Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Yehova Anatipatsa Nyonga Panthawi ya Nkhondo Komanso ya Mtendele

Yehova Anatipatsa Nyonga Panthawi ya Nkhondo Komanso ya Mtendele

Paul: Tinali na cimwemwe cacikulu! Munali mu November 1985, pamene tinali paulendo wopita ku Liberia, kumadzulo kwa Africa kukacita utumiki wathu woyamba wa umishonale. Ndeke imene tinakwela inaima m’dziko la Senegal. Anne anati: “Kwangokhala ola limodzi kuti tifike m’dziko la Liberia.” Kenako tinamva cilengezo cakuti: “Onse amene akupita ku Liberia atsike m’ndeke muno. Anthu ena m’dzikolo akufuna kulanda ulamulilo, n’cifukwa cake sitidzafikako.” Kwa masiku 10 otsatila, tinakhala ku Senegal na amishonale ena kumeneko. Tinali kumvetsela nyuzi za ku Liberia zakuti anthu ambilimbili aphedwa, ndiponso kuti boma silinali kulola anthu kucoka panyumba m’madzulo. Aliyense amene sanamvele lamulo limeneli anali kuphedwa.

Anne: Sindife anthu amene amafuna kukhala paulendo nthawi zonse. Ndipo nili mwana, n’nali kusamala kwambili pocita zinthu, moti anthu ananipatsa dzina lakuti Anne Wamantha. Nimacita mantha ngakhale pamene nikufuna kudutsa msewu! Koma tinali ofunitsitsa kupita ku Liberia kukacita utumiki wathu ngakhale kuti kucita zimenezo kukanaika moyo wathu pangozi.

Paul: Ine na Anne tinabadwila m’dela limodzi kumadzulo kwa England, ndipo tinali kukhala pamtunda wotalikilana makilomita 8. Makolo anga komanso amayi ake a Anne anali kutilimbikitsa kucita upainiya. Conco titangotsiliza sukulu, tonse tinayamba upainiya. Iwo anatithandiza kwambili kuti tithe kucita utumiki wa nthawi zonse. Nitakwanitsa zaka 19, n’naitanidwa kukatumikila ku Beteli. Kenako tinakwatilana na Anne mu 1982, ndipo anabwela kudzatumikila nane limodzi pa Beteli.

Titamaliza maphunzilo a Giliyadi pa September 8, 1985

Anne: Tinali kuukonda utumiki wa pa Beteli, koma tinalinso kufunitsitsa kukatumikila kumene kunali kufunikila alengezi ambili a Ufumu. Kugwila nchito pa Beteli limodzi na abale amene kale analipo amishonale, kunakulitsa cikhumbo cathu cofuna kukhala amishonale. Kwa zaka zitatu tinali kuipemphelela nkhaniyo usiku uliwonse. Conco mu 1985 tinasangalala kwambili pamene tinalandila ciitano cokaloŵa kalasi ya nambala 79 ya Giliyadi! Tinatumizidwa m’dziko la Liberia, kumadzulo kwa Africa.

CIKONDI CA ABALE NA ALONGO ATHU CINATILIMBIKITSA

Paul: Atapeleka cilolezo cakuti anthu angayambenso kuloŵa m’dziko la Liberia, tinakwela ndeke yoyamba yopita kumeneko. Anthu kumeneko anali akali na mantha aakulu, ndipo sanali kuloledwa kucoka panja m’madzulo. Anthu anali na mantha kwambili cakuti akangomva pokhoso la motoka anali kukuwa na kuthaŵa. Kuti tikhazike mitima yathu pansi tinali kuŵelengela limodzi buku la Masalimo usiku uliwonse. Ngakhale kuti zinthu zinali zovuta m’dzikolo, tinali kuukonda kwambili utumiki wathu. Anne anali mmishonale, conco anali kupita kukalalikila tsiku lililonse. Koma ine n’nali kutumikila pa Beteli ndipo n’nali kusewenza pamodzi na m’bale John Charuk. a N’naphunzila zambili kwa iye cifukwa anali atakhala m’dziko la Liberia kwa nthawi yaitali, ndipo anali kudziŵa bwino komanso kumvetsa zovuta zimene abale na alongo anali kukumana nazo.

Anne: N’cifukwa ciyani sipanatenge nthawi kuti tiyambe kuukonda utumiki wathu wa ku Liberia? Cifukwa ca abale na alongo athu. Iwo anali acikondi, aubwenzi, komanso okhulupilika. Tinakhala paubwenzi wolimba ndipo anakhala banja lathu latsopano. Anatipatsa malangizo abwino otithandiza ndipo anatilimbikitsa mwauzimu. Ulaliki unali wosangalatsa kumeneko, zinali kuoneka ngati maloto. Anthu anali kukhumudwa tikacokapo mwamsanga pakhomo lawo. Anthu anali kukambilana mafunso a m’Baibo kulikonse kumene ali. Conco zinali zosavuta kwa ife kuyamba makambilano na anthuwo. Tinali na maphunzilo ambili a Baibo moti zinali kutivuta kupeza nthawi yophunzila nawo onse. Linalidi gawo locititsa cidwi!

YEHOVA ANATIPATSA MPHAMVU PAMENE TINALI NA MANTHA

Tikusamalila abale othaŵa kwawo pa Beteli ya ku Liberia mu 1990

Paul: Kwa zaka zinayi, m’dziko la Liberia munali mtendele. Koma zinthu zinasintha mwadzidzidzi mu 1989 pamene m’dzikolo munabuka nkhondo ya paciweniweni. Ndipo podzafika pa July 2, 1990, gulu la anthu oukila boma linalanda malo ena ake apafupi na Beteli. Izi zinacititsa kuti kwa miyezi itatu tisathe kulankhulana na aliyense amene anali kunja kwa dzikolo, kuphatikizapo a m’banja lathu komanso akulikulu lathu la padziko lonse. Kunali kucitika zipolowe pena paliponse, kunali kucepekela kwa zakudya, ndipo akazi anali kugonedwa mwacikakamizo. Mavutowo anapitilizabe kwa zaka 14 ndipo anakhudza dziko lonse la Liberia.

Anne: Anthu a mitundu yosiyana-siyana anali kumenyana komanso kuphana. Asilikali oukila anali paliponse m’misewu. Anavala zovala zacilendo komanso zocititsa mantha ndipo anali kuloŵa m’nyumba iliyonse na kutenga ciliconse cimene anali kufuna. Ena a iwo anali kunena kuti kupha anthu kunali ngati “kupha nkhuku.” Mitembo ya anthu inaunjikidwa pa malodibuloko ndipo ina inaunjikidwa pafupi na Beteli. Mboni zokhulupilika zinaphedwa, kuphatikizapo amishonale aŵili okondedwa.

Anthu oukila amenewa anali kupha munthu aliyense wocokela ku mitundu imene anali kudana nayo. Conco abale athu anaika miyoyo yawo paciswe pobisa abale na alongo ocokela ku mitundu imeneyi kuti awapulumutse. Nawonso amishonale komanso atumiki a pa Beteli, anathandiza kubisa abale na alongo awo. Abale na alongo ena amene anathaŵa kwawo anali kugona pazipinda zapansi za pa Beteli ndipo ena tinali kugona nawo m’zipinda zathu zapamwamba. M’cipinda mwathu tinali na anthu ena 7 a banja limodzi.

Paul: Tsiku lililonse, oukila aja anali kufuna kuloŵa m’Beteli kuti aone ngati tinali kubisa anthu ena. Nthawi iliyonse oukilawo akabwela, aŵili a ife anali kupita pageti ya Beteli kukakambilana nawo, pamene ena aŵili anali kukhala pa windo n’kumaona zimene zikucitika. Ngati abale aŵili amene apita pagetiwo aika manja awo onse kutsogolo, tinali kudziŵa kuti zonse zili bwino. Koma akaika manja awo kumbuyo, zinali kutanthauza kuti oukilawo ni aukali. Zikakhala conco, amene anali kuonelela pa windo, mwamsanga anali kuthamanga na kukabisa abale na alongo athu.

Anne: Tsiku lina, abale analephela kuletsa gulu lina la oukila amene anali aukali kuloŵa m’Beteli. Ine na mlongo wina tinakazikhomela m’bafa mmene munali khabadi yomwe inali na kacipinda kakang’ono kobisalilamo pansi pa mashelufu. Mlongo uja anazipapatiza mpaka analoŵa pakacipinda kameneko. Oukila aja ananilondola mpaka m’zipinda zapamwamba atanyamula mfuti zamphamvu kwambili. Iwo anagogoda mwaukali pacitseko. Mwamuna wanga Paul anayesa kuwaletsa kuti asaloŵe ndipo anaŵauza kuti: “Mkazi wanga akusambilamo mmenemo.” Pamene n’nali kutseka citseko ca kacipinda mmene mlongo uja anabisala, citsekoco cinasokosela. Ndipo kubweza zinthu pa mashelufu m’khabadi muja kunatenga nthawi. N’kutheka kuti oukilawo anayamba kudzifunsa kuti nikucita ciyani. N’nacita mantha moti thupi langa lonse linayamba kunjenjemela. N’nali kufunika kukhazika mtima pansi n’sanatsegule citseko, cifukwa kupanda kutelo, oukilawo akanaona kuti nili na mantha ndipo akanayamba kunikaikila. Kodi n’kanacita ciyani? Ninapemphela camumtima, ndipo n’nacondelela Yehova kuti anithandize. Kenako n’natsegula citseko ndipo n’nawapatsa moni modekha. Mmodzi wa iwo ananikankhila kumbali, ndipo anapita kukhabati ija n’kuitsegula. Kenako anayamba kucotsa zinthu zonse zimene zinali pa mashelufu. Sanakhulupilile atapeza kuti mulibe ciliconse. Iye na gulu lake anafufuzanso m’zipinda zina komanso m’cipinda copezeka pansi pamtenje. Koma sanapezemo ciliconse.

COONADI CINAPITILIZA KUWALA

Paul: Tinalibe cakudya cokwanila kwa miyezi. Nthawi zambili tinalibe cakudya ca m’maŵa, koma kulambila kwa m’maŵa kwa pa Beteli kunali ngati cakudya cathu ca m’maŵa. Tinali kudziŵa kuti kuŵelenga komanso kuphunzila Baibo, kunali kutipatsa mphamvu zopilila tsiku lililonse.

Tinali kudziŵa kuti ngati zakudya komanso madzi zingatithele, moti n’kufunika kucoka pa Beteli kuti tikafunefune zinthu zimenezi, sitikanakwanitsa kuteteza abale athu amene tinali kuwabisa. Zimenezi zikanacititsa kuti aphedwe. Nthawi zina Yehova anali kutisamalila m’njila yodabwitsa kwambili, komanso panthawi yoyenela. Izi zinali kutithandiza kucepetsa mantha amene tinali nawo.

Pamene zinthu zinali kuipilaipila m’dzikolo, m’pamene coonadi cinawala kwambili. Nthawi zambili abale na alongo anafunika kuthaŵa kuti apulumutse miyoyo yawo. Ngakhale n’telo, iwo anakhalabe olimba komanso osatekeseka m’cikhulupililo cawo. Abale ena anali kunena kuti kupilila kwawo panthawi ya nkhondo imeneyi, kunali “kuwakonzekeletsa kaamba ka cisautso cacikulu.” Akulu komanso abale acinyamata analimba mtima na kucita zilizonse zotheka pothandiza abale na alongo awo komanso kuwatsogolela. Abale na alongo amene anathaŵila kumalo ena anali kuthandizana, ndipo anayamba kulalikila kumalo kumeneko. Iwo anali kugwilitsa nchito ciliconse cimene apeza mthengo kuti apange Nyumba za Ufumu zazing’ono, n’kuyamba kucita misonkhano. M’nthawi zovuta zimenezo, abale na alongo anali kulimbikitsidwa akapita kumisonkhano. Ndipo kulalikila kunali kuwathandiza kupilila. Pamene tinali kuthandiza abale na alongo mwa kuwapatsa cakudya, zovala, komanso zinthu zina zofunikila, tinali kudabwa kuona kuti abale ambili anali kutipempha zola za mu ulaliki m’malo mwa zovala. Anthu ambili anali na cisoni cifukwa ca zimene anaona komanso kukumana nazo panthawi ya nkhondo. Conco anali ofunitsitsa kumvetsela uthenga wabwino. Iwo anadabwa poona kuti Mboni za Yehova zinali na cimwemwe komanso zinali kucita zinthu mwacikondi panthawi yovuta imeneyo. Mboni za Yehova zinali kuwala ngati nyale panthawi ya mdima imeneyo. (Mat. 5:​14-16) Kukangalika kwa abale na alongo athu, kunacititsa kuti ena mwa oukila ankhaza aja atembenuke n’kukhala abale athu.

YEHOVA ANATIMBILIKITSA PAMENE TINALI KUCOKA KU LIBERIA

Paul: Nthawi zina tinali kufunika kucoka m’dziko la Liberia, ndipo zimenezi zinacitika maulendo asanu. Maulendo atatu, tinacoka m’dzikolo kwa kanthawi, koma pa maulendo aŵili tinacoka kwa caka cathunthu. Mlongo wina amene anali mmishonale anafotokoza bwino m’mene tinali kumvela. Iye anati: “Tili ku Giliyadi, tinaphunzitsidwa kuti tiyenela kuwakonda na mtima wonse abale na alongo mu utumiki umene tapatsidwa, ndipo n’zimene tinacita. Conco pamene tinafunika kucoka na kusiya abale athu mu mkhalidwe wovuta umenewu, zinatipweteka kwambili ndipo zinali ngati mtima wathu ukusweka.” Koma tinakhalabe acimwemwe cifukwa tinali kuthandizabe abale a ku Liberia pamene tinali m’maiko ena apafupi.

Tinakondwela kubwelela ku Liberia mu 1997

Anne: Mu May 1996, ine na mwamuna wanga pamodzi na abale ena aŵili, tinayamba ulendo wocoka ku Liberia m’galimoto ya Beteli ndipo tinali na mapepala ofunika okamba za nchito yolalikila ku Liberia. Tinali kufunika kuyenda mtunda wa makilomita 16 pa galimoto, kuti tifike m’dela lina kumene zinthu zinaliko bwino m’tauni imene tinali. Panthawi yomweyo, dela lathu linaukilidwa. Anthu oukila boma aukali anawombela mfuti zawo m’mwamba ndipo anatiimika. Anacotsa atatu a ife m’galimoto ndipo anatenga galimoto imeneyo limodzi na mwamuna wanga Paul. Tinangoimilila titathedwa nzelu. Mosayembekezela, tinangoona Paul akubwela kucokela pa gulu la anthuwo ndipo anali kutuluka magazi kumutu kwake. Poyamba tinaganiza kuti wawombeledwa mfuti, kenako tinazindikila kuti ngati zinali conco sakanakwanitsa kuyenda. Mmodzi mwa oukila aja anamumenya pamene anali kumucotsa m’galimoto. Zokondweletsa n’zakuti kanali kacilonda kakang’ono.

Capafupi nafe panali galimoto ya asilikali aboma yodzala na anthu amantha. Tinali kufuna kukwela galimotoyo, koma popeza inali yodzala tinangogwilila tunsimbi twa m’mbali. Galimotoyo itayamba kuyenda, dalaivala anaithamangitsa pa liwilo lalikulu moti tinasala pang’ono kugwa. Tinam’pempha kuti aimilile, koma popeza kuti nayenso anali na mantha sanamvele. Tinagwilila mwamphamvu moti sitinagwe. Koma galimoto ija itafika kumene inali kupita, tinali otopa kwambili komanso matupi athu anali kunjenjemela cifukwa ca mantha. Zovala zathu zinada kwambili ndipo zinang’ambika-ng’ambika.

Paul: Kenako tinayang’anana ndipo sitinakhulupilile kuti tinali moyo. Capafupi nafe panali ndeke ya helikoputala imene inawombeledwa zipolopolo ndipo inali kuoneka monga ingapasuke. Ndeke imeneyo ni imene inali kudzatipeleka ku Sierra Leone tsiku lotsatila. Conco tinagona pa malopo. Titafika ku Sierra Leone, tinali okondwela kuti tinapulumuka. Koma tinali kudela nkhawa abale athu a Cikhristu a ku Liberia.

YEHOVA ANATIPATSA NYONGA KUTI TIPILILE ZOVUTA ZINA

Anne: Tinafika bwino ku Beteli mu mzinda wa Freetown, ku Sierra Leone. Ndipo abale kumeneko anatisamalila bwino. Koma n’nayamba kukumbukila zinthu zoipa zimene zinacitika ku Liberia. Tsiku lililonse, n’nali kucita mantha kuti kungacitike zinthu zoipa ndipo sin’nali kuganiza bwino. Sin’nali kukhulupilila kuti tili pamalo amtendele. Ndipo nthawi zambili usiku n’nali kuuka nikunjenjemela, kucoka thukuta, komanso kucita mantha kuti cina cake coipa cingacitike. N’nali kuvutika kupuma. Mwamuna wanga Paul anali kunikumbatila na kupemphela nane limodzi. Tinali kuimba nyimbo za Ufumu mpaka mtima wanga utakhala pansi. N’namva ngati nayamba kudwala matenda a maganizo, ndiponso kuti siningapitilize kutumikila monga mmishonale.

Sinidzaiŵala zimene zinacitika pambuyo pake. Mlungu umenewo tinalandila magazini aŵili. Imodzi mwa magazini amenewo inali Galamukani! ya Cingelezi ya June 8, 1996. Inali na nkhani yakuti “Kodi Mungacite Ciyani Ngati Mumavutika Kwambili Maganizo?Galamukani! imeneyo inanithandiza kumvetsa cifukwa cake ninali kuvutika kwambili maganizo. Magazini yaciŵili imene inanithandiza inali Nsanja ya Olonda ya May 15, 1996, imene inali na nkhani ya mutu wakuti “Kodi Nyonga Yawo Amaipeza Kuti?” mu Nsanja ya Olonda imeneyo munali cithunzi ca gulugufe amene limodzi mwa mapiko ake linali lowonongeka. Nkhaniyo inafotokoza kuti gulugufe amapitiliza kudya komanso kuuluka ngakhale kuti limodzi mwa mapiko ake n’lowonongeka. Conco nafenso ngakhale kuti ndife ofooka cifukwa ca zoipa zimene zinaticitikila, Yehova angatipatse mphamvu kuti tipitilize kuthandiza ena. Cimeneci cinali cakudya colimbikitsa cocokela kwa Yehova ndipo cinalidi ca panthawi yake. (Mat. 24:45) N’nafufuza nkhani zina zofanana na zimenezi ndipo n’naziika pamodzi. Nkhanizi zinanilimbikitsa kwambili. M’kupita kwa nthawi, vuto langa la kuvutika maganizo cifukwa cokumbukila zoipa zimene zinaticitikila, linayamba kucepa ndipo sin’nali kuvutikanso maganizo ngati kale.

YEHOVA ANATIPATSA MPHAMVU KUTI TILANDILE UTUMIKI WATSOPANO

Paul: Nthawi zonse tikacoka m’dziko la Liberia, tinali kukhala acimwemwe tikabwelela. Ndipo podzafika kumapeto kwa caka ca 2004, tinakhala kuti tacita utumiki wathu ku Liberia kwa zaka pafupifupi 20. Ndipo panthawiyo, nkhondo inali itatha. Panali mapulani akuti tiyambe kumanga ofesi ya nthambi. Koma mosayembekezela, tinapemphedwa kuti ticite utumiki wina watsopano.

Kucita zimenezi kunakhala kovuta kwa ife. Tinali kuwakonda kwambili abale na alongo athu a ku Liberia. Iwo anakhala ngati banja lathu, ndipo sitinali kufuna kuwasiya. Koma cifukwa cakuti tinaona mmene Yehova anatidalitsila, pomwe tinasiya acibale athu pamene tinapita ku Giliyadi, tinaulandila utumiki watsopano umenewo. Tinatumizidwa kukatumikila ku Ghana, dziko lomwe lili pafupi na Liberia.

Anne: Tinalila kwambili pamene tinali kucoka ku Liberia. Tinadabwa kwambili pamene m’bale wina wacikulile komanso wanzelu dzina lake Frank anatiuza kuti: “Muyenela kuiŵalako za ife!” Kenako anafotokoza momveka bwino kuti: “Tidziwa kuti simungatiiŵale, koma mufunika kuika mtima wanu wonse pa utumiki watsopano umene mwapatsidwa wocokela kwa Yehova. Conco muyenela kuŵakonda abale na alongo anu kumeneko.” Zimene m’baleyo anakamba zinatilimbikitsa pamene tinali kupita ku dziko limene zonse zinali zatsopano kwa ife, komanso komwe kunali anthu ocepa amene anali kutidziŵa.

Paul: Koma sipanatenge nthawi yaitali kuti tiyambe kulikonda banja lathu lauzimu latsopano ku Ghana. Kunali Mboni zambili kumeneko. Ndipo tinaphunzila zambili kwa mabwenzi athu atsopano pa nkhani yokhala okhulupilika komanso kukhala na cikhulupililo. Titatumikila ku Ghana kwa zaka 13, cinthu cina cimene sitinali kuyembekezela cinacitika. Tinauzidwa kuti tikatumikile ku ofesi ya nthambi ya kum’mawa kwa Africa m’dziko la Kenya. Ngakhale kuti tinawayewa kwambili mabwenzi amene tinasiya ku Liberia komaso ku Ghana, mwamsanga tinayamba kupanga mabwenzi atsopano na okhulupilila anzathu ku Kenya. Ndipo monga mmene zinalili ku Ghana komanso ku Liberia, tikali kutumikila m’gawo lalikulu kwambili lofunika kulalikidwa kuno ku Kenya.

Tili na mabwenzi atsopano m’gawo la nthambi la kum’mawa kwa Africa mu 2023

KUGANIZILA MAPINDU AMENE TAPEZA

Anne: Nakumanapo na zovuta zambili paumoyo wanga ndipo nthawi zina n’nali kucita mantha kwambili. Tikamakhala m’madela amene mukucitika zinthu zoopsa, kapena tikamakumana na zovuta paumoyo wathu, nthawi zina timadwala ndipo zimaticititsa mantha kapena kutivutitsa maganizo. Sitimayembekezela kuti tidzatetezedwa mozizwitsa ku zinthu zimenezi. Ngakhale pali pano, nikangomva kulila kwa mfuti, nimacita mantha kwambili ndipo manja anga amacita dzanzi. Koma naphunzila kuti niyenela kudalila thandizo limene Yehova amapeleka kuti atilimbikitse kuphatikizapo limene amapeleka kucokela kwa abale na alongo athu. Naphunzilanso kuti tikapitilizabe kucita zinthu zauzimu nthawi zonse, Yehova adzatithandiza kupitiliza kucita utumiki wathu.

Paul: Nthawi zina anthu amatifunsa kuti, “Kodi mumaukonda utumiki wanu?” Maiko angakhale okongola, koma nthawi zina zinthu zingasinthe n’kuyamba kucitika zinthu zoopsa. Conco, kodi n’ciyani cimene timakonda kwambili kuposa dziko lomwe tikutumikilako? Ni abale na alongo athu okondeka amene ali ngati banja lathu. Ngakhale kuti timasiyana kumene tinacokela, ndife anthu a maganizo amodzi. Tinali kuganiza kuti tinatumizidwa n’colinga cakuti tikawalimbikitse, koma m’ceniceni iwo ni amene anatilimbikitsa.

Nthawi zonse tikapita ku dziko lina timapeza abale athu. Ubale wathu wa padziko lonse n’cozizwitsa cocokela kwa Yehova. Malinga ngati tili mbali ya mpingo, timapeza banja komanso malo acitetezo. Sitikaikila kuti tikapitiliza kudalila Yehova, iye adzatipatsa mphamvu zimene tikufunikila.—Afil. 4:13.

a Onani mbili ya moyo wa m’bale John Charuk, m’nkhani yakuti “I Am Grateful to God and Christ,” mu Nsanja ya Mlonda ya Cingelezi ya March 15, 1973.