Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuteteza Uthenga Wabwino Pamaso pa Akulu-akulu a Boma

Kuteteza Uthenga Wabwino Pamaso pa Akulu-akulu a Boma

“MUNTHU ameneyu ndi ciwiya canga cocita kusankhidwa cotengela dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu.” (Mac. 9:15) Mau amenewa anakambidwa ndi Ambuye Yesu. Apa anali kukamba za mwamuna wina amene anasintha n’kukhala Mkhiristu. Mwamuna waciyuda ameneyo anadzachedwa mtumwi Paulo.

Mmodzi wa “mafumu” amene Paulo anaima pamaso pake anali Nero, Mfumu ya Roma. Yelekezelani kuti mufunika kuteteza zimene mumakhulupilila pamaso pa mfumu yotelo. Kodi mungamvele bwanji? Akhiristu akulimbikitsidwa kutengela citsanzo ca Paulo. (1 Akor. 11:1) Iye anateteza uthenga wabwino pamaso pa akulu-akulu a boma a m’nthawi yake.

Aisiraeli anali kutsatila Cilamulo ca Mose, ndipo cilamuloco cinali kuthandiza Ayuda onse okhulupilika pa nkhani ya makhalidwe. Komabe, pambuyo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., olambila oona sanafunikenso kutsatila Cilamulo ca Mose. (Mac. 15:28, 29; Agal. 4:9-11) Ngakhale n’conco, Paulo ndi Akhiristu ena sananyoze Cilamulo cimeneco. Ndipo anali kulalikila m’madela ambili a Ayuda popanda cisokonezo. (1 Akor. 9:20) Iye nthawi zambili anali kulalikila m’masunagoge. Anali kulalikila anthu amene anali kudziŵa Mulungu wa Abulahamu, ndipo anali kukamba nawo mwa kuseŵenzetsa Malemba Aciheberi.—Mac. 9:19, 20; 13:5, 14-16; 14:1; 17:1, 2.

Atumwi anasankha Yerusalemu kukhala malo oyamba kulalikila. Ndipo iwo anali kuphunzitsa anthu m’kacisi nthawi zambili. (Mac.1:4; 2:46; 5:20) Mwa apa ndi apo, Paulo anali kupita ku Yerusalemu. Nthawi ina ali kumeneko anagwidwa. Kumeneku kunali kuyamba kwa kuimbidwa milandu imene inacititsa Paulo kufika mpaka ku Roma.

PAULO NDI MALAMULO A AROMA

Kodi akulu-akuku a boma la Aroma anaziona bwanji ziphunzitso zimene Paulo anali kulalikila? Kuti tipeze yankho, tiyenela kudziŵa mmene Aroma anali kuonela zacipembedzo. Aroma sanali kukakamiza anthu a mitundu ina kuleka cipembedzo cawo, pokhapo ngati cipembedzoco cicita zosemphana ndi boma kapena ngati sicicilikiza makhalidwe abwino.

Boma la Roma linapatsa Ayuda ufulu wambili. Buku lina linakamba kuti: “Ayuda anapatsidwa ufulu wambili m’boma la Roma. . . . Anali ndi ufulu wolambila, ndipo sanali kukakamizidwa kulambila milungu yaciroma. Iwo anali kukhala bwino-bwino motsatila cilamulo cawo.” (Backgrounds of Early Christianity) Ayuda sanali kukamizidwa kumenya nawo nkhondo. * Paulo anaseŵenzetsa ufulu umene Aroma anapatsa Ayuda, poteteza Cikhiristu pamaso pa akulu-akulu a boma la Aroma.

Adani a Paulo anayesetsa kucititsa anthu wamba komanso akulu-akulu a boma kuti aukile atumwi. (Mac. 13:50; 14:2, 19; 18:12, 13) Onani cocitika cimodzi ici. Akulu a mumpingo wa ku Yerusalemu anamva mphekesela zimene zinali kufalikila pakati pa Ayuda zakuti Paulo anali kalalikila anthu kuti “apandukile Cilamulo ca Mose.” Mabodzawa akanacititsa kuti Akhiristu aciyuda amene anangotembenuka kumene, aganize kuti Paulo sanali kulemekeza dongosolo la Mulungu. Komanso Khoti Lalikulu la Ayuda likanaona kuti Akhiristu akupandukila cipembedzo ca Ayuda. Ngati zotelozo zikanacitika, Ayuda amene anali kugwilizana na Akhiristu akanapatsidwa cilango, ndipo akanaletsedwa kulalikila m’kacisi ndi m’masunagoge. Conco, akuluwo analangiza Paulo kupita ku kacisi ndi kucita zinthu zimene zikanathetsa mabodzawo. Izi si zimene Mulungu anafuna kuti acite. Komabe, sizinali kuphwanya cilamulo ca Mulungu.—Mac. 21:18-27.

Paulo anacitadi zimenezi. Zimene anacitazi zinabweletsa mwayi ‘woteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo nchito ya uthenga wabwino.’ (Afil. 1:7) Pa kacisi, Ayuda anayamba kucita ciwawa, ndipo anafuna kupha Paulo. Mkulu wa asilikali aciroma anagwila Paulo. Pamene anafuna kum’kwapula, anafotokoza kuti anali nzika ya Roma. Aroma anali kulamulila Yudeya, ndipo likulu la Yudeya linali ku Kaisareya. Conco, Paulo anapelekedwa ku Kaisareya. Umenewu unali mwayi wapadela wakuti acitile umboni molimba mtima kwa akulu-akulu a boma. Izi zinapeleka mwayi wakuti anthu ena adziŵe zambili za Cikhiristu.

Caputa 24 ca Machitidwe, cifotokoza za Paulo pamene anapita kukaonekela kwa bwanamkubwa waciroma, Felike. Felike anali kulamulila Yudeya, ndipo panthawiyi anali atamvapo kale zimene Akhiristu amakhulupilila. Ayuda anaimba Paulo mlandu wophwanya malamulo a Aroma m’mbali zitatu. Iwo anakamba kuti Paulo akuyambitsa zoukila boma pakati pa Ayuda onse, akutsogolela gulu la mpatuko, ndi kuti akudetsa kacisi amene panthawiyo anali m’manja mwa Aroma. (Mac. 24:5, 6) Milandu yabodza imeneyi ikanacititsa kuti Paulo aphedwe.

Zimene Paulo anacita pa milandu yabodza zikutiphunzitsa mfundo zofunika. Iye anakhalabe wodzicepetsa ndi waulemu. Pokana milanduyo, Paulo anaseŵenzetsa Cilamulo ndi zolemba za aneneli. Anafotokozanso kuti unali ufulu wake wolambila ‘Mulungu wa makolo ake.’ (Mac. 24:14) Paulo anatetezanso uthenga wabwino ndi kulengeza za cikhulupililo cake kwa bwanamkubwa Porikiyo Fesito, ndi pamaso pa Mfumu Herode Agiripa.

Kuonjezela apo, kuti aweluzidwe mwacilungamo, Paulo ‘anapempha kuti akaonekele kwa Kaisara.’—Mac. 25:11.

PAULO AONEKELA PAMASO PA KAISARA M’KHOTI

Mngelo anauza Paulo kuti “Uyenela kukaima pamaso pa Kaisara.” (Mac. 27:24) Kuciyambi kwa ulamulilo wake, Nero, Mfumu ya Roma, anakambilatu kuti sadzaweluza milandu yonse payekha. Ndipo kwa zaka 8 zoyambilila, iye anali kuweluza milandu ndi anthu ena. Buku lina linakamba kuti Mfumu Nero akalandila mlandu, anali kuweluza mlanduyo limodzi ndi aphungu ake odziŵa bwino zinthu ndi anzelu. (The Life and Epistles of Saint Paul)

Baibulo siifotokoza kuti Nero anaweluza yekha mlandu wa Paulo kapena anasankha munthu wina kuti amve dandaulo la Paulo ndi kum’pelekela lipoti. Mulimonse mmene zinalili, Paulo ayenela kuti anafotokoza kuti amalambila Mulungu wa Ayuda ndi kuti anali kulimbikitsa anthu onse kulemekeza boma. (Aroma 13:1-7; Tito 3:1, 2) Apa n’zoonekelatu kuti Paulo anateteza uthenga wabwino pamaso pa akulu-akulu a boma, ndipo khoti la Kaisara inam’masula.—Afil. 2:24; Filim. 22.

TAPATSIDWA NCHITO YOTETEZA UTHENGA WABWINO

Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Adzakutengelani kwa abwanamkubwa ndi mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.” (Mat. 10:18) Ni mwayi waukulu kuimila Yesu m’njila imeneyi. Khama lathu poteteza uthenga wabwino limacititsa kuti tipambane. Koma zimene anthu opanda ungwilo angacite, sizingacititse kuti uthenga wabwino ‘ukhazikitsidwe mwalamulo’ pa mlingo wokwanila. Ni Ufumu wa Mulungu cabe umene udzacotsapo kupondeleza ndi kupanda cilungamo na kubweletsa mpumulo weni-weni.—Mlal. 8:9; Yer. 10:23.

Akhiristu masiku ano, angalemekeze dzina la Yehova mwa kuteteza cikhulupililo cawo. Monga Paulo, ifenso tingayesetse kukhala odekha, oona mtima, ndi kukamba motsimikiza. Yesu anauza otsatila ake kuti simufunika kucita “kukonzekela zoti mukayankhe podziteteza, cifukwa ine ndidzakuuzani mau oti munene ndi kukupatsani nzelu, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.”—Luka 21:14, 15; 2 Tim. 3:12; 1 Pet. 3:15.

Pamene Akhiristu ateteza cikhulupililo cawo pamaso pa mafumu, abwanamkubwa, kapena akulu-akulu a boma, amakhala kuti akulalikila anthu amene mwina sizikanatheka kuwalalikila. Milandu ina imene tawina yapangitsa makhoti ena kusintha malamulo awo. Izi zacititsa kuti tikhale na mwayi kapena kuti ufulu wa kulankhula ndi wolambila. Ngakhale kuti pamakhala zotulukapo zabwino, kulimba mtima kwa atumiki a Mulungu pokaonekela m’khoti kumakondweletsa mtima wa Mulungu.

Dzina la Yehova limalemekezedwa tikateteza cikhulupililo cathu

^ par. 8 Katswili wina, James Parkes, analemba kuti: “Ayuda . . . anali kuloledwa kucita miyambo yawo. Panalibe ciliconse capadela copelekela ufulu wotelo kwa Ayuda. Mwa kucita zimenezi, Aroma anali kutsatila mwambo wawo. Anali na mphamvu zopatsa munthu aliyense wa m’dziko lawo ciliconse cimene iwo afuna.”