Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Musaiŵale Kuceleza Alendo”

“Musaiŵale Kuceleza Alendo”

“Musaiŵale kuceleza alendo.”—AHEB. 13:2.

NYIMBO: 124, 79

1, 2. (a) Kodi alendo ambili amakumana na mavuto yabwanji masiku ano? (Onani pikica pamwamba.) (b) Kodi mtumwi Paulo akutikumbutsa ciani? Nanga zimenezi zibweletsa mafunso ati?

ZAKA zoposa 30 zapitazo, Osei wa ku Ghana [1] amene sanali Mboni panthawiyo, anayenda ku Europe. Iye anati: “N’naona kuti anthu ambili anali kuninyalanyaza. Nyengo nayo inali yozizila maningi. N’tacoka ku eyapoti, n’namvela kuzizila kumene sin’nakumvelepo cibadwile cakuti ninayamba kulila.” Cifukwa cosadziŵa bwino cinenelo, Osei sanapeze nchito yabwino kwa caka cimodzi. Popeza kuti banja lake linali kutali, anayamba kusungulumwa ndi kuyewa kunyumba.

2 Ganizilani zimene mukanakonda kuti ena akucitileni ngati munali mumkhalidwe wofanana ndi umenewo. Kodi simukanayamikila ngati akulandilani bwino ku Nyumba ya Ufumu, ngakhale kuti mwacokela kudziko lina kapena muli na khungu losiyanako? Baibo imalangiza Akhiristu eni-eni kuti: “Musaiŵale kuceleza alendo.” (Aheb. 13:2) Lomba tiyeni tikambilane mafunso otsatilawa: Kodi Yehova amawaona bwanji alendo? N’cifukwa ciani tingafunike kusintha mmene timaonela alendo? Kodi tingawathandize bwanji anthu ocokela ku maiko ena kukhala omasuka mumpingo mwathu?

MMENE YEHOVA AMAONELA ALENDO

3, 4. Malinga ndi Ekisodo 23:9, kodi Mulungu anauza anthu akale kuwaona bwanji alendo? Nanga n’cifukwa ciani?

3 Yehova atapulumutsa Aisraeli mu ukapolo ku Iguputo, anawapatsa malamulo. Malamulowo anaonetsa kuti iye anali kuganizila anthu amene sanali Aisraeli, omwe anayamba kulambila koona. (Eks. 12:38, 49; 22:21) Popeza kuti anthu anali kucitila tsankho alendo, Yehova anapeleka njila zowathandizila. Imodzi mwa njila zimenezo ni ufulu wokunkha za m’munda.—Lev. 19:9, 10.

4 Yehova anapempha Aisraeli kuti azikomela mtima alendo. (Ŵelengani Ekisodo 23:9.) Aisraeli anali kudziŵa “mmene zimakhalila ukakhala mlendo.” Ngakhale asanapite ku ukapolo, Aheberi anali kunyalanyazidwa ndi Aiguputo cifukwa ca kusiyana mtundu kapena kusankhana cipembedzo. (Gen. 43:32; 46:34; Eks. 1:11-14) Ngakhale kuti Aisraeli anali kuvutitsidwa pamene anali kudziko lacilendo, Yehova anawauza kuti aziona mlendo wokhala pakati pawo “ngati mbadwa.”—Lev. 19:33, 34.

5. N’ciani cingatithandize kuti tiziona anthu a ku maiko ena monga mmene Yehova amawaonela?

5 Ngakhale masiku ano, Yehova amaganizila anthu ocokela kumaiko ena amene amasonkhana mumpingo mwathu. (Deut. 10:17-19; Mal. 3:5, 6) Ngati tingadziŵe mavuto amene amakumana nawo monga kusankhidwa kapena kusadziŵa bwino cinenelo, tidzaona njila zimene tingawaonetsele cikondi na kuwakomela mtima.—1 Pet. 3:8.

KODI TINGAFUNIKILE KUSINTHA MMENE TIMAONELA ALENDO?

6, 7. N’ciani cionetsa kuti Akhiristu a m’zaka 100 anaphunzila kucotsa cidani?

6 Akhiristu a m’zaka 100 zoyambilila, anaphunzila kucotsa udani umene unakhazikika pakati pawo. Pa Pentekosite mu 33 C.E., Akhiristu okhala mu Yerusalemu analandila Akhiristu atsopano ocokela kumalo osiyana-siyana. (Mac. 2:5, 44-47) Cikondi cimene Akhiristu aciyuda anaonetsa kwa Akhiristu ocokela ku malo osiyana-siyana, cinaonetsa kuti anali kudziŵa tanthauzo la mau akuti “kuceleza,” amene amatanthauza kukomela mtima alendo.

7 Komabe, pamene mpingo wacikhiristu unali kukula, khalidwe la tsankho nalonso linayamba kukula. Ayuda okamba Cigiriki anadandaula kuti akazi amasiye awo anali kunyalanyazidwa. (Mac. 6:1) Pofuna kuthetsa vuto limeneli, atumwi anasankha amuna 7 okatsimikizila kuti aliyense asanyalanyazidwe. Amuna onse amene anasankhidwa, anali na maina a Cigiriki. Izi zionetsa kuti mwina atumwi anafuna kuthetsa mikangano imene iyenela kuti inabuka pakati pa Akhiristu oyambilila.—Mac. 6:2-6.

8, 9. (a) N’ciani cingaonetse kuti timacitila tsankho anthu a mtundu wina? (b) N’ciani cimene tifunika kucotselatu mumtima mwathu? (1 Pet. 1:22)

8 Kaya tidziŵa kapena ayi, kaonedwe kathu ka zinthu kamasonkhezeledwa ndi cikhalidwe ca kwathu. (Aroma 12:2) Mwina timamvela aneba, anzathu a kunchito, ndi a kusukulu, akukamba mau onyoza anthu a mtundu wina kapena a fuko lina. Timamvela bwanji tikaona zimenezi? Nanga timacita bwanji munthu wina akakamba mau osinjilila mbali zina za cikhalidwe ca kwathu?

9 Kwa kanthawi ndithu, mtumwi Petulo anali kucitila tsankho anthu amene sanali Ayuda. Koma m’kupita kwa nthawi anacotselatu tsankholo mumtima mwake. (Mac. 10:28, 34, 35; Agal. 2:11-14) Ifenso tikaona kuti tili na maganizo aliwonse a tsankho, kapena onyadila mtundu wathu, tifunika kuyesetsa kuwanyula mumtima mwathu. (Ŵelengani 1 Petulo 1:22.) Tizikumbukila kuti palibe aliyense amene anali kufunikila cipulumutso. Tonse ndife opanda ungwilo mosasamala kanthu kuti ndife a mtundu wanji. (Aroma 3:9, 10, 21-24) Ndiye ngati n’conco, pali cifukwa canji codzionela kuti ndife osiyana ndi ena? (1 Akor. 4:7) Tifunika kukhala na maganizo monga a mtumwi Paulo. Iye anauza Akhiristu anzake odzozedwa kuti: “Simulinso anthu osadziŵika kapena alendo m’dziko la eni, koma . . . a m’banja la Mulungu.” (Aef. 2:19) Ngati tiyesetsa kuona anthu mopanda tsankho, ndiye kuti tikuvala umunthu watsopano.—Akol. 3:10, 11.

MMENE TINGAKHALILE OKOMA MTIMA KWA ALENDO

10, 11. Kodi zimene Boazi anacitila Rute mkazi wacimoabu, zionetsa bwanji mmene Yehova amaonela alendo?

10 N’zosakayikitsa kuti zimene Boazi anacitila Rute mkazi wacimoabu zinaonetsa mmene Yehova amaonela alendo. Atapita kukayendela minda yake pa nthawi yokolola, Boazi anaona mkazi wacilendo akukunkha mwakhama m’mbuyo mwa anchito ake. Boazi atadziŵa kuti anacita kupempha kuti akunkheko, anamulola kukunkha ngakhale pa mitolo ya tiligu.—Ŵelengani Rute 2:5-7, 15, 16.

11 Zimene Boazi anakamba zionetselatu kuti anadela nkhawa Rute podziŵa kuti anali mlendo. Cina, Boazi anauza Rute kukhala pafupi ndi atsikana ake anchito kuti amuna amene anali kugwila nchito m’mundamo asamucite zacipongwe. Anamuuzanso kutenga cakudya ndi madzi okwanila mofanana ndi anchito ake. Kuwonjezela apo, Boazi sanakambe mau ofooketsa kwa mkazi wacilendoyu, m’malo mwake anamulimbikitsa.—Rute 2:8-10, 13, 14.

12. Kodi alendo angapindule bwanji ngati tiwakomela mtima?

12 Boazi anacita cidwi na cikondi ca Rute kwa mpongozi wake Naomi. Anacitanso cidwi kuona kuti wakhala mlambili wa Yehova. Kukoma mtima kwa Boazi kunaonetsa cisomo ca Yehova kwa mtsikana amene anathaŵila “m’mapiko mwa Mulungu wa Israeli kuti apeze citetezo.” (Rute 2:12, 20; Miy. 19:17) Nafenso masiku ano, kukoma mtima kwathu kungathandize “anthu kaya akhale a mtundu wotani” kudziŵa coonadi ndi kuona mmene Yehova amawakondela.—1 Tim. 2:3, 4.

Kodi timapatsa moni alendo akabwela pa Nyumba ya Ufumu? (Onani ndime 13, 14)

13, 14. (a) N’cifukwa ciani tifunika kuyesetsa kupatsa moni alendo amene asonkhana nafe? (b) Kodi mungathetse bwanji vuto losamasukila alendo?

13 Alendo ocokela kumaiko ena tingawaonetse kukoma mtima mwa kuŵapatsa moni mwacikondi pa Nyumba ya Ufumu. Mwina timaona kuti anthu ocokela kumaiko ena ndi amanyazi ndipo amadzipatula. Iwo akhoza kudziona osayenelela kukhala pakati pa mitundu ina cifukwa ca mmene analeledwela kapena cifukwa ca mmene zinthu zilli paumoyo wawo. Conco tifunika kuyamba kucitapo kanthu kuti tiwaonetse cikondi. Ngati muli na pulogilamu ya JW Language m’cinenelo canu, ingakuthandizeni kudziŵa mmene mungapatsile moni anthu ocokela ku maiko ena m’cinenelo cawo.—Ŵelengani Afilipi 2:3, 4.

14 Mwina mungakhale ndi vuto kumasukila anthu ocokela kudziko lina. Kuti mulithetse, mungafunike kuŵauza zinthu zina zokhudza inuyo. Mukacita zimenezi, mudzazindikila mwamsanga kuti mumafanana pa zinthu zina ngakhale kuti ndinu wosiyana mtundu. Paja cikhalidwe ciliconse cili na zabwino na zoipa zake.

THANDIZANI ONSE KUKHALA OMASUKA

15. N’ciani cidzatithandiza kuwamvetsetsa anthu amene akuzoloŵela dziko lacilendo?

15 Kuti muthandize ena kukhala omasuka mu mpingo, dzifunseni moona mtima kuti, ‘Sembe n’nali ku dziko lina, kodi nikanakonda kuti ena anicitile ciani?’ (Mat. 7:12) Muzicita zinthu moleza mtima ndi anthu amene akuyesetsa kuzoloŵela dziko lacilendo. Poyamba, sitingamvetsetse mmene amaganizila ndi mmene amacitila zinthu. Conco, m’malo mofuna kuti azicita zinthu mmene ife timacitila, bwanji osangowalandila mmene alili?—Ŵelengani Aroma 15:7.

16, 17. (a) Tingacite ciani kuti tidziŵane bwino na anthu ocokela ku maiko ena? (b) Tingawathandize m’njila ziti anthu ocokela ku maiko ena a mumpingo mwathu?

16 Tikaphunzila za dziko ndi cikhalidwe ca anthu ocokela ku maiko ena, cidzakhala copepuka kugwilizana nawo. Pakulambila kwathu kwa pabanja, tingapatule nthawi yofufuza zambili zokhudza anthu amene sitiwadziŵa bwino mu mpingo kapena m’gawo lathu. Njila ina imene ingatithandize kuti tidziŵane bwino na anthu ocokela ku maiko ena, ndi kuŵaitanila ku cakudya kunyumba kwathu. Yehova “anatsegulila anthu a mitundu ina khomo loloŵela m’cikhulupililo.” Kodi nafenso sitingatsegulile khomo anthu ocokela ku maiko ena amene ndi “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo”?—Mac. 14:27; Agal. 6:10; Yobu 31:32.

Kodi timaceleza alendo ocokela ku maiko ena? (Onani ndime 16, 17)

17 Kupeza nthawi yoceza na banja locokela ku dziko lina, kudzatipatsa mpata wabwino wowayamikila pa kuyesetsa kuti agwilizane ndi cikhalidwe cathu. Mwina tingazindikile kuti afunikila thandizo kuti adziŵe bwino cinenelo. Komanso, tingawathandize kupeza kumene kuli mabungwe m’dela lathu amene angawathandize kupeza nyumba yabwino kapena nchito. Kucita zimenezi kungathandize okhulupilila anzathu kukhala omasuka.—Miy. 3:27.

18. N’citsanzo citi cimene alendo angatengele poonetsa ulemu ndi kuyamikila?

18 Anthu ocokela ku maiko ena afunika kucita zimene angathe kuti agwilizane na cikhalidwe ca m’dziko lacilendo. Rute anapeleka citsanzo cabwino pa nkhani imeneyi. Coyamba, iye analemekeza miyambo ya m’dziko lacilendo, mwa kupempha cilolezo kuti akunkhe tiligu. (Rute 2:7) Rute anali na ufulu wokunkha, koma sanacite nawo dyela ufuluwo. Caciŵili anayamikila kukoma mtima kumene Boazi anamuonetsa. (Rute 2:13) Ngati alendo aonetsa khalidwe labwino limeneli, amalemekezedwa ndi anthu a m’dziko lacilendo, ndi okhulupilila anzawo.

19. N’cifukwa ciani tifunika kulandila alendo?

19 Timasangalala kuti Yehova mwacisomo cake, walola kuti anthu amitundu yosiyana-siyana amvele uthenga wabwino. N’kutheka kuti pamene anali kwawo, analibe mwayi wophunzila Baibo kapena wogwilizana ndi anthu a Yehova momasuka. Popeza tsopano ali na mwayi wogwilizana nafe, kodi sitingawathandize kuti asakhale ngati alendo pakati pathu? Ngakhale kuti tingakhale na ndalama kapena zinthu zocepa, zinthu zimene tingawacitile mokoma mtima zingawaonetse kuti Yehova amawakonda. Conco, monga ‘otsanzila Mulungu,’ tiyeni ticite zonse zimene tingathe kuti tizilandila alendo amene ali pakati pathu.—Aef. 5:1, 2.

^ [1] (ndime 1) Dzina talisintha.