NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA November 2016

Magaziniyi ili na nkhani zophunzila m’mlungu wa December26, 2016 mpaka January29, 2017.

Mau Amene Anali Atanthauzo Kwambili

Ni mau ati amene Yesu anaseŵenzetsa amene anali atanthauzo kwambili?

‘Pitilizani Kulimbikitsana Tsiku na Tsiku’

N’cifukwa ciani cilimbikitso n’cofunika? Tingaphunzile ciani tikaona mmene Yehova, Yesu, na Paulo anali kulimbikitsila ena? Nanga mungapeleke bwanji cilimbikitso cogwila mtima?

Gulu Lake Ladongosolo Monga mwa Buku la Mau Ake

Yehova alibe wolingana naye pa nkhani ya dongosolo. Kodi nawonso olambila ake sayenela kukhala adongosolo?

Kodi Mumalemekeza Buku Lake la Yehova?

Anthu a Mulungu amakhala na zotsatilapo zabwino ngati ayesetsa kuseŵenzetsa uphungu wa m’Mau ake na kucilikiza gulu lake mokhulupilika.

“Nchitoyi Ndi Yaikulu”

Muli na mwayi wothandiza panchitoyi.

Kuitaniwa Kucoka mu Mdima

Kodi anthu a Mulungu anakhala bwanji mu mdima kuyambila m’ma 100 C.E. kupita mtsogolo? N’ciani cimene anacita kuti ayambe kuona kuwala kwa coonadi? Nanga zimenezo zinacitika liti?

Anamasuka Kucoka ku Cipembedzo Conama

Ni liti pamene anthu a Mulungu anamasukilatu mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu?

“Ofalitsa Ufumu ku Britain—Galamukani!”

Ciŵelengelo ca ofalitsa Ufumu sicinali kuwonjezeka ku Britain pa zaka 10. N’ciani cinathandiza kuti zinthu zisinthe?