Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 47

NYIMBO 103 Abusa ni Mphatso za Amuna

Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mkulu?

Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mkulu?

“Ngati munthu akuyesetsa kuti akhale woyangʼanila, akufuna nchito yabwino.”1 TIM. 3:1.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Zina mwa ziyenelezo za m’Malemba zimene m’bale ayenela kukwanilitsa kuti akayenelele kukhala mkulu.

1-2. Kodi “nchito yabwino” imene mkulu amagwila imaphatikizapo ciyani?

 NGATI mwakhala mukutumikila monga mtumiki wothandiza kwa nthawi, muyenela kuti mwakulitsa kale ambili mwa makhalidwe amene angakuyenelezeni kutumikila monga mkulu. Kodi mungakonde kugwilako “nchito yabwino” imene akulu amacita?—1 Tim. 3:1.

2 Kodi mkulu amagwila nchito ziti? Amapeleka citsanzo cabwino pogwila nchito yolalikila mwakhama, amacita khama posamalila mpingo komanso pophunzitsa, ndipo amalimbikitsa mpingo m’zokamba na zocita zake. Tingathe kuona cifukwa cake Baibo imachula akulu kuti “mphatso za amuna.”—Aef. 4:8.

3. Kodi m’bale ayenela kucita ciyani kuti akayenelele kutumikila monga mkulu? (1 Timoteyo 3:​1-7; Tito 1:​5-9)

3 Muyenela kucita ciyani kuti mukayenelele kukhala mkulu? Kuyenelela kuti mutumikile monga mkulu sikufanana na kuyenelela kuti muloŵe nchito ina yake. Kuti muloŵe nchito ina yake, mumangofunika kukhala na maluso ena ake omwe wolemba nchitoyo akufuna. Mosiyana na zimenezi, ngati mungakonde kuti mukatumikile monga mkulu, kungokhala na maluso a kuphunzitsa komanso kulalikila si kokwanila. Muyenela kukwanilitsa ziyenelezo za m’Malemba za akulu zopezeka pa 1 Timoteyo 3:​1-7 na Tito 1:​5-9. (Ŵelengani.) M’nkhani ino, tikambilane mbali zitatu izi zofunikila kuti munthu ayenelele kukhala mkulu: kukhala na mbili yabwino mumpingo komanso kunja kwa mpingo, kukhala mutu wa banja wabwino, komanso kukhala wofunitsitsa kutumikila ena mumpingo.

KHALANI NA MBILI YABWINO

4. Kodi ‘kukhala wopanda cifukwa cokunenezelani’ kumatanthauza ciyani?

4 Kuti mukayenelele kukhala mkulu, mufunika ‘kukhala wopanda cifukwa cokunenezelani.’ Izi zitanthauza kuti anthu mumpingo ayenela kukuonani kuti muli na mbili yabwino cifukwa ca khalidwe lanu labwino, ndipo sangakunenezeni coipa ciliconse. Kuwonjezela apo, mufunika kukhalanso na “mbili yabwino kwa osakhulupilila.” Anthu osakhulupilila angakunenezeni zoipa pa zimene mumakhulupilila, koma sayenela kukhala na cifukwa ciliconse cokaikila ngati ndinu munthu woona mtima komanso wakhalidwe labwino. (Dan. 6:​4, 5) Dzifunseni kuti, ‘Kodi nili na mbili yabwino mumpingo komanso kwa anthu amene si Mboni?’

5. Kodi mungaonetse bwanji kuti ndinu munthu “wokonda zabwino”?

5 Ngati ndinu munthu “wokonda zabwino,” mumaona zabwino mwa ena, ndipo mumawayamikila cifukwa ca makhalidwe awo abwino. Mumakonda kucitila ena zabwino, ndipo mungawacitile zambili ngakhale kuposa zimene akuyembekezela. (1 Ates. 2:8) N’cifukwa ciyani m’pofunika kuti akulu akhale na khalidwe limeneli? Cifukwa akulu amaseŵenzetsa nthawi yawo yoculuka kusamalila abale na alongo mumpingo, komanso kusamalila maudindo awo. (1 Pet. 5:​1-3) Ngakhale n’telo, cimwemwe cimene amapeza potumikila ena cimaposa ciliconse cimene angadzimane.—Mac. 20:35.

6. Kodi mungaonetse bwanji kuti ndinu munthu “woceleza alendo”? (Aheberi 13:​2, 16; onaninso cithunzi.)

6 Mumaonetsa kuti ndinu “woceleza alendo” mukamacitila ena zabwino, kuphatikizapo awo amene simuceza nawo kaŵili-kaŵili. (1 Pet. 4:9) Buku lina lotanthauzila mawu a m’Baibo linakamba kuti, munthu woceleza amacitila ena zabwino, ngakhale anthu amene sakuwadziŵa, ndipo amawaitanila kunyumba kwake. Dzifunseni kuti, ‘Kodi anthu amanidziŵa kuti nili na mbili yotani pa nkhani yoceleza alendo?’ (Ŵelengani Aheberi 13:​2, 16.) Munthu woceleza amacitila anthu onse zabwino. Mwacitsanzo, amathandiza anthu osoŵa mwakuthupi. Amathandizanso atumiki amene amagwila nchito mwakhama polimbikitsa abale na alongo, monga oyang’anila madela komanso alendo odzakamba nkhani pampingo.—Gen. 18:​2-8; Miy. 3:27; Luka 14:​13, 14; Mac. 16:15; Aroma 12:13.

Banja la Cikhristu lalandila woyang’anila dela na mkazi wake kunyumba kwawo (Onani ndime 6)


7. Kodi mkulu amaonetsa bwanji kuti sakonda ndalama?

7 “Asakhalenso. . . wokonda ndalama.” Izi zitanthauza kuti simuyenela kuika kwambili maganizo anu pa zinthu zakuthupi. Kaya muli na cuma kapena ayi, muziika za Ufumu patsogolo m’mbali zonse zaumoyo wanu. (Mat. 6:33) Muziseŵenzetsa nthawi yanu, nyonga zanu, komanso cuma canu polambila Yehova, posamalila banja lanu, komanso potumikila mpingo. (Mat. 6:24; 1 Yoh. 2:​15-17) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndalama nimaziona bwanji? Kodi ndine wokhutila na zofunika za paumoyo zimene nili nazo? Kapena kodi nimangofuna kukhala na ndalama zambili komanso kuwonjezela cuma canga?’—1 Tim. 6:​6, 17-19.

8. Mungaonetse bwanji kuti simucita “zinthu mopitilila malile” komanso kuti ndinu “wodziletsa”?

8 Ngati simucita “zinthu mopitilila malile” komanso ndinu “wodziletsa,” ndiye kuti mumacita zinthu mwanzelu m’mbali zonse zaumoyo wanu. Izi ziphatikizapo kupewa kudya na kumwa kwambili, komanso kupewa kuvala na kudzikongoletsa monyanyila. Muzicitanso zinthu mwacikatikati pa nkhani ya zosangalatsa. Musalole kuumbidwa m’cikombole ca dzikoli potengela makhalidwe ake. (Luka 21:34; Yak. 4:4) Muyenela kucitabe zinthu modekha ngakhale pamene anthu ena akukhumudwitsani. Simuyenela kukhala “munthu womwa moŵa mwaucidakwa,” ndipo simuyenela kukhala na mbili yakuti mumamwa kwambili moŵa. Dzifunseni kuti, ‘Kodi mmene nimacitila zinthu paumoyo wanga zimaonetsa kuti sinicita zinthu mopitilila malile, komanso kuti ndine wodziletsa?’

9. Kodi kukhala “woganiza bwino” kumatanthauza ciyani? Nanga kucita “zinthu mwadongosolo” kumatanthauza ciyani?

9 Kukhala “woganiza bwino,” kutanthauza kuti muyenela kumafufuza mozamilapo kuti mupeze mfundo za m’Baibo zimene zimagwila nchito pa nkhani zosiyana-siyana. Muziganizila mfundozo mozamilapo, ndipo izi zidzakuthandizani kuti mukhale wozindikila komanso kuti muimvetse bwino nkhaniyo. Musamafulumile kugamula m’maganizo mwanu musanaimvetsetse nkhani yonse. M’malomwake, muzionetsetsa kuti muli na mfundo zonse zimene mukufunikila zokhudza nkhaniyo. (Miy. 18:13) Cotsatila cake, mudzapanga zisankho zanzelu zimene zimaonetsa kaganizidwe ka Yehova. Kuti muzicita “zinthu mwadongosolo,” muyenela kumalinganiza bwino zinthu komanso kusunga nthawi. Muzidziŵika kuti ndinu wodalilika komanso kuti mumatsatila malangizo pocita zinthu. Makhalidwe amenewa adzakuthandizani kuti mukhale na mbili yabwino. Tiyeni tsopano tikambilane zimene zingakuthandizeni kukwanilitsa ciyenelezo ca m’Malemba ca kukhala mutu wa banja wabwino.

KHALANI MUTU WA BANJA WABWINO

10. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti ‘amayang’anila bwino banja lake’?

10 Ngati ndinu mwamuna wokwatila, ndipo mukufuna kuyenelela kukakhala mkulu, dziŵani kuti mbili ya banja lanu ingakhudzenso ziyenelezo zanu. Conco, khalani “mwamuna woyang’anila bwino banja [lanu].” Izi zitanthauza kuti muyenela kusamalila banja lanu mwacikondi, komanso kupanga zisankho zabwino zokhudza banja lanu. Muyenelanso kukhala patsogolo potsogolela banja lanu pambali zonse za kulambila. N’cifukwa ciyani zimenezi n’zofunika? Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Ngati munthu sadziwa kuyangʼanila banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalile bwanji?”—1 Tim. 3:5.

11-12. Kodi zocita za anthu a m’banja la m’bale zingakhudze bwanji ziyenelezo zake? (Onaninso cithunzi.)

11 Ngati ndinu tate, ndipo muli na ana amene sanakwanitse zaka 18, anawo ayenela kukhala kuti ‘amakumvelani ndi mtima wonse.’ Muyenela kuwaphunzitsa na kuwalangiza mwacikondi. Mofanana na ana onse, nawonso adzayamba kukhala na nthawi yoseka komanso yoseŵela na anzawo. Koma cifukwa cakuti mumawaphunzitsa bwino, adzakhala omvela, aulemu, komanso a khalidwe labwino. Cinanso, muyenela kucita zonse zimene mungathe kuti muthandize ana anu kukhala paubale wabwino na Yehova, kutsatila mfundo za m’Baibo, komanso kupita patsogolo kuti akabatizike.

12 “Wa ana okhulupilila ndiponso osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulilika.” Ngati mwana wobatizika kapena amene akupita patsogolo kuti akabatizike, amenenso akukhala pa nyumba ya m’bale wacita chimo lalikulu, kodi zimenezi zingakhudze bwanji m’baleyo? Ngati m’baleyo sanali kuphunzitsa mwana wake komanso kumulangiza, n’kutheka kuti sangayenelele kutumikila monga mkulu.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1996, tsamba 21, ndime 6-7.

Mitu ya mabanja ikuphunzitsa ana awo kugwila nchito zosiyana-siyana potumikila Yehova komanso mpingo (Onani ndime 11)


TUMIKILANI ENA MUMPINGO

13. Mungaonetse bwanji kuti ndinu munthu “wololela,” osati “womva zake zokha”?

13 Abale amene ali na makhalidwe abwino a Cikhristu ni ofunika kwambili mumpingo. Munthu “wololela” amalimbikitsa mtendele. Ngati mufuna kuti ena azikuonani kuti ndinu wololela, muziwamvetsela akamafotokoza maganizo awo, komanso muzimvetsa mmene akumvela. Yelekezani kuti ndinu mkulu, ndipo muli pamiting’i ya bungwe la akulu. Ngati akulu anzanu angagwilizane pa cigamulo cimene sicisemphana na mfundo za m’Baibo, kodi mungagwilizanebe na cigamuloco ngakhale kuti n’cosiyana na zimene inuyo mukufuna? Mawu akuti “asakhale womva zake zokha,” amatanthauza kuti simuyenela kuumiliza ena kucita zinthu mmene inu mukufunila. Koma mumadziŵa kuti kumvetsela maganizo a anthu ena n’kothandiza. (Gen. 13:​8, 9; Miy. 15:22) Musakhale “wokonda kukangana” na ena kapena “wa mtima wapacala.” M’malo mosuliza zokamba za ena, kapena kukangana nawo, muzicita nawo zinthu mokoma mtima komanso mosamala. Pokhala munthu wokonda mtendele, muzicita khama kubwezeletsa mtendele ngakhale pamene zinthu zili zovuta. (Yak. 3:​17, 18) Mukamakambilana mokoma mtima na anthu ena, kuphatikizapo aja amene amatitsutsa, mungawakhazike mtima pansi.—Ower. 8:​1-3; Miy. 20:3; 25:15; Mat. 5:​23, 24.

14. Kodi mawu akuti “asakhale woti wangobatizidwa kumene” amatanthauza ciyani? Nanga mawu akuti “wokhulupilika” atanthauza ciyani?

14 M’bale amene angayenelele kukhala mkulu sayenela kukhala “woti wangobatizidwa kumene.” Ngakhale kuti mukabatizika sipayenela kupita zaka zambili kuti mukayenelele kukhala mkulu, mufunikilabe nthawi kuti mukhale Mkhristu wokhwima. Musanaikidwe kukhala mkulu, muyenela kuonetsa kuti ndinu wodzicepetsa, komanso kuti ndinu wokonzeka kuyembekezela modekha mpaka pamene Yehova angakupatseni mautumiki owonjezela, monga mmene Yesu anacitila. (Mat. 20:23; Afil. 2:​5-8) Mungaonetse kuti ndinu “wokhulupilika” mwa kukhalabe kumbali ya Yehova na kutsatila mfundo zake zolungama. Mungaonetsenso khalidweli mwa kutsatila malangizo omwe iye amapeleka kudzela m’gulu lake.—1 Tim. 4:15.

15. Kodi mkulu aliyense ayenela kukhala mlankhuli waluso kwambili? Fotokozani.

15 Malemba amanena momveka bwino kuti woyang’anila ayenela kukhala “wodziŵa kuphunzitsa.” Kodi izi zitanthauza kuti muyenela kukhala mlankhuli waluso kwambili? Ayi. Pali akulu ambili ofikapo amene si alankhuli aluso kwenikweni, koma amaphunzitsa bwino mu ulaliki komanso pocita maulendo aubusa. (Yelekezelani na 1 Akorinto 12:​28, 29 komanso Aefeso 4:11.) Ngakhale n’telo, mufunika kupitiliza kukulitsa luso la kuphunzitsa. Kodi mungacite bwanji zimenezi?

16. Mungacite ciyani kuti mukulitse luso lanu la kuphunzitsa? (Onaninso cithunzi.)

16 “Wogwila mwamphamvu mawu okhulupilika.” Kuti muziphunzitsa mogwila mtima, muziseŵenzetsa Mawu a Mulungu pophunzitsa komanso popeleka uphungu. Kuti mucite zimenezi, muyenela kumaŵelenga Baibo komanso zofalitsa zathu mwakhama. (Miy. 15:28; 16:23.) Poŵelenga, muziyesetsa kuona mmene mungagwilitsile nchito Malemba m’njila yoyenela. Ndipo pamene mukuphunzitsa, muziyesetsa kuwafika pamtima omvela anu. Cinanso cingakuthandizeni kukulitsa luso lanu la kuphunzitsa, ni kupempha thandizo kwa akulu ena aluso, na kuyesetsa kucita zimene akuuzani. (1 Tim. 5:17) Akulu ayenela kukhala oti ‘angathe kulimbikitsa’ abale na alongo awo. Nthawi zina akulu ayenela kupeleka uphungu kwa abale na alongo, ngakhale ‘kuwadzudzula’ kumene. Komabe, nthawi zonse akulu ayenela kucita zimenezi mokoma mtima. Ngati ndinu wokoma mtima komanso wacikondi, ndipo mumaseŵenzetsa Mawu a Mulungu pophunzitsa, mudzakhala mphunzitsi waluso cifukwa mudzakhala mukutengela Mphunzitsi Wamkulu, Yesu.—Mat. 11:​28-30; 2 Tim. 2:24.

Mtumiki wothandiza akuphunzila kwa mkulu waluso mmene angaseŵenzetsele Baibo pophunzitsa. Mtumiki wothandizayo akudziyang’ana pagalasi pamene akuyeseza nkhani yake (Onani ndime 16)


PITILIZANI KUYESETSA KUTI MUKAYENELELE

17. (a) N’ciyani cingathandize atumiki othandiza kupitiliza kuyesetsa kuti akayenelele kukhala akulu? (b) Kodi akulu ayenela kukumbukila ciyani pamene akukambilana zoika m’bale kukhala mkulu? (Onani danga lakuti “ Khalani Ololela Pokambilana Zoika Munthu Paudindo.”)

17 Poona ziyenelezo zimene munthu ayenela kukwanilitsa kuti akhale mkulu, atumiki othandiza ena angaone kuti sangayenelele kutumikila monga akulu. Koma muzikumbukila kuti Yehova na gulu lake sayembekezela kuti mukwanilitse ziyenelezo zimenezi mmene munthu wangwilo angacitile. (1 Pet. 2:21) Ndipo ni mzimu wamphamvu wa Yehova umene ungakuthandizeni kukwanilitsa ziyenelezo zimenezi. (Afil. 2:13) Kodi mukuona kuti pali khalidwe lina lake limene mufunika kukulitsa? Ngati n’conco, m’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kucita zimenezo. Fufuzani zambili zokhudza khalidwelo, ndipo funsilani kwa mmodzi wa akulu za mmene mungakulitsile khalidwelo.

18. Kodi atumiki othandiza onse akulimbikitsidwa kucita ciyani?

18 Conco, abale nonsenu, kuphatikizapo inuyo amene mukutumikila kale monga akulu, pitilizani kukulitsa makhalidwe amene takambilana m’nkhani ino. (Afil. 3:16) Kodi ndinu mtumiki wothandiza? Musaleke kupita patsogolo. Pemphani Yehova kuti akuphunzitseni na kukuumbani kuti mupitilize kucita zambili pomutumikila, komanso potumikila ena mumpingo. (Yes. 64:8) Mosakaika konse, Yehova adzakudalitsani pa zonse zimene mukucita kuti mukayenelele kukhala mkulu.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu