Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumalemekeza Buku Lake la Yehova?

Kodi Mumalemekeza Buku Lake la Yehova?

“Pamene munalandila mau a Mulungu . . . simunawalandile monga mau a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mau a Mulungu.”—1 ATES. 2:13.

NYIMBO: 96, 94

1-3. Kodi mkangano pakati pa Eodiya na Suntuke mwina unayamba bwanji? Nanga mavuto aconco tingawapewe bwanji? (Onani pikica pamwambapa.)

ATUMIKI a Yehova amalemekeza kwambili buku lake loyela, Baibo. Pokhala opanda ungwilo, tonse timapatsidwa uphungu wa m’Malemba nthawi zina. Kodi timacita bwanji tikapatsidwa uphungu? Ganizilani za Eodiya ndi Suntuke, alongo acikhiristu a m’zaka 100 zoyambilila. Mkangano waukulu unabuka pakati pa alongo odzozedwa amenewa. Kodi vuto linali ciani? Baibo siinakambe. Koma kuti tiimvetse bwino mfundo yake, tiyeni tingoiganizila motele nkhaniyo.

2 Tiyelekeze kuti Eodiya anaitana abale na alongo kunyumba kwake kuti akadye nawo cakudya na kusangalala ndi maceza. Suntuke sanaitanidwe, koma anamvela kuti kumeneko kunali maceza acisangalalo. Ndiye Suntuke anaganiza kuti: ‘Zoona Eodiya sananiitaneko ine! N’nali kuganiza kuti ni mnzanga wa pamtima!’ Kuyambila pamenepo, Suntuke anayamba kukayikila Eodiya na kumuganizila zoipa. Ndiyeno, Suntuke nayenso anakonza maceza ake, n’kuitana abale na alongo amodzi-modzi aja, koma osaitana Eodiya. Kunena zoona, vuto limene linabuka pakati pa Eodiya na Suntuke liyenela kuti linasokoneza mtendele wa mpingo wonse. Baibo sitiuza kuti nkhaniyi inatha bwanji. Koma ubwino wake ni wakuti alongo amenewa ayenela kuti analabadila uphungu wacikondi wa mtumwi Paulo.—Afil. 4:2, 3.

3 Ngakhale lelo lino, zocitika monga izi zimabweletsa mavuto aakulu m’mipingo ya anthu a Yehova. Komabe, tingathetse mavuto amenewa kapena kuwapewa mwa kutsatila uphungu wa m’Mau a Mulungu, Baibo. Ndipo ngati timalemekeza kwambili buku lake la Yehova, malangizo ake adzakhala umoyo wathu.—Sal. 27:11.

BAIBO IMATIPHUNZITSA KULAMULILA MKWIYO

4, 5. Kodi Mau a Mulungu amatilangiza ciani pa nkhani yolamulila mkwiyo?

4 Si capafupi kulamulila mkwiyo ngati wina watikhumudwitsa kapena waticitila zinthu zopanda cilungamo. Cimatiŵaŵa kwambili ngati wina aticitila zinthu zopanda cilungamo cabe cifukwa ndife acikhalidwe cosiyana, ndife a fuko lina, kapena cifukwa ca maonekedwe athu. Ndiye ganizani cabe mmene cimaŵaŵila ngati woticita zimenezo ni Mkhiristu mnzathu! Kodi Mau a Mulungu ali na malangizo otithandiza za conco zikaticitikila?

5 Yehova wakhala akuona mmene anthu akukhalila kucokela pamene anawalenga. Amadziŵa zimene timacita tikakwiya. Cifukwa ca maganizo athu ndi kukwiya, tingakambe mau ndi kucita zinthu zimene pambuyo pake tingamve nazo kuipa. Conco, n’cinthu canzelu kutsatila malangizo a m’Baibo kuti tizilamulila mkwiyo na kupewa mtima wapacala. (Ŵelengani Miyambo 16:32; Mlaliki 7:9.) Tonse tifunikila kuyesetsa kusakwiya msanga, na kukhululukila ena. Kwa Yehova na Yesu, nkhani ya kukhululukilana ndi yaikulu kwambili. (Mat. 6:14, 15) Kodi muona kuti mufunika kuwongolela pa nkhani ya kuleza mtima, kapena kulamulila mkwiyo wanu?

6. N’cifukwa ciani tifunika kupewa mkwiyo?

6 Anthu amene amalephela kulamulila mkwiyo nthawi zambili amakhala osakondwa. Izi zimapangitsa anthu ena kuwakhalilako patali. Munthu wokhumudwa amasokoneza mzimu wa mpingo. Angayese kubisa mkwiyo kapena cidani cake, koma m’kupita kwa nthawi maganizo oipa a mumtima mwake ‘adzaululika mumpingo.’ (Miy. 26:24-26) Akulu angathandize anthu aconco kuona kuti kukhumudwa, cizondi, ndi kusungila ena cakukhosi, ni makhalidwe amene safunika m’gulu la Mulungu. Buku lake la Yehova silipita m’mbali pankhani imeneyi. (Lev. 19:17, 18; Aroma 3:11-18) Kodi mugwilizana ndi malangizo ake?

YEHOVA AMATITSOGOLELA MWA DONGOSOLO LAKE

7, 8. (a) Kodi Yehova amatsogolela bwanji gulu lake la padziko lapansi? (b) Ni malangizo ena ati amene apezeka m’Mau a Mulungu? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuwatsatila?

7 Yehova amatsogolela na kudyetsa gulu lake la padziko lapansi kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Kapoloyo ali pansi pa utsogoleli wa Khiristu, “mutu wa mpingo.” (Mat. 24:45-47; Aef. 5:23) Molingana ndi bungwe lomulila la m’nthawi ya atumwi, kapolo ameneyu amatsatila mau ouzilidwa a Mulungu, ndipo amawalemekeza ngako. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.) Ni malangizo ena ati a m’Baibo amene amatipindulitsa?

8 Baibo imatilangiza kuti tizipezeka ku misonkhano nthawi zonse. (Aheb. 10:24, 25) Imatilangizanso kuti tizikhala ogwilizana pa ciphunzitso. (1 Akor. 1:10) Mau a Mulungu amatiuza kuika patsogolo Ufumu wa Mulungu mu umoyo wathu. (Mat. 6:33) Malemba amatikumbutsanso udindo na mwayi umene tili nawo wolalikila kunyumba ndi nyumba, mwamwayi, ndi ulaliki wapoyela. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:42; 17:17; 20:20) Buku lake la Mulungu limalangiza akulu mu mpingo kusungitsa ciyelo m’gulu la Mulungu. (1 Akor. 5:1-5, 13; 1 Tim. 5:19-21) Ndipo Yehova analamula kuti onse m’gulu lake afunika kukhala oyela kuthupi na kuuzimu.—2 Akor. 7:1.

9. N’ndani yekha amene Mulungu amam’gwilitsila nchito kutithandiza kumvetsetsa Mau Ake?

9 Pali anthu ena amene amaona kuti akhoza kuzindikila paokha matanthauzo a mfundo za m’Baibo. Koma Yesu anaika ‘kapolo wokhulupilika’ mmodzi yekha kuti ndiye azigaŵila cakudya cauzimu. Kuyambila mu 1919, Yesu Khiristu wakhala akugwilitsila nchito kapolo ameneyo kuthandiza otsatila ake kumvetsetsa Buku la Mulungu na kutsatila malangizo ake. Mwa kumvela malangizo a m’Baibo, timalimbikitsa ciyelo, mtendele, na mgwilizano mumpingo. Aliyense wa ife afunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimamvela malangizo a kapolo wamene Yesu akum’gwilitsila nchito?

GALETA YA YEHOVA ILI PALIŴILO!

10. Kodi gulu la kumwamba la Yehova alifotokoza bwanji m’buku la Ezekieli?

10 Mau olembedwa a Yehova amatiunikila za gulu lake lakumwamba. Mwacitsanzo, mneneli Ezekieli anaona masomphenya oonetsa gulu la Mulungu lakumwamba monga galeta. (Ezek. 1:4-28) Yehova ndiye akuyendetsa galeta imeneyi, ndipo imapita kulikonse kumene mzimu wake waitsogolela. Ndiponso, zimene gulu la Mulungu la kumwamba limacita zimakhudzanso gulu lake la padziko lapansi. Ndithudi, galetayi ili paliŵilo! Ganizilani cabe za masinthidwe amene acitika pa zaka 10 zapitazo, ndipo musaiŵale kuti Yehova ndiye wacititsa zimenezo. Khiristu na angelo ake ali pafupi kuwononga dziko loipali. Mwa ici, galeta ya Yehova ili pa liŵilo! Ikuthamanga kuti ucifumu wa Yehova ukwezedwe ndi kuti dzina lake liyeletsedwe.

Timayamikila ngako anchito odzipeleka amene ali kaliki-liki pa nchito zomanga (Onani palagilafu 11)

11, 12. Ni zinthu zina ziti zimene gulu la Yehova likucita masiku ano?

11 Tiyeni tione zimene gulu la Mulungu la padziko lapansi likucita masiku ano otsiliza. Nchito Yomanga. Abale na alongo ambili anali otangwanika ndi nchito yomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova ku Warwick ku America. Komanso, anchito odzifunila zungulile dziko lonse ali kaliki-liki pa nchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi kuwonjezela maofesi a nthambi. Zonsezi zikucitika pansi pa uyang’anilo wa dipatimenti ya zomanga-manga (Worldwide Design/Construction Department). Tiwayamikila kwambili anchito odzipeleka amenewa pogwila nchito imeneyi molimbika. Komanso, Yehova akudalitsa alengezi a ufumu padziko lonse amene, mokhulupilika ndi modzicepetsa, amapeleka ndalama zocilikiza nchito zimenezi.—Luka 21:1-4.

12 Maphunzilo. Ganizilaninso masukulu aumulungu osiyana-siyana. (Yes. 2:2, 3) Tili na Sukulu ya Apainiya, Sukulu ya Alengezi a Ufumu, Sukulu ya Giliyadi, Sukulu ya Atumiki Atsopano a pa Beteli, Sukulu ya Oyang’anila Madela ndi akazi awo, Sukulu ya Akulu, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, na Sukulu ya ziwalo za Makomiti a Nthambi ndi akazi awo. Ndithudi, Yehova amakonda ngako kuphunzitsa anthu ake. Webusaiti yathu ya jw.org, imene pamapezeka zofalitsa m’zinenelo zambili, imathandizanso anthu kuphunzila Baibo. Pa webusaiti imeneyi pali mbali za ana, mabanja, ndi zinthu zatsopano. Kodi mumaiseŵenzetsa webusaiti yathu mu ulaliki ndi pa kulambila kwanu kwa pabanja?

KHULUPILIKANI KWA YEHOVA, CILIKIZANI GULU LAKE

13. Kodi tili na udindo wanji monga atumiki a Yehova okhulupilika?

13 Ha, ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala m’gulu la Yehova! Kudziŵa kwathu zimene Mulungu amafuna ndi miyezo yake, kumatipatsa udindo wocita zinthu zoyenela, na kukweza ucifumu wake. Pamene dzikoli likutitimila m’makhalidwe oipa, tifunika kudana ndi zoipa, monga mmene Yehova amazizondela. (Sal. 97:10) Tisatengele anthu osaopa Mulungu, mwa kukamba kuti: “Cabwino n’coipa ndipo coipa n’cabwino.” (Yes. 5:20) Cifukwa timafuna kukondweletsa Mulungu, timayesetsa kukhala oyela kuthupi, m’makhalidwe, na kuuzimu. (1 Akor. 6:9-11) Timakonda Yehova na kum’dalila. Ndiye cifukwa cake mu umoyo wathu, timafuna kukhala okhulupilika kwa iye ndi kutsatila malangizo ake olembewa m’Buku lake lopatulika. Ndipo timalimbikila kutsatila malangizo amenewo kulikonse kumene tili, kunyumba, mumpingo, kunchito, kapena kusukulu. (Miy. 15:3) Tiyeni tionenso njila zina zoonetsela kuti ndife okhulupilika kwa Mulungu.

14. Makolo acikhiristu angaonetse bwanji kuti ni okhulupilika kwa Mulungu?

14 Kulela ana. Makolo acikhiristu amaonetsa kukhulupilika kwawo kwa Yehova mwa kuphunzitsa ana awo mogwilizana na Mau a Mulungu. Makolo oopa Mulungu amapewa kungotengela cikhalidwe cakwawo colelela ana. Mabanja acikhiristu ayenela kupewelatu mzimu wa dziko. (Aef. 2:2) Tate wobatizika sayenela kuganiza kuti, ‘M’cikhalidwe ca kwathu kuphunzitsa ana ni nchito ya mkazi.’ Baibo imakamba momveka bwino pankhaniyi kuti: “Abambo, . . . muwalele [ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Makolo oopa Mulungu amafuna ana awo kukhala monga Samueli, amene Yehova sanamusiye pamene anali kukula.—1 Sam. 3:19.

15. Timaonetsa bwanji kukhulupilika kwathu kwa Yehova popanga zosankha zazikulu?

15 Kupanga zosankha. Popanga zosankha zazikulu, njila imodzi yoonetsela kukhulupilila Mulungu ndiyo kupeza thandizo m’Mau ake ndi gulu lake. Kuti tione kufunika kwa mfundo imeneyi, tiyeni tikambepo za nkhani ina yodetsa nkhawa imene imakhudza makolo ambili. Makolo ena amene anapita kukakhala ku maiko ena amatumiza ana awo akhanda kwa abululu ŵawo kuti akaŵasamalile. Amacita izi kuti apeze bwino mpata wogwila nchito ndi kupanga ndalama m’dziko lacilendo. N’zoona kuti nkhaniyi n’cosankha ca munthu. Koma tizikumbukila kuti tidzayankha mlandu kwa Mulungu pa zosankha zimene timapanga. (Ŵelengani Aroma 14:12.) Kodi n’cinthu canzelu kupanga zosankha zokhudza banja lathu kapena nchito yathu popanda kufufuza coyamba mfundo za m’Baibo? Yankho lake n’lacidziŵikile! Timafunikila thandizo la Atate wathu wakumwamba, cifukwa sitingakwanitse kuwongolela mapazi athu.—Yer. 10:23.

16. N’cosankha citi cimene mayi wina anafunika kupanga mwana wake atabadwa? Nanga n’ciani cinamuthandiza kusankha mwanzelu?

16 Mayi wina atakhala na mwana wamwamuna kudziko lacilendo, anafuna kutumiza mwanayo kudziko la kwawo kuti makolo ake akamusungile. Panthawi imeneyo, mayiyo anayamba kuphunzila Baibo na Mboni ya Yehova. Atapita patsogolo m’kuphunzila kwake, anazindikila kuti Mulungu anapatsa iye udindo wolela mwana wake, na kum’phunzitsa kulambila Yehova. (Sal. 127:3; Miy. 22:6) Monga amatiuzila Malemba, mayiyu anam’tulila Yehova nkhaniyo m’pemphelo. (Sal. 62:7, 8) Anafotokozelanso amene anali kum’phunzitsa Baibo, komanso ena mu mpingo. Ngakhale kuti abululu ake na anzake anam’limbikitsa kuti atumize mwana wake kwa makolo ake, iye anaona kuti kucita zimenezo n’kosayenela. Mwamuna wake anayamikila kwambili kuona mmene mpingo unatetezela mkazi wake na mwana wake. Cifukwa ca izi, anavomela kuphunzila Baibo ndipo anayamba kupezeka ku misonkhano pamodzi na mkazi wake ndi mwana wake. Kodi muganiza kuti mayiyu anaona kuti Yehova anayankha pemphelo lake? Mosakayikila!

17. Ni malangizo ati amene tinapatsidwa okhudza maphunzilo athu a Baibo?

17 Kutsatila malangizo. Njila yofunika kwambili yoonetsa kukhulupilika kwathu kwa Mulungu ni kutsatila malangizo a gulu lake. Mwacitsanzo, kumbukilani malangizo amene tinapatsidwa okhudza maphunzilo athu a Baibo. Tinalangizidwa kuti, tikangokhazikitsa phunzilo la Baibo m’buku ya Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, timafunika kupatula mphindi zocepa tikatsiliza phunzilo lathu, kuti tizifotokozela wophunzilayo za gulu la Mulungu. Tingagwilitsile nchito vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? kapena kukambilana naye bulosha yakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano? Anatilangizanso kuti tikatsiliza kuphunzila buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse na wophunzila amene akupita patsogolo, tiziyamba naye buku lakuti Khalanibe M’cikondi ca Mulungu,ngakhale kuti munthuyo ni wobatizika. Gulu la Mulungu linapeleka malangizo amenewa kuti ophunzila atsopano azikhazikika bwino m’cikhulupililo. (Akol. 2:7) Kodi mumatsatila malangizo a gulu la Yehova amenewa?

18, 19. Tili na zifukwa ziti zoyamikilila Yehova?

18 Ha, tili na zifukwa zambili cotani nanga zoyamikilila Yehova! Iye ndiye kasupe wa moyo wathu. Popanda iye sitikanakhalako. (Mac. 17:27, 28) Watipatsanso mphatso yamtengo wapatali—Buku lake, Baibo. Timailandila moyamikila monga uthenga wocokeladi kwa Mulungu, mmenenso Akhiristu a ku Tesalonika anacitila.—1 Ates. 2:13.

19 Cifukwa ca Mau Ake, tayandikila kwa Yehova ndipo nayenso watiyandikila. (Yak. 4:8) Sizokhazo, Atate wathu wakumwamba watipatsa mwayi wokhala m’gulu lake. Kodi si pake ndithu kuwayamikila madalitso onsewa? Wamasalimo anaimbadi mokongola kuti: “Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino. Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” (Sal. 136:1) Mu Salimo 136, mau akuti “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale” amachulidwa nthawi 26. Tikapitiliza kukhala okhulupilika kwa Yehova na gulu lake, tidzaona kukwanilitsika kwa mau okhudza mtima amenewa cifukwa tidzakhala na moyo mpaka muyaya.