Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 45

NYIMBO 138 Kukongola kwa Imvi

Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba

Zimene Tiphunzilapo pa Mawu Othela Omwe Amuna Okhulupilika Anakamba

“Kodi si paja okalamba amakhala ndi nzelu, ndipo amene akhala moyo wautali si paja amamvetsa zinthu?”YOBU 12:12.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Kumvela Yehova Mulungu kudzatibweletsela madalitso pali pano komanso moyo wosatha m’tsogolo.

1. N’cifukwa ciyani tingapeze malangizo othandiza kucokela kwa acikulile?

 TONSEFE timafunika malangizo otithandiza popanga zisankho zofunika paumoyo. Nthawi zambili malangizowo tingawapeze kucokela kwa akulu mu mpingo, komanso kwa Akhristu anzathu okhwima kuuzimu. Ngati iwo ni acikulile kwambili kuposa ife, sitiyenela kukana malangizo awo poganiza kuti ni acikale-kale. Yehova akufuna kuti tizipeza malangizo othandiza kwa acikulile. Iwo akhala padziko lapansi kwa nthawi yaitali kuposa ife, ndipo adziŵa zambili zokhudza umoyo, amamvetsa zinthu, ndipo ali na nzelu.—Yobu 12:12.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

2 M’nthawi za m’Baibo, Yehova anaseŵenzetsa atumiki acikulile okhulupilika kulimbikitsa na kutsogolela anthu ake. Mwacitsanzo, iye anaseŵenzetsa Mose, Davide, na mtumwi Yohane. Iwo anakhalako pa nthawi zosiyana, ndipo zinthu paumoyo wawo zinali zosiyana kwambili. Cakumapeto kwa moyo wawo, iwo anapeleka malangizo anzelu kwa anthu ena. Ena mwa anthuwo anali ocepelapo msinkhu pa iwo. Aliyense wa amuna acikulile okhulupilika amenewa, anagogomeza kufunika kokhala womvela kwa Mulungu. Yehova analemba mawu awo anzelu m’Baibo kuti atithandize masiku ano. Kaya ndife acinyamata kapena acikulile, tingapindule mwa kuŵelenga malangizo awo. (Aroma 15:4; 2 Tim. 3:16) M’nkhani ino tikambilane mawu othela amene amuna atatu amenewa anakamba, komanso maphunzilo amene tingatengepo pa mawuwo.

“KUTI MUKHALE NDI MOYO KWA NTHAWI YAITALI”

3. Kodi Mose anacitapo mautumiki ati?

3 Mose anali wodzipeleka na mtima wake wonse potumikila Yehova. Iye anatumikilapo monga mneneli, woweluza, mkulu wa asilikali a nkhondo, komanso wolemba mbili. Mose anali kudziŵa zambili cifukwa ca zinthu zosiyana-siyana zimene zinamucitikilapo paumoyo wake. Iye anatulutsa mtundu wa Isiraeli mu ukapolo ku Iguputo, ndipo anaona zozizwitsa zambili za Yehova. Yehova anamuseŵenzetsa kulemba mabuku asanu oyambilila a m’Baibo, kuphatikizapo Salimo 90, ndipo mwinanso ndiye analemba Salimo 91. N’kuthekanso kuti ndiye analemba buku la Yobu.

4. Kodi Mose analimbikitsa ndani? Nanga n’cifukwa ciyani?

4 Mose atatsala pang’ono kumwalila, ali na zaka 120, anasonkhanitsa Aisiraeli onse kuti awakumbutse za zinthu zimene iwo anaona Yehova akuwacitila. Ena mwa anthu amene anali kumumvetsela anaona zizindikilo komanso zozizwitsa zimene Yehova anacita, komanso mmene anapelekela cilango kwa Aiguputo. Koma pamene zinthu zonsezi zinali kucitika, ena mwa iwo anali acinyamata. (Eks. 7:​3, 4) Iwo anaona pamene Yehova anagawa Nyanja Yofiila ndipo anadutsa pakati pa nyanjayo. Anaonanso pamene Yehova anagonjetsa magulu ankhondo a Farao. (Eks. 14:​29-31) Anaonanso mmene Yehova anawasamalila komanso kuwateteza m’cipululu. (Deut. 8:​3, 4) Ndipo pamene Aisiraeli anali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anatengelapo mwayi wowalimbikitsa anthuwo. a

5. Kodi mawu othela a Mose opezeka pa Deuteronomo 30:​19, 20 anawatsimikizila za ciyani Aisiraeli?

5 Kodi Mose anakamba ciyani? (Ŵelengani Deuteronomo 30:​19, 20.) Mtundu wa Isiraeli unali kuyembekezela kulandila zinthu zabwino kwambili m’tsogolo. Mothandizidwa na Yehova, Aisiraeli anali kudzakhala nthawi yaitali m’dziko limene iye anawalonjeza. Ndipo dzikolo linali lokongola komanso laconde. Powafotokozela za dzikolo, Mose anawauza kuti: Mudzapeza “mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu, yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyana-siyana zabwino zimene simunagwilile nchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu, komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu.”—Deut. 6:​10, 11.

6. N’cifukwa ciyani Mulungu analola mitundu ina kugonjetsa Aisiraeli?

6 Mose anapelekanso cenjezo kwa Aisiraeli. Anawauza kuti iwo anafunika kumvela malamulo a Yehova kuti apitilize kukhala m’dziko lokongola limenelo. Mose anawalimbikitsa ‘kusankha moyo’ mwa kumvela Yehova, komanso “kukhala okhulupilika kwa iye.” Koma Aisiraeli sanamvele Yehova. Conco m’kupita kwa nthawi Mulungu analola Asuri, kenako Ababulo, kuwagonjetsa na kuwatenga kupita nawo ku ukapolo.—2 Maf. 17:​6-8, 13, 14; 2 Mbiri 36:​15-17, 20.

7. Kodi tiphunzilapo ciyani pa mawu a Mose? (Onaninso cithunzi.)

7 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tikakhala omvela tidzapeza moyo wosatha. Mofanana na Aisraeli amene anatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, nafenso tangotsala pang’ono kuloŵa m’dziko latsopano limene Mulungu anatilonjeza. Posacedwa dziko lapansi lidzakhalanso paradaiso. (Yes. 35:1; Luka 23:43) Satana na ziŵanda zake sadzakhalaponso. (Chiv. 20:​2, 3) Sikudzakhalanso zipembedzo zonyenga zimene zimaphunzitsa mabodza ponena za Yehova. (Chiv. 17:16) Maboma a anthu amene amapondeleza anthu amene amawalamulila, nawonso sadzakhalakonso. (Chiv. 19:​19, 20) M’paradaiso simudzakhala anthu ocita zoipa. (Sal. 37:​10, 11) Anthu onse m’paradaiso adzamvela malamulo olungama a Yehova, conco pa dziko padzakhala mtendele na mgwilizano. Anthu onse adzakondana komanso kukhulupililana. (Yes. 11:9) Tikuziyembekezela mwacidwi zinthu zimenezi! Ndipo cina cabwino coposa zonsezi n’cakuti, tikamvela Yehova, tidzapitiliza kukhala na moyo m’paradaiso padziko lapansi. Tidzakhala na moyo osati kwa zaka mahandiledi cabe, koma kosatha.—Sal. 37:29; Yoh. 3:16.

Tikamamvela Yehova, tidzakhala na moyo m’paradaiso padziko lapansi, osati kwa zaka mahandiledi cabe, koma kosatha (Onani ndime 7)


8. Kodi lonjezo la moyo wosatha linathandiza bwanji mmishonale wina? (Yuda 20, 21)

8 Ngati tipitiliza kusunga lonjezo la Mulungu la moyo wosatha mu mtima mwathu, tidzayesetsa kukhalabe okhulupilika ngakhale tikumane na mavuto. (Ŵelengani Yuda 20, 21.) Lonjezo limeneli lingatithandizenso kugonjetsa zofooka zathu. M’bale wina amene anatumikila monga mmishonale ku Africa kwa nthawi yaitali, anakamba kuti nthawi zambili anali kufuna kucita zinthu zomwe sizingakodweletse Yehova. Iye anati: “Kuzindikila kuti kucita zimenezo kukananitayitsa mwayi wokakhala na moyo wosatha m’tsogolo, kunanithandiza kuti nikhale wofunitsitsa kugonjetsa vutolo. N’nali kucondelela Yehova mobweleza-bweleza kuti anithandize. Na thandizo lake, n’nakwanitsa kuligonjetsa vutolo.”

“ZINTHU ZIDZAKUYENDELA BWINO”

9. Ni zovuta ziti zimene Davide anakumana nazo paumoyo wake?

9 Davide anali mfumu ya anthu a Yehova, ndipo anali wokhulupilika kwa Mulungu. Iye anali kudziŵa kuimba, kulemba ndakatulo, anali msilikali, komanso mneneli. Davide anakumanapo na zovuta zosiyana-siyana paumoyo wake. Kwa zaka zambili iye anali kukhala umoyo wothaŵa-thaŵa, cifukwa Mfumu Sauli, amene anali kumucitila nsanje, anali kufuna kumupha. Atakhala mfumu, Davide anafunikanso kuthaŵa kuti apulumutse moyo wake cifukwa mwana wake Abisalomu anali kufuna kumulanda ufumu. Ngakhale kuti Davide anakumanapo na zovuta zonsezi, ndipo analakwitsapo zinthu zina, iye anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu mpaka kumapeto kwa moyo wake. Ponena za Davide, Yehova anati iye ni “munthu wapamtima panga.” Conco m’poyenela kumvetsela malangizo amene Davide anakamba!—Mac. 13:22; 1 Maf. 15:5.

10. N’cifukwa ciyani Davide anapeleka malangizo kwa mwana wake, Solomo, asanakhale mfumu?

10 Tiyeni tikambilane malangizo amene Davide anapatsa mwana wake Solomo, amene anali kudzamuloŵa m’malo. Yehova anasankha Solomo kuti amange kacisi, komanso kuti alimbikitse anthu kupitiliza kulambila Mulungu m’njila yoyenela. (1 Mbiri 22:5) Solomo anali kudzakumana na zovuta. Kodi Davide anamupatsa malangizo otani Solomo? Tiyeni tione.

11. Malinga na 1 Mafumu 2:​2, 3, kodi Davide anapeleka malangizo otani kwa Solomo? Nanga n’ciyani cinacitika Solomo atatsatila malangizowo? (Onaninso cithunzi.)

11 Kodi Davide anakamba ciyani? (Ŵelengani 1 Mafumu 2:​2, 3.) Davide anauza mwana wake kuti ngati adzamvela Yehova, zinthu zidzamuyendela bwino pa umoyo. Kwa zaka zambili, zinthu zinali kumuyendela bwino Solomo. (1 Mbiri 29:​23-25) Iye anamanga kacisi waulemelelo, analembako mabuku ena a m’Baibo, ndipo mawu ake amapezekanso m’mabuku ena a m’Baibo. Solomo anachuka cifukwa ca nzelu komanso cuma cimene anali naco. (1 Maf. 4:34) Koma monga mmene Davide anakambila, zinthu zikanapitiliza kumuyendela bwino Solomo malinga ngati anakhalabe womvela kwa Yehova Mulungu. N’zacisoni kuti m’kupita kwa nthawi, Solomo anayamba kulambila milungu ina. Yehova sanasangalale naye, conco analeka kumupatsa nzelu komanso kumuthandiza kuti apitilize kulamulila mwacilungamo.—1 Maf. 11:​9, 10; 12:4.

Mawu othela a Davide kwa mwana wake Solomo, amatithandiza kuona kuti tikakhala omvela kwa Yehova, iye adzatipatsa nzelu kuti tipange zisankho zabwino (Onani ndime 11-12) b


12. Kodi tiphunzilapo ciyani pa zimene Davide anakamba?

12 Kodi tiphunzilapo ciyani? Tikakhala omvela zinthu zidzatiyendela bwino paumoyo. (Sal. 1:​1-3) N’zoona kuti Yehova sanatilonjeze kutipatsa cuma komanso ulemelelo monga wa Solomo. Koma tikamamvela Mulungu wathu, iye adzatipatsa nzelu zimene zidzatithandiza kupanga zisankho zabwino. (Miy. 2:​6, 7; Yak. 1:5) Mfundo zake zingatithandize pamene tikupanga zisankho pa nkhani zokhudza nchito, maphunzilo, zosangalatsa, komanso ndalama. Kutsatila mfundo zake kudzateteza ubwenzi wathu na iye, ndipo tidzakhala na moyo wosatha. (Miy. 2:​10, 11) Kudzatithandizanso kukhala na mabwenzi abwino, komanso kukhala na banja lacimwemwe.

13. N’ciyani cinathandiza Carmen kupanga cisankho canzelu paumoyo?

13 Carmen wa ku Mozambique, anali kuganiza kuti maphunzilo apamwamba ni amene angamupatse umoyo wabwino. Conco iye anapita ku yunivesite, ndipo anayamba kucita maphunzilo a zomangamanga. Iye anakamba kuti: “N’nali kuzikonda zimene n’nali kuphunzila, koma zinali kunitengela nthawi yanga yoculuka komanso mphamvu zanga. N’nali kupita ku sukulu na nthawi ya 7:​30, ndipo n’nali kucokako na nthawi ya 18:00. N’nali kuvutika kupezeka kumisonkhano, ndipo ninayamba kufooka kuuzimu. Pansi pa mtima, ninazindikila kuti nikutumikila ambuye aŵili.” (Mat. 6:24) Mlongoyu anaipemphelela nkhaniyi ndipo anafufuza m’zofalitsa zathu. Iye anawonjezela kuti: “Pambuyo popatsidwa malangizo na akulu komanso amayi anga, ninasiya maphunzilo a ku yunivesite, ndipo ninayamba kutumikila Yehova mu utumiki wa nthawi zonse. Ninaona kuti n’napanga cisankho canzelu, ndipo ndine wokondwela kuti ninacita zimenezo.”

14. Kodi mfundo yaikulu yopezeka m’mawu a Mose na Davide ni yotani?

14 Mose na Davide anali kumukonda Yehova, ndipo anali kudziŵa kuti kumumvela n’kofunika kwambili. M’mawu awo othela, iwo analimbikitsa amene anali kuwamvetsela kutengela citsanzo cawo na kukhalabe okhulupilika kwa Yehova Mulungu wawo. Onse aŵili anacenjeza kuti amene sadzamvela Yehova sadzapitiliza kukhala mabwenzi ake, ndipo iye sadzawadalitsa. Malangizo awo ni othandizabe kwa ife masiku ano. Patapita zaka mahandiledi, mtumiki wina wa Yehova nayenso anaonetsa kufunika kokhalabe okhulupilika kwa Mulungu.

“CIMENE CIMANISANGALATSA KWAMBILI”

15. Ni zinthu ziti zimene mtumwi Yohane anaona paumoyo wake?

15 Yohane anali mtumwi amene Yesu Khristu anali kumukonda kwambili. (Mat. 10:2; Yoh. 19:26) Iye anagwila nchito yolalikila pamodzi na Yesu, ndipo anamuona akucita zozizwitsa. Yohane anakhalabe na Yesu m’nthawi zovuta. Anali kuona pamene Yesu anali kuphedwa, ndipo anamuonanso pamene anaukitsidwa. Anaonanso pamene Cikhristu cinali kufalikila m’zaka za zana loyamba, kucoka pa kagulu kocepa ka anthu okhulupilila mpaka pamene uthenga wabwino “unalalikidwa padziko lonse.”—Akol. 1:23.

16. Kodi ndani wapindula na makalata amene Yohane analemba?

16 Yohane anakhala moyo wautali, ndipo cakumapeto kwa moyo wake anauzilidwa kulembako ena mwa mabuku a m’Baibo. Iye analemba zinthu zocititsa cidwi zokhudza “chivumbulutso cimene Yesu Khristu anapeleka.” (Chiv. 1:1) Yohane analemba buku la Uthenga Wabwino lodziŵika na dzina lake. Ndipo analembanso makalata atatu ouzilidwa. Kalata yake yacitatu anali kulembela Mkhristu wina wake wokhulupilika dzina lake Gayo, amene anali kumuona ngati mwana wake wakuuzimu wokondeka. (3 Yoh. 1) N’kutheka kuti panthawiyo, panalinso ena ambili amene Yohane anali kuwaona ngati ana ake akuuzimu. Zimene mtumiki wokhulupilikayo analemba atakalamba, zakhala zikulimbikitsa otsatila onse a Yesu kufikila masiku ano.

17. Malinga na 3 Yohane 4, n’ciyani cimabweletsa cimwemwe cacikulu?

17 Kodi Yohane analemba ciyani? (Ŵelengani 3 Yoh. 4.) M’kalata yake yacitatu, Yohane analemba za cimwemwe cimene cimabwela munthu akakhala womvela kwa Mulungu. Panthawiyo, anthu ena anali kufalitsa ziphunzitso zabodza na kubweletsa magaŵano mumpingo. Ngakhale n’telo, ena anali ‘kuyendabe m’coonadi.’ Iwo anali kumvela Yehova ndipo anali “kuyenda motsatila malamulo ake.” (2 Yoh. 4, 6) Zimene Akhristu okhulupilikawo anacita, zinasangalatsa Yohane komanso Yehova.—Miy. 27:11.

18. Kodi tiphunzilapo ciyani pa mawu a Yohane?

18 Kodi tiphunzilapo ciyani? Kukhala wokhulupilika kumabweletsa cimwemwe. (1 Yoh. 5:3) Mwacitsanzo, timakhala acimwemwe podziŵa kuti timakondweletsa Yehova. Yehova amakondwela tikakaniza mayeselo a dzikoli na kutsatila malamulo ake. (Miy. 23:15) Nawonso angelo kumwamba amasangalala. (Luka 15:10) Nafenso timakhala acimwemwe tikaona Mkhristu mnzathu akukhalabe wokhulupilika, maka-maka akamazunzidwa kapena akayesedwa kucita zoipa. (2 Ates. 1:4) Ndipo dongosolo loipali likadzapita, tidzakhala acimwemwe podziŵa kuti tinakhala okhulupilika kwa Yehova m’dziko lolamulidwa na Satana.

19. Kodi mlongo Rachel anakamba ciyani pa nkhani ya kuphunzitsa ena coonadi? (Onaninso cithunzi.)

19 Timakhalanso na cimwemwe cacikulu tikamauzako ena coonadi. Rachel amene akhala ku Dominican Republic, amaona kuti ni mwayi wosaneneka kuphunzitsa munthu za Yehova Mulungu wathu wabwino amene timatumikila. Ponena za ana ake akuuzimu, iye anati: “Nimacita kusoŵa mawu amene ningaseŵenzetse pofotokoza cimwemwe cimene nimakhala naco nikaona anthu amene nikuphunzitsa Baibo akukulitsa cikondi cawo pa Yehova, kumukhulupilila, komanso kupanga masinthidwe paumoyo wawo kuti amukondweletse. Cimwemwe cimeneci, cimaposa zilizonse zimene ninacita komanso kudzimana kuti niwaphunzitse.”

Timapeza cimwemwe tikamaphunzitsa ena kukonda Yehova na kumumvela (Onani ndime 19)


TENGAM’PONI PHUNZILO PA MAWU OTHELA OMWE AMUNA OKHULUPILIKA ANAKAMBA

20. Kodi timafanana m’njila ziti na Mose, Davide, komanso Yohane?

20 Papita nthawi yaitali kwambili kucokela pamene Mose, Davide, na Yohane anali na moyo padziko lapansi. Ndipo panthawi imene anali moyo, zinthu zinali zosiyana kwambili na mmene zilili masiku ano. Ngakhale n’telo, pali zambili zimene timafanana nawo. Iwo anali kutumikila Mulungu woona. Nafenso n’zimene timacita. Mofanana na iwo, timapemphela kwa Yehova, timamudalila, ndipo timayang’ana kwa iye kuti atitsogolele. Ndipo monga mmene zinalili na amuna akale amenewa, nafenso timakhulupilila kuti Yehova amadalitsa anthu amene amamumvela.

21. Kodi anthu amene amatsatila malangizo a atumiki akale okhulupilika monga Mose, Davide, na Yohane adzapeza madalitso otani?

21 Conco, tiyeni tipitilize kumvela malamulo a Yehova. Tikatelo tidzakhala tikutsatila zimene amuna akale amenewa anakamba m’mawu awo othela. Ndipo tikacita zimenezi, zinthu zidzatiyendela bwino mu zonse zimene tikucita. ‘Tidzakhala na moyo kwa nthawi yaitali,’ inde kwamuyaya! (Deut. 30:20) Tidzakhalanso na cimwemwe podziŵa kuti tikukondweletsa Atate wathu wacikondi wakumwamba amene amakwanilitsa malonjezo ake onse m’njila imene sitimaiyembekezela kapena kuiganizila.—Aef. 3:20.

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

a Aisiraeli ambili amene anaona cozizwitsa cimene Yehova anacita pa Nyanja Yofiila sanaloŵemo m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:​22, 23) Yehova anakamba kuti anthu onse a zaka 20 kupita m’tsogolo adzafela m’cipululu. (Num. 14:29) Komabe, Yoswa, Kalebe, komanso ena ambili amene anali asanakwanitse zaka 20, kuphatikizapo anthu ambili a fuko la Levi, anapulumuka. Iwo anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yehova pamene anawoloka Mtsinje wa Yorodano n’kuloŵa m’dziko la Kanani.—Deut. 1:​24-40.

b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kumanzele: Davide akupatsa mwana wake malangizo othela. Kulamanja: Abale na alongo akulandila malangizo ku Sukulu ya Apainiya