Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makolo, Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo

Makolo, Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo

‘Anyamata ndi inunso anamwali, . . . tamandani dzina la Yehova.’—SAL. 148:12, 13.

NYIMBO: 88, 115

1, 2. (a) Ni vuto lanji limene makolo amakhala nalo? Nanga angacitepo ciani? (b) Tikambilane mfundo zinayi ziti?

M’BALE wina na mkazi wake ku France anati: “Ngakhale kuti timakhulupilila Yehova, sindiye kuti basi ana athu nawonso adzakhala okhulupilila.” Anapitiliza kuti: “Cikhulupililo sicili ngati coloŵa. Ana athu afunika kucikulitsa pang’ono-pang’ono.” M’bale wina ku Australia analemba kuti: “Palibe nchito yovuta monga kuthandiza ana ako kukhala na cikhulupililo. Ufunika kugwilitsila nchito njila iliyonse. Nthawi zina ungaone kuti mwana wako wamuyankha mom’khutilitsa pa funso lake. Umangodabwa kuti tsiku lina akufunsanso funso limodzimodzilo. Mfundo ni yakuti, mayankho amene angakhutilitse mwana wanu lelo, tsiku lina adzakhala osam’khutilitsanso. Nkhani zina zimafunika kuzifotokozanso mwa njila ina.”

2 Ngati ndinu kholo, kodi nthawi zina mumaona kuti udindo wophunzitsa ndi kuumba ana anu kuti adzakhale amuna ndi akazi acikhulupililo ni nchito yovuta moti simungaikwanitse? Kunena zoona, palibe aliyense amene angaikwanitse nchitoyi mwa nzelu zake. (Yer. 10:23) Koma ngati tidalila citsogozo ca Mulungu tidzapambana. Nazi zinthu zinayi zokuthandizani kuti ana anu akulitse cikhulupililo cawo: (1) Kuwadziŵa bwino ana anu. (2) Kuwaphunzitsa mocokela pansi pa mtima. (3) Kugwilitsila nchito mafanizo oyenelela. (4) Kukhala oleza mtima ndi odalila pemphelo.

ADZIŴENI BWINO ANA ANU

3. Kodi makolo angatengele bwanji citsanzo ca Yesu pophunzitsa?

3 Yesu sanadodome kufunsa otsatila ake zimene anali kukhulupilila. (Mat. 16:13-15) Tengelani citsanzo cake. Nthawi yabwino yocita zimenezi m’pamene muceza. Apempheni kuti akambe maganizo awo, kuphatikizapo zilizonse zimene amakaikila. M’bale wina wa zaka 15 ku Australia analemba kuti: “Atate amakonda kukambilana nane za cikhulupililo canga ndi kunithandiza kuganiza. Amanifunsa kuti: ‘Baibulo imati ciani?’ ‘Kodi ukhulupilila zimene ikamba?’ ‘Nanga n’cifukwa ciani umaikhulupilila?’ Amafuna kuti n’ziyankha m’mau anga-anga, osati kungotengela iwo kapena amayi. Popeza tsopano nikukula, nimayankha mofikapo.”

4. N’cifukwa ciani simuyenela kupeputsa mafunso a ana anu? Pelekani citsanzo.

4 Ngati mwana wanu akaikila ciphunzitso cina cake, osayankha mokhumudwa. Moleza mtima muthandizeni kuganizilapo pa nkhaniyo. Tate wina anati: “Osatenga mafunso a mwana wanu mopepuka. Musawaone ngati osafunika, ndipo musawapewe poona kuti ni ocititsa manyazi.” Mafunso a mwana wanu ni umboni wakuti amafuna kuti mudziŵe, kuti mum’thandize kumvetsetsa zinthu. Yesu anayamba kufunsa mafunso ofunika akali ndi zaka 12 cabe. (Ŵelengani Luka 2:46.) Mnyamata wina wa zaka 15 ku Denmark anati: “N’tauza makolo anga kuti nikaikila ngati cipembedzo cathu n’coona, anacita nane modekha ngakhale kuti mumtima anali ndi nkhawa. Anayankha mafunso anga onse kucokela m’Baibulo.”

5. Kodi makolo angathandize bwanji ana kukhala ndi cikhulupililo cawo-cawo?

5 Adziŵeni bwino ana anu—maganizo awo, mmene amvelela, ndi nkhawa zawo. Musangoona kuti malinga amapezeka ku misonkhano, ndi kupita nanu mu ulaliki, ndiye kuti ali na cikhulupililo. Muzikambilana nawo nkhani zauzimu m’zocita zanu za tsiku ndi tsiku. Muziwapemphelela komanso kupemphela nawo pamodzi. Yesani kudziŵa mayeselo amene amakumana nawo omwe angafooketse cikhulupililo cawo. Ndipo athandizeni mmene angacitile nawo.

APHUNZITSENI MOCOKELA PANSI PA MTIMA

6. Makolo afunika kukhomeleza coonadi ca m’Baibulo m’mitima ya iwo eni. Cifukwa ciani?

6 Yesu monga mphunzitsi, anali kuwafika pamtima anthu cifukwa cokonda Yehova, Mau a Mulungu, ndi anthu. (Luka 24:32; Yoh. 7:46) Cikondi cotelo cingathandizenso makolo kuwafika pamtima ana awo. (Ŵelengani Deuteronomo 6:5-8; Luka 6:45.) Conco inu makolo, coyamba muzicita khama inu eni kuphunzila Baibulo na zofalitsa zathu. Muzikonda zacilengedwe ndi kuŵelenga mabuku athu ofotokoza za cilengedwe. (Mat. 6:26, 28) Kucita zimenezi kudzawonjezela cidziŵitso canu, mudzamukonda kwambili Yehova, ndipo mudzakhala okonzeka kuphunzitsa bwino ana anu.—Luka 6:40.

7, 8. N’ciani cingacitike ngati makolo akonda coonadi? Pelekani citsanzo.

7 Coonadi ca m’Baibulo cikadzaza mumtima mwanu, mudzayamba kulakalaka kuuzako ana anu. Muzicita zimenezi nthawi iliyonse, osati cabe pokonzekela misonkhano, kapena pa kulambila kwa pabanja. Komabe, makambilano amenewa safunika kucitokakamiza. M’malomwake, azicitika momasuka pamene mukuceza nthawi iliyonse. Makolo ena ku America ndi ana awo, amayamikila Yehova akacita cidwi ndi cilengedwe, kapena pamene asangalala ndi zakudya zinazake. Iwo anati: “Timathandizila ana athu kuona cikondi ca Yehova ndi kutiganizila kwake pa zonse zimene anatipatsa.” Makolo ena ku South Africa, polima m’dimba ndi atsikana awo aŵili, amawafotokozela kudabwitsa kwa mbewu, mmene zimamelela ndi kukula. Anati: “Timathandiza ana athu kuti azilemekeza moyo ndi kudziŵa kuti ni wodabwitsa kwambili.”

8 Tate wina ku Australia anayenda ndi mwana wake wa zaka pafupi-fupi 10 ku miziyamu (malo osungilako zinthu zakale). Anatengelapo mwayi womuthandiza kulimbitsa cikhulupililo cake mwa Mulungu ndi m’cilengedwe. Anati: “Tinaonako tuzolengedwa tam’madzi twakufa tamakedzana (ma ammonoids ndi ma trilobites). Tinadabwa ndi kukongoka kwake, kucolowana kwa cipangidwe cake, ndi kuti matupi ake anali athunthu bwino-bwino, ndendende ndi twamoyo tumene tuliko lelo.” Conco, ngati amati moyo unasandulika kucokela ku twamoyo tung’ono-ng’ono tosacolowana kufika ku zamoyo zikulu-zikulu zocolowana, n’cifukwa ciani twamoyo twamakedzanato tunali tocolowana kale kwambili? Mfundoyi inanigwila mtima cakuti n’nauzako mwana wanga.”

SEŴENZETSANI MAFANIZO OMVEKA BWINO

9. N’cifukwa ciani mafanizo ni othandiza? Nanga mayi wina anaonetsa bwanji zimenezi?

9 Nthawi zambili Yesu anagwilitsila nchito mafanizo othandiza anthu kuganiza, owafika pamtima, ndi owathandiza kumakumbukila zimene aphunzila. (Mat. 13:34, 35) Ana amakumbukila bwino zinthu zocitika. Conco makolo, muzikonda kuseŵenzetsa mafanizo powaphunzitsa. N’zimene mayi wina ku Japan anacita. Anafotokozela ana ake, wina wa zaka 8 wina 10, za cifungadziko (atmosphere, ndiwo mpweya wozungulila dziko lapansi), na kuwaonetsa mmene Yehova amatisamalila potiikila cifungadziko. Pocita zimenezo anapatsa anawo shuga, mkaka, na masamba a khofi. Ndiyeno anapempha kuti mwana aliyense am’pangile khofi. “Aliyense anacita khama kwambili,” anatelo mayiyo. “N’tawafunsa kuti n’cifukwa ciani anacita mosamala conco, aliyense anati anafuna kuti anipangile khofi yabwino mmene nimaikondela. Ndiyeno n’nawauza kuti ni mmenenso Mulungu naye anacitila khama posakaniza bwino mipweya yopanga cifungadziko (atmosphere) kuti tikhalepo na moyo pa dziko lapansi.” Fanizo limeneli linawayenelela kwambili pa msinkhu wawo. N’zosakaikitsa kuti anawo sanaiŵale zimene anaphunzilapo.

Mungaseŵenzetse zinthu zodziŵika bwino kuti muthandize ana anu kukulitsa cikhulupililo mwa Mulungu na cilengedwe (Onani ndime 10)

10, 11. (a) Ni fanizo liti limene mungakonde kuseŵenzetsa kuti muthandize mwana wanu kukulitsa cikhulupililo mwa Mulungu? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Ni mafanizo othandiza ati amene mwaseŵenzetsapo?

10 Mungapelekenso citsanzo ca lesipi (malangizo ophikila), kuti muthandize mwana wanu kukulitsa cikhulupililo mwa Mulungu. Motani? Mukapanga keke kapena masikono, mufotokozeleni nchito ya lesipi. Ndiyeno mupatseni cipatso ciliconse, mwina apozi, na kum’funsa kuti: “Kodi udziŵa kuti apozi inapangidwa motsatila ‘lesipi’?” Ndiyeno icekeni pakati na kum’patsa kambeu kake. Mungamuuze kuti lesipi ya apozi imeneyi “inalembedwa” mkati mwa kambewu aka, koma m’malangizo amene ife anthu sitingamvetsetse. Ndiye mungam’funse kuti: “Ngati lesipi ya keke inalembewa na winawake, nanga n’ndani analemba lesipi yovuta kuimvetsetsa ya apozi?” Kwa mwana wosinkhulilapo, mungamufotokozele kuti lesipi ya apozi—kapena ya mtengo wake weniweniwo, inalembedwa mu DNA yake, kapena kuti m’majini ake. Mungakambilanenso mafanizo amene ali patsamba 10 mpaka 20 mu kabuku kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking.

11 Makolo ambili amakonda kukambilana ndi ana awo nkhani za mu Galamukani! zakuti “Kodi Zinangocitika Zokha?” Ena amaphunzitsa ana awo ang’ono-ang’ono mfundo zosavuta poseŵenzetsa nkhani zimenezi. Mwacitsanzo, makolo ena ku Dernmark anafanizila ndeke ndi mbalame. Anauza ana awo kuti: “Ndeke zimaoneka monga mbalame. Koma kodi ndeke zingaikile mazila na kukonkhomola tuŵana twa ndeke? Kodi mbalame zimafunikila eyapoti yotelapo? Ndipo n’ciani cimacita congo pouluka, mbalame kapena ndeke? Conco, uganiza wanzelu kwambili n’ndani, wopanga ndeke olo amene anapanga mbalame?” Mfundo za conco, pamodzi na mafunso oyenelela, mungathandize nazo mwana wanu kuyamba ‘kuganiza bwino,’ na kukulitsa cikhulupililo mwa Mulungu.—Miy. 2:10-12.

12. Kodi mafanizo angathandize bwanji ana anu kukhulupilila Baibulo?

12 Mafanizo abwino angathandizenso mwana kukhulupilila kuti Baibulo n’loona. Mwacitsanzo, ganizilani Yobu 26:7. (Ŵelengani.) Mungamuonetse bwanji kuti lembali linauzilidwa zoona? M’malo mongomufotokozela mfundo cabe, mungamuthandize kuyelekeza m’maganizo zocitikazo. M’thandizeni kuona kuti kale-kalelo m’nthawi ya Yobu kunalibe makina oonela zinthu zakumwamba, kapena zoombo zopitila kuthambo. Naye mwana wanu angafotokoze mmene kunalili kovuta panthawiyo kukhulupilila kuti cinthu cacikulu monga dziko lapansi cingalenjekeke m’malele popanda kanthu. Angatenge bola (mpila) kapena mwala ndi kuonetsa kuti cinthu ciliconse colema sicingakhazikike m’malele. Kuyelekezela kwa mtundu umenewu kungathandize mwana wanu kuona kuti Yehova analembelatu kale-kale m’Baibulo zinthu zoona zimene zatengela anthu zaka zambili-mbili kuti apeze umboni wake.—Neh. 9:6.

AONETSENI PHINDU LA MFUNDO ZA M’BAIBULO

13, 14. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuona phindu la mfundo za m’Baibulo?

13 N’kofunika kwambili kuti muziphunzitsa ana anu kuona phindu la mfundo za m’Baibulo. (Ŵelengani Salimo 1:1-3.) Mungacite zimenezi m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, mungauze ana kuyelekeza kuti akupita kukakhala pa cisumbu cakutali, ndipo afunika kusankha anthu amene angakonde kukakhala nawo kumeneko. Ndiyeno afunseni kuti: “Kuti nonse mukakhale mwamtendele pa cisumbupo, kodi mungasankhe anthu a makhalidwe anji?” Mungakambilanenso nawo malangizo othandiza ali pa Agalatiya 5:19-23.

14 Apa angaphunzilepo zinthu ziŵili zofunika. Coyamba, angaphunzile kuti mfundo za m’Baibulo zimalimbikitsa mgwilizano ndi umodzi. Caciŵili, zimene Yehova akutiphunzitsa pali pano, akutikonzekeletsa kukakhala bwino m’dziko latsopano. (Yes. 54:13; Yoh. 17:3) Kuti mukhomeleze mfundo zimenezi mwa iwo mukhoza kusankha cocitika kapena cokumana naco m’zofalitsa zathu. Mungacitenge m’nkhani zakuti “Baibulo Imasintha Anthu” mu Nsanja ya Mlonda. Ndiponso, ngati mumpingo mwanu muli munthu amene anacita masinthidwe aakulu mu umoyo wake kuti ayambe kutumikila Yehova, mungam’pemphe kuti adzakusimbilenkoni cimene cinam’thandiza kusintha. Zitsanzo za conco zimaonetsa kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandizadi.—Aheb. 4:12.

15. Kodi pophunzitsa ana anu, colinga canu cacikulu ciyenela kukhala ciani?

15 Mfundo ni yakuti: Pophunzitsa ana anu, osaseŵenzetsa njila imodzi-modzi nthawi zonse. Yesani kuganizilako njila zina. Pezani njila zingawathandize kuganiza, koma zogwilizana na msinkhu wawo. Aphunzitseni m’njila yokondweletsa komanso yolimbikitsa cikhulupililo. Tate wina anati: “Osalema kuyesa njila zatsopano pokambilana nkhani za m’Baibulo.”

KHALANI OKHULUPILIKA, OLEZA MTIMA, NDI ODALILA PEMPHELO

16. Pophunzitsa ana, n’cifukwa ciani kuleza mtima n’kofunika? Pelekani citsanzo.

16 N’zosatheka kukhala na cikhulupililo colimba popanda mzimu wa Mulungu. (Agal. 5:22, 23) Mofanana ndi cipatso ceni-ceni, cikhulupililo cimatenga nthawi kuti cikule. Conco, kuleza mtima ndi kupilila n’kofunika pophunzitsa ana. “Ine na mkazi wanga tinali kuonetsa cidwi kwambili kwa ana athu,” anatelo tate wina ku Japan wa ana aŵili. Anawonjezela kuti: “Kuyambila ali ana, n’nali kuphunzila nawo kwa mphindi 15 cabe tsiku lililonse, kupatulapo masiku osonkhana. Mphindi 15 sizinali nthawi yolemetsa kwa ise ndi kwa iwo.” Wadela wina analemba kuti: “Pamene n’nali wacicepele, n’nali na mafunso ambili mu mtima mwanga. Koma m’kupita kwa nthawi, mafunso anga ambili anayankhidwa pa misonkhano, pa kulambila kwa pabanja kapena pocita phunzilo laumwini. Ndiye cifukwa cake makolo safunika kuleka kuphunzitsa ana awo.”

Kuti mukhale mphunzitsi wabwino, coyamba Mau a Mulungu ayenela kukhala pamtima panu (Onani ndime 17)

17. N’cifukwa ciani citsanzo ca makolo n’cofunika kwambili? Nanga makolo ena anaonetsa citsanzo canji kwa ana awo?

17 Cinthu cina cofunika kwambili ni citsanzo canu. Ana amaona zimene mumacita ndipo zimawakhudza. Conco, monga makolo, pitilizani kukulitsa cikhulupililo canunso. Ana anu aziona kuti Yehova ni weni-weni kwa inu. Makolo ena ku Bermuda amati akakhala ndi nkhawa, amapemphela pamodzi ndi ana awo, kupempha citsogozo ca Yehova. Amalimbikitsanso ana awo kumapemphela pawokha. Anati: “Timauzanso mtsikana wathu wamkulu kuti ‘Uzidalila Yehova, osada nkhawa kwambili, uziika patsogolo zinthu za Ufumu.’ Akaona kuti zimenezi zamuthandiza, amadziŵa kuti Yehova ali nafe. Izi zalimbitsa kwambili cikhulupililo cake mwa Mulungu ndi Baibulo.”

18. Kodi makolo afunika kuzindikila ciani?

18 Koma zindikilani kuti pothela pake, anawo afunika kucita mbali yawo kuti akulitse cikhulupililo cawo. Monga makolo, mungabyale na kuthilila. Koma Mulungu yekha ndiye amakulitsa. (1 Akor. 3:6) Conco m’pempheni mzimu woyela, ndipo citani khama kuphunzitsa ana anu okondedwawo. Mukacita zimenezi, Yehova adzakudalitsani kwambili.—Aef. 6:4.