Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 46

NYIMBO 49 Tikondweletse Mtima wa Yehova

Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mtumiki Wothandiza?

Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mtumiki Wothandiza?

“Kupatsa kumaticititsa kukhala osangalala kwambili kuposa kulandila.”MAC. 20:35.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kulimbikitsa abale obatizika kuyesetsa kuti akayenelele kukhala atumiki othandiza.

1. Kodi mtumwi Paulo anali kuwaona bwanji atumiki othandiza?

 ATUMIKI othandiza amagwila nchito zofunika kwambili m’mipingo. N’zoonekelatu kuti mtumwi Paulo anali kuwaona kukhala ofunika amuna okhulupilika amenewa. Mwacitsanzo, m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Filipi, iye popeleka moni kwa akulu anachulanso atumiki othandiza.—Afil. 1:1.

2. Kodi m’bale Luis amamva bwanji kutumikila monga mtumiki wothandiza?

2 Abale ambili, kaya akhale acikulile kapena acinyamata, amapeza cimwemwe cacikulu potumikila monga atumiki othandiza. Mwacitsanzo, Devan anali na zaka 18 pamene anaikidwa kukhala mtumiki wothandiza. Koma m’bale Luis anakhala mtumiki wothandiza ali na zaka za m’ma 50. Kodi m’bale Luis amamva bwanji kutumikila monga mtumiki wothandiza? Mofanana na atumiki othandiza ambili, iye anati: “Nimapeza cimwemwe cosefukila cifukwa cotumikila monga mtumiki wothandiza, maka-maka nikaganizila cikondi cimene abale na alongo amanionetsa.”

3. Tikambilane mafunso ati m’nkhani ino?

3 Ngati ndinu m’bale wobatizika ndipo sindinu mtumiki wothandiza, kodi mungadziikile colinga codzakhala mtumiki wothandiza? N’ciyani cingakulimbikitseni kucita zimenezi? Nanga ni ziyenelezo ziti za m’Malemba zimene muyenela kuzikwanilitsa kuti mukakhale mtumiki wothandiza? M’nkhani ino, tikambilane mayankho a mafunso amenewa. Koma coyamba tiyeni tikambilane nchito zimene mtumiki wothandiza amagwila.

KODI MTUMIKI WOTHANDIZA AMAGWILA NCHITO ZITI?

4. Kodi mtumiki wothandiza amagwila nchito ziti? (Onaninso cithunzi.)

4 Mtumiki wothandiza ni m’bale wobatizika amene amasankhidwa na mzimu woyela kuti athandize akulu mwa kugwila nchito zina zofunika mumpingo. Atumiki othandiza ena amathandiza ofalitsa kukhala na magawo okwanila komanso zofalitsa zoseŵenzetsa mu ulaliki. Ena amathandiza kusamalila Nyumba ya Ufumu kuti ikhale yosamalika bwino komanso yaukhondo. Atumiki othandiza ena amatumikila monga akalinde, akusaundi, komanso otambitsa mavidiyo pa misonkhano ya mpingo. Koma cofunika koposa, atumiki othandiza amakonda zinthu zauzimu, amakonda Yehova, ndipo amacita zinthu mogwilizana na mfundo zake zolungama. Iwo amakonda kwambili abale na alongo awo mumpingo. (Mat. 22:​37-39) Kodi m’bale wobatizika ayenela kucita ciyani kuti ayenelele kukhala mtumiki wothandiza?

Atumiki othandiza amatengela citsanzo ca Yesu potumikila ena modzipeleka (Onani ndime 4)


5. Kodi m’bale ayenela kucita ciyani kuti ayenelele kukhala mtumiki wothandiza?

5 Baibo imatiuza zimene m’bale ayenela kucita kuti ayenelele kukhala mtumiki wothandiza. (1 Tim. 3:​8-10, 12, 13) Kuti muyenelele utumiki umenewu, muyenela kuŵelenga ziyenelezo za m’Malemba zimenezi na kucita khama kuti muzikwanilitse. Koma coyamba muyenela kudzifufuza kuti mudziŵe colinga canu pofuna kukhala mtumiki wothandiza.

N’CIFUKWA CIYANI MUFUNA KUDZAKHALA MTUMIKI WOTHANDIZA?

6. N’ciyani ciyenela kukulimbikitsani kutumikila abale na alongo anu? (Mateyo 20:28; onaninso cithunzi .)

6 Ganizilani citsanzo cabwino koposa ca Yesu Khristu. Zilizonse zimene iye anacita, anazicita cifukwa cokonda Atate wake komanso anthu. Cikondi cimeneco cinamulimbikitsa kugwila nchito molimbika, komanso kucitila ena zinthu zimene zinali kuoneka zotsika. (Ŵelengani Mateyo 20:28; Yoh. 13:​5, 14, 15) Ngati mufuna kukhala mtumiki wothandiza cifukwa cokonda anthu komanso Mulungu, Yehova adzakuthandizani kukwanilitsa colinga canu.—1 Akor. 16:14; 1 Pet. 5:5.

Mwa citsanzo cake, Yesu anaphunzitsa atumwi ake kutumikila ena modzicepetsa m’malo mofuna malo apamwamba (Onani ndime 6)


7. N’cifukwa ciyani m’bale ayenela kupewa kukhala wodzikuza komanso wadyela?

7 Nthawi zambili, anthu m’dzikoli amakhumbila anthu amene amadziona apamwamba kuposa anzawo. Koma si mmene zilili m’gulu la Yehova. M’bale amene amakonda anthu monga mmene Yesu anali kucitila, sakhala na cikhumbo cofuna kulamulila ena kapena kufuna kuti azimuona wapamwamba. Ngati munthu amene amafuna kuti ena azimuona wapamwamba angapatsidwe udindo mumpingo, n’kutheka kuti angayambe kukana kugwilako nchito zina zooneka zotsika zimene angapatsidwe posamalila nkhosa zamtengo wapatali za Yehova. Iye sangamagwileko nchito zina cifukwa codziona kuti ni wapamwamba. (Yoh. 10:12) Yehova sadalitsa munthu amene amacita zinthu cifukwa codzikuza kapena cifukwa cadyela.—1 Akor. 10:​24, 33; 13:​4, 5.

8. Kodi Yesu anawapatsa uphungu wotani atumwi ake?

8 Panthawi ina, ngakhale mabwenzi apamtima a Yesu anafunapo maudindo pa zifukwa zadyela. Ganizilani zimene atumwi aŵili a Yesu, Yakobo na Yohane, anacita. Iwo anapempha Yesu kuti akawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Yesu sanakondwele nalo pempho lawo. M’malomwake, iye anauza atumwi onse 12 kuti: “Aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala woyamba pakati panu, akhale kapolo wa onse.” (Maliko 10:​35-37, 43, 44) Abale amene amatumikila ena na zolinga zabwino amakhala dalitso mumpingo.—1 Ates. 2:8.

N’CIYANI CINGAKULIMBIKITSENI KUTI MUFUNE KUDZAKHALA MTUMIKI WOTHANDIZA?

9. N’ciyani cingakulimbikitseni kufuna kukhala mtumiki wothandiza?

9 Mosakaika konse, Yehova mumam’konda ndipo ndinu ofunitsitsa kutumikila ena. Ngakhale n’conco, n’kutheka kuti mulibe cifuno cocitako nchito zowonjezela zimene atumiki othandiza amacita. Kodi n’ciyani cingakuthandizeni kufuna kugwilako nchito zimenezi? Muziganizila cimwemwe cimene mungakhale naco potumikila abale na alongo anu. Yesu anati: “Kupatsa kumaticititsa kukhala osangalala kwambili kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Ndipo iye mwini anatsatila mfundo imeneyi. Anapeza cimwemwe ceniceni potumikila ena, inunso mudzakhala acimwemwe mukatelo.

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali wofunitsitsa kutumikila ena? (Maliko 6:​31-34)

10 Tsopano tiyeni tikambilane citsanzo coonetsa kuti Yesu anali wofunitsitsa kutumikila ena. (Ŵelengani Maliko 6:​31-34.) Panthawi ina, Yesu na atumwi ake atalema ananyamuka kupita kumalo kwaokha kuti akapumule. Koma gulu la anthu linali litatsogola kale kumeneko pofuna kuti Yesu akawaphunzitse. Iye akanafuna, akanakana kuwaphunzitsa cifukwa iye na atumwi ake “analibe nthawi yopumula ngakhale yoti adye cakudya.” Akanafunanso, akanangowaphunzitsa mfundo imodzi kapena ziŵili za coonadi, n’kuwamasula kuti apite. Koma cifukwa cakuti anali kuwakonda, iye “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.” Ndipo anapitiliza kuwaphunzitsa mpaka “madzulo dzuŵa litatsala pang’ono kuloŵa.” (Maliko 6:35) Sanangocita zimenezi cifukwa n’zimene anafunika kucita, koma anatelo cifukwa “anawamvela cisoni.” Anafuna kuwaphunzitsa cifukwa cakuti anali kuwakonda. Yesu anapeza cimwemwe cacikulu potumikila ena.

11. Kodi Yesu anali kuwathandiza bwanji anthu? (Onaninso cithunzi.)

11 Yesu potumikila gulu la anthu lija, anawacitilanso zina kuwonjezela pa kuwaphunzitsa. Anasamalila zosoŵa zawo zakuthupi. Mozizwitsa, iye anaculukitsa cakudya ndipo anapatsa ophunzila ake kuti agaŵile anthuwo. (Maliko 6:41) Pocita zimenezi, anaphunzitsa ophunzila ake zimene angacite kuti atumikile ena. Anawaonetsanso kuti kuthandiza ena mwa njila imeneyi n’kofunika, monga mmene atumiki othandiza amacitila. Ganizilani cimwemwe cimene atumwiwo anali naco pothandiza kugaŵila cakudya cimene Yesu anali ataculukitsa mozizwitsa. Iwo anacita zimenezi mpaka “onse anadya n’kukhuta.” (Maliko 6:42) Ici n’citsanzo cimodzi cabe coonetsa nthawi pamene Yesu anaika zofuna za ena patsogolo. Ali padziko lapansi, iye anatumikila ena kwa moyo wake wonse. (Mat. 4:23; 8:16) Yesu anapeza cimwemwe pophunzitsa ena komanso posamalila zosoŵa za ena modzicepetsa. Mosakaikila, inunso mudzakhala na cimwemwe cacikulu pamene mukuyesetsa kukwanilitsa colinga canu codzakhala mtumiki wothandiza muli na zolinga zabwino.

Ngati mumakonda Yehova komanso mumafuna kutumikila ena, mudzakhala ofunitsitsa kulandila utumiki ulionse umene mungapatsidwe mumpingo (Onani ndime 11) a


12. N’cifukwa ciyani palibe aliyense mumpingo amene ayenela kudziona kuti ni wosafunika?

12 Ngati muona kuti mulibe luso lina lake lapadela, musalefuke. Mosakaikila, pali luso limene muli nalo lomwe lingakhale lothandiza mumpingo. Ganizilani zimene Paulo anakamba pa 1 Akorinto 12:​12-30, ndipo m’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kuona mmene zimenezi zigwilila nchito kwa inu. Mawu a Paulo amenewa amaonetsa kuti mtumiki wa Yehova aliyense, kuphatikizapo inuyo, ali na mbali yofunika imene angacite mumpingo. Ngati pali pano simukwanilitsa ziyenelezo zofunika kuti mukhale mtumiki wothandiza, musalefuke. M’malomwake, citani zonse zimene mungathe kuti mutumikile Yehova na abale anu. Dziŵani kuti akulu amakuganizilani, ndipo adzakupatsani utumiki uliwonse umene mungakwanitse kucita.—Aroma 12:​4-8.

13. N’cifukwa ciyani n’cosavuta kwambili kuti m’bale ayenelele kukhala mtumiki wothandiza?

13 Cina cimene cingakulimbikitseni kuti muyesetse kuyenelela kudzakhala mtumiki wothandiza ni ici: Makhalidwe ambili amene Baibo imakamba kuti atumiki othandiza ayenela kukhala nawo, ni amenenso Akhristu onse ayenela kukhala nawo. Akhristu onse ayenela kuyandikila Yehova, kukhala ofunitsitsa kupatsa ena, komanso kukhala umoyo umene umakondweletsa Mulungu. Conco n’kutheka kuti pali pano, muli nawo kale makhalidwe ambili ofunikila kuti mukhale mtumiki wothandiza. Kodi m’bale ayenela kucita ciyani maka-maka kuti akayenelele kukhala mtumiki wothandiza?

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUKAYENELELE KUKHALA MTUMIKI WOTHANDIZA

14. Kodi kukhala ‘wopanda cibwana’ kumatanthauza ciyani? (1 Timoteyo 3:​8-10, 12)

14 Tsopano tiyeni tikambilane ziyenelezo zochulidwa pa 1 Timoteyo 3:​8-10, 12. (Ŵelengani.) Mtumiki wothandiza ayenela kukhala ‘wopanda cibwana.’ Mawu amenewa angamasulidwenso kuti “kucita zinthu m’njila imene ingapangitse ena kumupatsa ulemu.” Izi sizitanthauza kusasekako kapena kucitako zinthu zina zosangalatsa. (Mlal. 3:​1, 4) Zitanthauza kuti muyenela kugwila nchito mwakhama kuti mukwanilitse maudindo anu onse. Mukamadziŵika kuti mumamalizitsa nchito imene mwapatsidwa ndipo mumaigwila bwino, abale na alongo adzakudalilani ndipo adzakulemekezani.

15. Kodi kukhala “wosanena paŵili” kumatanthauza ciyani? Nanga mawu akuti kukhala “wosakonda kupeza phindu mwacinyengo” atanthauza ciyani?

15 Kukhala “wosanena paŵili” kumatanthauza kuti muyenela kukhala woona mtima m’zokamba na zocita zanu. Kumatanthauzanso kuti muyenela kumakwanilitsa malonjezo anu na kupewa kucita zinthu mwaciphamaso. (Miy. 3:32) Kukhala “wosakonda kupeza phindu mwacinyengo” kutanthauza kuti muyenela kukhala woona mtima pocita malonda na ena komanso pa nkhani zokhudza ndalama. Simuyenela kuwadyela masuku pamutu Akhristu anzanu cifukwa ca ubale umene muli nawo, monga njila yopezelapo ndalama.

16. (a) Kodi mawu akuti “osamwa vinyo wambili” atanthauza ciyani? (b) Nanga kukhala na “cikumbumtima coyela” kutanthauza ciyani?

16 Mawu akuti “osamwa vinyo wambili” atanthauza kuti simuyenela kumwa moŵa mopitilila muyeso, kapena kudziŵika kuti ndinu cidakwa. Kukhala na “cikumbumtima coyela” kutanthauza kuti muyenela kumatsatila malamulo a Yehova paumoyo wanu. Pa cifukwa cimeneci, ngakhale kuti ndinu wopanda ungwilo, mumakhala na mtendele wa mumtima cifukwa cokhala paubale wabwino na Mulungu.

17. Kodi m’bale angaonetse bwanji kuti ni wodalilika pamene akuyesedwa ngati ali oyenelela? (1 Timoteyo 3:10; onaninso cithunzi.)

17 ‘Kuyesedwa ngati muli woyenelela’ kumatanthauza kuti muyenela kuonetsa kuti ndinu wodalilika mukapatsidwa zocita. Conco akulu akakupatsani nchito, muzitsatila malangizo awo pogwila nchitoyo, komanso muzitsatila malangizo amene gulu limapeleka okhudzana na nchitoyo. Akakupatsani nchito, muzitsimikiza kuti mwamvetsa zimene akufuna kuti mucite komanso kuti muyenela kuimaliza liti nchitoyo. Mukamagwila nchito iliyonse mwakhama, ena mumpingo adzaona zimenezi ndipo adzayamikila kupita kwanu patsogolo. Akulu, muzionetsetsa kuti mukuwaphunzitsa nchito abale obatizika. (Ŵelengani 1 Timoteyo 3:10.) Kodi mumpingo mwanu muliko abale obatizika a zaka 10 mpaka 14 kapena kucepelapo? Kodi amacita phunzilo la munthu mwini mokhazikika? Kodi nthawi zonse amapelekapo ndemanga pa misonkhano? Ndipo kodi amatengako mbali mokhazikika mu ulaliki? Ngati alimo, muziwapatsako nchito zimene angakwanitse kucita malinga na maluso awo komanso msinkhu wawo. Mwa kutelo, abale acinyamata amenewa adzakhala akuyesedwa kuti muone ngati ali oyenelela. Ndipo pamene adzakwanitsa zaka 17 mpaka 19, n’kutheka kuti adzayenelela kukhala atumiki othandiza.

Mwa kupatsa abale zocita mumpingo, akulu angayese abalewo kuti aone “ngati ali oyenelela” (Onani ndime 17)


18. Kodi kukhala ‘wopanda cifukwa cokunenezelani’ kutanthauza ciyani?

18 Kukhala ‘wopanda cifukwa cokunenezelani’ kutanthauza kuti munthu aliyense sangakuimbeni mlandu wakuti munacita colakwa cacikulu. Koma n’zotheka Mkhristu kunamizilidwa mlandu. Anthu ananamizilapo Yesu zinthu zabodza, ndipo iye anakamba kuti otsatila ake nawonso adzakumana nazo zimenezi. (Yoh. 15:20) Koma ngati muli na makhalidwe abwino monga mmene Yesu analili, mudzakhala na mbili yabwino mumpingo.—Mat. 11:19.

19. Kodi Baibo imatanthauza ciyani ikanena kuti abale ayenela kukhala “amuna a mkazi mmodzi”?

19 “Amuna a mkazi mmodzi.” Pamene Mulungu anamangitsa ukwati woyamba, ananena kuti ukwati uzikhala pakati pa mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi. Izi n’zimene Akhristu onse ayenela kutsatila. (Mat. 19:​3-9) Mwamuna wa Cikhristu sayenela kucita ciwelewele m’pang’ono pomwe. (Aheb. 13:4) Izi zitanthauza kuti nthawi zonse, m’bale ayenela kukhala wokhulupilika kwa mkazi wake. Ndipo ayenela kupewelatu kucita zinthu mokopana na akazi ena.—Yobu 31:1.

20. Kodi mwamuna angaonetse bwanji kuti amasamalila bwino banja lake?

20 “Oyangʼanila bwino ana awo ndi mabanja awo.” Ngati ndinu mutu wa banja, muziona udindo wanu kukhala wofunika kwambili, ndipo muzicita zonse zimene mungathe kuti muukwanilitse. Muzicititsa kulambila kwa pabanja mokhazikika. Kaŵili-kaŵili muzipita mu utumiki na mkazi wanu komanso ana anu mmene mungathele. Muzithandiza ana anu kulimbitsa ubwenzi wawo na Yehova. (Aef. 6:4) Mwamuna amene amakwanitsa kusamalila bwino banja lake, angasamalilenso mpingo.—Yelekezelani na 1 Timoteyo 3:5.

21. Ngati pali pano sindinu mtumiki wothandiza, kodi muyenela kucita ciyani?

21 Inu abale obatizika, ngati pali pano sindinu mtumiki wothandiza, conde ŵelengani nkhani ino mwacifatse, ndipo pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuti mukayenelele kukhala mtumiki wothandiza. Ŵelengani ziyenelezo za atumiki othandiza na kucita khama kuti muzikwanilitse. Kulitsani cikondi canu pa Yehova ndiponso pa abale na alongo anu, ndipo ganizilani cifukwa cake mufuna kuwatumikila. (1 Pet. 4:​8, 10) Mukayesetsa kuti mukayenelele kukhala mtumiki wothandiza, mudzapeza cimwemwe cacikulu cifukwa cotumikila banja lanu lauzimu. Pemphelo lathu n’lakuti, Yehova akudalitseni pamene mukuyesetsa kuti mukayenelele kukhala mtumiki wothandiza!—Afil. 2:13.

NYIMBO 17 “Nifuna”

a MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Cithunzi ca kumanzele cionetsa Yesu akutumikila anthu ena modzicepetsa. Cithunzi ca kulamanja cionetsa mtumiki wothandiza akuthandiza m’bale wacikulile wa mumpingo.