Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Tingalimbitse Bwanji Mgwilizano Pakati Pathu?

Kodi Tingalimbitse Bwanji Mgwilizano Pakati Pathu?

‘Kucokela kwa iye, thupi lonselo . . . ndi lolumikizika bwino ndi logwilizana.’​—AEFESO 4:16.

NYIMBO: 53, 107

1. Kuyambila paciyambi, kodi Mulungu wakhala akugwila bwanji nchito ndi ena?

KUCOKELA paciyambi ca cilengedwe, Yehova ndi Yesu akhala akugwila nchito mogwilizana. Yehova analenga Yesu asanalenge cina ciliconse. Kenako, Yesu anayamba kugwila nchito ndi Mulungu, ndipo anali “pambali pake monga mmisili waluso.” (Miyambo 8:30) Atumiki a Yehova naonso anali kugwila nchito pamodzi mogwilizana. Mwacitsanzo, Nowa ndi banja lake anamanga cingalawa. Patapita nthawi, Aisiraeli anagwilila nchito limodzi pomanga cihema, ndipo posamuka anali kucipasula ndi kukacimanga pa malo ena. Iwo anali kuimbila pamodzi nyimbo zosangalatsa zotamanda Yehova m’kacisi. Atumiki a Yehova anatha kucita zonsezi cifukwa cakuti anali ogwilizana.—Genesis 6:14-16, 22; Numeri 4:4-32; 1 Mbiri 25:1-8.

2. (a) Kodi Akristu oyambilila anali kudziŵika ndi mzimu wotani? (b) Kodi tikambilana mafunso ati?

2 Akristu oyambilila naonso anali kucita zinthu mogwilizana. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Akristuwo anali ogwilizana ngakhale kuti anali ndi maluso ndiponso mautumiki osiyanasiyana. Onse anali kutsatila citsanzo ca Mtsogoleli wao, Yesu Kristu. Paulo anawayelekezela ndi thupi lopangidwa ndi ziwalo zosiyanasiyana zimene zimagwila nchito mogwilizana. (Ŵelengani 1 Akorinto 12:4-6, 12.) Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Kodi tingalimbitse bwanji mgwilizano pa nchito yolalikila, mumpingo, komanso m’banja?

KHALANI OGWILIZANA PA NCHITO YOLALIKILA

3. Kodi mtumwi Yohane anaona masomphenya otani?

3 M’nthawi ya atumwi, Yohane anaona masomphenya a angelo 7 amene anali kuliza malipenga. Mngelo wacisanu ataliza lipenga, Yohane anaona “nyenyezi imene inagwela kudziko lapansi kucokela kumwamba.” “Nyenyezi” imeneyo inali ndi kiyi ya dzenje lolowela kuphompho ndipo inatsegula dzenjelo. Itatsegula, m’dzenjemo munatuluka utsi wambili ndipo mu utsimo munatuluka dzombe. Dzombelo silinaononge mitengo kapena zomela. M’malomwake, linavulaza ‘anthu amene analibe cidindo ca Mulungu pamphumi pao.’ (Chivumbulutso 9:1-4) Yohane anadziŵa kuti dzombe lingaononge zinthu zambili monga mmene linaonongela ku Iguputo m’nthawi ya Mose. (Ekisodo 10:12-15) Dzombe limene Yohane anaona likuimila Akristu odzozedwa amene akhala akulengeza uthenga wamphamvu wotsutsa cipembedzo conama. Ndipo anthu mamiliyoni ambili amene ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi akulengeza nao uthenga umenewo. Onse akugwila nchito yolalikila mogwilizana. Nchito imeneyi yathandiza anthu ambili kutuluka m’cipembedzo conama ndi kumasulidwa ku ulamulilo wa Satana.

Timatha kugwila nchito yolalikila padziko lonse cifukwa cakuti ndife ogwilizana

4. Kodi anthu a Mulungu ali ndi nchito yotani? Nanga kuti aikwanilitse ayenela kucita ciani?

4 Tili ndi nchito yolengeza “uthenga wabwino” kwa anthu padziko lonse lapansi mapeto asanafike. Imeneyi ndi nchito yaikulu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Tiyenela kuitana anthu onse a “ludzu” kuti adzamwe “madzi a moyo,” kutanthauza kuti tiyenela kuphunzitsa anthu amene afuna kumva coonadi ca m’Baibulo. (Chivumbulutso 22:17) Koma tingathe kucita zimenezi ngati ndife ‘olumikizana bwino,’ ndiponso ngati ticita zinthu mogwilizana mumpingo.—Aefeso 4:16.

5, 6. Kodi kugwila nchito yolalikila kumatithandiza bwanji kukhala ogwilizana?

5 Kuti tifikile anthu ambili, tifunika kulalikila mwadongosolo ndiponso mogwilizana. Malangizo amene timapatsidwa pampingo amatithandiza kuti ticite zimenezi. Pambuyo pa msonkhano wokonzekela utumiki, timapita kukauza anthu uthenga wabwino wa Ufumu. Timawagaŵilanso zofalitsa zofotokoza Baibulo. Ndipo tagaŵila zofalitsa zambili padziko lonse lapansi. Nthawi zina, timakhala ndi makonzedwe apadela a ulaliki. Pamene tikugwila nao nchitoyi, timakhala tikulalikila uthenga umodzi ndi abale athu padziko lonse lapansi mogwilizana. Timakhalanso tikugwila nchito limodzi ndi angelo, amene akuthandiza anthu a Mulungu kulalikila uthenga wabwino.—Chivumbulutso 14:6.

6 Pamene tiŵelenga Buku Lapacaka, timasangalala kumva zotsatilapo za nchito yolalikila padziko lonse lapansi. Ganizilaninso za mgwilizano umene timakhala nao padziko lonse poitanila anthu ku msonkhano wacigawo. Kumeneko, tonse timaphunzitsidwa zinthu zofanana. Nkhani zimene zimapelekedwa, maseŵelo, ndi zitsanzo, zimatilimbikitsa kucita zimene tingathe potumikila Yehova. Timaonetsanso kuti ndife ogwilizana ndi abale ndi alongo athu padziko lonse pamene tipezeka pa Cikumbutso caka ciliconse. (1 Akorinto 11:23-26) Tonse timasonkhana pa tsiku limodzi, pa Nisani 14, dzuŵa litangoloŵa poonetsa kuyamikila zinthu zimene Yehova waticitila ndi kumvela lamulo la Yesu. Ndipo pakangotsala milungu yocepa, timagwila nchito mogwilizana poitanila anthu ku Cikumbutso.

7. N’ciani cimene timakwanitsa kucita tikamagwila nchito yolalikila mogwilizana?

7 Dzombe limodzi palokha silingacite zambili. Mofananamo, munthu mmodzi sangathe kulalikila anthu onse padziko lapansi. Koma cifukwa cakuti timagwila nchitoyi mogwilizana, timatha kuphunzitsa anthu ambili za Yehova ndi kuwathandiza kuti azim’tamanda ndi kum’lemekeza.

KHALANI OGWILIZANA PAMPINGO

8, 9. (a) Ndi fanizo lotani limene Paulo anapeleka kuti athandize Akristu kukhala ogwilizana? (b) Tingatani kuti tikhale ogwilizana mumpingo?

8 Paulo anafotokozela Akristu a ku Efeso mmene mpingo ulili wogwilizana, ndipo anakamba kuti Mkristu aliyense mumpingo ayenela ‘kukula m’zinthu zonse.’ (Welengani Aefeso 4:15, 16.) Paulo anagwilitsila nchito citsanzo ca thupi pofotokoza kuti Mkristu aliyense angathandize kuti mpingo ukhale wogwilizana ndi kutsatila Yesu amene ndi Mtsogoleli wa mpingo. Iye anakamba kuti mbali zonse za thupi ndi zogwilizana “mwa mfundo iliyonse yogwila nchito yake yofunikila.” Conco, kodi tonsefe tiyenela kucita ciani mosasamala kanthu za msinkhu wathu kapena thanzi lathu?

Kodi mungathandize bwanji mpingo kukhala wogwilizana?

9 Yesu wasankha akulu kuti azitsogolela mpingo, ndipo amafuna kuti tiziwalemekeza ndi kutsatila malangizo amene amatipatsa. (Aheberi 13:7, 17) Nthawi zina, kucita zimenezi kumakhala kovuta. Koma tiyenela kupempha Yehova kuti atithandize. Mzimu wake woyela udzatithandiza kumvela malangizo onse amene akulu amatipatsa. Ngati ndife odzicepetsa ndipo timagwilizana ndi akulu, mpingo wathu udzakhala wogwilizana ndiponso tidzayamba kukondana kwambili.

10. Kodi atumiki othandiza amathandiza bwanji kuti mpingo ukhale wogwilizana?

10 Atumiki othandiza naonso amathandiza kuti mpingo ukhale wogwilizana. Iwo amagwila nchito mwakhama pothandiza akulu, ndipo timawayamikila pa zonse zimene amacita. Mwacitsanzo, atumiki othandiza amaonetsetsa kuti tili ndi zofalitsa zokwanila zimene tidzagwilitsila nchito mu ulaliki, ndiponso amalandila alendo amene amabwela ku misonkhano. Iwo amayesetsa kukonza zinthu zoonongeka pa Nyumba ya Ufumu ndi kuiyeletsa. Tikamagwilizana ndi abale amenewa, timathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino komanso mwadongosolo mumpingo.—Yelekezelani ndi Machitidwe 6:3-6.

11. Kodi acinyamata angacite ciani kuti athandize mpingo kukhala wogwilizana?

11 Akulu ena atumikila mumpingo modzipeleka kwa zaka zambili. Koma cifukwa ca ukalamba, sakwanitsa kucita zimene anali kucita kale. Conco, abale acinyamata ayenela kuwathandiza. Ngati io aphunzitsidwa bwino, angasamalile maudindo ambili mumpingo. Ndipo mtumiki wothandiza akamatumikila modzipeleka, mtsogolo angadzayenelele kukhala mkulu. (1 Timoteyo 3:1, 10) Akulu ena acinyamata, apita patsogolo kwambili mwakuuzimu. Iwo akutumikila monga oyang’anila a madela ndipo akuthandiza abale ndi alongo ambili m’mipingo. Timayamikila tikaona acinyamata amene amatumikila abale ndi alongo modzipeleka.—Ŵelengani Salimo 110:3; Mlaliki 12:1.

KHALANI OGWILIZANA M’BANJA

12, 13. N’ciani cingathandize kuti onse m’banja azigwilizana?

12 Kodi tingacite ciani kuti tikhale ogwilizana m’banja? Kucita kulambila kwa pabanja mlungu uliwonse kungatithandize. Makolo ndi ana akamapatula nthawi yophunzila za Yehova pamodzi, amayamba kukondana kwambili. Panthawi ya kulambila kwa pabanja, io angayeseze zimene angakambe mu ulaliki. Kucita zimenezi kungathandize kuti aliyense m’banja akhale wokonzeka kulalikila mwaluso. Komanso aliyense akamaona kuti onse m’banjamo amakonda kukamba za coonadi ndi kuti amakonda Yehova ndipo amafuna kum’kondweletsa, ubwenzi wao umalimba.

Ngati mwamuna ndi mkazi amakonda Yehova ndi kum’tumikila, banja lao limakhala lacimwemwe ndi logwilizana

13 N’ciani cingathandize mwamuna ndi mkazi kukhala ogwilizana? (Mateyu 19:6) Ngati onse amakonda Yehova ndi kum’tumikila, banja lao limakhala lacimwemwe ndi logwilizana. Iwo afunika kuonetsana cikondi cacikulu monga mmene Abulahamu ndi Sara, Isaki ndi Rabeka, komanso Elikana ndi Hana, anacitila. (Genesis 26:8; 1 Samueli 1:5, 8; 1 Petulo 3:5, 6) Mwamuna ndi mkazi akamacita zimenezi, amakhala ogwilizana ndipo amayandikila Yehova kwambili.—Ŵelengani Mlaliki 4:12.

Kulambila kwa pabanja kumathandiza acinyamata ndi acikulile kuti azikondana kwambili (Onani ndime 12 ndi 15)

14. Ngati mwamuna kapena mkazi wanu satumikila Yehova, kodi mungacite ciani kuti banja likhalebe lolimba?

14 Baibulo limakamba momveka bwino kuti sitiyenela kuloŵa m’banja ndi munthu amene satumikila Yehova. (2 Akorinto 6:14) Koma pali abale ndi alongo ena amene ali m’banja ndi munthu amene si wa Mboni za Yehova. Ena anaphunzila coonadi pambuyo pokwatilana, koma mnzawo sanafune kukhala Mboni. Ena anakwatilana ndi mtumiki wa Yehova, koma mwamuna kapena mkazi wao anasiya coonadi. Ngati zili conco, Mkristu afunika kuyesetsa kulimbitsa cikwati cake mwa kupitilizabe kumvela malangizo a m’Baibulo. Koma nthawi zina kucita zimenezi kumakhala kovuta. Mwacitsanzo, Mary ndi amuna ake, a David anali kutumikila Yehova pamodzi. Kenako, a David anasiya kupezeka pamisonkhano. Koma Mary anapitilizabe kukhala mkazi wabwino ndi kuonetsa makhalidwe acikristu. Iye anaphunzitsa coonadi ana ake 6, ndipo anapitilizabe kupezeka pamisonkhano yampingo ndi ikuluikulu. Patapita zaka, ana ake atakula ndi kucoka panyumba, Mary anapitiliza kutumikila Yehova ngakhale kuti zinali zovuta. Koma kenako, a David anayamba kuŵelenga magazini amene Mary anali kuwapatsa. M’kupita kwa nthawi, anayambanso kupezeka pamisonkhano. Nthawi zonse, mdzukulu wao wamwamuna wa zaka 6 anali kuwasungila malo okhala, ndipo ngati a David sanabwele kumisonkhano, mdzukuluyo anali kuwauza kuti, “Ndinakusoŵani kumisonkhano lelo Ambuya.” Patapita zaka 25, a David anabwelela kwa Yehova, ndipo io ndi akazi ao tsopano akutumikilanso Yehova pamodzi mosangalala.

15. Kodi Akristu amene akhala m’banja kwa zaka zambili angathandize bwanji acinyamata amene ali pabanja?

15 Masiku ano, Satana akuukila kwambili mabanja. Ndiye cifukwa cake mwamuna ndi mkazi amene akutumikila Yehova ayenela kukhala ogwilizana. Kaya mwakhala m’banja kwa nthawi yaitali kapena ai, muziganizila zimene mungakambe ndi kucita kuti mulimbitse banja lanu. Ngati mwakhala m’banja kwa zaka zambili, muyenela kukhala citsanzo cabwino kwa acinyamata amene ali pabanja. Mungaitane banja lacinyamata kuti lidzapezeke pa kulambila kwanu kwa pabanja. Iwo adzaona kuti ngakhale anthu amene akhala m’banja kwa zaka zambili, amafunika kusonyezana cikondi ndi kugwilizana.—Tito 2:3-7.

“TIYENI TIPITE KUKAKWELA PHILI LA YEHOVA”

16, 17. Ndi ciyembekezo cotani cimene atumiki a Mulungu ali naco?

16 Popita ku cikondwelelo ca Pasika ku Yerusalemu, Aisiraeli anali kucita zinthu mogwilizana. Iwo anali kukonza zinthu zonse zofunikila paulendo. Kenako anali kupitila limodzi ndipo m’njila anali kuthandizana. Pa kacisi, anali kulambila ndi kutamanda Yehova mogwilizana. (Luka 2:41-44) Masiku ano, pamene tikuyembekezela moyo wosatha m’dziko latsopano, tifunika kucita zonse zimene tingathe kuti tipitilizebe kukhala ogwilizana. Kodi n’ciani cimene tingacite kuti tilimbitse mgwilizano pakati pathu?

17 Anthu m’dzikoli sagwilizana pa zinthu zambili, ndipo ena amacita kumenyana cifukwa cosiyana maganizo. Koma ife timayamikila Yehova cifukwa cakuti watithandiza kukhala pamtendele ndi kumvetsetsa coonadi. Ndipo anthu a Mulungu padziko lonse akum’lambila monga mmene iye amafunila. Anthu a Yehova ndi ogwilizana kwambili masiku otsiliza ano kuposa kale. Monga mmene Yesaya ndi Mika analoselela, tikukwela “phili la Yehova” mogwilizana. (Yesaya 2:2-4; ŵelengani Mika 4:2-4.) Tidzasangalala kwambili pamene anthu onse padziko lapansi adzakhala ‘olumikizana bwino’ ndi ogwilizana polambila Yehova.