Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mau Amene Anali Atanthauzo Kwambili

Mau Amene Anali Atanthauzo Kwambili

“MAYI.” Awa ni mau amene nthawi zina Yesu anali kuseŵenzetsa pokamba na azimayi. Mwacitsanzo, pocilitsa munthu wolemala msana kwa zaka 18, anati: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” (Luka 13:10-13) Mwa cikhalidwe cawo, Yesu anaseŵenzetsanso mau amenewa ngakhale kwa amayi ake. Mau amenewa anali aulemu m’nthawi za m’Baibo. (Yoh. 19:26; 20:13) Koma panalinso mau ena amene anali ofunika kuposa pamenepa.

Baibo imagwilitsila nchito mau apadela pokamba za akazi ena. Yesu anaseŵenzetsa mau amenewo pokamba na mkazi amene anali na matenda otaya magazi kwa zaka 12. Mkaziyu anafikila Yesu m’njila yosaloleka na Cilamulo ca Mulungu. Cilamuloco cinali kukamba kuti munthu wodwala matendawo anali wodetsedwa. Tingatelo kuti mkaziyo anafunika kukhala kwa yekha cifukwa ca matenda ake. (Lev. 15:19-27) Koma iye anali atasoŵelatu mtengo wogwila. “Madokotala ambili anam’cititsa kumva zopweteka zambili. Iye anawononga cuma cake conse koma osapindula kanthu, m’malomwake matendawo ankangokulila-kulila.”—Maliko 5:25, 26.

Mzimayiyu analoŵa m’cigulu ca anthu mwakacete-cete, n’kufika kumbuyo kwa Yesu, na kugwila kunsi kwa covala cake. Pamenepo matenda ake anathelatu! Mzimayiyo sanafune kuti Yesu adziŵe. Koma Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwila?” (Luka 8:45-47) Pakumva izi, mzimayi uja ali nje nje nje ndi mantha, anagwada kwa Yesu “ndi kumuuza zoona zonse.”—Maliko 5:33.

Koma Yesu pofuna kumukhazika mtima pansi, anamuuza kuti: “Mwanawe, limba mtima.” (Mat. 9:22) Akatswili a Baibo amakamba kuti mau a Ciheberi ndi a Cigiriki amene anawamasulila kuti “mwanawe,” amatanthauzanso “kukoma mtima na cifundo.” Yesu analimbikitsanso mzimayiyo mwa kumuuza kuti: “Cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, matenda ako aakuluwo atheletu.”—Maliko 5:34.

“Mwanawe.” Ni mmenenso Mwiisiraeli wina wolemela dzina lake Boazi anachulila Rute, mkazi wacimoabu. Nayenso anali ndi nkhawa cifukwa anali kukunkha m’munda mwa munthu amene sanali kum’dziŵa. Boazi anati: “Tamvela mwana wanga.” Ndiyeno, anauza Rute kuti apitilize kukunkha m’munda mwake. Rute anagwada pamaso pa Boazi na kum’funsa cifukwa cake anamuonetsa cisomo cotelo, iye pokhala mlendo. Poyankha, Boazi anam’limbikitsa na mau akuti: “Ndamva zonse zimene wacitila apongozi ako [Naomi mkazi wamasiye] . . . Yehova akudalitse cifukwa ca zimene wacita.”—Rute 2:8-12.

Ha, n’citsanzo cabwino cotani nanga cimene Yesu na Boazi anapeleka kwa akulu acikhiristu! Nthawi zina, akulu aŵili angafikile mlongo wofunika thandizo na cilimbikitso ca m’Malemba. Pambuyo popempha citsogozo kwa Yehova m’pemphelo, na kumvetsela bwino-bwino pamene mlongo afotokoza nkhawa yake, akulu angam’limbikitse na kum’tonthoza pogwilitsila nchito Mau a Mulungu.—Aroma 15:4.