Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene Muyembekezela

Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene Muyembekezela

“Cikhulupililo ndico ciyembekezo cotsimikizika ca zinthu zoyembekezeledwa.”—AHEB. 11:1.

NYIMBO: 81, 134

1, 2. (a) Kodi ciyembekezo ca Akhiristu oona cimasiyana bwanji na ciyembekezo ca anthu a m’dziko la Satana? (b) Ni mafunso ofunika ati amene tidzakambilana tsopano?

AKHIRISTU oona ali na ciyembekezo cabwino maningi. Tonse kaya ndife odzozedwa kapena a nkhosa zina, tiyembekezela kuona kukwanilitsika kwa colinga cimene Mulungu anali naco poyamba, ndi kuyeletsedwa kwa dzina lake. (Yoh. 10:16; Mat. 6:9, 10) Zimenezi n’zinthu zabwino ngako zimene munthu angayembekezele. Tiyembekezelanso kudzalandila moyo wosatha, wa “kumwamba kwatsopano” kapena wa pa “dziko lapansi latsopano.” (2 Pet. 3:13) Koma pali pano, tiyembekezela gulu la Mulungu kupitilizabe kukula.

2 Nawonso anthu amene ali kumbali ya dziko la Satana amakhala na ciyembekezo, koma amakayikila ngati zimene akuyembekezela zingacitike. Mwacitsanzo, ochova njuga mamiliyoni ambili amayembekezela kuti tsiku lina adzawina ndalama zambili, koma sakhala otsimikiza kuti angawinedi. Komabe, cikhulupililo ceni-ceni ni “ciyembekezo cotsimikizika” cimene Akhiristu ali naco. (Aheb. 11:1) Mwina mungadzifunse kuti, kodi ciyembekezo cingakhale bwanji cotsimikizika? Nanga ni mapindu abwanji amene mungapeze ngati mwakhala na cikhulupililo colimba pa zimene muyembekezela?

3. Kodi cikhulupililo ca Mkhiristu woona cimazikidwa pa mfundo iti?

3 Cikhulupililo si khalidwe limene anthu ocimwa amabadwa nalo, ndipo silibwela lokha. Mzimu woyela wa Mulungu ndiwo umathandiza Mkhiristu kukhala na cikhulupililo. (Agal. 5:22) Baibo sikamba kuti Yehova ali na cikhulupililo kapena kuti afunika kukhala na cikhululupilo. Popeza Yehova ni Wamphamvuyonse ndipo ni wanzelu zonse, palibe cingamulepheletse kukwanilitsa malonjezo ake. Atate wathu Wakumwamba ndi wotsimikiza kuti adzakwanilitsadi malonjezo ake, ndipo kwa iye zili ngati kuti akwanilitsidwa kale. Ndiye cifukwa cake anakamba kuti: “Zakwanilitsidwa!” (Ŵelengani Chivumbulutso 21:3-6.) Cikhulupililo ca Mkhiristu cimazikidwa pa mfundo yakuti Yehova ni “Mulungu wokhulupilika,” amene amakwanilitsa zimene walonjeza.—Deut. 7:9.

PHUNZILANI PA ZITSANZO ZA ANTHU AKALE ACIKHULUPILILO

4. Ni ciyembekezo canji cimene amuna ndi akazi akale acikhulupililo anali naco?

4 Chaputa 11 ca buku ya Aheberi cimachula maina 16 a amuna ndi akazi amene anali na cikhulupililo. Wolemba buku limeneli anakamba za iwo ndi ena kuti “anacitilidwa umboni cifukwa ca cikhulupililo cawo.” (Aheb. 11:39) Onse anali na “ciyembekezo cotsimikizika” cakuti Mulungu adzapeleka mbeu imene idzaphwanya Satana na kukwanilitsa colinga cake ca poyamba. (Gen. 3:15) Pamene Yesu Khiristu, amene ni “mbeu” yolonjezedwa, anatsegula njila yamoyo wakumwamba, anthu okhulupilika amenewa anali atafa kale. (Agal. 3:16) Koma cifukwa cakuti Yehova salephela kukwanilitsa malonjezo ake, anthu amenewa adzaukitsidwa na kukhala ndi moyo wangwilo m’paradaiso padziko lapansi.—Sal. 37:11; Yes. 26:19; Hos. 13:14.

5, 6. Kodi Abulahamu na banja lake anaika maganizo ake pa ciani? Nanga n’ciani cinawathandiza kukhalabe na cikhulupililo colimba? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)

5 Lemba la Aheberi 11:13, imakamba za anthu ena akale kuti: “Onsewa anafa ali ndi cikhulupililo, ngakhale kuti sanaone kukwanilitsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali ndi kuwalandila.” Mmodzi wa anthuwa anali Abulahamu. Kodi iye anali kuona cithunzi m’maganizo mwake ca umoyo wosangalatsa umene tidzakhala nawo cifukwa ca “mbeu” yolonjezedwa? Yesu anapeleka yankho yomveka bwino pamene anauza omutsutsa kuti: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezela kuona tsiku langa, ndipo analiona moti anakondwela.” (Yoh. 8:56) N’cimodzi-modzi na Sara, Isaki, Yakobo ndi ena ambili. Iwo anaika maganizo awo pa Ufumu wa kutsogolo, “umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.”—Aheb. 11:8-11.

6 N’ciani cinathandiza Abulahamu na banja lake kukhalabe na cikhulupililo colimba? Ayenela kuti anaphunzila za Mulungu mwa kumvetsela kwa acikulile okhulupilika, kwa Mulungu, kapena anali kuŵelenga mipukutu yakale yodalilika. Koposa zonse, iwo sanaiŵale zimene anaphunzila. Anali kukumbukila ndi kusinkha-sinkha malonjezo a Mulungu ndi malamulo ake. Cifukwa cakuti ciyembekezo cawo cinali cotsimikizika, amuna ndi akazi amenewa anali ofunitsitsa kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu olo akumane ndi mavuto abwanji.

7. Kuti atithandize kukhala na cikhulupililo colimba, Yehova watipatsa ciani mokoma mtima? Nanga tifunika kucita nazo bwanji?

7 Pofuna kutithandiza kuti tikhalebe na cikhulupililo colimba, Yehova mokoma mtima watipatsa mau ake Baibo. Kuti tikhale osangalala ndi kuti zinthu ‘zitiyendele bwino,’ tifunika kuŵelenga Mau a Mulungu tsiku lililonse ngati zingatheke. (Sal. 1:1-3; ŵelengani Machitidwe 17:11.) Ndiyeno, mofanana ndi alambili a Yehova akale, tifunika kupitiliza kusinkha-sinkha malonjezo a Mulungu ndi kumvela malamulo ake. Ifenso Yehova watidalitsa. Iye amatipatsa cakudya cauzimu coculuka kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Conco, ngati tiyamikila zimene tiphunzila m’zofalitsa zimene Yehova watipatsa, tidzafanana ndi anthu okhulupilika akale amene anali na “ciyembekezo cotsimikizika” ca Ufumu.

8. Kodi pemphelo lingalimbikitse bwanji cikhulupililo cathu?

8 Cina cimene cinathandiza anthu akale kukhalabe na cikhulupililo colimba, ni pemphelo. Akaona kuti Mulungu wayankha mapemphelo awo cikhulupililo cawo cinali kulimba. (Neh. 1:4, 11; Sal. 34:4, 15, 17; Dan. 9:19-21) Ifenso tingamuuze Yehova nkhawa zathu podziŵa kuti iye adzatimvela ndi kutilimbikitsa kuti tipilile mosangalala. Ndipo mapemphelo athu akayankhiwa, cikhulupililo cathu cimalimbilako. (Ŵelengani 1 Yohane 5:14, 15.) Popeza cikhulupililo ni khalidwe limene mzimu woyela umatulutsa, tifunika kupitiliza ‘kupemphabe’ mzimu wa Mulungu monga mmene Yesu anatiuzila.—Luka 11:9, 13.

9. Kuwonjezela pa kupempha zosoŵa zathu, kodi tifunika kupemphelelanso ndani?

9 Komabe, popemphela kwa Mulungu, sitiyenela kupempha cabe zinthu zaumwini yayi. Pali “zinthu zambili zodabwitsa” zimene ‘sitingathe kuzifotokoza zomwe Yehova amaticitila. Tingamuyamikile na kumutamanda tsiku lililonse cifukwa ca zinthuzo. (Sal. 40:5) Komanso, mapemphelo athu ayenela kuonetsa kuti ‘timakumbukila amene ali m’ndende ngati kuti tamangidwa nawo pamodzi.’ Tifunikanso kupemphelela abale athu padziko lonse, makamaka “amene akutsogolela pakati [pathu].” Mitima yathu imakhudzika tikaona mmene Yehova amayankhila mapemphelo athu.—Aheb. 13:3, 7.

SANAGONJE PA CIKHULUPILILO CAWO

10. Ni zitsanzo ziti za atumiki a Mulungu amene sanataye cikhulupililo? Nanga n’ciani cinawalimbikitsa kucita zimenezo?

10 M’caputa 11 ca Aheberi, mtumwi Paulo anachula mayeselo amene atumiki a Mulungu ambili osachulidwa maina anapilila. Mwacitsanzo, mtumwiyu anakamba za akazi acikhulupililo amene ana awo anafa. Pambuyo pake anawalandilanso pamene anaukitsidwa. Ndiyeno, anakambanso za anthu amene “sanalole kusiya cikhulupililo cawo kuti amasulidwe. Iwo anacita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambili.” (Aheb. 11:35) Ngakhale kuti sindife otsimikiza za anthu amene Paulo anali kukamba, ena monga Naboti na Zekariya, anaphedwa mwa kuponyedwa miyala cifukwa comvela Mulungu ndi kucita cifunilo cake. (1 Maf. 21:3, 15; 2 Mbiri 24:20, 21) Danieli na anzake anali na ufulu wosankha kusiya cikhulupililo cawo kuti amasulidwe. Koma cikhulupililo cawo mu mphamvu za Mulungu, cinawacititsa ‘kutseka mikango pakamwa’ ndi ‘kugonjetsa mphamvu ya moto, titelo kukamba kwake.’—Aheb. 11:33, 34; Dan. 3:16-18, 20, 28; 6:13, 16, 21-23.

11. Ni mayeselo ati amene aneneli ena anapilila cifukwa ca cikhulupililo cawo?

11 Cifukwa ca cikhulupililo cawo, aneneli monga Mikaya na Yeremiya ‘analandila mayeselo awo mwa kutonzedwa . . . ndi [kuikidwa] m’ndende.’ Enanso monga Eliya, “anayenda uku ndi uku m’zipululu, m’mapili, m’mapanga, ndi m’maenje a dziko lapansi.” Onsewa anapilila cifukwa anali na “ciyembekezo cotsimikizika ca zinthu zoyembekezeledwa.”—Aheb. 11:1, 36-38; 1 Maf. 18:13; 22:24-27; Yer. 20:1,  2; 28:10, 11; 32:2.

12. N’ndani anapeleka citsanzo copambana pa kupilila mayeselo? Ndipo n’ciani cinam’thandiza?

12 Pambuyo pochula amuna ndi akazi osiyana-siyana okhulupilika, Paulo anaunika citsanzo copambana onse—Ambuye wathu Yesu Khiristu. Pa Aheberi 12:2 pamati: “Cifukwa ca cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake, anapilila mtengo wozunzikilapo. Iye sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu.” Zoona, tifunika ‘kuganizila mozama’ citsanzo ca kukhulupilika kwa Yesu pokumana na mayeselo osiyana-siyana. (Ŵelengani Aheberi 12:3.) Mofanana ndi Yesu, Akhiristu oyambilila amene anafela cikhulupililo, monga wophunzila Antipa, sanagonje pa cikhulupililo cawo. (Chiv. 2:13) Iwo anali kuyembekezela mphoto yaciukililo ca moyo wakumwamba. Mphoto imeneyo inali yoposa “kuuka kwabwino kwambili,” kumene amuna akale okhulupilika anali kuyembekezela. (Aheb. 11:35) Pambuyo pa kukhadzikitsidwa kwa Ufumu mu 1914, odzozedwa okhulupilika onse amene anali m’manda anaukitsidwa ku moyo wauzimu kumwamba kuti akathandizane na Yesu kulamulila anthu padziko.—Chiv. 20:4.

ZITSANZO ZAMAKONO ZA CIKHULUPILILO

13, 14. Ni mayeselo ati amene Rudolf Graichen anakumana nawo? Nanga n’ciani cinam’thandiza kupilila?

13 Masiku ano, alambili a Mulungu ofika m’mamiliyoni, amatsatila citsanzo ca Yesu. Iwo amasumika maganizo pa ciyembekezo cawo, ndipo salola kuti mayeselo awafooketse. Ganizilani citsanzo ca Rudolf Graichen, amene anabadwila ku Germany mu 1925. Iye anakumbukila zithunzi za nkhani za m’Baibo zokoloŵeka ku cipupa m’nyumba mwake. Analemba kuti: “Pa cithunzi cina panali mmbulu ndi mwana wa nkhosa, mwana wa mbuzi na nyalugwe, mwana wa ng’ombe na mkango, zonse zili pamtendele. Ndipo mwana wamng’ono ndiye anali kuzitsogolela. . . . Siniiŵala zithunzi-thunzi zimenezo.” (Yes. 11:6-9) Ngakhale kuti Rudolf anazunzidwa kwa zaka zambili, koyamba ndi acipani ca Nazi, kaciŵili ndi a cipani ca Stasi ku East Germany, cikhulupililo cake sicinagwedezeke poyembekezela paradaiso padziko lapansi.

14 Mayeselo ena ovuta amene anagwela Rudolf ni kumwalila kwa amayi ake ndi matenda a pakhungu m’ndende ya ku Ravensbrück. Cina ni pamene atate ake anafooka m’cikhulupililo na kusaina cikalata coleka kukhala Mboni ya Yehova. Pamene anatuluka m’ndende, Rudolf anakhala na mwayi wotumikila monga woyang’anila dela. Pambuyo pake anaitanidwa ku Sukulu ya Giliyadi. Atatsiliza maphunzilo, anam’tumiza ku Chile monga mmishonale kumene anakatumikilanso monga woyang’anila dela. Kenako, anakwatila mmishonale mnzake Patsy. Komabe, mayeselo a Rudolf anali asanathe. Panangopita caka cimodzi mwana wawo wamkazi n’kumwalila. Komanso pambuyo pake, mkazi wake anamwalila ali na zaka 43 cabe. Rudolf anapilila mayeselo onsewa. Ngakhale kuti anali wokalamba ndi wathanzi lofooka, anali mpainiya komanso mkulu pamene nkhani ya mbili yake inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1997, masamba 20-25. [1]

15. Ni zitsanzo za Mboni za Yehova ziti zimene zikupilila mosangalala cizunzo?

15 Mboni za Yehova zimasangalalabe ndi ciyembekezo cawo ngakhale pamene zikuzunzidwa moopsa. Mwacitsanzo, abale na alongo athu ambili ali m’ndende ku Eritrea, Singapore, ndi South Korea, cifukwa amamvela mau a Yesu akuti osagwila lupanga. (Mat. 26:52) Pakati pa mahandiledi a abale athu amene ali m’ndende pali Isaac, Negede, ndi Paulos amene akhala m’ndende ya ku Eritrea kwa zaka zoposa 20. Ngakhale kuti abalewa alibe mwayi wosamalila makolo awo okalamba kapena wokwatila, ndipo amazunzidwa kwambili, sanagwedezeke pa cikhulupililo cawo. Mungaone mmene nkhope zawo zionekela zacimwemwe pa jw.org. Aonekelatu kuti asunga cikhulupililo cawo colimba. Ngakhale owayang’anila m’ndende afika powalemekeza kwambili.

Kodi mukupindula ndi zitsanzo za anthu okhulupilika a mumpingo mwanu? (Onani ndime 15, 16)

16. Kodi cikhulupililo colimba cingakutetezeni bwanji?

16 Si atumiki onse a Yehova amene akumana ndi mazunzo oopsa. Ena akumana ndi mayeso osiyanako. Ambili ni osauka kapena akuvutika cifukwa ca nkhondo ndi ngozi za cilengedwe. Ena atengela citsanzo ca Mose ndi makolo ake, mwa kusiya umoyo wabwino ndi wochuka. Iwo amacita zimene angathe kuti asabwelele ku umoyo wakale wokonda zinthu zakuthupi ndiponso wodzikonda. N’ciani cawathandiza kusintha? Asintha cifukwa cokonda Yehova ndiponso cifukwa ca cikhulupililo cawo colimba m’malonjezo a Yehova. Iye analonjeza kuti adzacotsapo kupanda cilungamo ndi kudalitsa atumiki ake okhulupilika mwa kuwapatsa moyo wosatha m’dziko latsopano la cilungamo.—Ŵelengani Salimo 37:5, 7, 9, 29.

17. Kodi ndinu ofunitsitsa kucita ciani? Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 M’nkhani ino, taphunzila mmene kusinkha-sinkha malonjezo a Mulungu na kupemphela nthawi zonse kungalimbitsile cikhulupililo cathu. Kucita zimenezi kudzatithandiza kupilila mayeselo pamene tisumika maganizo pa “ciyembekezo cotsimikizika” ca Cikhiristu. Koma cikhulupililo cimene Baibo imakamba, ciphatikizapo zambili. Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.

^ [1] (ndime 14) Onaninso nkhani yakuti “Despite Trials, My Hope Has Remained Bright” mu Galamukani! ya Cizungu ya April 22, 2002, imene ifotokoza mbili ya Andrej Hanák wa ku Slovakia.