Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuitaniwa Kucoka mu Mdima

Kuitaniwa Kucoka mu Mdima

“[Yehova] anakuitanani kucoka mu mdima kuloŵa m’kuwala kwake kodabwitsa.”—1 PET. 2:9.

NYIMBO: 95, 74

1. Fotokozani zimene zinacitika pa ciwonongeko ca Yerusalemu.

MU 607 B.C.E., asilikali acibabulo motsogolelewa na Mfumu Nebukadinezara Waciŵili, anawononga mzinda wa Yerusalemu. Pokamba za anthu ambili amene anaphedwa, Baibo imati: “[Mfumu Nebukadinezara] inapha anyamata awo ndi lupanga m’nyumba yopatulika. Sinacitile cisoni mnyamata kapena namwali, wacikulile kapena nkhalamba yothelatu. . . . Inatentha nyumba ya Mulungu woona ndi kugwetsa mpanda wa Yerusalemu. Ababulo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambili za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwino-zabwino, mpaka zonse zinawonongedwa.”—2 Mbiri 36:17, 19.

2. Ni cenjezo lanji limene Yehova anapeleka pa za ciwonongeko ca Yerusalemu? Nanga n’ciani cinali kudzacitikila Ayuda?

2 Ciwonongeko ca Yerusalemu sicinali codabwitsa kwa anthu okhala mmenemo. Kwa zaka zambili, aneneli a Mulungu anacenjeza Ayuda kuti ngati apitiliza kusamvela malamulo a Mulungu, adzapelekedwa m’manja mwa Ababulo. Ambili anali kudzaphedwa ndi lupanga, ndipo aliyense wopulumuka anali kudzatengeledwa ku ukapolo ku Babulo, nukakhala kumeneko umoyo wake wonse. (Yer. 15:2) Kodi akapolo anali kukhala umoyo wabwanji kumeneko? Kodi Akhiristu pa nthawi ina anakhalapo mu ukapolo molingana na Ayuda ku Babulo?

UMOYO WAUKAPOLO

3. Kodi ukapolo wa ku Babulo unasiyana bwanji na ukapolo wa Aisiraeli ku Iguputo?

3 Zimene aneneli analosela zinacitikadi. Kupitila mwa Yeremiya, Yehova anauzilatu Ayuda amene anali kukatengedwa ukapolo kuti anafunika kukavomeleza umoyo watsopano umenewo. Iye anati: “Mangani nyumba [ku Babulo] ndi kukhalamo. Limani minda ndi kudya zipatso zake. Komanso mzinda umene ndakucititsani kukhalamo monga akapolo, muziufunila mtendele. Muziupemphelela kwa Yehova, pakuti mzindawo ukakhala pa mtendele inunso mudzakhala pa mtendele.” (Yer. 29:5, 7) Amene anasunga mau a Mulungu anakhala umoyo wabwinoko ku Babulo. Kumeneko anawapatsa kaufulu kocitako zinthu zaumwini, ndi kuyenda kulikonse kumene anafuna m’dzikomo. M’nthawi zakale, mzinda wa Babulo unali likulu la zamalonda. Mipukutu yofukulidwa m’matongwe ionetsa kuti Ayuda ambili anaphunzila zamalonda kumeneko, ndipo ena anakhala akatswili a zopanga-panga. Ayuda ena anafika polemela. Ukapolo wa ku Babulo unali wosiyana kothelatu na ukapolo wa Aisiraeli ku Iguputo zaka zambili kumbuyoko.—Ŵelengani Ekisodo 2:23-25.

4. Kuwonjezela pa Aisiraeli opanduka, n’ndani ena anatengeledwa ku ukapolo ku Babulo? Nanga n’cifukwa ciani zinali zosatheka kutsatila malamulo onse a m’Cilamulo?

4 Ngakhale kuti kuukapolo kuja Ayuda anali kupeza zosoŵa zawo zakuthupi, nanga bwanji zinthu zauzimu? Kacisi wa Yehova na guwa lake la nsembe zinali zitawonongedwa, ndipo ansembe sanali kugwila nchito yawo mwadongosolo. Pakati pa Ayuda otengedwa ukapolo panali atumiki a Mulungu okhulupilika. Iwo anavutitsidwa pamodzi na mtundu wocimwawo. Ngakhale n’conco, atumikiwo anayesetsa kumvela Cilamulo ca Mulungu. Mwacitsanzo Danieli. Iye ndi anzake atatu—Sadirake, Mesake ndi Abedinego—anakana kudya zakudya zoletsedwa kwa Ayuda. Monga tidziŵila, Danieli anapitiliza kukamba na Mulungu m’pemphelo nthawi zonse. (Dan. 1:8; 6:10) Komabe, pansi pa ulamulilo wacikunja, zinali zosatheka kwa Myuda woopa Mulungu kutsatila zonse zolembewa m’Cilamulo.

5. N’lonjezo liti limene Yehova anapatsa anthu ake? Nanga n’cifukwa ciani lonjezoli linali locititsa cidwi?

5 Kodi zinali zotheka kuti Aisiraeli adzamasukanso ndi kukalambila Mulungu mwaufulu? Panthawiyo zinaoneka zosatheka cifukwa Ababulo sanali kumasula akapolo awo. Koma imeneyo siinali nkhani kwa Yehova Mulungu. Iye anali atalonjeza kuti anthu ake adzamasulidwa, ndipo zinacitikadi. Malonjezo a Mulungu salephela kukwanilitsika.—Yes. 55:11.

PALI KULINGANA KWANJI NA MASIKU ANO?

6, 7. N’cifukwa ciani n’koyenela kusintha kamvedwe kathu ka ukapolo kwa Babulo wamakono?

6 Kodi Akhiristu akumanapo na zilizonse zolingana na ukapolo wa Ayuda ku Babulo? Kwa zaka zambili, magazini ino yafotokoza kuti atumiki a Mulungu amakono analoŵa mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu mu 1918, na kuti anamasulidwa mu ukapolowo mu 1919. Komabe, pa zifukwa zimene tifotokoze m’nkhani ino na yotsatila, tidzaona kuti kwakhala kofunika kuipendanso nkhaniyi.

7 Ganizilani izi: Babulo Wamkulu ni ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama. Kuti anthu a Mulungu akhale akapolo a Babulo Wamkulu mu 1918, cipembedzo conama cinafunikila kuwatengela mu ukapolo mwa njila inayake panthawiyo. Komabe, zocitika zionetsa kuti mkati mwa zaka zambili zokafikitsa ku nkhondo yoyamba ya dziko lonse, atumiki a Mulungu odzozedwa anali kumasuka mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu, osati kuloŵamo yayi. N’zoona kuti odzozedwa anazunzidwa panthawi ya nkhondo yoyamba. Koma amene anali kuwasautsa anali olamulila a dziko, osati Babulo Wamkulu. Conco, zioneka kuti anthu a Yehova sanaloŵe mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu mu 1918.

KODI UKAPOLO WA M’BABULO WAMKULU UNAYAMBA LITI?

8. Fotokozani mmene ciphunzitso conama cinayambila kuloŵa m’Cikhiristu coona. (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)

8 Pa Pentekosite mu 33 C.E., Ayuda ambili pamodzi na ŵanthu otembenukila ku Ciyuda anadzozedwa na mzimu woyela. Akhiristu atsopano onsewo anakhala “fuko losankhidwa mwapadela, ansembe acifumu, mtundu woyela, anthu odzakhala cuma capadela.” (Ŵelengani 1 Petulo 2:9, 10.) Panthawi yonse imene atumwi analipo na moyo, iwo anali kusamalila bwino mpingo wa Mulungu. Koma maka-maka pamene atumwi onse anafa, anthu ena anayamba kuphunzitsa “zinthu zopotoka” kuti “apatutse ophunzila aziwatsatila.” (Mac. 20:30; 2 Ates. 2:6-8) Ambili anali amuna a maudindo mumpingo. Anali kutumikila monga oyang’anila, koma m’kupita kwanthawi, anakhala “mabishopu.” Ici ndiye cinali ciyambi ca kagulu ka akulu-akulu a chechi, ngakhale kuti Yesu anali atauza otsatila ake kuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mat. 23:8) Amuna a maudindo mumpingo anatengeka kwambili na ziphunzitso za Aristotle ndi Plato. Pang’ono ndi pang’ono analoŵetsa ziphunzitso zabodzazo mumpingo m’malo mwa coonadi ca m’Mau a Mulungu.

9. Kodi Cikhiristu campatuko cinacilikizidwa bwanji na Ufumu wa Roma? Nanga panakhala zotsatilapo zabwanji?

9 Mu 313 C.E., Mfumu ya Roma yacikunja dzina lake Constantine, inavomeleza mwalamulo Cikhiristu ca mpatuko kukhala Chechi yovomelezeka. Kuyambila nthawi imeneyo, Chechi na Boma zinayamba kuseŵenzela pamodzi. Mwacitsanzo, Msonkhano wa ku Nicaea utatha, Constantine, amene analipo pa msonkhanowo, anapitikitsa wansembe wina dzina lake Arius kuti acoke m’dziko lake cifukwa cokana kuvomeleza kuti Yesu ni Mulungu. M’kupita kwa nthawi, mu ulamulilo wa Mfumu Theodosius Woyamba (379 mpaka 395 C.E.), Chechi ya Akatolika (Cikhiristu codetsedwa), inakhala cipembedzo covomelezedwa ndi Ufumu wa Roma. Akatswili a mbili yakale amati dziko la Roma “linavekedwa Cikhiristu” panthawi ya ulamulilo wa Theodosius. Zoona n’zakuti nthawi imeneyo, Cikhiristu campatuko cinagwilizana na zipembedzo zacikunja za mu Ufumu wa Roma. Zipembedzo zonsezo zinapanga Babulo Wamkulu. Komabe, panali Akhiristu odzozedwa ocepa amene anali monga tiligu. Iwo anali kuyesetsa kulambila Mulungu m’njila yoyenela, ngakhale kuti anali kupondelezedwa. (Ŵelengani Mateyu 13:24, 25, 37-39.) Iwo analidi mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu.

10. N’cifukwa ciani anthu oona mtima anayamba kukana ziphunzitso za cipembedzo m’zaka ma 100 angapo oyambilila?

10 M’zaka ma 100 angapo oyambilila, anthu ambili anali nayo Baibo m’Cigiriki kapena m’Cilatini. Conco, anali kuyelekezela kuti aone ngati ziphunzitso za chechi zinali zogwilizana ndi Mau a Mulungu. Poona kuti ziphunzitso za chechi zinali zosagwilizana ndi malemba, iwo anayamba kuzikana. Koma amene anali kulankhula zimenezi poyela, anali kupatsidwa cilango coopsa, ngakhale kuphedwa kumene.

11. Kodi zinacitika bwanji kuti akulu-akulu a chechi akhale na mphamvu zonse pa Baibo?

11 M’kupita kwanthawi, anthu ambili sanali kukambanso Cigiriki na Cilatini. Koma akulu-akulu a chechi anali kuletselatu kumasulila Mau a Mulungu m’zinenelo zimene anthu analukamba. Cifukwa ca ici, akulu-akulu a chechi okha, na anthu ŵena ophunzila ndiwo anali kukwanitsa kuŵelenga Baibo. Komanso, si atsogoleli acipembedzo onse amene analudziŵa kuŵelenga na kulemba. Aliyense wotsutsa ziphunzitso za chechi anali kulangiwa moopsa. Mwa ici, atumiki a Mulungu odzozedwa anali kukumana mwakabisila m’tumagulu kukakhala kotheka. Monga mmene zinalili ku Babulo wakale, “ansembe acifumu” odzozedwa sanali kutumikila monga mwa makonzedwe ake. Inde, Babulo Wamkulu anali ataŵafyanthilatu anthu mu ukapolo.

KUWALA KUYAMBA KUONEKELA

12, 13. N’zifukwa ziŵili ziti zinapangitsa Babulo Wamkulu kuyamba kucepa mphamvu pa anthu? Fotokozani.

12 Kodi zinali zotheka kuti Akhiristu oona akamasuke ndi kulambila Mulungu mwaufulu? Inde! Capakati pa zaka za m’ma 1400, kuwala kwauzimu kunayamba kuonekela pang’ono-pang’ono pa zifukwa ziŵili izi: Coyamba cinali kupangidwa kwa mashini opulinthila mabuku. Mashini opulinthila akalibe kufika ku America, anthu anali kucitolemba pamanja makope a Baibo. Ndipo inalidi nchito yoŵaŵa! Ndiye cifukwa cake Baibo inali yosoŵa ngati nyanga yagalu, titelo kukamba kwake, ndipo mtengo wake unali woboola m’thumba. Akuti katswili panchitoyo zinali kum’tengela miyezi 10 kukopa Baibo imodzi cabe. Ndiponso, zolembapo zake za pepa ya gumbwa kapena zacikumba zinali zodula maningi. Koma kuseŵenzetsa mashini yopulinthila na mapepa, munthu anali kukwanitsa kupulintha mapeji 1,300 tsiku limodzi cabe.

Zimene zinayambitsa kucepako mphamvu kwa Babulu Wamkulu pa akapolo ake ni kubwela kwa mashini opulinthila mabuku, ndi anthu olimba mtima omasulila Baibo (Onani palagilafu 12 na 13)

13 Cifukwa caciŵili n’cakuti kuciyambi kwa zaka za m’ma 1500, amuna ena analimba mtima ndi kumasulila Mau a Mulungu m’zinenelo zimene anthu analukamba. Ambili pogwila nchitoyi anangosaina kuti cicitike cicitike! Poona zimenezi, akulu-akulu a chechi anada nkhawa kwambili. Anadziŵa kuti Baibo ikhoza kukhala cida coopsa m’manja mwa munthu woopa Mulungu. Ndipo n’zimene zinacitikadi. Anthu atayamba kuŵelenga Baibo anayamba kufunsa kuti: ‘Kodi pegatoli yowochelako mizimu ya anthu ocimwa inalembewa pati? Nanga zolipila misa ya pamalilo, kapena kulipila misa ya apapa kapena abusa zinalembewa pati?’ Kwa akulu-akulu a chechi, cimeneci cinali cipanduko. Anati anthu angathe bwanji mantha na kuyamba kukaikila zimene akuwaphunzitsa! Anati adzaciona! Amuna na akazi anapatsidwa milandu yopandukila chechi na ziphunzitso zake, imene cilango cake cinali kuphedwa. Zina mwa ziphunzitso zimenezo zinali zocokela kwa anthu akunja aja, Aristotle na Plato, amene anakhalako Yesu Khiristu asanabadwe. Chechi ndiye inali kugamula cilango ca kunyongewa, Boma ndiye inali kunyonga anthu. Colinga cinali cakuti anthu azicita kuopelatu kuŵelenga Baibo na kukaikila ziphunzitso za chechi. Zimenezi zinaseŵenza kwa anthu ambili. Koma panali anthu ena ocepa amene anati cicitike cicitike, sadzamuyopa Babulo Wamkulu! Popeza anali atalaŵa Mau a mulungu na kumvela kuwama kwake, mtima unali dyoko-dyoko kufuna kuphunzila zambili! Apa lomba kumasuka ku cipembedzo conama kunali pafupi.

14. (a) Kodi ca kumapeto kwa ma 1800, panacitika ciani cinathandiza anthu ena kuyamba kumvetsa coonadi? (b) Kodi M’bale Russell anayamba bwanji kufuna-funa coonadi?

14 Anthu ambili amene anali na njala ya coonadi ca m’Baibo anathaŵila ku maiko ena kumene chechi siinali na mphamvu zopitilila. Iwo anafuna kuti azikaŵelenga Mau a Mulungu, kuwaphunzila, na kuwakambilana popanda kukakamizidwa zokhulupilila. Limodzi la maiko amenewo linali America. Kumeneko, Charles Taze Russell na anzake oŵelengeka anayamba kuphunzila Baibo mwakhama. Izi zinacitika mu 1870. Poyamba, colinga ca M’bale Russell cinali kudziŵa machechi amene anali kuphunzitsa coonadi. Anali atayelekezela mosamala ziphunzitso za machechi ambili, kuphatikizapo zipembedzo zina zosakhala za Cikhiristu, kuti aone ngati zinali kugwilizana na zimene Baibo imaphunzitsa. Posakhalitsa, anazindikila kuti panalibe cipembedzo olo cimodzi cimene cinali kutsatila Mau onse a Mulungu. Panthawi ina, Russell anakakumana na akulu-akulu a machechi, poganiza kuti adzavomeleza coonadi cimene iye na anzake anali atacipeza m’Baibo, kuti nawonso akaphunzitseko anthu awo. Koma azibusawo sanagwilizane nazo. Ophunzila Baibo anaiona mfundo yake, yakuti sangakhale pa mgwilizano na ŵanthu okangamila ku cipembedzo conama.—Ŵelengani 2 Akorinto 6:14.

15. (a) Kodi Akhiristu analoŵa liti mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu? (b) Nanga nkhani yotsatila idzayankha mafunso ofunika ati?

15 Pofika pano, taona kuti Akhiristu oona analoŵa mu ukapolo m’Babulo Wamkulu pamene atumwi onse anafa. Komabe, pakubuka mafunso angapo: Kodi pali maumboni ena ati oonetsa kuti m’zaka zambili zokafikitsa ku 1914, odzozedwa anali kumasuka mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu? Kodi n’zoona kuti Yehova anali wokhumudwa na atumiki ake cifukwa cobwelela m’mbuyo panchito yolalikila, mkati mwa nkhondo yoyamba ya dziko lonse? Ndipo panthawi ya nkhondoyo, kodi abale athu ena anataya cikhulupililo cawo ndi kutengako mbali m’za ndale, cakuti Yehova anakhumudwa nawo? Lothela, ngati Akhiristu analoŵa mu ukapolo ku cipembedzo conama m’zaka za m’ma 100 C.E. kupita m’tsogolo, kodi anamasukamo liti? Aya ni mafunso ofunika ngako, koma adzayankhiwa m’nkhani yotsatila.