene lomba ali ndi zaka za m’ma 30, anayankha kuti: “Kwa zaka zambili, n’nali kufuna kukatumikila ku dziko lina losoŵa, koma n’nali kuona monga siningakwanitse.” N’ciani cinacititsa kuti asinthe maganizo? Iye anati: “Mu 2004 banja lina limene linali kutumikila ku Belize linanipempha kuti nikawacezele ndi kucita nawo upainiya kwa mwezi umodzi. Ninapita, ndipo ninasangalala kwambili. Patapita caka cimodzi cabe, ninayenda ku Ghana kukatumikila monga mpainiya.”

Aaron na Stephanie

Zaka zambili zapitazo, mlongo wina dzina lake Stephanie, wa ku United States, amene lomba ali ndi zaka pafupifupi 30, atapenda mmene zinthu zinalili pa umoyo wake, anati mumtima mwake: ‘Nili ndi thanzi labwino ndipo nilibe udindo uliwonse wosamalila banja. Nikhoza kucita zambili mu utumiki wa Yehova kuposa mmene nicitila tsopano.’ Kudzipenda moona mtima kumeneko kunam’limbikitsa kusamukila ku Ghana kuti awonjezele utumiki wake. Filip ndi Ida, amene ali pa banja ndipo anacokela ku Denmark, nthawi zambili anali kulakalaka kusamukila kudela lina kumene kufunika ofalitsa ambili. Iwo anacita zonse zotheka kuti akwanilitse zolinga zawo. Filip anati: “Pamene mwayi unapezeka, tinali kumvela monga Yehova akutiuza kuti ‘Lomba mungapite.’” Mu 2008, anapita ku Ghana ndipo anatumikila kumeneko kwa zaka zoposa zitatu.

Brook na Hans

Hans ndi Brook, amene ali pa banja, ali ndi zaka za m’ma 30 ndipo ndi apainiya. Iwo atumikila ku United States. Mu 2005, m’dzikolo mutawomba cimphepo camphamvu cochedwa Hurricane Katrina, iwo anagwilako nchito m’gulu lothandiza pakagwa masoka. Patapita nthawi, anafunsila kuti akathandize pa nchito yomanga malo olambilila m’maiko ena koma sanaitanidwe. Hans anati: “Tsiku lina tinamvetsela nkhani pa msonkhano wacigawo imene inafotokoza kuti pamene Mfumu Davide anauzidwa kuti sayenela kumanga kacisi, anavomeleza ndipo anasintha colinga cake. Mfundo imeneyo inatithandiza kuona kuti tikhoza kusintha zolinga zathu zauzimu.” (1 Mbiri 17:1-4, 11, 12; 22:5-11) Nayenso Brook anati: “Yehova anafuna kuti tigogode pa citseko cina.”

Hans ndi Brook atamva zocitika zolimbikitsa zimene anzawo amene anatumikilako ku maiko ena anawasimbila, anaganiza zoyenda ku dziko lina kukacita upainiya. Mu 2012, iwo anayenda ku Ghana ndipo anatumikilako miyezi 4. Kumeneko anali kucilikiza mpingo wa cinenelo ca manja. Ngakhale kuti anabwelela ku United States, kutumikila ku Ghana kunawathandiza kuti aziika patsogolo zinthu za Ufumu. Pano pamene tikamba, iwo akuthandiza pa nchito yomanga ofesi ya nthambi m’dziko la Micronesia.

ZIMENE ANACITA KUTI AKWANILITSE COLINGA CAWO

Munakonzekela bwanji kuti mukatumikile ku malo osoŵa? Stephanie anati: “N’nafufuza ndi kuŵelenga nkhani zokhudza kutumikila ku malo osoŵa mu Nsanja ya Mlonda. * N’nakambilananso ndi akulu ndiponso woyang’anila dela ndi mkazi wake za colinga canga cokatumikila ku dziko lina. Koposa zonse, popemphela n’nali kuuzanso Yehova za colinga canga.” Stephanie analinso kukhala ndi umoyo wosafuna zinthu zambili. Zimenezi zinamuthandiza kuti asunge ndalama zina kuti zikamuthandize pamene akutumikila ku dziko lina.

Hans anafotokoza kuti: “Popeza tinali kufuna kuyenda kumene Yehova afuna, tinamupempha kuti atitsogolele. Tinacita kuchula deti imene tinali kufuna kuyenda kumeneko.” Banja limenelo linatumiza makalata ku maofesi a nthambi anayi. Pambuyo pakuti ayankhidwa ndi nthambi ya ku Ghana, anayenda kumeneko kuti akatumikileko miyezi iŵili cabe. Hans anati: “Tinali kusangalala kwambili ndi utumiki cakuti tinawonjezela masiku okhala kumeneko.”

Adria na George

George ndi mkazi wake Adria, ali ndi zaka pafupi-fupi 40, ndipo anacokela ku Canada. Nthawi zonse iwo anali kukumbukila kuti Yehova amadalitsa anthu amene amapanga zosankha zabwino osati amene amakhala cabe ndi zolinga zabwino koma osacitapo kanthu. Cifukwa ca ici, anacitapo kanthu kuti akwanilitse colinga cawo. Iwo anakambilana ndi mlongo wina amene anali kutumikila ku malo osoŵa ku Ghana ndi kumufunsa mafunso ambili. Analembelanso kalata nthambi ya ku Canada ndi ya ku Ghana. Adria anati: “Ngakhale kuti tinali titasintha zinthu zina mu umoyo wathu, tinasinthanso zina ndi zina kuti tikhale ndi umoyo wosalila zambili.” Kucita zimenezo kunawathandiza, ndipo anasamukila ku Ghana mu 2004.

ZIMENE ANACITA POLIMBANA NDI MAVUTO

Ni mavuto a bwanji amene munakumana nawo pamene munasamuka? Nanga munalimbana nawo bwanji? Kwa Amy, vuto lalikulu linali kuyewa kunyumba. Iye anati: “Zonse zinali zosiyana kwambili ndi zimene ninajaila.” N’ciani cinamuthandiza? Iye anati: “A bululu anga anali kunitumila ma foni ndi kuniuza kuti amayamikila kwambili utumiki umene nimacita. Zimenezi zinanithandiza kumakumbukila cifukwa cimene ninayendela kumeneko. Patapita nthawi, ninayamba kuceza ndi banja langa uku tikuonana pa vidiyo. Cifukwa cakuti tinali kuonana pa vidiyo, sininali kuona kuti banja langa lili kutali kwambili.” Amy anakamba kuti kupanga ubwenzi ndi mlongo wofikapo wa ku maloko kunamuthandiza kudziŵa zikhalidwe zosiyanasiyana za kumeneko. Iye anati: “N’nayamba kudalila kwambili mnzangayo cakuti nikadabwa ndi mmene anthu anali kucitila zinthu, ninali kupita kukamufunsa ndi kupempha thandizo. Iye ananithandiza kudziŵa zimene niyenela kucita ndi zimene niyenela kupewa, ndipo zimenezi zinanithandiza kucita utumiki wanga mosangalala.”

George ndi Adria anafotokoza kuti nthawi yoyamba kusamukila ku Ghana, anamvela monga abwelela ku umoyo wakale kwambili. “Tinali kuseŵenzetsa ma baketi powasha m’malo mwa mashini yowashila,” anatelo Adria. Anakambanso kuti: “Kuphika cakudya kunali kutenga nthawi yaitali kuwilikiza ka 10 ndi nthawi imene tinali kutenga pophika cakudya kwathu. Koma patapita nthawi ing’ono, tinazoloŵela umoyo watsopano umenewo cakuti zinthu zimenezo sizinaonekenso monga n’zovuta.” Brook anati: “Ngakhale kuti nthawi zina apainiyafe timakumana ndi mavuto, timakhalabe okhutila ndi umoyo wathu. Tikayamba kufotokozelana zinthu zabwino zimene zinaticitikila, timalimbikitsidwa kwambili.”

UTUMIKI WOKONDWELETSA

N’cifukwa ciani mungakonde kuti ena aciteko utumiki umenewu? Stephanie anayankha kuti: “Kukamba zoona, kulalikila m’gawo limene anthu amafunitsitsa kuphunzila coonadi, ndipo ni okonzeka kuphunzila Baibulo tsiku lililonse, n’kosangalatsa kwambili. Nimaona kuti n’nasankha mwanzelu kwambili pamene ninayenda kukatumikila kosoŵa.” Mu 2014, Stephanie anamanga banja ndi Aaron, ndipo pano tikamba, atumikila pa Beteli ku Ghana.

Christine, mpainiya wa ku Germany amene ali ndi zaka za m’ma 30 anati: “Zoona, kutumikila ku malo osoŵa n’kosangalatsa.” Iye anali kutumikila ku Bolivia akalibe kuyenda ku Ghana. Anakambanso kuti: “Popeza n’nali kukhala kutali ndi banja langa, nthawi zonse n’nali kudalila Yehova kuti anithandize. Tsopano, iye wakhala bwenzi langa lapamtima. Kuwonjezela pamenepo, nimasangalala ndi mgwilizano umene uli pakati pa anthu a Yehova. Utumiki umenewu wanithandiza kukhala ndi umoyo wa tanthauzo.” Posacedwa, Christine anamanga banja ndi Gideon, ndipo atumikila pamodzi ku Ghana.

Christine na Gideon

Filip ndi Ida anafotokoza zimene anacita kuti athandize ophunzila Baibulo kupita patsogolo. Iwo anati: “Tinali kuphunzila ndi anthu 15 kapena kuposa pamenepo, koma tinacepetsako maphunzilo a Baibulo. Tinali kucititsa maphunzilo 10 cabe. Tinacita izi kuti tizikwanitsa kuwaphunzitsa bwino-bwino.” Kodi izi zinawathandiza bwanji ophunzila? Filip anati: “Ninali kuphunzila ndi mnyamata wina dzina lake Michael. Iye anasankha kuti tiziphunzila tsiku lililonse, ndipo anali kukonzekela bwino cakuti m’mwezi umodzi cabe tinatsiliza kuphunzila buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa. Ndiyeno, Michael anakhala wofalitsa wosabatizika. Tsiku loyamba kupita mu utumiki, iye ananipempha kuti, ‘Kodi munganithandizeko kuphunzitsa maphunzilo anga a Baibulo?’ Ninamuyang’ana modabwa. Michael anakamba kuti anayambitsa maphunzilo atatu ndipo afuna thandizo powaphunzitsa.” Mwaona ka, pafunika aphunzitsi a Baibulo ambili cakuti ngakhale ophunzila Baibulo acita kukhala aphunzitsi a Baibulo.

Ida na Filip

Amy anafotokoza kuti atafika ku Ghana anadziŵa mwamsanga kuti kufunika ofalitsa ambili. Iye anati: “Pamene tinafika ku Ghana, tinayamba kulalikila m’mudzi wina ung’ono ndipo tinayamba kufunafuna anthu amene sakwanitsa kumvela. Tinadabwa kwambili. M’mudzi umodzi cabe umenewo tinapezamo anthu 8 amene sakumva. Tsopano, Amy anamanga banja ndi Eric, ndipo onse atumikila monga apainiya apadela. Iwo atumikila mumpingo wa anthu osamva, ndipo amacilikiza mpingo wa cinenelo ca manja pothandiza ofalitsa osamva ndi ena a cidwi 300 a m’dzikolo. Kwa George ndi Adria, kutumikila ku malo osoŵa kunawathandiza kudziŵa mmene kukhala amishonale kumamvekela. Iwo anasangalala kwambili pamene anawaitana kuti akaloŵe Sukulu ya Gileadi ya nambala 126. Masiku ano, akucita umishonale ku Mozambique.

ANADZIPELEKA CIFUKWA CA CIKONDI

N’zolimbikitsa kwambili kuona anthu ambili ocoka m’maiko ena akugwila nchito yokolola pamodzi ndi abale ndi alongo a ku malo osoŵa. (Yohane 4:35) Ku Ghana, pa avaleji anthu 120 amabatizika mlungu uliwonse. Mofanana ndi abale ndi alongo okwana 17 amene anasamukila ku Ghana, ofalitsa ambili “adzipeleka ndi mtima wonse” cifukwa cokonda Yehova. Iwo atumikila ku malo kumene kufunika olengeza Ufumu ambili. N’zoonekelatu kuti Yehova amakondwela kwambili ndi anchito odzipeleka amenewa.—Sal. 110:3; Miy. 27:11.

^ par. 9 Mwacitsanzo, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Ofalitsa Ufumu Ambiri?” ndi yakuti “Kodi Mungawolokere ku Makedoniya?” mu Nsanja ya Olonda, ya April 15 ndi ya December 15, 2009.