NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA October 2016

Magazini ino ili na nkhani zophunzila kuyambila mlungu wa November 28 mpaka December 25, 2016.

MBILI YANGA

Kusiilana Citsanzo Cabwino

Cilimbikitso cocokela kwa Akhiristu ofikapo cingathandize ena kukwanilitsa zolinga zabwino. Thomas McLain asimba mmene ena anamusiila citsanzo cabwino na mmene iyenso anasiilako ena.

“Musaiŵale Kuceleza Alendo”

Kodi Mulungu amawaona bwanji alendo? Kodi mungathandize bwanji aliyense wa ku dziko lina amene ali mumpingo mwanu kukhala womasuka?

Khalanibe Auzimu Potumikila Mumpingo wa Cinenelo Cina

Kuteteza umoyo wanu wauzimu ndi wa banja lanu n’kofunika kwambili kwa Akhiristu. Koma ngati mutumikila mumpingo wa cinenelo cina, mudzakumana ndi zopinga.

Kodi ‘Mumasunga Nzelu Zopindulitsa’?

N’ciani cimasiyanitsa nzelu zopindulitsa na cidziŵitso ndi kumvetsa zinthu? Kudziŵa mmene zimasiyanilana n’kopindulitsa.

Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene Muyembekezela

Tingalimbikitsidwe kwambili ndi zitsanzo zabwino za anthu acikhulupililo, zakale ndi zatsopano. Mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu?

Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova

Kodi cikhulupililo n’ciani kweni-kweni? Nanga tingacionetse bwanji?

Kodi Mudziŵa?

M’nthawi ya atumwi, ni ufulu wabwanji umene Aroma anapatsa olamulila aciyuda ku Yudeya? Kodi n’zoona kuti kale munthu wina anali kubyala namsongole m’munda wa mnzake?