Zimene Zingakuthandizeni Kucita Phunzilo la Munthu Mwini Mokhazikika
KODI zimakuvutani kucita phunzilo la munthu mwini mlungu uliwonse? Kodi nthawi zina mumamva kuti simusangalala nako kuŵelenga Baibo? Tonsefe timamva conco nthawi zina. Koma ganizilani zinthu zina zimene timacita nthawi zonse, monga kusamba. Kusamba kumafuna nthawi na khama, koma pambuyo pake timamva bwino kwambili ndipo timatsitsimulidwa. Kuŵelenga Baibo nakonso kuli ngati ‘kusamba m’madzi a mawu a Mulungu.’ (Aef. 5:26) Tiyeni tikambilane zina zimene zingakuthandizeni:
Pangani ndandanda. Kuphunzila Baibo panokha ni cimodzi mwa zinthu “zofunikadi kwambili” cimene Mkhristu sayenela kunyalanyaza. (Afil. 1:10) Kuti musamaiŵale nthawi yanu yoŵelenga, lembani tsiku na nthawi imene muzicita phunzilo la munthu mwini papepala na kuliika pa malo amene mungamalione mosavuta. Mwina mungaliike pa bolodi kapena pa filiji. Kapenanso mungaike alamu pafoni yanu kuti izikukumbutsani kukatsala nthawi yocepa kuti muyambe kuŵelenga.
Sankhani nthawi na njila yophunzilila imene ingakukomeleni. Kodi mungakonde kumaŵelenga motani? Mwacitsanzo, kodi mungathe kumvetsa zimene mukuŵelenga ngati mungaŵelenge kwa ola limodzi popanda kupumula? Kapena kodi mungakonde kuŵelenga kwa nthawi yocepa koma pafupi-pafupi? Inu ndinu amene mungadziŵe zimene zingakukomeleni. Conco ganizilani mfundo zimenezi pamene musankha nthawi yoŵelenga. Ngati nthawi yoŵelenga yakwana koma mwagwa ulesi, mungayese kuŵelengako kwa mphindi 10 cabe. Ngakhale mutaŵelenga kwa mphindi 10 cabe, mungaphunzile zambili. Ndipo mukangoyamba kuŵelenga, mungasangalale na kufuna kupitiliza.—Afil. 2:13.
Pasadakhale sankhani nkhani zimene mufuna kuŵelenga. Ngati nthawi yanu yoŵelenga ikakwana m’pamene mumayamba kuganizila zimene mudzaŵelenga, ndiye kuti ‘simukugwilitsa nchito bwino nthawi yanu.’ (Aef. 5:16) Yesani kulemba nkhani zimene mungakonde kuŵelenga. Mwacitsanzo, ngati muli na funso limene simukulimvetsetsa, lembani funsolo pena pake. Ndipo nthawi zonse mukamaliza kuŵelenga, mungawonjezele zinthu zina papepala lanu lomwe munalembapo zimene mungakonde kuŵelenga.
Khalani okonzeka kusintha pakafunikila kutelo. Cofunika kwambili n’cakuti muzicita phunzilo la munthu mwini mlungu uliwonse. Kuti zimenezi zitheke, muyenela kusinthako tsiku na nthawi yoŵelenga pakakhala pofunikila. Mungasinthenso nkhani zimene mumaŵelenga kapena utali umene mumathela poŵelenga.
Timapindula kwambili tikamacita phunzilo la munthu mwini mlungu uliwonse. Timamuyandikila Yehova, timaphunzila kucita zinthu mwanzelu, ndipo timatsitsimulidwa.—Yos. 1:8.