Kodi Mudziŵa?
M’nthawi ya atumwi, ni ufulu wabwanji umene Aroma anapatsa olamulila aciyuda ku Yudeya?
PANTHAWIYI, Yudeya anali kulamulidwa ndi Aroma, moimilidwa ndi bwanamkubwa pamodzi na gulu lake la asilikali. Udindo wa bwanamkubwayo unali kutengela Aroma misonkho kwa anthu na kukhazikitsa mtendele ndi dongosolo. Aroma anali kulanga aliyense amene waphwanya malamulo na kubweletsa msokonezo. Aroma anapatsa mphamvu atsogoleli a ndale kuti aziyang’anila zocitika mumzinda wawo.
Khoti Yapamwamba ya Ayuda inali kuweluza nkhani zokhudza malamulo aciyuda. Mu Yudeya monse munali makhoti ang’ono-ang’ono. Ndipo m’makhotiwo anali kuweluzilamo milandu ing’ono-ing’ono popanda Aroma kuloŵelelapo. Komabe, makhoti aciyuda sanapatsidwe mphamvu zakuti azipha zigaŵenga. Aroma okha ndiwo anali na mphamvu yocita zimenezo. Koma mosiyanako, mamembala a Khoti Yapamwamba ya Ayuda anaimba mlandu Sitefano, ndi kumupha mwa kum’ponya miyala.—Mac. 6:8-15; 7:54-60.
Conco, Khoti Yapamwamba ya Ayuda inapatsidwa ulamulilo waukulu. Koma Pulofesa Emil Schürer, anati: “Mphamvu zimene khotiyi inapatsidwa zinali na malile cifukwa Aroma anali kucita ciliconse cimene afuna popanda wina kuwaletsa, maka-maka ngati munthu walakwila boma. Mwacitsanzo, Kalaudiyo Lusiya, mkulu wa asilikali amene anali kulamulila, anateteza Paulo amene anali Mroma.”—Mac. 23:26-30.
Kodi n’zoona kuti kale anthu anali kubyala namsongole m’munda mwa munthu wina?
PA MATEYU 13:24-26, Yesu anati: “Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbeu zabwino m’munda wake. Koma anthu ali m’tulo, kunabwela mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole m’munda wa tiliguwo, n’kucoka. Tsopano mmelawo utakula ndi kutulutsa ngala, namsongole nayenso anaonekela.” Olemba mabuku ambili amakayikila ngati fanizo limeneli linali kukamba zinthu zimene zinali kucitikadi. Komabe, mabuku a zamalamulo a Aroma amakamba kuti zinali kucitikadi.
Dikishonale ina inati: “Kubyala namsongole m’munda wa munthu wina pofuna kumukhaulitsa . . . unali mlandu malinga ndi malamulo a Aroma. Lamulo limene anakhazikitsa pankhaniyi, lionetsa kuti khalidwe loipali linali kucitika kaŵili-kaŵili.” Pulofesa wa zamalamulo dzina lake Alastair Kerr anafotokoza kuti mu 533 C.E., Mfumu ya Roma Justinian, inafalitsa kope yokamba za malamulo a Aroma amene akatswili a zamalamulo anapanga (ca m’ma 100-250 C.E.). Malinga ndi kopeyo (Digest, 9.2.27.14), katswili wa zamalamulo dzina lake Ulpian anakambapo za mlandu umene wolamulila waciroma Celsus anaweluza. Panthawiyo, munthu wina anabyala namsongole m’munda wa mnzake cakuti zonse zimene mwinimunda anabyala zinawonongeka. Kopeyo inakambanso kuti oweluza anali kugamula ndalama zimene wolakwayo anayenela kulipila mwinimunda cifukwa ca zinthu zimene wawononga.
Conco, mkhalidwe woipawu umene unali kucitika mu ulamulilo wa Aroma uonetsa kuti fanizo limene Yesu anakamba linali loona.