Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Gulu Lake Ladongosolo Monga mwa Buku la Mau Ake

Gulu Lake Ladongosolo Monga mwa Buku la Mau Ake

“Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzelu. Anakhazikitsa kumwamba mozindikila.”—MIY. 3:19.

NYIMBO: 6, 24

1, 2. (a) Kodi anthu amaganiza bwanji pa mfundo yakuti Mulungu ali na gulu? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

KODI Mulungu ali na gulu lake? Anthu ena angakambe kuti: “Munthu safunikila kutsogoleledwa na gulu. Cofunika ni kukhala cabe pa unansi na Mulungu.” Kodi mfundo imeneyi ni ya zoona? Nanga zocitika zimaonetsa ciani?

2 M’nkhani ino, tidzakambilana umboni woonetsa kuti Yehova, Mulungu wamtendele, ni wadongosolo kupambana wina aliyense. Tidzakambilananso mmene tiyenela kucitila tikalandila malangizo a gulu la Yehova. (1 Akor. 14:33, 40) M’zaka 100 zoyambilila ndi masiku ano, Malemba athandiza gulu la Yehova la padziko lapansi kugwila nchito yofunika kwambili yolalikila uthenga wabwino. Popeza timatsatila malangizo a m’Baibo ndi a gulu, timalimbikitsa ukhondo, mtendele, na mgwilizano mumpingo.

YEHOVA ALIBE WOLINGANA NAYE PA NKHANI YA DONGOSOLO

3. N’ciani cimakukhutilitsani kuti Yehova ni wadongosolo kupambana wina aliyense?

3 Cilengedwe cimationetsa kuti palibe angapose Mulungu pa nkhani ya dongosolo. Baibo imakamba kuti: “Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzelu. Anakhazikitsa kumwamba mozindikila.” (Miy. 3:19) Ise timadziŵako “kambali kakang’ono cabe ka zocita zake,” ndipo “timangomva kunong’ona kwapansi-pansi kwa mau ake.” (Yobu 26:14) Ngakhale n’conco, zocepa zimene timadziŵako za mapulaneti, nyenyezi, na milalang’amba, zimatipangitsa kuvomeleza kuti zinthu zakuthambo zinalinganizidwa mwa dongosolo lodabwitsa. (Sal. 8:3, 4) Mwacitsanzo, milalang’amba ili ndi nyenyezi mamiliyoni ambili, koma zonsezo zimayenda mwadongosolo. Mapulaneti amayenda mozungulila dzuŵa monga kuti akutsatila bwino-bwino malamulo a pa mseu. Kukamba zoona, maumboni a zakuthambo ogometsa maganizo amenewa amatithandiza kudziŵa kuti Yehova, amene “anapanga kumwamba mwanzelu” na dziko lapansi, afunika kum’tamanda, kum’lambila, ndi kukhala okhulupilika kwa iye.—Sal. 136:1, 5-9.

4. N’cifukwa ninji asayansi akangiwa kuyankha mafunso ambili?

4 Asayansi atulukila zinthu zambili kuthambo komanso pa dziko lapansi, ndipo agwilitsila nchito zinthuzo kuti umoyo ukhale wabwinoko. Komabe, pali mafunso ambili amene asayansi sanapeze mayankho ake. Mwacitsanzo, akatswili a zakuthambo sangatiuze bwino-bwino mmene thambo linakhalilako, kapena cifukwa cake tili pa Dziko Lapansi, ndi zamoyo zina zambili-mbili. Komanso, anthu sangafotokoze cifukwa cake timalaka-laka kukhalabe na moyo osafa. (Mlal. 3: 11) N’cifukwa ciani pali mafunso ambili conco opanda mayankho? Cifukwa cimodzi n’cakuti asayansi na akatswili ena amalimbikitsa mfundo yakuti kulibe Mulungu, na kuti zinthu zonse zinakhalako mwa kusandulika. Koma m’buku la Mau ake, Yehova amapeleka mayankho pa mafunso amene avutitsa anthu maganizo kulikonse.

5. Kodi timadalila malamulo a cilengedwe m’njila ziti?

5 Ife tonse timadalila malamulo odalilika a cilengedwe amene Yehova ndiye anawakhazikitsa. A zamalaiti, mapulamba, mainjiniya, oyendetsa ndeke, madokota, na ena onse amadalila malamulo amenewo kuti agwile bwino nchito zawo. Mwacitsanzo, madokota amadalila dongosolo la cipangidwe ca thupi la munthu kuti agwile bwino nchito yawo. Conco, dokota savutika kucita kusakila pali mtima wa munthu wodwala. Ndipo tonse timalemekeza malamulo a cilengedwe. Mwacitsanzo, ngati munthu walumpha mumtengo na kuyesa kumbululuka monga mbalame, akhoza kudzibweletsela mavuto.

ZIMENE MULUNGU ANALINGANIZA

6. N’cifukwa ciani m’pake kuti alambili a Yehova ni anthu a dongosolo?

6 Zakuthambo zinalinganizidwa mwadongosolo lodabwitsa ngako. Ndithudi, izi zionetselatu kuti Yehova amafunanso alambili ake kucita zinthu mwadongosolo. Kuti zimenezi zitheke, Mulungu anatipatsa Baibo kuti izititsogolela. Conco, zotulukapo za umoyo wosadalila gulu la Mulungu na malangizo ake ni kupanda cimwemwe ndi mavuto ena ambili-mbili.

7. N’ciani cionetsa kuti Baibo ni buku ya dongodolo?

7 Baibo si buku longophatikiza pamodzi mabuku osagwilizana aciyuda ndi acikhiristu. Ni buku yolinganizika bwino, youzilidwa na Mulungu. Mabuku onse a m’Baibo ni ogwilizana bwino-bwino. Mwacitsanzo, kuyambila ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso, Baibo ili na mfundo yaikulu imodzi. Mfundoyo ni kukweza ucifumu wa Yehova na kukwanilitsika kwa colinga cake ca dziko lapansi. Zimenezi zidzatheka kupitila mwa Ufumu wake wolamulidwa na Khiristu, “mbeu” yolonjezedwa.—Ŵelengani Genesis 3: 15; Mateyu 6:10; Chivumbulutso 11:15.

8. Kodi pakati pa Aisiraeli panali dongosolo? Fotokozani.

8 Aisiraeli a m’nthawi yakale anali citsanzo cabwino ca dongosolo la Mulungu. Mwacitsanzo, panthawi ya Cilamulo ca Mose, kunali “akazi otumikila, amene anali kutumikila mwadongosolo pacipata ca cihema cokumanako.” (Eks. 38:8) Ngakhale kusamuka kwa msasa na cihema kunali kucitika mwa dongosolo lake. M’kupita kwa nthawi, Mfumu Davide analinganiza Alevi ndi ansembe m’magulu awo. (1 Mbiri 23:1-6; 24:1-3) Ndipo pamene Aisiraeli anamvela Yehova, anali kudalitsidwa. Anali kukhala mwa dongosolo, mwa mtendele, ndi mogwilizana.—Deut. 11:26, 27; 28:1-14.

9. N’ciani cionetsa kuti mpingo wacikhiristu woyambilila unali wadongosolo?

9 Mpingo wacikhiristu woyambilila nawonso unali wadongosolo. Ndipo unali kupindula ndi malangizo ocokela ku bungwe lolamulila. Amene anali kutumikila m’bungwelo anali atumwi poyamba. (Mac. 6:1-6) M’kupita kwa nthawi, abale enanso anaikidwa m’bungwe lolamulila. (Mac. 15:6) Amuna a m’bungwe lolamulila ndi owathandiza anali kupeleka uphungu na malangizo kwa Akhiristu kupitila m’makalata ouzilidwa. (1 Tim. 3:1-13; Tito 1:5-9) Kodi mipingo inapindula bwanji potsatila malangizo ocokela ku bungwe lolamulila?

10. Kodi panthawiyo, mipingo inapindula bwanji potsatila malamulo a bungwe lolamulila? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)

10 Ŵelengani Machitidwe 16:4, 5. Abale oyendela oimilako bungwe lolamulila, anali kufikitsa kumipingo “malamulo oyenela kuwatsatila, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula.” Ndipo mipingo potsatila malamulo amenewo, “inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciŵelengelo cinapitiliza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.” Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo cawo?

KODI MUMATSATILA MALANGIZO?

11. Kodi amuna apaudindo ayenela kucita ciani akalandila malangizo a gulu la Mulungu?

11 Masiku ano, kodi abale a m’Makomiti ya Nthambi, amadela, ndi akulu mumpingo, ayenela kucitanji akalandila malangizo a gulu la Mulungu? Buku la Mau a Yehova limalangiza ise tonse kumvela na kugonjela. (Deut. 30:16; Aheb. 13:7, 17) Mzimu wosuliza kapena kukana malangizo ulibe malo m’gulu la Mulungu. Ni wosokoneza cikondi, mtendele, na mgwilizano m’mipingo. Palibe Mkhiristu wokhulupilika amene angafune kukhala wopanda ulemu kapena wosakhulupilika monga Diotirefe. (Ŵelengani 3 Yohane 9, 10.) Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ine nimalimbikitsa abale na alongo kukhalabe okhulupilika kwa Yehova? Kodi nimalabadila mofulumila malangizo ocokela kwa otiyang’anila ndi kuwacilikiza?’

12. Kodi pakhala kusintha kwanji pa kaikidwe ka akulu na atumiki othandiza paudindo?

12 Ganizilani za kusintha kumene Bungwe Lolamulila linapanga posacedwa. Nkhani yakuti “Mafunso Ocekela kwa Aŵelengi” mu Nsanja ya Mlonda ya November 15, 2014, inafotokoza za kusintha kaikidwe ka akulu na atumiki othandiza paudindo. Nkhaniyo inakamba kuti bungwe lolamulila la m’nthawi ya atumwi, inapatsa mphamvu oyang’anila oyendela kuika abale paudindo. Potengela citsanzo cimeneco, oyang’anila madela akhala akuika akulu na atumiki othandiza paudindo kuyambila pa September 1, 2014. Wadela amayesetsa kudziŵa abale onse amene alingalilidwa paudindo, ndipo amaseŵenza nawo mu ulaliki ngati n’kotheka. Wadela amapendanso umoyo wauzimu wa banja la m’bale amene akulingalilidwa. (1 Tim. 3:4, 5) Bungwe la akulu pamodzi na wadela amapenda bwino-bwino ziyeneletso za m’Malemba za akulu ndi atumiki othandiza.—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; 1 Pet. 5:1-3.

13. Tingaonetse bwanji kuti timamvela malangizo a akulu?

13 Tifunika kutsatila malangizo a m’Baibo amene akulu amatipatsa. Abusa okhulupilika amenewa amatsogoleledwa na mau “olondola” opezeka m’buku ya Mulungu. (1 Tim. 6:3) Kumbukilani malangizo a Paulo okamba za anthu oyenda mosalongosoka mumpingo. Akhiristu ena ‘sanali kugwila nchito, koma anali kuloŵelela nkhani zimene sizinali kuwakhudza.’ Iwo anapitiliza kusuliza uphungu wa akulu. Kodi mpingo unafunikila kucita naye bwanji munthu wa conco? Paulo analangiza kuti: “Muikeni cizindikilo ndipo lekani kucitila naye zinthu limodzi.” Koma anapelekanso cenjezo lakuti sayenela kumuona monga mdani. (2 Ates. 3:11-15) Masiku ano, akulu angapeleke nkhani yocenjeza mpingo cifukwa ca munthu wina amene akupitiliza kucita zinthu zobweletsa citonzo pa mpingo, monga kukhala pacibwenzi na munthu amene si Mboni. (1 Akor. 7:39) Kodi mumamvela bwanji akulu akapeleka nkhani yacenjezo? Ngati mwadziŵa munthu wokhudzidwa ndi nkhaniyo, kodi mudzacita mwanzelu ndi kupewa kuyanjana ndi munthu ameneyo? Kucita zimenezi ni cikondi, ndipo kungathandize munthuyo kuleka njila yake yoipa. [1]

KHALANIBE OYELA, AMTENDELE, NDI OGWILIZANA

14. Tingathandizile bwanji kusunga ciyelo ca mpingo?

14 Timathandizila kusunga ciyelo ca mpingo ngati titsatila malangizo ocokela m’Mau a Mulungu. Onani mmene zinthu zinalili mumpingo wa ku Korinto. Paulo anadzipeleka ngako kulalikila mumzinda umenewo, ndipo anali kukonda “oyela” anzake. (1 Akor. 1:1, 2) Inali nkhani yomumvetsa cisoni powalembela za khalidwe loipa laciwelewele limene iwo anali kulekelela mu mpingo. Paulo analangiza akulu kuti apeleke munthu woipayo kwa Satana—kutanthauza kum’cotsa mumpingo. Kuti asunge ciyelo ca mpingo, akulu anafunika kucotsa “cofufumitsa” pakati pawo. (1 Akor. 5:1, 5-7, 12) Ngati akulu agamula kuti munthu wosalapa acotsedwe mumpingo, ife tiyenela kuciliciza cigamulo cimeneco. Kucita zimenezi kudzathandiza kuti mpingo ukhalebe woyela. Kungathandizenso wolakwayo kulapa na kupempha Yehova kuti amukhululukile.

15. Tingalimbikitse bwanji mtendele mumpingo?

15 Mu mpingo wa ku Korinto munalinso vuto lina. Abale ena anali kutengelana ku makhoti. Conco, Paulo anawafunsa kuti: “Bwanji osangolola kulakwilidwa?” (1 Akor. 6:1-8) Zimenezi zikucitikanso lelo lino. Nthawi zina, mtendele pakati pa abale umataika cifukwa bizinesi imene anapangana siinayende bwino kupangitsa wina kuluza ndalama zake, mwinanso cifukwa wina wadyela mnzake masuku pamutu. Pa zifukwa zimenezi abale ena atengela anzawo kukhoti. Koma Buku la Mau ake a Mulungu limatilangiza kuti ciliko bwino kuluza cinacake kusiyana n’kubweletsa citonzo pa dzina la Mulungu, kapena kusokoneza mtendele wa mpingo. [2] Njila yabwino yotsilizila mavuto aakulu ndi mikangano pakati pathu, nikutsatila uphungu wa Yesu. (Ŵelengani Mateyu 5:23, 24; 18:15-17.) Tikatelo, tidzalimbikitsa mgwilizano m’gulu lathu, limene ni banja la alambili a Yehova.

16. N’cifukwa ciani anthu a Mulungu afunika kukhala ogwilizana?

16 Buku la Mau ake Yehova limationetsa cifukwa cake anthu ake afunika kukhala ogwilizana. Wamasalimo anaimba kuti: “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!” (Sal. 133:1) Pamene Aisiraeli anali omvela Yehova, anali kukhala adongosolo ndi ogwilizana. Pokambilatu za anthu ake a m’tsogolo, Mulungu anati: “Ndidzawabweletsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola.” (Mika 2:12) Ndiponso, Yehova anakambilatu mwa mneneli Zefaniya kuti: “Ndidzapatsa mitundu ya anthu cilankhulo coyela [ca coonadi ca m’Malemba] kuti onse aziitanila pa dzina la Yehova ndi kumutumikila mogwilizana.” (Zef. 3:9) Ndife oyamikila cotani nanga, kukhala na mwayi wolambila Yehova mogwilizana!

Akulu amayesetsa kupeleka thandizo lauzimu kwa amene atenga njila yolakwika (Onani ndime 17)

17. Kuti mpingo ukhale woyela ndi wogwilizana, kodi akulu afunika kucita motani?

17 Kuti mpingo upitilize kukhala woyela ndi wogwilizana, akulu afunika kusamalila nkhani zaciweluzo mwamsanga komanso mwacikondi. Paulo anali kudziŵa kuti cikondi ca Mulungu siciyang’ana nkhope, komanso Iye salekelela zolakwa. (Miy. 15:3) Ndiye cifukwa cake Paulo sanadodome kulembela Akorinto kalata yoyamba. Inali kalata ya uphungu wamphamvu koma wacikondi. Kalata yaciŵili, imene analemba patapita miyezi ingapo, ionetsa kuti kuwongokela kunalipo, kutanthauza kuti akulu anatsatila malangizo a Paulo. Ngati Mkhiristu akuloŵela njila yolakwika popanda iye kuzindikila, amuna ofikapo ayenela kum’thandiza ndi mzimu wofatsa.—Agal. 6:1.

18. (a) Kodi uphungu wa m’Mau a Mulungu unathandiza bwanji Akhiristu akale? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 N’zoonekelatu kuti uphungu wa m’Buku lake la Mulungu unathandiza Akhiristu ku Korinto ndi kwina kusunga ciyelo, mtendele, ndi mgwilizano m’mipingo yawo. (1 Akor. 1:10; Aef. 4:11-13; 1 Pet. 3:8) Izi zinathandiza abale ndi alongo amenewo kucita zambili m’nchito yolalikila. N’cifukwa cake Paulo anakamba kuti uthenga wabwino “unalalikidwa m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Lelo linonso, uthenga wabwino wokamba za cifunilo ca Mulungu ukulalikidwa pa dziko lonse. Izi zatheka cifukwa ca khama la anthu a m’gulu la Mulungu logwilizana. M’nkhani yotsatila, tidzaona maumboni ena oonetsa kuti anthu a Mulungu amenewa amalemekeza kwambili Baibo. Mtima wawo uli pa kulemekeza Yehova, Ambuye Wamkulukulu.—Sal. 71:15, 16.

^ [1] (palagilafu 13) Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mas. 134-136.

^ [2] (palagilafu 15) Kuti mudziŵe zocita ngati Mkhiristu aona kuti m’pofunika kupeleka Mkhiristu mnzake kukhoti, onani buku lakuti Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu,” tsa. 223.