Kodi Mungathandize Ena Mumpingo Wanu?
YESU asanapite kumwamba, anauza ophunzila ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Kodi io akanakwanitsa bwanji kulalikila padziko lonse lapansi?
Pulofesa Martin Goodman, wa pa Univesite ya Oxford, anakamba kuti: “Kumayambililo kwa ulamulilo wa Roma, nchito yolalikila inasiyanitsa Akristu ndi magulu ena a zipembedzo, kuphatikizapo Ayuda.” Yesu anali kuyenda m’madela osiyanasiyana kukalalikila. Akristu oona anatengela citsanzo cake mwa kulalikila “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu” kulikonse. Iwo anali kufunafuna anthu amene anali kufuna kudziŵa coonadi. (Luka 4:43) Ndiye cifukwa cake kale kunali Akristu amene anali kuchedwa “atumwi.” Liu limeneli limatanthauza anthu amene atumidwa kuti akacite cina cake. (Maliko 3:14) Yesu analamula otsatila ake kuti: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.”—Mateyu 28:18-20.
Atumwi 12 a Yesu salinso padziko lapansi, koma atumiki ambili a Yehova akutengela citsanzo cao pa nchito yolalikila. Iwo akapemphedwa kukatumikila kumalo osoŵa, amakamba kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yesaya 6:8) Akristu ambili, monga amene analowa Sukulu ya Giliyadi, anasamukila kumaiko akutali. Ena anasamukila kumalo osoŵa m’dziko lao. Ena anaphunzila cinenelo catsopano kuti athandize mpingo kapena gulu la cinenelo cimeneco. Kucita zimenezi sikunali kopepuka, koma abale ndi alongo amenewa anadzipeleka ndi mtima wonse cifukwa cokonda Yehova ndi anthu. Iwo anasintha zinthu zina paumoyo wao ndi kugwilitsila nchito nthawi yao, mphamvu zao, ndi ndalama zao kuti akalalikile kumalo osoŵa. (Luka 14:28-30) Tikuyamikila kwambili abale ndi alongo amenewa cifukwa ca zimene amacita.
Si tonse amene tingapite kumalo osoŵa kapena kuphunzila cinenelo cina. Koma tonsefe tikhoza kukhala monga amishonale mumpingo wathu.
KHALANI MONGA AMISHONALE MUMPINGO WANU
M’nthawi ya atumwi, Akristu ambili anali kulalikila mwakhama ngakhale kuti ambili a io anali kukhalabe kumadela ao ndipo sanali amishonale. Paulo anauza Timoteyo kuti: “Gwila nchito ya mlaliki, ndipo ukwanilitse mbali zonse za utumiki wako.” (2 Timoteyo 4:5) Mau amenewa anagwila nchito kwa Akristu akale, ndipo amagwilanso nchito kwa ife masiku ano. Akristu onse ayenela kumvela lamulo limeneli mwa kulalikila Uthenga wa Ufumu ndi kupanga ophunzila. Ngakhale mumpingo wathu, muli zinthu zambili zimene tingacite potengela citsanzo ca amishonale.
Mwacitsanzo, amishonale akasamukila ku dziko lina, zinthu kumeneko zimakhala zosiyana ndi za kwao ndipo amafunika kucita khama kuti azoloŵele umoyo watsopano. Ngakhale kuti sitingapite kumalo osoŵa, tikhoza kupeza njila zatsopano zimene tingalalikilile. Mu 1940, abale athu analimbikitsidwa kuti azicita ulaliki wa mumseu tsiku limodzi mlungu uliwonse. Kodi munacitako ulaliki wa mumseu? Nanga kodi munalalikilapo ndi mashelufu a mawilo? Mfundo pamenepa ndi yakuti, tiziyesetsa kugwilitsila nchito njila zatsopano zolalikilila uthenga wabwino.
Ngati mumaona zinthu moyenela, mudzacita utumiki mwakhama ndiponso mofunitsitsa. Akristu amene amasamukila kumalo osoŵa kapena kuphunzila cinenelo catsopano, nthawi zambili amakhala ofalitsa aluso ndipo amathandiza kwambili kuti mpingo upite patsogolo. Mwacitsanzo, io amatsogolela panchito yolalikila. Nthawi zambili amishonale amatsogolela mpingo mpaka pamene abale akumeneko akhala oyenelela kutsogolela mpingo. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi ‘mukuyesetsa’ 1 Timoteyo 3:1.
kuti muyenelele kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu kuti muzitumikila abale ndi alongo mumpingo wanu?—KHALANI ‘OLIMBIKITSA’
Palinso njila zina zimene tingathandizile mpingo wathu. Tonse, acicepele ndi acikulile, abale ndi alongo, ‘tingalimbikitse’ Akristu anzathu amene afunikila thandizo.—Akolose 4:11.
Kuti tithandize abale ndi alongo athu, tiyenela kuwadziŵa bwino coyamba. Baibulo limatilangiza kuti “tiganizilane,” kutanthauza kuti pamene tasonkhana pamodzi ndi abale ndi alongo athu, tiziganizila zosoŵa zao. (Aheberi 10:24) Koma zimenezi sizitanthauza kuti tiyenela kulowelela nkhani za ena. Zitanthauza kuti tiziyesetsa kudziŵa zimene abale ndi alongo athu akukumana nazo ndi thandizo limene akufunikila. Iwo angafunikile kuwathandiza mwacindunji pa zinthu zina, kuwatonthoza, ndi kuwalimbikitsa ndi Malemba. N’zoona kuti nkhani zina zimafunika cisamalilo ca akulu ndi atumiki othandiza. (Agalatiya 6:1) Koma tonse tikhoza kuthandizako abale ndi alongo acikulile, kapena mabanja ena amene akukumana ndi mavuto.
M’bale wina, dzina lake Salvatore analandilako thandizo kucokela kwa abale. Atakumana ndi vuto la zacuma, anagulitsa bizinesi yake, nyumba yake, ndi zinthu zambili zimene banja lake linali nazo. Iye anali kuda nkhawa kuti asamalila bwanji banja lake. Banja lina mumpingo wao linazindikila kuti io afunikila thandizo. Banjalo linapatsa Salvatore ndalama ndi kuthandiza iye ndi mkazi wake kupeza nchito. Anali kuwacezela kaŵilikaŵili m’madzulo ndi kumamvetsela mavuto ao ndiponso kuwalimbikitsa. Iwo anakhala mabwenzi apamtima. Masiku ano, mabanja amenewo amasangalala kwambili akakumbukila mmene anathandizilana panthawi ya mavuto.
Akristu oona sanyalanyaza kuuzako ena zimene amakhulupilila. Tiyenela kutengela Yesu mwa kuthandiza anthu onse kudziŵa zinthu zabwino zimene Mulungu watilonjeza. Kaya tingakwanitse kusamukila ku malo osoŵa kapena ai, tonse tiyenela kucita zimene tingathe kuti tithandize ena mumpingo wathu. (Agalatiya 6:10) Ngati tithandiza ena, tidzakhala osangalala ndipo ‘tidzapitiliza kubala zipatso m’nchito iliyonse yabwino.’—Akolose 1:10; Machitidwe 20:35.