Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Pitilizani Kulimbikitsana Tsiku na Tsiku’

‘Pitilizani Kulimbikitsana Tsiku na Tsiku’

“Ngati muli ndi mau alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.”—MAC. 13:15.

NYIMBO: 121, 45

1, 2. N’cifukwa ciani cilimbikitso n’cofunika?

CRISTINA, mtsikana wa zaka 18 [1] anati: “Makolo anga sanilimbikitsako olo pang’ono. Kwawo ni kunitsutsa na kuninyoza nthawi zonse. Ndipo cimaniŵaŵa ngako. Amakamba kuti, ‘Sudzakula, ndiwe cibeketebenzi, cidumbo iwe.’ Nimalila nthawi zambili, ndipo nimangoleka kukamba nawo. Nimadziona kuti ndine wacabe-cabe.” Kukamba zoona, ngati anthufe sitilimbikitsana umoyo umakhala wovuta.

2 Cilimbikitso cimathandiza munthu kupitiliza kucita zabwino. Rubén anati: “Zaka zambili nakhala nikuvutika na maganizo odziona kukhala wosafunika. Koma tsiku lina pamene n’nali mu ulaliki na mkulu wina, anaona kuti sin’nali wokondwela. Pamene n’namuuza mmene n’nali kumvelela anamvetsela mwacifundo. Ndiyeno ananikumbutsa zinthu zabwino zimene n’nali kucita. Ananikumbutsanso mau a Yesu akuti, aliyense wa ife ni wofunika kuposa mbalame zambili zampheta. Nthawi zonse nikakumbukila lembali, nimalimbikitsika kwambili. Mau a mkuluyo ananithandiza maningi.”—Mat. 10:31.

3. (a) Kodi mtumwi Paulo anati ciani za kulimbikitsana? (b) Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Ndiye cifukwa cake Baibo imagogomeza kulimbikitsana nthawi zonse. Mtumwi Paulo analembela Akhiristu Aciheberi kuti: “Cenjelani abale, kuti pakati panu, wina asacoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda cikhulupililo. M’malomwake, pitilizani kudandaulilana [“kulimbikitsana,” nwt] tsiku ndi tsiku, . . . kuopela kuti cinyengo camphamvu ca ucimo cingaumitse mtima wa wina wa inu.” (Aheb. 3:12, 13) Mumadziŵa kuti cilangizo cimeneci n’cofunika kwambili maka-maka mukakumbukila pamene munthu wina anakuuzani mau amene anakulimbikitsani kwambili. Conco, tiyeni tikambilane mafunso aya: N’cifukwa ciani cilimbikitso n’cofunika? Tingaphunzilenji tikaona mmene Yehova, Yesu na Paulo anali kulimbikitsila ena? Nanga tingapeleke bwanji cilimbikitso cogwila mtima?

TONSE TIMAFUNIKA CILIMBIKITSO

4. N’ndani amafunikila cilimbikitso? Nanga n’cifukwa ciani n’cosoŵa masiku ano?

4 Tonse timafunikila cilimbikitso, maka-maka pamene tikukula. Mphunzitsi wina dzina lake Timothy Evans anati: “Ana amafunika kulimbikitsiwa monga mmene zomela zimafunikila madzi. Mwana akalimbikitsidwa, amadziona kukhala wofunika.” Koma m’dzikoli anthu ni odzikonda, sakondanso abululu awo, ndipo kulimbitsana n’kosoŵa. (2 Tim. 3:1-5) Makolo ena sayamikila ana awo cifukwa makolo awo sanali kuwalimbikitsa. Mabwana ambili sayamikila anchito awo. Conco, anchito ambili amadandaula kuti amasoŵa owalimbikitsako.

5. Kodi tingawalimbilitse bwanji ena?

5 Nthawi zambili kulimbikitsa ena kumaloŵetsamo kuwayamikila pa zabwino zimene acita. Tingalimbikitsenso ena mwa kuwayamikila cifukwa ca makhalidwe awo abwino, kapena kukamba mau ‘olimbikitsa kwa a mtima wacisoni.’ (1 Ates. 5:14) Pamene titumikila pamodzi na abale ndi alongo athu, timakhala na mipata yambili yowalimbikitsa. (Ŵelengani Mlaliki 4:9, 10.) Kodi timatengela mwayi mipata yabwino imeneyo kuuza ena cifukwa cake timawakonda na kuwayamikila? Musanayankhe funso imeneyi, ganizilani mwambi uwu umene umati: “Mau onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili.”—Miy. 15:23.

6. N’cifukwa ciani Mdyelekezi amafuna kutilefula? Pelekani citsanzo.

6 Satana Mdyelekezi amafuna kutilefula cifukwa adziŵa kuti tikalefuka tidzafooka kuuzimu. Miyambo 24:10 imati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.” Satana ananeneza Yobu, munthu wolungama uja, na kumubweletsela mavuto aakulu kuti amufooketse. Koma ciwembu cake cinalephela. (Yobu 2:3; 22:3; 27:5) Ifenso tingalimbane na nchito za Mdyelekezi mwa kulimbikitsa a m’banja lathu ndi Akhiristu anzathu. Tikamacita zimenezi, nyumba zathu ndi Nyumba za Ufumu zidzakhala malo acimwemwe na citetezo.

AMENE TIYENELA KUTENGELAKO CITSANZO

7, 8. (a) Ni zitsanzo ziti za m’Baibo zimene zionetsa kuti Yehova amafuna kuti tizilimbikitsana? (b) Kodi makolo angatengele bwanji citsanzo ca Yehova? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)

7 Yehova. Wamasalimo anaimba kuti: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Sal. 34:18) Panthawi ina, mneneli wokhulupilika Yeremiya anafooka ndi kucita mantha. Koma Yehova anam’thandiza kukhala na cidalilo. (Yer. 1:6-10) Ganizani cabe mmene mneneli wacikalambile Danieli anamvelela pamene Mulungu anatuma mngelo kukam’limbikitsa. Mngeloyo anacha Danieli kuti “munthu wokondedwa kwambili.” (Dan. 10:8, 11, 18, 19) Nanga imwe, simungalimbikitseko ofalitsa, apainiya, na okalamba mumpingo mwanu amene mphamvu zawo zikucepela-cepela?

8 Mulungu sanaganize kuti, ‘Popeza Yesu n’naseŵenza naye kwa zaka zambili-mbili kuno kumwamba, palibe cifukwa comuyamikilila na kumulimbikitsa pamene ali pa dziko lapansi, ayi.’ M’malomwake, kaŵili konse Yesu anamvela Atate wake akukamba kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.” (Mat. 3:17; 17:5) Apa Mulungu anayamikila Yesu na kumtsimikizila kuti anali kucita zabwino. Ndipo Yesu analimbikitsika ngako atamvela mau amenewa kaŵili konse—kuciyambi kwa utumiki wake na pamene anali pafupi kuphedwa. Yehova anatumanso mngelo kukalimbikitsa Yesu atavutika maganizo usiku wakuti mawa aphedwa. (Luka 22:43) Makolo, tengelani citsanzo ca Yehova mwa kulimbikitsa ana anu nthawi zonse, na kuwayamikila akacita zabwino. Ndipo pamene ayang’anizana na mayeselo kusukulu, acilikizeni kwambili.

9. Tiphunzilapo ciani tikaona mmene Yesu anacitila ndi atumwi ake?

9 Yesu. Usiku umene Yesu anayambitsa Cikumbutso, anaona kuti atumwi ake anali atayamba kudzikuza. Conco, modzicepetsa Yesu anasambitsa mapazi awo. Ngakhale n’conco, iwo anali kukanganabe zakuti n’ndani anali wamkulu pakati pawo. Ndipo Petulo anadzithemba kuti sangasiye Yesu. (Luka 22:24, 33, 34) Komabe, Yesu anawayamikila atumwi ake okhulupilika cifukwa cosamusiya panthawi ya mayeselo. Iye anakambilatu kuti iwo adzacita nchito zambili kuposa iye. Kuwonjezela apo, anawatsimikizila kuti Mulungu amawakonda. (Luka 22:28; Yoh. 14:12; 16:27) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi nimatengelako citsanzo ca Yesu mwa kuyamikila ana anga ndi ena pa zabwino zimene amacita, m’malo mongoyang’ana pa zimene amalakwitsa?’

10, 11. Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji kuti kulimbikitsa ena n’kofunika?

10 Mtumwi Paulo. Paulo anaŵayamikila kwambili Akhiristu anzake m’makalata amene anawalembela. Ena a iwo anagwila nawo nchito yolalikila kwa zaka zambili, ndipo mosapeneka, iye anali kudziŵa zofooka zawo. Koma anakamba zinthu zabwino zimene iwo anacita. Mwacitsanzo, Paulo anacha Timoteyo kuti “mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupilika mwa Ambuye,” amene anali kudzasamalila zosoŵa za Akhiristu na mtima wonse. (1 Akor. 4:17; Afil. 2:19, 20) Ndipo polembela mpingo wa ku Korinto, mtumwiyu anayamikila Tito kuti: “Ndi mnzanga komanso ndikugwila naye nchito limodzi pothandiza inuyo.” (2 Akor. 8:23) Timoteyo ndi Tito ayenela kuti analimbikitsika kwambili atamvela mmene Paulo anali kuwaonela.

11 Paulo na Baranaba anaika miyoyo yawo paciswe mwa kubwelelanso kumene anamenyedwa. Mwacitsanzo, iwo anabwelela ku Lusitara kuti akalimbikitse ophunzila atsopano m’cikhulupililo, olo kuti anali atakumanapo ndi anthu aciwawa kumeneko. (Mac. 14:19-22) Nakonso ku Efeso, Paulo anakumana ndi gulu la anthu okwiya. Machitidwe 20:1, 2 imati: ‘Cipolowe . . . citatha, Paulo anaitanitsa ophunzila. Atawalimbikitsa na kulailana nawo, ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya. Iye anayenda-yenda m’madela akumeneko ndi kulimbikitsa ophunzila ndi mawu ambili, kenako anafika ku Girisi.’ Zoonadi, kulimbikitsa ena kunali cinthu cofunika kwambili kwa Paulo.

KULIMBIKITSANA MASIKU ANO

12. Kodi misonkhano yathu imathandiza bwanji kuti tizilimbikitsana wina na mnzake?

12 Atate wathu wakumwamba anaika makonzedwe akuti tizisonkhana nthawi zonse. Colinga n’cakuti tizilimbikitsana wina na mnzake. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Monga zinalili kwa otsatila a Yesu akale, timasonkhana pamodzi kuti tiphunzile na kulimbikitsana. (1 Akor. 14:31) Cristina, amene tamutomola kuciyambi kwa nkhani ino anati: “Cimene nimakonda kwambili ku misonkhano ni cikondi na cilimbikitso cimene nimalandila kumeneko. Nthawi zina nimafika ku Nyumba ya Ufumu ndili wosakondwa. Koma alongo amanikumbatila na kuniuza kuti naoneka bwino. Amaniuza kuti amanikonda ndi kuti amayamikila mmene napitila patsogolo kuuzimu. Mau awo amanilimbikitsa kwambili!” Kukamba zoona, zimatsitsimula ngati aliyense wa ife acitako mbali yake kuti ‘tizilimbikitsana.’—Aroma 1:11, 12.

13. N’cifukwa ciani ngakhale amkhalakale m’coonadi amafunikila cilimbikitso?

13 Ngakhale atumiki a Mulungu aciyambakale amafunikila cilimbikitso. Ganizilani za Yoswa. Olo kuti anali atatumikila Mulungu mokhulupilika zaka zambili, Yehova anauza Mose kuti amulimbikitse. Anati: “Uike Yoswa kukhala mtsogoleli ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, cifukwa ndiye adzawolotsa anthuwa ndi kuwacititsa kulandila dziko limene ulionelo kukhala colowa cawo.” (Deut. 3:27, 28) Apa Yoswa anali kudzapatsidwa udindo waukulu wotsogolela Aisiraeli ku Dziko Lolonjezedwa. Patsogolo pake panalinso zolefula zambili, komanso kugonjetsedwa pankhondo. (Yos. 7:1-9) Inde, mpake kuti Yoswa anafunikila cilimbikitso. Conco, ifenso tiyeni tizilimbikitsa akulu, kuphatikizapo amadela, cifukwa cogwila nchito molimbika kuti asamalile nkhosa za Mulungu. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:12, 13.) Wadela wina anati: “Nthawi zina abale na alongo amatilembela makalata otiyamikila. Amakamba mmene asangalalila pa kucezetsa kwathu. Timawasunga makalata amenewa. Tikafunika cilimbikitso, timawatenga n’kumaŵelenga. Amatilimbikitsa ngako.”

Ana athu amakula bwino ngati timawalimbikitsa (Onani palagilafu 14)

14. N’ciani cionetsa kuti ciyamikilo na cilimbikitso zimathandiza popeleka uphungu?

14 Akulu acikhiristu na makolo amaona kuti kuyamikila na kulimbikitsa munthu pomupatsa uphungu wa m’Baibo kumam’thandiza kuuseŵenzetsa. Pamene Paulo anayamikila Akorinto cifukwa cogwilitsila nchito uphungu umene anawapatsa, analimbikitsidwa kupitiliza kucita zabwino. (2 Akor. 7:8-11) Andreas amene alela ana aŵili anati: “Kulimbikitsa ana kumawathandiza kukula kuuzimu na m’nzelu. Njila yabwino yokhomelezela uphungu mwa ana ni kuwalimbikitsa. Ana athu amadziŵa kusiyanitsa cabwino na coipa. Koma cimene cimawathandiza kucita cabwino nthawi zonse ni cilimbikitso cathu cosalekeza.”

CILIMBIKITSO COGWILA MTIMA

15. Tingacite ciani kuti tilimbikitse ena?

15 Tiziyamikila makhalidwe abwino a akhiristu anzathu na zimene amacita. (2 Mbiri 16:9; Yobu 1:8) Yehova na Yesu amayamikila ngako zimene timacita pocilikiza zinthu za Ufumu, ngakhale kuti sitingacite zambili cifukwa ca mmene zinthu zilili pa umoyo wathu. (Ŵelengani Luka 21:1-4; 2 Akorinto 8:12.) Mwacitsanzo, ena mwa okalamba athu amayesetsa movutikila kupezeka ku misonkhano na kutengako mbali, komanso kulalikila nthawi zonse. Kodi sitiyenela kuwayamikila na kuwalimbikitsa?

16. N’cifukwa ciani sitiyenela kuleka kulimbikitsa ena?

16 Tiziona mipata yolimbikitsila ena. Ngati taona kuti wina wacita cabwino, n’kulekelanji kumuyamikila? Kumbukilani zimene zinacitika pamene Paulo na Baranaba anali ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Atsogoleri a sunagoge kumeneko anawauza kuti: “Amuna inu, abale athu, ngati muli ndi mau alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.” Paulo anacita zimenezo mwa kukamba nkhani yolimbikitsa. (Mac. 13:13-16, 42-44) Tikakhala na mau olimbikitsa ouza munthu, n’kukhalilanji zii osawakamba? Ngati takhala na cizoloŵezi colimbikitsa ena, nawonso azitilimbikitsa.—Luka 6:38.

17. Cofunika n’ciani kuti ciyamikilo cathu cikhale cogwila mtima?

17 Chulani zimene muyamikila, osati mwacisawawa cabe. Kuyamikila munthu n’kothandiza. Koma zimene Yesu anauza Akhiristu a ku Tiyatira zionetsa kuti kuchula cimene tikuyamikila ndiye kumathandiza kwambili. (Ŵelengani Chivumbulutso 2:18, 19.) Mwacitsanzo, ngati ndinu kholo, mungauze ana anu zimene mumayamikila pa kupita kwawo patsogolo kuuzimu. Poyamikila mlongo amene alibe mwamuna, tingamuchulile zimene zimatikondweletsa tikaona mmene akulelela ana ake ngakhale kuti zinthu n’zovuta mu umoyo wake. Kuyamikila na kulimbikitsa ena mwa njila imeneyo kumakhala na zotulukapo zabwino ngako.

18, 19. Kodi tingacite bwanji kuti tizilimbikitsa ena?

18 Masiku ano, Yehova sangatiuze mwacindunji kuti tilimbikitse munthu winawake monga mmene anauzila Mose kulimbikitsa Yoswa. Komabe, Mulungu amakondwela kwambili ngati tilimbikitsa Akhiristu anzathu ndi ena. (Miy. 19:17; Aheb. 12:12) Mwacitsanzo, tingauze m’bale amene wakamba nkhani mmene nkhaniyo yatithandizila panthawi yake, kapena mmene watithandizila kumvetsetsa lemba lina lake. Mlongo wina analembela mlendo amene anakamba nkhani kuti: “Olo kuti tinakambilana kwa mphindi zocepa cabe, munanitonthoza na kunitsitsimula monga kuti munali kudziŵa bwino cisoni conse cinali mumtima mwanga. Dziŵani kuti pamene munali kukamba mokoma mtima pa pulatifomu, ndi pokamba na ine mwacindunji, n’naona kuti ni mphatso yocokela kwa Yehova.”

19 Tidzapeza njila zambili zolimbikitsila ena mwauzimu ngati titsatila malangizo a Paulo akuti: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukucitila.” (1 Ates. 5:11) Inde, Yehova adzakondwela kwambili ngati tonse ‘tipitiliza kulimbikitsana tsiku na tsiku.’

^ [1] (palagilafu 1) Maina ena tawasintha.