Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Mau a Mulungu ndi amoyo”

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kodi “mau a Mulungu” amene lemba la Aheberi 4:12 limakamba kuti ndi “amoyo ndi amphamvu” n’ciani?

Mavesi ozungulila lemba limeneli, aonetsa kuti Paulo anali kukamba za uthenga kapena kuti colinga ca Mulungu cochulidwa m’Baibulo.

Nthawi zambili, lemba la Aheberi 4:12 limalembedwa m’zofalitsa zathu pofuna kuonetsa kuti Baibulo ili na mphamvu yosintha anthu. Mpake kuti lembali limagwilitsidwa nchito motele. Ngakhale zili conco, tiyeni tipende lembali mozamilapo. Paulo anali kulimbikitsa Akhiristu aciheberi kucita zinthu mogwilizana ndi colinga ca Mulungu. Colinga cimeneci cinalembedwa m’malemba oyela. Pofuna kufotokoza colingaco, Paulo anagwilitsila nchito citsanzo ca Aisiraeli amene anapulumutsidwa kwa Aiguputo. Iwo anali kuyembekezela dziko lolonjezedwa “loyenda mkaka ndi uci.” M’dzikolo akanapeza mpumulo weni-weni.—Eks. 3:8; Deut. 12:9, 10.

Ici cinali colinga ca Mulungu. Koma m’kupita kwa nthawi, Aisiraeli anaumitsa mitima yawo ndi kutaya cikhulupililo cawo. Conco, ambili analephela kuloŵa mu mpumulo umenewo. (Num. 14:30; Yos. 14:6-10) Komabe, Paulo anakamba kuti “lonjezo loloŵa mu mpumulo [wa Mulungu] lidakalipo.” (Aheb. 3:16-19; 4:1) Mwacionekele, lonjezo limeneli ni mbali ya colinga ca Mulungu. Monga mmene Akhiristu aciheberi anacitila, ifenso tingaŵelenge ndi kucita zinthu mogwilizana na colinga ca Mulungu cimeneci. Pofuna kuonetsa kuti lonjezo limeneli ndi la m’Malemba, Paulo anagwila mau ena a pa Genesis 2:2 ndi Salimo 95:11.

N’zolimbikitsa kudziŵa kuti “lonjezo loloŵa mu mpumulo [wa Mulungu] lidakalipo.” Ndipo tikhulupilila kuti n’zotheka kuloŵa mu mpumulo wa Mulungu umenewu. Tayamba kale kucita zoyenela kuti tiloŵemo. Koma sitinacite zimenezo mwa kumamatila Cilamulo ca Mose, kapena mwa kucita zinthu zina kuti Yehova atiyanje iyai. M’malomwake, timaloŵa mu mpumulowo mwa kupitiliza kucita zinthu mwacikhulupililo mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu. Ndipo monga mmene takambila poyamba, anthu masauzande ambili padziko lonse akuphunzila Baibulo ndi colinga ca Mulungu. Zimenezi zathandiza ambili kusintha umoyo wawo, kukhala ndi cikhulupililo colimba, ndi kubatizika. Kusintha kumene acita ni umboni wakuti “mau a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” Uthenga wa Mulungu wochulidwa m’Baibulo wakhudza kwambili umoyo wathu, ndipo udzapitilizabe kukhala wamphamvu pa ife.