Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU

Pezani Malo Abwino Oŵelengela

Pezani Malo Abwino Oŵelengela

Kodi mufuna kuti muzipindula kwambili pocita phunzilo la munthu mwini? Yesani kucita zotsatilazi kuti muzipindula kwambili pamene muŵelenga:

  •  Pezani malo abwino. Ngati n’kotheka, pezani malo aukhondo komanso amene ali na kuwala kokwanila kuti muzitha kuona bwino. Ndipo mukhoza kuŵelengela pa thebulo kapena pa malo ena abwino panja.

  •  Pezani malo omwe mungakhale nokha. Yesu anali kupemphela “m’mamaŵa kukali mdima,” ndipo anali kupemphela “kwayekha.” (Maliko 1:​35) Ngati n’zosatheka kupeza malo akwanokha kuti muŵelenge, mungadziŵitse a m’banja lanu kapena amene mukhala nawo za ndandanda yanu yoŵelenga na kuwapempha kuti asakusokonezeni pamene mukuŵelenga.

  •  Ikani maganizo anu pa zimene mukuŵelenga. Pewani zimene zingakusokonezeni. Ngati mumagwilitsa nchito foni kapena tabuleti poŵelenga, muziika pa sailenti kuti isakusokonezeni. Ndiye mukaganizila nchito ina yake imene mufunika kugwila kapena kwina kwake kumene mufunika kupita, zilembeni pena pake. Maganizo anu akayamba kuyenda-yenda, pumulan’koni pang’ono. Pamene mukupumula mungayendeko kuti muwongoleko thupi.