Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Manja Anu Asakhale Olefuka”

“Manja Anu Asakhale Olefuka”

“Manja anu asakhale olefuka.”—ZEF. 3:16. Buku Lopatulika

NYIMBO: 81, 32

1, 2. (a) Ni mavuto abwanji amene anthu ambili amakumana nawo masiku ano? Nanga pamakhala zotulukapo za bwanji? (b) Ni lonjezo lodalilika liti lopezeka pa Yesaya 41:10, 13?

MLONGO wina amene ni mpainiya ndipo anakwatiwa ndi mkulu, anakamba kuti: “Ngakhale kuti nimacita zinthu za kuuzimu nthawi zonse, nakhala nikuvutika ndi nkhawa kwa zaka zambili. Zimenezi zacititsa kuti nizisoŵa tulo, nisakhale ndi nthanzi labwino, ndipo zakhudza mmene nimacitila zinthu ndi ena. Nthawi zina, izi zimanicititsa kubwelela m’mbuyo ndi kulakalaka kufa.”

2 Kodi inunso mumamvela monga mmene mlongoyu anamvelela? N’zacisoni kuti dziko loipa la Satanali, limatibweletsela mavuto amene amacititsa kuti tikhale na nkhawa. Ndipo nkhawa zimenezo zingatifooketse. Mavutowo tingawayelekezele ndi nangula amene amaimitsa boti kuti isapite kutsogolo. (Miy. 12:25) Nanga ni mavuto abwanji amene angakufooketseni? Mwina muvutika na cisoni cifukwa ca imfa ya munthu amene mumakonda. Mwinanso muvutika na matenda aakulu, kapena mukulephela kusamalila bwino banja lanu cifukwa ca mavuto a zacuma. N’kutheka kuti ena a inu mukutsutsidwa. M’kupita kwa nthawi, mavutowa angakufooketseni mwauzimu ngakhalenso kukulandani cimwemwe. Komabe, musataye mtima. Mulungu adzakuthandizani ndi dzanja lake la mphamvu.—Ŵelengani Yesaya 41:10, 13.

3, 4. (a) Kodi liwu lakuti “dzanja” limagwilitsidwa nchito bwanji m’Baibulo? (b) N’ciani cingacititse dzanja lathu kulefuka?

3 Nthawi zambili, Baibulo limachula ziwalo za thupi pofuna kuyelekezela zinthu kapena zocitika zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, limachula dzanja nthawi mahandiledi ambili. Kulimbitsa dzanja la munthu kungatanthauze kumulimbikitsa, kum’thandiza, kapena kumusonkhezela kuti acitepo kanthu. (1 Sam. 23:16; Ezara 1:6) Kungatanthauzenso kuthandiza wina kukhala ndi ciyembekezo ca mtsogolo.

4 Nthawi zina, timakamba mau ophiphilitsa akuti manja olefuka kutanthauza munthu amene ni wofooka, wovutika maganizo, kapena amene alibe ciyembekezo. (2 Mbiri 15:7; Aheb. 12:12) N’zosavuta kwa munthu wotelo kubwelela m’mbuyo. Ngati mwakumana ndi mavuto amene akucititsani kukhala ndi nkhawa, kufooka mwakuthupi kapena mwauzimu, kodi mungapeze kuti thandizo? Nanga n’ciani cingakuthandizeni kupilila ndi kukhala wacimwemwe?

‘DZANJA LA YEHOVA SILINGALEPHELE KUTIPULUMUTSA’

5. (a) Tifunika kucita ciani tikakumana na mavuto? Nanga tiyenela kukumbukila ciani? (b) Tidzaphunzila ciani m’nkhani ino?

5 Ŵelengani Zefaniya 3:16, 17. M’malo mocita mantha kapena kufooka, kumene kuli ngati kulola manja athu kulefuka, Atate wathu wacikondi Yehova, akutipempha kuti ‘timutulile nkhawa zathu zonse.’ (1 Pet. 5:7) Tiyenela kukumbukila mau amene Mulungu anauza Aisiraeli kuti ‘dzanja lake la mphamvu silalifupi moti n’kulephela kupulumutsa’ atumiki ake okhulupilika. (Yes. 59:1) M’nkhani ino, tidzaphunzila zitsanzo zitatu zocititsa cidwi za m’Baibulo zoonetsa kuti Yehova ndi wofunitsitsa, ndipo ali na mphamvu zothandiza anthu ake kucita cifunilo cake, ngakhale panthawi ya mavuto aakulu. Tiyeni tione mmene zitsanzo zimenezi zingatilimbikitsile mwauzimu.

6, 7. Tiphunzilapo ciani tikaona mmene Aisiraeli anagonjetsela Aamaleki?

6 Aisiraeli atangomasulidwa mozizwitsa ku ukapolo ku Iguputo, Aamaleki anawaukila. Potsatila malangizo a Mose, Yoswa anatsogolela Aisiraeli ku nkhondo. Ndiyeno, Mose anatenga Aroni ndi Hura ndi kupita nawo pa phili. Malowo anali akuti angathe kuona bwino-bwino pamene Aisiraeli akumenya nkhondo. Kodi amuna amenewa anathaŵa nkhondo cifukwa ca mantha? Kutalitali!

7 Mose anacita zinthu zimene zinathandiza Aisiraeli kupambana nkhondo. Iye ananyamula ndodo ya Mulungu woona m’mwamba ndi manja ake. Zimene zinali kucitika n’zakuti, Mose akangokweza manja ake m’mwamba, Yehova anali kuthandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamaleki. Koma akangowatsitsa cifukwa colema, Aamaleki anali kupambana. Mwanzelu, Aroni ndi Hura “anatenga mwala ndi kumuikila [Mose], ndipo anakhalapo. Aroni ndi Hura anacilikiza manja ake, wina mbali ina winanso mbali ina, moti manja ake anakhalabe conco mpaka dzuŵa kuloŵa.” Apa Mulungu anathandiza Aisiraeli kupambana nkhondo ndi dzanja lake lamphamvu.—Eks. 17:8-13.

8. (a) Kodi Asa anacita ciani pamene Aitiyopiya anaopseza Ayuda? (b) Tingatengele bwanji citsanzo ca Asa codalila Mulungu?

8 Yehova anaonetsanso kuti dzanja lake silalifupi kwa Mfumu Asa. Nkhondo zambili zimene zinacitika zinalembedwa m’Baibulo. Pa magulu onse a asilikali, gulu la Zera Mwiitiyopiya ndi imene inali na asilikali ambili. Iye anali ndi asilikali 1,000,000 amene anali akatswili pankhondo. Anali ambili kuwilikiza pafupi-fupi kaŵili pa ciŵelengelo ca asilikali a Asa. Mungaone kuti zinali zosavuta kwa Asa kukhala na nkhawa komanso kucita mantha. Zimenezi zikanacititsa dzanja lake kulefuka. Koma panthawi yovuta imeneyo, Asa anapemphela kwa Yehova kuti amuthandize. Malinga ndi kuona kwa umunthu, zinaoneka zosatheka kugonjetsa Aitiyopiya. Koma “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Mat. 19:26) Mulungu anaonetsa mphamvu zake zazikulu mwa ‘kugonjetsa Aitiyopiyawo pamaso pa Asa,’ amene “anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu masiku ake onse.”—2 Mbiri 14:8-13; 1 Maf. 15:14.

9. (a) N’ciani cikanalepheletsa Nehemiya kumanganso mpanda wa Yerusalemu? (b) Kodi Mulungu anayankha bwanji pemphelo la Nehemiya?

9 Ganizilani mmene Nehemiya anamvelela atapita ku Yerusalemu. Mzindawu sunali wotetezeka, ndipo Ayuda anzake anali ovutika maganizo kwambili. Anthu otsutsa a mitundu ina anali kuwopseza Ayuda. Izi zinacititsa kuti alefuke pa nchito yawo yomanganso mpanda wa Yerusalemu. Kodi zimenezi zinacititsa kuti Nehemiya nayenso alefuke? Iyai. Mofanana ndi Mose, Asa, ndi atumiki ena a Yehova okhulupilika, Nehemiya anali kale na cizolowezi copemphela kwa Yehova kuti am’thandize. Conco, panthawiyi sanacitile mwina koma kupemphela kwa Mulungu. Ayuda anali kuona kuti mavuto amene anakumana nawo panthawiyi anali aakulu kwambili cakuti sangawathetse. Koma Yehova anayankha pemphelo la Nehemiya locokela pansi pamtima. Mulungu anaseŵenzetsa ‘mphamvu zake zazikulu’ ndi ‘dzanja lake lamphamvu’ kuti athandize Ayuda olefuka manja amenewo. (Ŵelengani Nehemiya 1:10; 2:17-20; 6:9.) Kodi inu mumakhulupilila kuti Yehova amaseŵenzetsa ‘mphamvu zake zazikulu’ ndi ‘dzanja lake lamphamvu’ kuti akuthandizeni?

YEHOVA ADZALIMBITSA DZANJA LANU

10, 11. (a) Kodi Satana amayesa bwanji kulefula dzanja lathu? (b) Nanga Yehova amatilimbikitsa bwanji? (c) Kodi inu mwapindula bwanji ndi maphunzilo a kuuzimu?

10 Mdyelekezi amayesa-yesa kuti atilefule pa utumiki wathu wacikhiristu. Iye amagwilitsila nchito mabodza ndi ziwopsezo zocokela kwa maboma, atsogoleli acipembedzo, ndi anthu ampatuko. Kodi colinga cake n’ciani? Afuna kuti alefule dzanja lathu kuti tileke kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Komabe, Yehova akhoza ndipo ni wokonzeka kutipatsa mphamvu mwa kugwilitsila nchito mzimu wake woyela. (1 Mbiri 29:12) Motelo, tifunika kudalila mzimu umenewu kuti utithandize kulimbana ndi mavuto amene Satana ndi dziko lake loipa angatibweletsele. (Sal. 18:39; 1 Akor. 10:13) Ndife okondwa kuti tilinso ndi Mau a Mulungu, ouzilidwa ndi mzimu wake woyela. Ndiponso, tili na cakudya ca kuuzimu cozikidwa pa Baibulo cimene timalandila mwezi uliwonse. Mau a pa Zekariya 8:9, 13 (ŵelengani) ni othandiza kwambili kwa ife. Mau amenewa anakambidwa pamene kacisi wa ku Yerusalemu anali kumangidwanso.

11 Kuwonjezela apo, Mulungu amatilimbikitsa kupitila m’maphunzilo a kuuzimu amene timalandila pa misonkhano ya mpingo, ya dela, ya cigawo, ndi m’masukulu osiyana-siyana. Maphunzilo amenewa amatilimbikitsa kucita zabwino, kukhala na zolinga za kuuzimu, ndi kukwanilitsa nchito zathu zacikhiristu. (Sal. 119:32) Kodi inu mumacita kulakalaka kuti mulimbikitsidwe ndi maphunzilo amenewa?

12. Tingacite ciani kuti tikhalebe olimba mwauzimu?

12 Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamaleki ndi Aitiyopiya. Anathandizanso Nehemiya ndi anzake mwa kuwapatsa mphamvu panchito yawo yomanganso mpanda. Mofananamo, Mulungu adzatipatsa mphamvu kuti tikhale olimba tikakumana ndi anthu otsutsa kapena amene alibe cidwi mu ulaliki. Adzatithandizanso kulimbana ndi nkhawa kuti tikwanilitse nchito yathu yolalikila. (1 Pet. 5:10) Sitiyenela kuyembekezela kuti Yehova adzatithandiza mozizwitsa. M’malomwake, tiyenela kucita mbali yathu. Tiyenela kuŵelenga Mau a Mulungu tsiku lililonse, kukonzekela ndi kupezeka pa misonkhano mlungu uliwonse, kucita phunzilo laumwini ndi kulambila kwa pabanja, ndi kupemphela kwa Yehova nthawi zonse. Conco, tisalole kuti zinthu zina zititsekele njila zimene Yehova amagwilitsila nchito kuti atilimbikitse. Ngati muona kuti dzanja lanu lalefuka pa zinthu zimene takambilanazi, pemphani Mulungu kuti akuthandizeni. Mukatelo, yembekezani kuti muone mmene mzimu wake ‘udzalimbikitsila zolakalaka zanu kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.’ (Afil. 2:13) Nanga inu mungacite ciani kuti mulimbitse dzanja la ena?

LIMBITSANI MANJA OLEFUKA

13, 14. (a) Kodi m’bale wina analimbikitsidwa bwanji mkazi wake atamwalila? (b) Tingacite ciani kuti tilimbikitse ena?

13 Yehova watipatsa gulu la padziko lonse la abale amene amatikonda ndi kutilimbikitsa. Kumbukilani mau a mtumwi Paulo akuti: “Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka, ndipo pitilizani kuwongola njila zimene mapazi anu akuyendamo.” (Aheb. 12:12, 13) Ambili m’nthawi ya atumwi analimbikitsidwa mwauzimu ndi Akhiristu anzawo. N’cimodzi-modzi masiku ano. Mwacitsanzo, m’bale wina mkazi wake atamwalila, anakumananso ndi mavuto ena aakulu. Iye anati: “Naphunzila kuti sitingasankhe mayeselo, nthawi yokumana nawo, kapena kuculuka kwa mayeselowo. Kupemphela na kucita phunzilo laumwini zinanithandiza kukhala wolimba mwauzimu. Kuwonjezela apo, abale ndi alongo ananithandiza cakuti n’nalimbikitsidwa kwambili. Naphunzilanso kuti n’kofunika kwambili kukhala pa unansi wabwino ndi Yehova tisanakumane ndi mavuto.”

Tonse mumpingo tili na udindo wolimbikitsana (Onani ndime 14)

14 Aroni na Hura anathandiza Mose mwa kucilikiza manja ake panthawi ya nkhondo. Nafenso tingapeze njila zimene tingathandizile anthu ena. N’ndani amene tingathandize? Tingathandize okalamba, anthu amene ali na vuto la thanzi, amene akutsutsidwa ndi a m’banja mwawo, osungulumwa, ndi ofeledwa. Tingathandizenso acicepele amene akukamizidwa kucita zoipa, kapena amene afuna kukhala na “umoyo wapamwamba” m’dzikoli, monga kucita maphunzilo apamwamba, kulemela, kapena kufuna kukhala katswili. (1 Ates. 3:1-3; 5:11, 14) Pezani njila za mmene mungaonetsele cikondi ceni-ceni kwa ena mukakhala pa Nyumba ya Ufumu, mu ulaliki, pamene mukudya ndi ena, kapena pamene mukambilana ndi wina pa foni.

15. Kodi mau olimbikitsa angakhudze bwanji Akhiristu anzathu?

15 Mfumu Asa atagonjetsa Aitiyopiya, mneneli Azariya anam’limbikitsa pamodzi ndi anthu ake mwa kukamba kuti: “Koma inuyo khalani olimba mtima ndipo musagwe ulesi, pakuti mudzapeza mphoto cifukwa ca nchito yanu.” (2 Mbiri 15:7) Izi zinalimbikitsa kwambili Asa cakuti anakonza zinthu kuti abwezeletse kulambila koona. Inunso mau anu olimbikitsa angasonkhezele ena kucitapo kanthu. Mungawalimbikitse kuti azitumikila Yehova na mtima wonse. (Miy. 15:23) Timalimbikitsanso ena mwa mayankho athu ogwila mtima pa misonkhano ya mpingo. Conco, simuyenela kuutenga mopepuka mwayi umenewu.

16. Mofanana ndi Nehemiya, akulu angalimbikitse bwanji manja a abale ndi alongo? Fotokozani mmene Akhiristu anzanu anakuthandizilani.

16 Yehova analimbitsa dzanja la Nehemiya ndi anzake kuti agwile nchito yomanga. Anamanga mpanda wa Yerusalemu m’masiku 52 cabe. (Neh. 2:18; 6:15, 16) Nehemiya sanali kungoyang’anila cabe nchito. Iye anagwila nawo nchito yomanganso mpandawo. (Neh. 5:16) Masiku ano, akulu acikondi amatengela citsanzo ca Nehemiya. Ambili amagwila nawo nchito zomanga-manga, kapena kuyeletsa ndi kukonzanso Nyumba ya Ufumu imene amasonkhanamo. Kuwonjezela apo, akulu amalimbikitsanso manja amene ali lende ndi onse amene ali na nkhawa mwa kulalikila nawo ndi kucita maulendo aubusa.—Ŵelengani Yesaya 35:3, 4.

“MANJA ANU ASAKHALE OLEFUKA”

17, 18. Tikakhala na nkhawa kapena tikakumana ndi mavuto, sitiyenela kukaikila za ciani?

17 Kugwila nchito limodzi na abale ndi alongo kumalimbikitsa mgwilizano. Kumatithandiza kuwakonda kwambili, ndi kukhulupilila kwambili malonjezo a Ufumu wa Mulungu. Pamene tilimbitsa dzanja la abale athu, timawathandiza kulimbana na mavuto osiyana-siyana, ndi kuti akhalebe ndi ciyembekezo ca mtsogolo. Mwakutelo, ifenso zimatithandiza kuika maganizo athu pa zinthu zauzimu, ndi kuyembekeza mwacidwi zimene Mulungu watisungila mtsogolo. Kukamba zoona, dzanja lathu nalonso limalimba.

18 Kale, Yehova anateteza ndi kuthandiza atumiki ake okhulupilika pa zocitika zosiyana-siyana. Kuganizila zimenezi kungalimbitse cikhulupililo cathu mwa iye. Conco, mukakumana na mavuto, “manja anu asakhale olefuka.” M’malomwake, muzipemphela kwa Yehova, ndi kulola kuti dzanja lake lamphamvu likulimbitseni ndi kukutsogolelani kuti mukalandile madalitso a Ufumu.—Sal. 73:23, 24.