NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA March 2016

Mangazini ino ili ndi nkhani zophunzila mlungu wa May 2 mpaka May 29, 2016.

Kodi Mungathandize Ena Mumpingo Wanu?

Kodi mungaonetse mzimu wa umishonale mumpingo wanu?

Acinyamata Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?

Mafunso atatu amene angakuthandizeni kupanga cosankha.

Acinyamata​—Kodi Mungakonzekele Bwanji Ubatizo?

Nanga bwanji ngati muona kuti si ndinu okonzeka kubatizidwa? Kodi muyenela kucita ciani ngati muona kuti ndinu okonzeka, koma makolo anu akuuzani kuti muyembekeze coyamba kuti mukuleko ndi kudziŵa zambili?

Kodi Tingalimbitse Bwanji Mgwilizano Pakati Pathu?

Masomphenya olembedwa m’buku la Civumbulutso caputala 9 amaonetsa cifukwa cake tifunika kukhala ogwilizana.

Yehova Amatsogolela Anthu Ake m’Njila ya ku Moyo

Tingaonetse bwanji kuti timafuna kutsogoleledwa ndi Mulungu?

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Ndi liti pamene anthu a Mulungu anakhala akapolo a Babulo Wamkulu? Kodi Satana anatenga Yesu mwacindunji ndi kupita naye kukacisi kukamuyesa?