Kodi Mudziŵa Bwino Zoona Zake?
“Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.”—MIY. 18:13.
1, 2. (a) Ni luso lanji limene tifunika kukulitsa? Nanga n’cifukwa ciani? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?
POKHALA Akhristu oona, tifunika kukulitsa luso lopenda mosamala zimene tamvela tisanazikhulupilile. (Miy. 3:21-23; 8:4, 5) Ngati tilibe luso limeneli, Satana na dziko lake angasokoneze kaganizidwe kathu mosavuta. (Aef. 5:6; Akol. 2:8) Ndipo ngati sitidziŵa zoona zeni-zeni pa nkhani inayake, tingayambe kukhulupilila mabodza. Miyambo 18:13 imati, “munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.”
2 M’nkhani ino, tidzakambilana zinthu zingapo zimene zingatilepheletse kudziŵa zoona zeni-zeni pa nkhani inayake na kuikhulupilila. Tidzaonanso mfundo za m’Baibo na zitsanzo zimene zingatithandize kukulitsa luso lopenda mosamala nkhani imene tamva.
MUSAMAKHULUPILILE “MAU ALIONSE”
3. N’cifukwa ciani tifunika kuseŵenzetsa mfundo ya pa Miyambo 14:15? (Onani pikica pamwambapa.)
3 Masiku ano, timamvela nkhani zambili-mbili komanso zosiyana-siyana. Nkhanizo timazimvela pa mawebusaiti, pa TV, komanso m’njila zina zofalitsila nkhani. Anthu ena amamvelanso nkhani zambili pa imelo, mameseji, kapena kwa anzawo. Koma popeza kuti anthu amakonda kufalitsa nkhani zabodza komanso zosoceletsa, tifunika kukhala osamala. Tiyenela kumapenda mosamala zimene Miyambo 14:15 imati: “Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mau alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.”
tamvela kuti tidziŵe ngati n’zoona. Kodi ni mfundo ya m’Baibo iti imene ingatithandize pa mbaliyi?4. Kodi Afilipi 4:8, 9 ingatithandize bwanji kusankha bwino nkhani zoŵelenga? Nanga n’cifukwa ciani kudziŵa zoona zeni-zeni n’kofunika? (Onani kabokosi kakuti “ Zinthu Zingapo Zimene Gulu Lapeleka Zotithandiza Kudziŵa Zoona.”)
4 Kuti tipange cosankha cabwino pa nkhani inayake, tifunika kudziŵa zoona zake za nkhaniyo. Conco, sitifunika kuŵelenga zilizonse, koma tiyenela kusankha mosamala nkhani zoŵelenga. (Ŵelengani Afilipi 4:8, 9.) Tisawononge nthawi yathu kumvetsela nkhani za pa mawebusaiti okayikitsa kapena kuŵelenga maimelo na mameseji a nkhani zopanda umboni. Tifunikanso kupewelatu mawebusaiti oyendetsedwa ndi anthu ampatuko. Iwo colinga cawo cimakhala kufooketsa anthu a Mulungu na kupotoza coonadi. Kuŵelenga na kumvetsela nkhani zabodza kungatipangitse zosankha zolakwika. Tifunika kupewelatu nkhani zabodza cifukwa zikhoza kuwononga kwambili maganizo na mtima wathu.—1 Tim. 6:20, 21.
5. Ni lipoti yoipa iti imene Aisiraeli anauzidwa? Nanga inawakhudza bwanji?
5 Kukhulupilila nkhani zabodza kungatibweletsele mavuto. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika m’nthawi ya Mose pamene azondi 10 mwa azondi 12 anabweletsa lipoti yoipa pambuyo pokazonda Dziko Lolonjezedwa. (Num. 13:25-33) Zokamba zawo zabodza komanso zosinjilila zinacititsa kuti anthu a Yehova ataye mtima. (Num. 14:1-4) Cifukwa? Mwina anaganiza kuti popeza azondi ambili ndiwo anabweletsa lipoti yoipa, ndiye kuti lipoti yawo inali yoona. Anthuwo sanamvele lipoti yabwino imene amuna odalilika, Yoswa na Kalebe, anabweletsa. (Num. 14:6-10) M’malo momvetsela lipoti ya zoona na kudalila Yehova, iwo anasankha kukhulupilila lipoti yoipayo. Kodi sikunali kupanda nzelu kumeneku?
6. N’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa tikamvela nkhani zoipa zoneneza anthu a Yehova?
6 Tifunika kukhala wosamala kwambili maka-maka ngati tamvela nkhani inayake yokhudza anthu a Yehova. Tisaiŵale kuti Satana amaneneza atumiki okhulupilika a Mulungu. (Chiv. 12:10) N’cifukwa cake Yesu anakamba kuti otsutsa ‘adzatinamizila zoipa’ za mtundu uliwonse. (Mat. 5:11) Ngati tikumbukila mfundo imeneyi, sitidzadabwa tikamvela nkhani zoipa zoneneza anthu a Yehova.
7. Tifunika kuganizila ciani tisanatume meseji kapena imelo?
7 Kodi mumakonda kutuma imelo kapena mameseji kwa anzanu? Ngati n’conco, ndiye kuti mukamvela nkhani inayake yocititsa cidwi imene yangofalitsidwa kumene, mwina mumalakalaka kukhala woyamba kuuzako anzanu nkhaniyo. Komabe, musanatume meseji kapena imelo, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani imene nifuna kutumayi ni ya zoona? Kodi nidziŵadi zoona pa nkhaniyi?’ Ngati mulibe umboni, simuyenela kuitumiza, cifukwa mosadziŵa, mungafalitse nkhani yabodza pakati pa abale. M’malomwake, muyenela kungoifafaniza.
8. Kodi anthu otsutsa m’maiko ena amacita ciani? Nanga mosadziŵa tingawacilikize bwanji?
8 Palinso vuto lina limene lingakhalepo ngati tili na cizoloŵezi cothamangila kutumila ena imelo kapena mameseji amene talandila. Ku maiko ena, cipembedzo ca Mboni za Yehova n’coletsedwa. M’maiko aconco, otsutsa angafalitse mwadala nkhani zabodza pofuna kutiyofyeza kapena kuticititsa kuyamba kukayikilana. Ganizilani zimene zinacitika m’dziko limene kale linali kuchedwa Soviet Union. Gulu la apolisi acisinsi, lochedwa KGB, linafalitsa nkhani yabodza yakuti abale ena oyang’anila pa nthambi anapandukila gulu la Yehova. * Ambili anakhulupilila nkhaniyo cakuti anadzilekanitsa na gulu la Yehova. Zinali zomvetsa cisoni kwambili! Koma cokondweletsa n’cakuti ambili anabwelela. Ngakhale zinali conco, ena sanabwelele. Cikhulupililo cawo cinasweka ngati ngalawa. (1 Tim. 1:19) Kodi tingapewe bwanji vuto ngati limeneli? Musamafalitse nkhani zofooketsa kapena zopanda umboni. Musamangokhulupilila zilizonse zimene mwamva. Koma muziyesetsa kudziŵa zoona zeni-zeni pa nkhaniyo.
KUSADZIŴA MFUNDO ZONSE ZOKHUDZA NKHANI
9. N’ciani cina cimene cingatipangitse cigamulo colakwika pa nkhani inayake?
9 Ngati sitidziŵa mfundo zonse zokhudza nkhani inayake imene tamvela, n’zosavuta kupanga cigamulo colakwika pa nkhaniyo. Ndipo nkhani yabodza imene ili na mfundo zina zolondola imakhala yosoceletsa kwambili. Kodi tingapewe bwanji kusoceletsedwa na nkhani zaconco?—Aef. 4:14.
10. N’ciani cinacititsa kuti Aisiraeli atsale pang’ono kupha abale awo? Nanga n’ciani cinathandiza kuti zimenezi zisacitike?
10 Ganizilani zimene Aisiraeli okhala ku madzulo kwa mtsinje wa Yorodano anacita m’masiku a Yoswa. (Yos. 22:9-34) Nthawi ina, iwo anamvela kuti Aisiraeli okhala kum’maŵa kwa mtsinje wa Yorodano, (mafuko a Rubeni, Gadi, na hafu ya fuko la Manase) anamanga guwa lansembe lalikulu ndi laulemelelo pafupi na mtsinjewo. Mfundo imeneyi inali yoona. Atangomvela zimenezi, Aisiraeli okhala ku madzulo kwa Yorodano anaganiza kuti abale awo apandukila Yehova. Conco iwo anasonkhana kuti akawathile nkhondo Aisiraeli okhala kum’maŵa kwa mtsinjewo. (Ŵelengani Yoswa 22:9-12.) Koma mwayi wake unali wakuti asanacite izi, anatuma amuna odalilika kuti akafufuze zoona zeni-zeni za nkhaniyo. Kodi anapeza zotani? Anapeza kuti guwa limene Aisiraeli a fuko la Rubeni, Gadi, ndi hafu ya fuko la Manase anamanga, silinali lopelekelapo nsembe, koma linali cabe monga cikumbutso. Iwo analimanga n’colinga cakuti m’tsogolo, Aisiraeli onse akadziŵe kuti nawonso anali atumiki a Yehova okhulupilika. Mwacionekele, Aisiraeli enawa anakondwela ngako kuti sanaphe abale awo cifukwa cokhulupilila mphekesela, koma anafufuza coyamba kuti adziŵe zoona zeni-zeni za nkhaniyo.
11. (a) N’ciani cinacititsa kuti Mefiboseti acitilidwe zinthu zopanda cilungamo? (b) Nanga Davide akanapewa bwanji kucita zinthu zopanda cilungamo zimenezo?
2 Sam. 9:6, 7) Koma pambuyo pake, Davide anauzidwa zinthu zina zabodza zokhudza Mefiboseti. Popanda kufufuza zoona pa nkhaniyo, Davide analanda Mefiboseti zinthu zake zonse. (2 Sam. 16:1-4) Koma pambuyo pokamba naye Mefiboseti, Davide anazindikila kuti analakwitsa, ndipo anam’bwezela Mefiboseti zinthu zake. (2 Sam. 19:24-29) Davide akanayamba wafufuza zoona zeni-zeni za nkhaniyo, m’malo mofulumila kucitapo kanthu, akanapewa kucita colakwa cimeneci.
11 Aliyense wa ise nthawi ina angacitilidwe zinthu zopanda cilungamo cifukwa cakuti anthu ena anafalitsa nkhani yabodza yokhudza ise. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pakati pa Mfumu Davide na Mefiboseti. Davide anaonetsa kuwoloŵa manja na kukoma mtima kwa Mefiboseti mwa kum’bwezela munda wonse wa Sauli, ambuye ake. (12, 13. (a) Kodi Yesu anacita ciani pamene anthu ena anamunenela zoipa? (b) Tingacite ciani ngati munthu wina wafalitsa nkhani yabodza ponena za ise?
12 Nanga bwanji ngati munthu wina wakunenelani zinthu zoipa? Yesu na Yohane M’batizi anakumanapo na vuto limeneli. (Ŵelengani Mateyu 11:18, 19.) Kodi Yesu anacita ciani pamene anthu ena anamunenela zoipa? Sanataye nthawi na mphamvu zake poyesa kuteteza mbili yake. M’malomwake, anangolimbikitsa anthu kuti adzionele okha zimene iye anali kucita na kuphunzitsa. Iye anati, “nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.”—Mat. 11:19.
13 Pamenepa pali phunzilo labwino limene tiyenela kutengapo. Nthawi zina, anthu angakambe zinthu zabodza kapena zoipa ponena za ise. Ndipo tingakhale wofunitsitsa kucitapo kanthu kuti titeteze mbili yathu komanso kuti cilungamo cionekele. Kodi n’ciani cothandiza cimene tingacite? Ngati wina wafalitsa nkhani yabodza ponena za ise, tiyenela kucita zinthu m’njila yakuti anthu adzionele okha kuti zimene munthuyo anakamba n’zabodza. Citsanzo ca Yesu pankhaniyi cionetsa kuti mbili yathu ya khalidwe labwino ingathe kufafaniza mabodza onse amene anthu angatinenele.
PEWANI KUDZIDALILA
14, 15. Kodi kudalila luso lathu lomvetsa zinthu kungakhale bwanji msampha?
14 Kusapeza mfundo zolondola pa nkhani inayake imene tamva ni vuto limodzi limene lingatilepheletse kufika pa cigamulo colondola pa nkhaniyo. Koma vuto lina lalikulu n’lakuti ndise anthu opanda ungwilo. Nanga bwanji ngati takhala tikutumikila Yehova mokhulupilika kwa zaka zambili? Ndiye kuti mwina tinakulitsa luso la kulingalila na kuzindikila. Ndipo anthu angayambe kutilemekeza kwambili cifukwa cocita zinthu moganiza bwino. Koma kodi izi zingakhalenso msampha kwa ise?
15 Inde, zingakhale msampha ngati tayamba kudalila kwambili luso lathu lomvetsa zinthu. Tingayambe kuyendela cabe zofuna za mtima wathu na maganizo athu. Komanso tingayambe kuganiza kuti tikangoona kapena kumva zinthu zina zake, tikhoza kuzimvetsetsa olo kuti sitidziŵa mfundo zonse. Kucita zinthu mwanjila imeneyi n’koopsa. Baibo imaticenjeza momveka bwino kuti sitiyenela kudalila luso lathu lomvetsa zinthu.—Miy. 3:5, 6; 28:26.
16. M’nkhani yongoyelekezela imeneyi, n’ciani cinacitika mu lesitilanti? Nanga nthawi yomweyo m’bale Tom anayamba kuganiza zotani?
16 Ganizilani nkhani iyi yongoyelekezela. Tinene kuti tsiku lina m’madzulo, mkulu wina amene watumikila kwa zaka zambili, dzina lake Tom analoŵa mu lesitilanti inayake. Ali mmenemo, anaona mkulu mnzake, dzina lake John, ali kudya pa thebulo ina na mzimayi
wina amene sanali mkazi wake. Tom anawaona aŵiliwo akuseka na kuceza mwaubwenzi komanso moonetsa kuti amakondana kwambili. Iye anayamba kuda nkhawa. Mumtima anati, ‘Kodi zimene m’baleyu akucita sizimuwonongela cikwati? Nanga mkazi wake angamvele bwanji? Nanga ana ake zidzawakhudza bwanji?’ Tom anaonapo kale zinthu zopweteka mtima ngati zimenezo zikucitika m’mabanja ena. Mukanakhala imwe, mukanaganiza bwanji?17. Pa nkhani yongoyelekezela imeneyi, kodi m’bale Tom pambuyo pake anazindikila ciani? Nanga pamenepa tiphunzilapo ciani?
17 Koma kodi zinatha bwanji? Olo kuti panthawiyo m’bale Tom anaganiza kuti m’bale John ni wosakhulupilika kwa mkazi wake, iye sanali kudziŵa zoona zeni-zeni pa nkhaniyo. Tsiku lomwelo, m’bale Tom anatumila foni m’bale John. Yelekezelani cabe mmene m’bale Tom anamvelela atamva kuti mzimayiyo anali mlongosi wake wa John, amene anangopatukilako m’tauniyo kucokela kwinakwake. Panali patatenga zaka zambili aŵiliwo osaonanapo. Popeza mlongosi wakeyo anali kungopitilako cabe m’tauniyo, m’bale John atakumana naye, anangopita naye ku lesitilanti kuti akamugulileko cakudya. Mkazi wake sanakwanitse kupezekapo. Komabe, cokondweletsa n’cakuti m’bale Tom sanauzeko aliyense maganizo olakwika amene anali nawo poyamba. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Olo kuti ndise aciyambakale m’coonadi ndipo timadziŵa zambili, tifunikabe kufufuza kuti tidziŵe zoona zeni-zeni pa zimene tamvela kapena kuona.
18. Kodi kusemphana maganizo cifukwa cosiyana zibadwa kungatipangitse bwanji kukhulupilila nkhani zabodza?
18 Kusemphana maganizo na Mkhristu mnzathu mu mpingo cifukwa cosiyana zibadwa, ni vuto linanso limene lingatilepheletse kufufuza zoona pa nkhani imene tamvela. Ngati nthawi zonse timaganizila pa zimene anatilakwila, tingayambe kumukayikila m’bale wathuyo. Ndipo tikamvela nkhani inayake yoipa yokhudza m’baleyo, mwamsanga tingaikhulupilile. Tiphunzilanji pamenepa? Kusungila abale athu cakukhosi kungatilengetse kukhulupilila zinthu zabodza zimene tilibe nazo umboni. (1 Tim. 6:4, 5) Tingapewe vuto limeneli mwa kusalola nsanje na kaduka kuzika mizu mu mtima mwathu. M’malo mwake, tiyenela kukwanilitsa udindo umene tili nawo, wokonda Akhristu anzathu na kuwakhululukila na mtima wonse.—Ŵelengani Akolose 3:12-14.
MFUNDO ZA M’BAIBO ZIDZATITETEZA
19, 20. (a) Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingatithandize kupenda nkhani mosamala kuti tidziŵe zoona zeni-zeni? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
19 Kudziŵa zoona zeni-zeni na kuzipenda mosamala n’kovuta masiku ano cifukwa pali nkhani zambili zabodza komanso zosoceletsa. Vuto linanso n’lakuti ndise opanda ungwilo. Nanga n’ciani cingatithandize? Tiyenela kudziŵa mfundo za m’Baibo na kuziseŵenzetsa. Imodzi mwa mfundozo ni yakuti sitiyenela kuyankhila nkhani tisanaimvetsetse. Kucita zimenezi n’kupusa, ndipo zotulukapo zake tikhoza kucititsidwa manyazi. (Miy. 18:13) Mfundo ina ya m’Baibo ni yakuti, sitiyenela kukhulupilila mau aliwonse amene tamvela. (Miy. 14:15) Ndipo yothela ni yakuti, olo kuti ndise aciyambakale m’coonadi ndipo timadziŵa zambili, sitiyenela kudalila luso lathu lomvetsa zinthu. (Miy. 3:5, 6) Mfundo za m’Baibo zidzatiteteza ngati popanga zosankha tiyesetsa kuseŵenzetsa mfundo zolondola zimene tamvela kucokela ku magwelo odalilika.
20 Koma pali vuto lina limene tikalibe kukambilana. Ni vuto lokonda kuweluza ena mwa maonekedwe awo akunja. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zizoloŵezi zingapo zolakwika zimene tingakhale nazo pa nkhaniyi komanso mmene tingazipewele.
^ par. 8 Onani buku la Cizungu la Yearbook la 2004, mape. 111-112, ndi Yearbook ya 2008, mape. 133-135.