N’cifukwa Ciani Tiyenela ‘Kukhalabe Maso’?
“Simukudziŵa tsiku limene Ambuye wanu adzabwele.”—MAT. 24:42.
NYIMBO: 136, 129
1. Fotokozani citsanzo cimene cionetsa kufunika kodziŵa nthawi imene tikukhalamo ndi zimene zikucitika. (Onani cithunzi cili pamwamba.)
TIYENI tiyelekeze kuti tilipo pa cocitika ici: Tili pamalo a msonkhano, ndipo kutsogolo kuli ci TV cikulu cimene cili na nkholoko. Nthawi yakuti msonkhano uyambe yatsala pang’ono kukwana. Tonse tadziŵa kuti ni nthawi yokhala pansi ndi kumvela nyimbo zamalimba pulogalamu ikalibe kuyamba. Imeneyi ni nthawi yokonzekeletsa maganizo athu kuti timvele nkhani zimene abale adzakamba. Koma anthu ena saikako nzelu ku zimene zicitika. Ali nu! kupitana-pitana ndi kukambitsana ndi anzawo. Saona kuti msonkhano uli pafupi kuyamba. Zaonekelatu kuti sali maso, sadziŵa kuti ni nthawi bwanji, ndipo saona zimene zicitika. Sadziŵanso kuti cheyamani ali pa pulatifomu, nyimbo zamalimba zilila, ndi kuti anthu onse akhala pamipando yawo. Kuganizila cocitika ici kungatithandize kuona kufunika kokhala maso ku cocitika cacikulu cimene cidzacitika posacedwa. N’ciani cidzacitika?
2. N’cifukwa ciani Yesu anauza ophunzila ake kuti ‘akhalebe maso’?
2 Pokamba za “mapeto a nthawi ino,” Yesu Khiristu anacenjeza ophunzila ake kuti: “Khalani maso, khalani chelu, Mat. 24:3; ŵelengani Maliko 13:32-37.) Buku la Mateyu limaonetsanso kuti Yesu anacenjeza ophunzila ake kukhala maso. Anati: “Khalanibe maso cifukwa simukudziŵa tsiku limene Ambuye wanu adzabwele. . . . Khalani okonzeka, cifukwa pa ola limene simukuliganizila, Mwana wa munthu adzabwela.” Anabwelezanso kuti: “khalanibe maso cifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—Mat. 24:42-44; 25:13.
pakuti simukudziŵa pamene nthawi yoikidwilatu idzafika.” Ndiyeno, anawacenjeza mobweleza-bweleza kuti: “Khalani maso.” (3. N’cifukwa ciani timaikako nzelu ku macenjezo a Yesu?
3 Mboni za Yehova zimaikako nzelu ku macenjezo amene Yesu anakamba. Ife tidziŵa kuti tili mkati mweni-mweni mwa “nthawi yamapeto,” ndipo “cisautso cacikulu” cidzayamba lomba apa. (Dan. 12:4; Mat. 24:21) Paliponse m’dzikoli timaona nkhondo, makhalidwe oipa ndi kusamvela malamulo, njala, matenda, ndi zivomezi. Kuwonjezela apo, m’machalichi ambili muli msokonezo. Panthawi imodzi-modzi, anthu a Yehova akulalikila uthenga wabwino wokamba za Ufumu pa dziko lonse. (Mat. 24:7, 11, 12, 14; Luka 21:11) Apa tingoyembekezela mwacidwi mmene kubwela kwa Yesu kudzatipindulitsila ndi kukwanilitsika kwa cifunilo ca Mulungu.—Maliko 13:26, 27.
TSIKULO LILI PAFUPI
4. (a) N’cifukwa ciani tikhulupilila kuti Yesu adziŵa tsiku la Aramagedo? (b) Ngakhale kuti sitidziŵa tsiku limene cisautso cacikulu cidzayamba, kodi tiyenela kutsimikiza za ciani?
4 Tikayenda ku msonkhano, timadziŵa nthawi imene mapulogilamu adzayamba. Koma ngakhale tiyese bwanji, sitingadziŵe caka, kapena tsiku ndi ola limene cisautso cacikulu cidzayamba. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anati: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziŵa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mat. 24:36) Koma apa Yesu kumwamba anapatsidwa mphamvu zowononga dziko la Satana. (Chiv. 19:11-16) Conco, n’zoonekelatu kuti Yesu adziŵa tsiku limene Aramagedo idzabwela. Koma ife sitidziŵa. Ndiye cifukwa cake tifunika kukhala maso mpaka pamene cisautso cidzayamba. Yehova adziŵa bwino-bwino tsiku limene cisautso cacikulu cidzayamba cifukwa anacita kusankhilatu tsikulo. Iye adziŵa kuti tsiku lililonse timayandikila tsiku limenelo. Zoona, mapeto “sadzacedwa.” (Ŵelengani Habakuku 2:1-3.) Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila zimenezi?
5. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti maulosi a Yehova amakwanilitsika panthawi yake.
5 Maulosi a Yehova amakwanilitsika panthawi yake. Mwacitsanzo, ganizilani za tsiku limene anamasula anthu ake ku Iguputo. Pamene anali kukamba za tsiku la Nisani 14, caka ca 1513 B.C.E., Mose anati: “Zaka 430 zimenezi zitatha, pa tsiku lomwe zinatha, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko la Iguputo.” (Eks. 12:40-42) “Zaka 430” zinayamba pamene pangano la Yehova ndi Abulahamu linakwanilitsika mu 1943 B.C.E. (Agal. 3:17, 18) Patapita nthawi, Yehova anauza Abulahamu kuti: “Udziŵe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni, ndipo idzatumikila eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.” (Gen. 15:13; Mac. 7:6) “Zaka 400” zovuta zimenezo zinayamba mu 1913 B.C.E. pamene Isimaeli anayamba kuvutitsa Isaki. Ndipo zinatha pamene Yehova anamasula Aisiraeli ku Iguputo mu 1513 B.C.E. (Gen. 21:8-10; Agal. 4:22-29) Zoona, Yehova anali ataikilatu tsiku limene adzamasula anthu ake kutatsala zaka zambili kuti zicitike.
6. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Yehova adzapulumutsa anthu ake?
Yos. 23:2, 14) Yehova analonjeza kuti adzapulumutsa anthu ake pa cisautso cacikulu ndi kuwapatsa moyo wosatha m’dziko latsopano. Sitikayikila olo pang’ono kuti lonjezo lake limeneli lidzakwanilitsika. Conco, ngati tifuna kuti tikapulumuke pamene dzikoli lidzawonongedwa, tifunika kukhalabe maso.
6 Yoswa anali mmodzi wa Aisiraeli amene anamasulidwa ku Iguputo. Patapita zaka zambili anakumbutsa anthu zimene zinacitika. Iye anati: “Inu mukudziŵa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwanilitsidwe. Onse akwanilitsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwanilitsidwe.” (KHALANIBE MASO KUTI MUKAPULUMUKE
7, 8. (a) Kodi kale alonda anali ndi nchito yanji? Nanga tiphunzilapo ciani? (b) Fotokozani citsanzo ca zimene zingacitike ngati mlonda wagona pa nchito.
7 Tikaona mmene alonda akale anali kulondela mizinda, tingaphunzilepo cinthu cimodzi. Mizinda yambili monga Yerusalemu, inali kucinjilizidwa ndi zipupa zitali-zitali kuti adani asakwanitse kuloŵa mkati. Alonda anali kuimilila pamwamba pa zipupa. Ali pamenepo, anali kukwanitsa kuona malo onse ozungulila mzindawo. Alonda ena anali kuimilila pa geti ya mzinda usana ndi usiku. Nchito yawo inali kulonda mzinda, ndipo akaona kuti adani akubwela, anali kucenjeza anthu mu mzindawo. (Yes. 62:6) Alondawo anafunika kukhala maso nthawi zonse. Ngati akanalephela kucita zimenezo, sembe anthu ambili anafa.—Ezek. 33:6.
8 Josephus wolemba mbili ya Ayuda, anafotokoza kuti asilikali aciroma analanda nsanja ya Antonia mu Yerusalemu m’caka ca 70 C.E., ndi kuukila mzinda wonse. Anakwanitsa kucita zimenezi cifukwa cakuti alonda amene anali pa mageti a mzindawo anali m’tulo. Ataloŵa mkacisi, anauwocha ndi kuwononga mzinda wonse wa Yerusalemu. Apa panali pacimake pa cisautso cacikulu cimene cinacitika mu Yerusalemu.
9. Kodi anthu ambili masiku ano sadziŵa ciani?
9 Kuti ateteze malile a dziko, maboma ambili amaikapo asilikali ndi zipangizo zina zamakono za citetezo. Alonda amenewa amayang’anila kuti adani kapena cinthu cina cisaopseze dziko lawo. Koma “alonda” amenewo amakwanitsa cabe kuteteza dziko lawo ku ziwopsezo zocokela kwa maboma kapena anthu. Sadziŵa kuti kuli boma la kumwamba la Mulungu limene Yesu Khiristu alamulila, ndi kuti posacedwa lidzapeleka ciweluzo ku maboma onse. (Yes. 9:6, 7, 56:10; Dan. 2:44) Conco ngati tikhala maso mwauzimu, tidzakhala okonzekela tsiku la ciweluzo.—Sal. 130:6.
MUSALOLE CINTHU CINA KUKULEPHELETSANI KUKHALA MASO
10, 11. (a) N’ciani cimene tiyenela kusamala naco? Cifukwa? (b) N’ciani cimakucititsani kutsimikiza kuti Mdyelekezi wacititsa anthu kunyalanyaza ulosi wa m’Baibulo?
10 Mlonda amavutika kwambili na tulo kukatsala pang’ono kuca. Zimakhala conco cifukwa panthawiyo amakhala wolema kwambili. Mofananamo, ife tikhala m’masiku otsiliza a dzikoli. Ndipo pamene tiyandikila mapeto, m’pamene cidzakhala covuta kwambili kukhala maso. Cidzaipa kwambili panthawiyo kukumana ndi mavuto cifukwa cosakhala maso. Lomba tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimene zingatilepheletse kukhala maso.
Yoh. 12:31; 14:30; 16:11) Yesu anali kudziŵa kuti Mdyelekezi adzacititsa anthu kukhala mum’dima wa kuuzimu n’colinga cakuti asaone kuti maulosi amene Mulungu anakamba ali pafupi kukwanilitsika. (Zef. 1:14) Satana amaseŵenzetsa zipembedzo zabodza kuti acititse khungu maganizo a anthu. Mumaona bwanji ngati mukambilana ndi ena? Kodi simuvomeleza kuti Mdyelekezi “wacititsa khungu maganizo a anthu osakhulupilila” kuti asadziŵe kuti mapeto a dzikoli ali pafupi, ndi kuti Khiristu tsopano akulamulila mu Ufumu wa Mulungu? (2 Akor. 4:3-6) Ni kangati pamene anthu amakuyankhani kuti “Sinifuna” mukafuna kuwalalikila? Nthawi zambili amatitsutsa tikawauza kuti dzikoli liwonongedwa posacedwa.
11 Mdyelekezi amacititsa kuti anthu agone mwauzimu. Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anacenjeza ophunzila ake katatu za “wolamulila wa dzikoli.” (12. N’cifukwa ciani sitiyenela kulola kuti Mdyelekezi atinamize?
12 Musalole kuti zokamba kapena zocita za ena zikufooketseni ndi kucititsa kuti musakhale maso. Kumbukilani zimene Paulo analembela Akhiristu anzake. Iye anati: “Inu eni mukudziŵa bwino kuti tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku.” (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:1-6.) Yesu anaticenjezanso kuti: “Khalani okonzeka, cifukwa pa ola limene simukuliganizila, Mwana wa munthu adzafika.” (Luka 12:39, 40) Posacedwa, Satana adzanamizanso anthu mwa kuwacititsa kuganiza kuti ali pa “bata ndi mtendele” m’dziko lawoli. Iye adzawanama mwa kuwacititsa kuganiza kuti zinthu zonse zili bwino-bwino. Nanga ife? Tsiku laciweluzo silidzatifikila “ngati mbala” ‘tikakhalabe maso ndi oganiza bwino.’ Ndiye cifukwa cake tiyenela kuŵelenga Mau a Mulungu tsiku lililonse ndi kuganizila zimene Yehova amatiuza.
13. Kodi mzimu wa dziko umawakhudza bwanji anthu? Nanga tingacite ciani kuti tiupewe?
13 Mzimu wa dzikoli umacititsa kuti anthu agone kuuzimu. Anthu ambili ali yakali-yakali kufuna-funa zinthu zakuthupi cakuti ‘sazindikila zosoŵa zawo zakuuzimu.’ (Mat. 5:3) Iwo amakopeka kwambili ndi zinthu za m’dzikoli zimene zimacititsa kuti akhale ndi ‘cilakolako ca thupi ndi cilakolako ca maso.’ (1 Yoh. 2:16) Ndipo masiku ano kuposa kale, kuli zinthu zosangalatsa zambili zimene zimakopa anthu ndi kuwalimbikitsa ‘kukonda zinthu zosangalatsa.’ (2 Tim. 3:4) Ndiye cifukwa cake Paulo anauza Akhiristu kuti ‘asamakonzekele kucita zilakolako za thupi,’ zimene zimayambitsa tulo twauzimu.—Aroma 13:11-14.
14. Ni cenjezo ya bwanji imene ili pa Luka 21:34, 35?
14 Ife tifuna kuti tizitsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu osati mzimu wa dziko. Ndi mzimu wake, Yehova watithandiza kumvetsetsa bwino-bwino zimene zili pafupi kucitika. [1] (1 Akor. 2:12) Koma tifunika kusamala. Ngakhale zinthu za mu umoyo zimene zioneka monga sizingacititse munthu kugona mwauzimu, zikhoza kutisokoneza kuti tilephele kucita zinthu za kuuzimu. (Ŵelengani Luka 21:34, 35.) Anthu ena angatione monga tilibe nzelu cifukwa cokhala maso. Koma sitiyenela kuleka kukhala maso. (2 Pet. 3:3-7) M’malomwake, tiyenela kugwilizana ndi Akhiristu anzathu mwa kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, cifukwa n’kumene kumapezeka mzimu wa Mulungu.
15. N’ciani cinacitikila Petulo, Yakobo, ndi Yohane? Nanga zimenezo zingaticitikile bwanji?
15 Zofooka zathu zingatilepheletse kukhala maso. Yesu anali kudziŵa bwino kuti n’zosavuta kwa anthu opanda ungwilo kugonja cifukwa ca zofooka za thupi. Ganizilani zimene zinacitika usiku wakuti maŵa Yesu aphedwa. Iye anapemphela kwa Atate wake wakumwamba kuti am’thandize kupitiliza kukhala wokhulupilika. Yesu popita kukapemphela, anauza Petulo, Yakobo, ndi Yohane kuti ‘akhalebe maso.’ Koma iwo anaitenga mopepuka nkhaniyo. M’malo mokhala maso ndi kuyang’anila Mbuye wawo, iwo anagonja ku zofooka zathupi ndipo anagona. Ngakhale kuti Yesu nayenso anali wolema, anakhala maso mwa kulimbikila kupemphela kwa Atate wake. Izi n’zimene anzake anafunika kucita.—Maliko 14:32-41.
16. Mogwilizana ndi lemba la Luka 21:36, kodi Yesu anatilangiza kucitanji?
16 ‘Kukhalabe maso’ mwauzimu kumatanthauza zambili kuposa kungocita zoyenela. Kutatsala masiku ocepa kuti ayende m’munda wa Getsemane, Yesu anauza ophunzila ake amodzi-modziwo kuti alimbikile kupemphela kwa Yehova. (Ŵelengani Luka 21:36.) Conco, kuti tipitilize kukhala maso mwauzimu, tiyenela kupemphela kwa Yehova nthawi zonse.—1 Pet. 4:7.
MUZIKHALA MASO NTHAWI ZONSE
17. Tingacite ciani kuti tikhale okonzekela zimene zidzacitika posacedwapa?
17 Popeza Yesu anakamba kuti mapeto adzabwela ‘pa ola limene sitiliganizila, ino si nthawi yogona mwauzimu, yofuna-funa zinthu zosatheka za m’dziko la Satana, kapena zimene timalakalaka. (Mat. 24:44) Kupitila m’Baibulo, Mulungu na Khiristu watiuza madalitso amene atisungila kutsogolo, na zimene tingacite kuti tikhalabe maso. Tiyenela kuteteza umoyo wathu wakuuzimu ndi unansi wathu ndi Yehova. Cina, tiyenela kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo. Tiyenelanso kuzindikila nthawi imene tikhalamo na zimene zicitika, kuti tikonzekele zimene zidzacitika posacedwa. (Chiv. 22:20) Tikakangiwa kucita zimenezi, palibe cathu.