Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cilimikani pa Kulimbana Kuti Mupeze Madalitso a Yehova

Cilimikani pa Kulimbana Kuti Mupeze Madalitso a Yehova

“Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo potsilizila pake wapambana.”—GEN. 32:28.

NYIMBO: 60, 38

1, 2. Kodi atumiki a Yehova amalimbana ndi ciani?

KUYAMBILA pa Abele, munthu woyamba wokhulupilika, alambili a Mulungu akhala akulimbana ndi mayeselo. Mtumwi Paulo analembela Akhiristu aciheberi kuti: “Munapilila mayeselo aakulu ndi masautso.” Iwo anacita izi pofuna kuti Yehova awayanje ndi kuwadalitsa. (Aheb. 10:32-34) Paulo anayelekezela mayeselo amene Akhiristu amalimbana nawo ndi maseŵela a mpikisano amene Agiriki anali kucita. Maseŵela amenewo anali kuphatikizapo mpikisano wothamanga, maseŵela ogwebana, ndi a nkhonya. (Aheb. 12:1, 4) Nafenso tili pa mpikisano wa ku moyo. Ndipo pa mpikisanowu, tikulimbana ndi adani amene afuna kuticenjeneka, kutigwetsa, kutigonjetsa, ndi kutilanda cimwemwe na mphoto ya mtsogolo.

2 Mdani wamkulu amene tikulimbana naye ni Satana ndi dziko lake loipa. (Aef. 6:12) Pa cifukwa cimeneci, tifunika kupewelatu “zinthu zozikika molimba” za m’dzikoli. Zinthu zimenezi ziphatikapo ziphunzitso zabodza, nzelu za anthu, makhalidwe oipa monga ciwelewele, kupepa fwaka, kukolewa, ndi mankhwala osokoneza ubongo. Kuwonjezela apo, tifunikanso kulimbana ndi zofooka zathu ndi zinthu zina zokhumudwitsa.—2 Akor. 10:3-6; Akol. 3:5-9.

3. Kodi Mulungu amatiphunzitsa bwanji kulimbana ndi adani athu?

3 Kodi adani amphamvu amenewa tingakwanitse kuwagonjetsa? Inde, koma tifunika kulimbikila. Pogwilitsila nchito citsanzo ca woponya nkhonya, Paulo anati: “Mmene ndikuponyela nkhonya zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi.” (1 Akor. 9:26) Monga mmene wankhonya amachingila kuti adziteteze kwa mdani wake, nafenso tifunika kudziteteza kwa adani athu. Yehova amatithandiza notiphunzitsa kuti tipambane. Amacita zimenezi mwa kutipatsa malangizo opatsa moyo kupitila m’Mau ake. Amatiphunzitsanso mwa zofalitsa zophunzilila Baibulo, misonkhano ya mpingo, ya dela, ndi ya cigawo. Kodi mumagwilitsila nchito zimene mumaphunzila? Ngati ayi, zidzakhala ngati ‘mukungomenya mphepo,’ ndipo mungalephele kugonjetsa adani anu.

4. Tiyenela kucita ciani kuti tisagonje ku coipa?

4 Adani athu angatiukile na kutigonjetsa panthawi imene tikugona mwauzimu. Conco tifunika kukhala maso nthawi zonse. Baibulo imaticenjeza kuti: “Musalole kuti coipa cikugonjetseni, koma pitilizani kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.” (Aroma 12:21) Mau akuti “musalole kuti coipa cikugonjetseni,” aonetsa kuti tingakwanitse kugonjetsa coipa. Izi zingatheke ngati tipitiliza kukhala ocilimika mwauzimu. Koma tikasiya, tingagonje kwa Satana, dziko lake, na zofooka zathu. Conco, musaope olo pang’ono pamene Satana akuwopsezani kuti mugonje.—1 Pet. 5:9.

5. (a) N’ciani cingatithandize kukhala ocilimika kuti tipeze madalitso a Mulungu? (b) Tidzakambilana za anthu ati ochulidwa m’Baibulo?

5 Kuti tipambane, tifunika kudziŵa ceni-ceni cimene tikulimbanilana ndi adani athu. Nthawi zonse, tiyenela kuganizila mfundo yolimbikitsa ya pa Aheberi 11:6, kuti Mulungu atiyanje ndi kutidalitsa. Mfundoyo imati: “Aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” Liu lacigiriki limene analimasulila kuti ‘kufunafuna ndi mtima wonse,’ limatanthauza kulimbikila. (Mac. 15:17) M’Baibulo, muli zitsanzo zolimbikitsa za amuna ndi akazi amene anacilimika kuti apeze madalitso a Yehova. Ena a iwo ni Yakobo, Rakele, Yosefe, na Paulo. Iwo anakumana ndi mavuto amene anawafooketsa maganizo ndi kuwalefula. Komabe, anapilila ndipo analandila madalitso osaneneka. Tingatengele bwanji citsanzo ca anthu anayi amenewa?

KUCILIMIKA KUMABWELETSA MADALITSO

6. N’ciani cinathandiza Yakobo kucilimika? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

6 Kholo lakale Yakobo, anacilimika cifukwa cokonda Yehova na zinthu zauzimu. Anakhulupililanso kwambili lonjezo la Yehova lakuti adzadalitsa mbeu yake. (Gen. 28:3, 4) N’cifukwa cake Yakobo atakwanitsa zaka pafupi-fupi 100, anacita zonse zotheka kuti akandile madalitso a Mulungu. Iye anacita kulimbana na mngelo amene anavala thupi laumunthu. (Ŵelengani Genesis 32:24-28.) Kodi Yakobo akanakwanitsadi kulimbana ndi mngelo wamphamvuyo? Iyai. Koma iye analimbikila kulimbana naye, ndipo sanafune kum’leka mngeloyo. Potsilizila pake, anadalitsidwa cifukwa colimbikila. Anapatsidwa dzina loyenelela lakuti Isiraeli, (kutanthauza “Wolimbana ndi Mulungu” kapena kuti “Mulungu Walimbana Nawe”). Yehova anadalitsa Yakobo kwambili. Nafenso tifuna kuti Mulungu atidalitse.

7. (a) Ni vuto lanji limene Rakele anali nalo? (b) Kodi anacilimika bwanji? Nanga anadalitsidwa bwanji?

7 Rakele, mkazi wa Yakobo, nayenso anali kuyembekezela mwacidwi kuona mmene Yehova adzakwanilitsila lonjezo lake kwa mwamuna wake. Ngakhale zinali conco, panali vuto limene linaoneka ngati sangaligonjetse. Iye sanali kubeleka. Panthawiyo, nkhaniyi inali yovutitsa maganizo kwambili. Kodi Rakele anakwanitsa bwanji kucilimika polimbana ndi vuto lalikululi? Iye sanataye mtima. M’malomwake, anacilimika mwa kucita khama kupemphela. Yehova anamvetsela mapembedzelo a Rakele, ndipo anam’dalitsa mwa kum’patsa ana. N’cifukwa cake panthawi ina, Rakele anakamba mokondwela kuti: “Ndalimbana mwamphamvu . . . ndipo ndapambananso.”—Gen. 30:8, 20-24.

8. Ni vuto lalikulu liti limene Yosefe anakumana nalo? Nanga citsanzo cake n’colimbikitsa bwanji kwa ife?

8 Mosakaikila, citsanzo cabwino ca Yakobo ndi Rakele cinathandiza mwana wawo Yosefe. Anaphunzila zimene angacite pokumana ndi mavuto oyesa cikhulupililo cake. Pamene Yosefe anali ndi zaka 17, umoyo wake unasintha kwambili. Cifukwa ca nsanje, abale ake anam’gulitsa monga kapolo. Ndiyeno, anapilila kwa zaka zambili m’ndende ku Iguputo pa mlandu umene sanacite. (Gen. 37:23-28; 39:7-9, 20-21) Yosefe sanafooke iyai, kapena kuwasungila cakukhosi abale ake. M’malomwake, anali kuganizila kwambili za unansi wake ndi Yehova. (Lev. 19:18; Aroma 12:17-21) Citsanzo ca Yosefe n’colimbikitsa kwa ife. Mwacitsanzo, ngati tinakumanapo ndi mavuto tili ana, kapena ngati pali pano tikukumana ndi mavuto amene amatisoŵetsa mtendele, tiyenela kupitiliza kupilila ndi kucilimika. Tikatelo, Yehova adzatidalitsa.—Ŵelengani Genesis 39:21-23.

9. Tiyenela kulimbikila kucita ciani kuti tipeze madalitso a Yehova, potengela citsanzo ca Yakobo, Rakele, ndi Yosefe?

9 Ganizilani zimene mukumana nazo, zimene zingakhale ciyeso kwa inu. Mwina pali anthu amene akukucitilani zinthu zoipa, kukupatulani, kapena kukunyozani. Mwinanso pali munthu wina amene akunamizilani zabodza cifukwa cokucitilani nsanje. M’malo mogonja ku ziyeso zimenezi, kumbukilani zimene zinathandiza Yakobo, Rakele, ndi Yosefe kupitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe. Yehova anawalimbikitsa ndi kuwadalitsa cifukwa cakuti anali kukonda kwambili zinthu zauzimu. Analimbikilabe kucita zinthu mogwilizana ndi mapemphelo awo. Popeza tili m’nthawi ya mapeto a dzikoli, tifunika kugwilitsitsa ciyembekezo cathu. Kodi mwatsimikiza mtima kuti mudzalimbana ndi mayeselo pofuna kupeza madalitso a Yehova?

CILIMIKANI KUTI MUPEZE MADALITSO

10, 11. (a) Ni mbali ziti zimene tingafunike kugonjetsa kuti tipeze madalitso a Mulungu? (b) N’ciani cidzatithandiza kusankha mwanzelu kuti tipambane polimbana ndi zinthu zofooketsa ndi zosokoneza utumiki wathu?

10 Ni mbali ziti zimene tingafunike kugonjetsa kuti tipeze madalitso a Mulungu? Mbali yoyamba imene anthu ambili akulimbana nayo ni zofooka zathupi. Ena afunika kupitiliza kucita khama kuti azikonda ulaliki. Mwina ena a inu mukupilila matenda kapena zoofoka zaukalamba, ngakhalenso kusungulumwa. Enanso angavutike kuti akhululukile munthu amene anawakhumudwitsa kapena kuwalakwila. Kaya tatumikila Yehova kwa zaka zingati, tonse tifunika kugonjetsa zinthu zimene zingasokoneze utumiki wathu kwa Mulungu, amene amapeleka mphoto kwa anthu okhulupilika.

Kodi mukucilimika pa kulimbana kuti mupeze madalitso a Mulungu? (Onani ndime 10, 11)

11 Nthawi zina, kusankha mwanzelu na kucita zinthu mwacikhiristu kungakhale kovuta. Zingakhale conco makamaka ngati mtima wathu wonyenga watisonkhezela kucita zosiyana. (Yer. 17:9) Ngati mwaona kuti penapake zinthu sizinayende bwino, pemphani mzimu woyela kuti ukutsogoleleni. Pemphelo ndi mzimu woyela zidzakuthandizani kusankha mwanzelu, ndipo Yehova adzadalitsa zosankhazo. Ndiyeno, muzicita zinthu mogwilizana ndi mapemphelo anu. Muziŵelenga Baibulo tsiku lililonse ndi kupatula nthawi yocita phunzilo laumwini ndi Kulambila kwa Pabanja.—Ŵelengani Salimo 119:32.

12, 13. N’ciani cinathandiza wacicepele ndi mlongo wina kugonjetsa zilakolako zoipa?

12 Tili na zitsanzo zambili zoonetsa mmene Mau a Mulungu, mzimu woyela, ndi mabuku athu zathandizila Akhiristu kugonjetsa zilakolako zoipa. Mwacitsanzo, wacicepele wina ataŵelenga nkhani yakuti “Kodi Mungalimbane Bwanji ndi Zilakolako Zoipa?” mu Galamukani! ya December 8, 2003, anakamba kuti: “Nimayesa-yesa kuti nigonjetse maganizo olakwika. N’taŵelenga kuti ‘kwa anthu ambili, nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa ndi yaikulu kwambili, n’naona kuti sinili nekha.” Wacicepele ameneyu anapindulanso ndi nkhani yakuti “Kodi Mulungu Amavomeleza Makhalidwe a Kugonana Kwachilendo?” mu Galamukani! ya October 8, 2003. Magazini imeneyo inakamba kuti vutoli kwa ena lili monga “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Ngati apitiliza kucilimika kuti akhale ndi khalidwe labwino, angakhale ndi cidalilo cakuti adzapambana. Wacicepeleyo anati: “Pa cifukwa cimeneci, niona kuti n’zotheka kukhala wokhulupilika tsiku lililonse. Niyamikila Yehova kwambili cifukwa coseŵenzetsa gulu lake kutipatsa malangizo othandiza kuti tikhale osiyana ndi dziko loipali.”

13 Ganizilani citsanzo cina ca mlongo wa ku America. Iye analemba kuti: “Nikuyamikilani cifukwa copitiliza kutipatsa malangizo amene tifunikila panthawi yake. Nthawi zambili, nimaona kuti nkhani ngati zimenezi amalembela ine. Kwa zaka zambili, nakhala nikulimbana ndi cizoloŵezi coipa cimene Yehova amadana naco. Nthawi zina, nimangofuna kuleka kumenya nkhondoyo. Nidziŵa kuti Yehova ni wacifundo ndipo amakhululukila. Koma cifukwa cakuti nikulimbanabe na cizoloŵezi coipa cimeneci ndipo sinisintha, nimaona kuti siningalandile thandizo lake. Vuto limeneli lakhudza kwambili umoyo wanga.  . . Pambuyo poŵelenga nkhani yakuti ‘Kodi Muli Ndi “Mtima Wodziŵa” Yehova?’ mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2013, n’naonadi kuti Yehova afuna kunithandiza.”

14. (a) Kodi Paulo anamvela bwanji polimbana ndi zilakolako zoipa? (b) N’ciani cingatithandize kupambana polimbana ndi zofooka zathupi?

14 Ŵelengani Aroma 7:21-25. Paulo anadzionela yekha mmene zimavutila kulimbana ndi zilakolako na zofooka za thupi lopanda ungwilo. Komabe, iye anali na cidalilo cakuti angapambane nkhondoyo mwa kupemphela kwa Yehova ndi kukhulupilila nsembe ya dipo la Yesu. Nanga bwanji ife? Nafenso tingapambane ngati tilimbikila kugonjetsa zofooka zathu. N’ciani cingatithandize kuti tipambane? Ni kudalila kwambili Yehova osati mphamvu zathu, komanso kukhulupilila dipo, monga mmene Paulo anacitila.

15. Kodi pemphelo limathandiza bwanji?

15 Nthawi zina, Mulungu angalole kuti tikumane ndi vuto linalake, kuti tionetse cikhulupililo cathu mwa iye. Mwacitsanzo, bwanji ngati inu, kapena m’bululu wanu, wadwala matenda aakulu, kapena wakumana ndi zinthu zina zoipa. Kodi tidzaonetsa kuti timakhulupilila Yehova mwa kum’pempha kuti atithandize kukhalabe okhulupilika ndi acimwemwe? (Afil. 4:13) Zitsanzo za anthu a m’nthawi ya Paulo ndi zamakono, zionetsa kuti kupemphela kumatithandiza kuti tikhalenso ndi mphamvu ndi kupilila.

CILIMIKANI PA KULIMBANA KUTI MUPEZE MADALITSO A YEHOVA

16, 17. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?

16 Mdyelekezi angakondwele kwambili ngati tingagonje. Conco, tiyeni tikhale otsimikiza mtima ‘kugwila mwamphamvu cimene cili cabwino.’ (1 Ates. 5:21) Tikatelo, tidzapambana polimbana ndi Satana, dziko lake, ndi zizoloŵezi zoipa. Tingapambane mwa kudalila thandizo la Mulungu.—2 Akor. 4:7-9; Agal. 6:9.

17 Citani ciliconse cotheka kuti mupitilize kukhala ocilimika. Khalani ndi cidalilo conse kuti Yehova ‘adzakukhuthulilani madalitso osoŵa powalandilila.’—Mal. 3:10.