Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Musamaweluze Poona Maonekedwe Akunja

Musamaweluze Poona Maonekedwe Akunja

“Lekani kuweluza poona maonekedwe akunja, koma muziweluza ndi ciweluzo colungama.”—YOH. 7:24.

NYIMBO: 142, 123

1. Kodi Yesaya analosela ciani pokamba za Yesu? Nanga n’cifukwa ciani izi n’zolimbikitsa?

ZIMENE Yesaya anakamba mu ulosi wake wonena za Ambuye wathu Yesu Khristu n’zolimbikitsa kwambili. Iye anakamba kuti Yesu “sadzaweluza potengela zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengela zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweluza mwacilungamo anthu onyozeka.” (Yes. 11:3, 4) N’cifukwa ciani zimenezi n’zolimbikitsa? Cifukwa m’dzikoli anthu ambili ni atsankho ndipo amacita zinthu mokondela. Conco, tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene tidzakhala na woweluza wacilungamo, Yesu Khristu, amene sadzatiweluza poona maonekedwe athu akunja.

2. Kodi Yesu anatilamula kucita ciani? Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Tsiku lililonse timaweluza anthu ena. Koma popeza ndise opanda ungwilo, sitikwanitsa kuweluza mwacilungamo ngati mmene Yesu amacitila. Timakonda kuweluza motengela zimene timaona. Koma pamene Yesu anali pa dzikoli, anatilamula kuti: “Lekani kuweluza poona maonekedwe akunja, koma muziweluza ndi ciweluzo colungama.” (Yoh. 7:24) Mwa ici, n’zoonekelatu kuti Yesu amafuna kuti titengeleko citsanzo cake mwa kupewa kuweluza ena poona maonekedwe awo akunja. M’nkhani ino, tidzakambilana zinthu zitatu zimene nthawi zambili anthu amaziona monga maziko oweluzila anzawo. Zinthu zimenezi ni mtundu wa munthu, kulemela kapena kusauka kwake, komanso zaka zakubadwa. Pa ciliconse mwa zinthuzi, tidzakambilana zimene tingacite pomvela lamulo la Yesu limeneli.

KUWELUZA ENA POTENGELA MTUNDU WAWO

3, 4. (a) N’zinthu ziti zimene zinapangitsa mtumwi Petulo kusintha mmene anali kuonela anthu a mitundu ina? (Onani pikica kuciyambi.) (b) Kodi Yehova anathandiza Petulo kuzindikila mfundo iti ya coonadi?

3 Ganizilani cabe mmene mtumwi Petulo anamvelela ataitanidwa kuti apite ku Kaisareya, ku nyumba kwa Koneliyo, munthu amene sanali Myuda. (Mac. 10:17-29) Mofanana ndi Ayuda ena, Petulo anakula na maganizo akuti anthu amene sanali Ayuda anali odetsedwa. Koma pofika nthawiyi, Petulo anali ataona zocitika zimene zinamulimbikitsa kusintha maganizo ake pa nkhaniyi. Mwacitsanzo, iye anali ataona masomphenya. (Mac. 10:9-16) Kodi anaona ciani m’masomphenyawo? Anaona cinthu cokhala ngati cinsalu codzala na nyama zodetsedwa cikutsitsidwa, ndipo kunamveka mau ocokela kumwamba akuti: “Nyamuka Petulo, ipha udye!” Katatu konse, Petulo anakana kwamtu wagalu. Koma akakana, kumwamba kunali kumveka mau akuti “zinthu zimene Mulungu waziyeletsa usiyiletu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.” Masomphenyawo atatha, Petulo anathedwa nzelu cifukwa sanamvetsetse tanthauzo la zimene anamvazo. Nthawi yomweyo, kunafika amuna otumidwa na Koneliyo. Ndiyeno atalamulidwa mwa mzimu woyela, Petulo ananyamuka pamodzi na amunawo kupita ku nyumba ya Koneliyo.

4 Petulo akanakhalabe na mtima woweluza ena motengela maonekedwe akunja, sembe sanangene m’nyumba ya Koneliyo. Panthawiyo, Ayuda sanali kuloŵa m’nyumba za anthu a mitundu ina. Nanga n’cifukwa ciani Petulo analimba mtima mpaka kungena m’nyumba ya Koneliyo? Analimbikitsidwa na masomphenya amene anaona, komanso citsimikizo ca mzimu woyela. Mwacionekele, Petulo atamvetsela zimene Koneliyo anakamba, anakhudzidwa kwambili. N’cifukwa cake anati: “Ndazindikila ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Petulo anakondwela ngako atamvetsetsa mfundo ya coonadi imeneyi. Mfundoyi inakhudza Akhristu onse. Motani?

5. (a) Kodi Yehova amafuna kuti Akhristu onse amvetsetse mfundo iti? (b) Olo kuti timadziŵa coonadi, ni khalidwe lanji limene tingakhalebe nalo mumtima?

5 Kupitila mwa Petulo, Yehova anathandiza Akhristu onse kuzindikila kuti iye ni Mulungu wopanda tsankho. Saona anthu ena kukhala ofunika kwambili cifukwa ca mtundu wawo, cikhalidwe, dziko, kapena citundu cawo. Mulungu amalandila munthu aliyense amene amamuopa na kucita cilungamo. (Agal. 3:26-28; Chiv. 7:9, 10) Mwacionekele, mumakhulupilila mfundo imeneyi. Koma bwanji ngati munakulila m’banja kapena m’dziko limene anthu ni atsankho kwambili? N’zoona kuti pokhala Mkhristu, mukhoza kumadziona kuti mulibe tsankho. Koma mkati mwa mtima, mzimu wa tsankho ungakhalemo. Ngakhale Petulo, amene anali na mwayi wounikila ena kuti Yehova alibe tsankho, pa nthawi ina anaonetsa mzimu watsankho. (Agal. 2:11-14) Kodi tingatsatile bwanji malangizo a Yesu akuti tisamaweluze ena potengela maonekedwe awo akunja?

6. (a) N’ciani cingatithandize kucotselatu tsankho mu mtima mwathu? (b) Kodi lipoti imene m’bale wina analemba inavumbula ciani?

6 Tifunika kudzipenda mosamala poseŵenzetsa Mau a Mulungu kuti tidziŵe ngati tikali na tsankho mu mtima na m’maganizo mwathu. (Sal. 119:105) Nthawi zina tingakhale na tsankho, koma osazindikila kuti tili nalo. Conco tingafunike kuthandizidwa na anthu ena kuti tizindikile vuto lathu. (Agal. 2:11, 14) Mwina sitingazindikile kuti tili na tsankho cifukwa cakuti khalidweli linazika mizu kwambili mwa ise. Mwacitsanzo, ganizilani za m’bale wina wa paudindo amene anatumiza lipoti yokhudza banja lina lacitsanzo cabwino, limene lili mu utumiki wanthawi zonse. Mwamuna wa banjalo anali wocokela mu mtundu wa anthu amene anali kuonedwa monga otsalila. Mwacionekele, m’bale wolemba lipotiyo sanadziŵe kuti nayenso anali kuwaona molakwika anthu a mtundu umenewo. M’lipoti yake, iye anakamba zinthu zambili zabwino zokhudza mwamunayo. Koma anatsiliza lipotiyo na mau akuti: “Ngakhale kuti iye ni wocokela [mu mtundu umenewu], khalidwe lake na umoyo wake zimathandiza ena kuzindikila kuti si anthu onse ocokela [mu mtundu umenewu] amene ni adothi komanso ocita zinthu motsalila. Komabe, ambili [mu mtundu umenewu] ni otelo.” Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Mosasamala kanthu za udindo umene tili nawo, tifunika kudzipenda mosamala na kupempha thandizo kwa ena kuti tidziŵe ngati tikali na tsankho mu mtima mwathu. Nanga n’ciani cina cimene tingacite?

7. Tingaonetse bwanji kuti tikufutukula mtima wathu?

7 Ngati tiyesetsa kuyanjana ndi anthu osiyana-siyana, cikondi cidzakula mu mtima mwathu ndipo tsankho lidzatha. (2 Akor. 6:11-13) Kodi muli na cizoloŵezi coceza cabe ndi anthu okamba citundu canu, kapena a mtundu wanu, cikhalidwe, kapena dziko lanu? Ngati n’conco, muyenela kufutukula mtima wanu. Bwanji osapemphako m’bale kapena mlongo wa citundu cina, cikhalidwe, kapena wocokela ku dziko lina kuti mukayendeko naye mu ulaliki, kapena kuti akabwele kunyumba kwanu kudzadya namwe cakudya kapena kudzaceza? (Mac. 16:14, 15) Mukacita izi, cikondi cidzakula kwambili mu mtima mwanu cakuti simudzakhalanso na tsankho. Koma palinso zinthu zina zimene nthawi zambili timaziona monga maziko oweluzilapo ena poona maonekedwe awo akunja. Tiyeni lomba tikambilane za kulemela na kusauka.

KUWELUZA ENA POTENGELA KUTI NI OLEMELA KAPENA OSAUKA

8. Malinga ndi Levitiko 19:15, kodi cuma na umphawi zingakhudze bwanji mmene timaonela ena?

8 Nthawi zina timaona anthu molakwika cifukwa cakuti ni osauka kapena ni olemela. Pa Levitiko 19:15 pamati: “Musamakondele munthu wosauka, ndiponso musamakondele munthu wolemela. Mnzako uzimuweluza mwacilungamo.”

9. Kodi Solomo anafotokoza vuto lanji limene tili nalo? Nanga tiphunzilapo ciani pa zimene anafotokoza?

9 Kodi cuma kapena umphawi zingakhudze bwanji mmene timaonela munthu? Mouzilidwa na mzimu woyela, Solomo anafotokoza vuto limene ise anthu opanda ungwilo tili nalo. Pa Miyambo 14:20, iye anati: “Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake, koma munthu wolemela amakhala ndi anzake ambili.” Kodi tiphunzilapo ciani pa lembali? Ngati sitisamala, tingayambe kukonda abale olemela na kumanyalanyaza abale osauka. Tingayambe kuona Akhristu ena kukhala ofunika kwambili kuposa ena cifukwa cakuti ni acuma. N’cifukwa ciani kucita izi n’koopsa?

10. Ni vuto lanji limene Yakobo anafotokoza?

10 Ngati timakonda Akhristu ena cifukwa cakuti ni acuma kapena osauka, tingayambitse magaŵano mu mpingo. Mtumwi Yakobo anakamba kuti vuto laconco linayambitsa magaŵano m’mipingo ina ya m’nthawi ya atumwi. (Ŵelengani Yakobo 2:1-4.) Pa cifukwa ici, tifunika kusamala kuti maganizo aconco asasokoneze mpingo wathu masiku ano.

11. Kodi kulemela na kusauka kumakhudza bwanji ubwenzi wa munthu na Yehova? N’cifukwa ciani mwayankha conco?

11 Tifunika kumaona abale athu monga mmene Yehova amawaonela. Yehova saona munthu kukhala wofunika kwambili kwa iye cifukwa cakuti ni wolemela kapena wosauka. Cimene cimacititsa munthu kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova si cuma kapena umphawi. N’zoona kuti Yesu anakamba kuti “zidzakhalatu zovuta kuti munthu wolemela adzaloŵe mu ufumu wakumwamba.” Koma sanakambe kuti wolemela sadzaloŵa mu Ufumuwo. (Mat. 19:23) Komanso Yesu anakamba kuti: “Odala ndinu osaukanu, cifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.” (Luka 6:20) Komabe, izi sizinatanthauze kuti anthu onse osauka anali odalitsidwa mwapadela komanso kuti anamvetsela uthenga wa Yesu. Panali anthu ambili osauka amene sanamvetsele. Conco, mfundo ni yakuti: Kulemela kapena kusauka si cizindikilo cakuti munthu ali pa ubwenzi wabwino na Yehova.

12. Ni malangizo anji amene Malemba amapeleka kwa Akhristu olemela na osauka?

12 Ndise odala kuti tili na abale na alongo ambili, osauka na olemela, amene amakonda Yehova na kum’tumikila na mtima wonse. Malemba amalangiza Akhristu olemela kuti “asamadalile cuma cosadalilika, koma adalile Mulungu.” (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:17-19.) Koma Mau a Mulungu amacenjeza anthu onse a Mulungu, olemela na osauka omwe, kuti ayenela kupewa kukonda ndalama. (1 Tim. 6:9, 10) Zoonadi, ngati tiyesetsa kuona abale athu monga mmene Yehova amawaonela, tidzapewa kuwaweluza potengela kuti ni olemela kapena osauka. Nanga bwanji zaka zakubadwa? Kodi ni maziko oyenelela oweluzilapo ena? Tiyeni tikambilane.

KUWELUZA ENA POTENGELA ZAKA ZAKUBADWA

13. Kodi Malemba amatiphunzitsanji pa nkhani yolemekeza acikulile?

13 Nthawi zambili, Malemba amatilimbikitsa kuti tiyenela kulemekeza acikulile. Mwacitsanzo, pa Levitiko 19:32 pamati: “Anthu aimvi uziwagwadila, munthu wacikulile uzim’patsa ulemu ndipo uziopa Mulungu wako.” Miyambo 16:31 nayonso imati: “Imvi ndizo cisoti cacifumu ca ulemelelo zikapezeka m’njila yacilungamo.” Komanso, Paulo analangiza Timoteyo kuti sanafunike kudzudzula m’bale wacikulile mokalipa, koma anafunika kumuona monga atate wake. (1 Tim. 5:1, 2) Olo kuti Timoteyo anali na mphamvu ya ulamulilo pa abale acikulile amenewo, anafunika kucita nawo zinthu mwacifundo komanso mwaulemu.

14. Ni pa nthawi iti pamene kungakhale kofunikila kupeleka uphungu kapena cilangizo kwa munthu wamkulu kuposa ise?

14 Koma tifunika kusamala kuti tisatenge mfundo imeneyi molakwika. Mwacitsanzo, bwanji ngati Mkhristu wina wacikulile amacita chimo mwadala kapena amalimbikitsa ena kucita zinthu zimene Yehova amazonda? Kodi tiyenela kumulekelela? Iyai. Yehova sadzaweluza anthu poona maonekedwe awo akunja, komanso sadzalekelela munthu wocita macimo mwadala cifukwa cakuti ni wacikulile. Yesaya 65:20 imati: “Wocimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, tembelelo lidzamugwela.” Mfundo yolingana na imeneyi inachulidwanso m’masomphenya amene Ezekieli anaona. (Ezek. 9:5-7) Conco, colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala kulemekeza ‘Wamasiku Ambiliyo,’ Yehova Mulungu. (Dan. 7:9, 10, 13, 14) Ngati ticita izi, sitidzayopa kupeleka uphungu mwaulemu kwa munthu wofunikila thandizo, ngakhale kuti ni wacikulile.—Agal. 6:1.

Kodi mumaonetsa ulemu kwa abale acinyamata? (Onani palagilafu 15)

15. Kodi tiphunzila ciani kwa mtumwi Paulo pa nkhani yoonetsa ulemu kwa abale acinyamata?

15 Nanga bwanji abale acinyamata mu mpingo? Kodi mumawaona bwanji? Paulo polembela kalata m’bale wacinyamata Timoteyo, anam’patsa malangizo akuti: “Usalole kuti munthu aliyense akudelele poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale citsanzo kwa okhulupilika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’cikondi, m’cikhulupililo, ndi pa khalidwe loyela.” (1 Tim. 4:12) Pamene Paulo anali kulemba mauwa, mwina Timoteyo anali atangokwanitsa kumene zaka 30. Komabe, Paulo anali atamupatsa udindo waukulu. Olo kuti sitidziŵa cimene anam’patsila malangizo amenewa, mfundo imene tiphunzilapo ni yoonekelatu. Tisamaweluze abale acinyamata potengela cabe zaka zawo zakubadwa. Tizikumbukila kuti ngakhale Ambuye wathu Yesu, anacita utumiki wawo wa pa dziko lapansi atangokwanitsa kumene zaka za m’ma 30.

16, 17. (a) Kodi akulu amadziŵa bwanji kuti m’bale ni woyenelela kuikidwa kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu? (b) Kodi nthawi zina maganizo athu kapena miyambo ya anthu zingasemphane bwanji na Malemba?

16 N’kutheka kuti malinga na cikhalidwe ca kumene tikhala, anthu ambili salemekeza acinyamata. Conco, akulu mu mpingo akhoza kumazengeleza kuyeneleza abale acinyamata kuti atumikile monga atumiki othandiza kapena akulu. Koma akulu onse ayenela kukumbukila mfundo yakuti, Malemba sachula ciŵelengelo ca zaka zakubadwa zimene munthu afunika kufika kuti ayenelele kutumikila monga mtumiki wothandiza kapena mkulu. (1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Ngati akulu akhazikitsa lamulo lawo pankhaniyi potengela cikhalidwe ca kwawo, ndiye kuti sakucita zinthu mogwilizana na Malemba. Abale acinyamata afunika kupendedwa mogwilizana na ziyenelezo za m’Mau a Mulungu, osati maganizo kapena miyambo ya anthu.—2 Tim. 3:16, 17.

17 Kutengela miyambo ya anthu yaconco kungapangitse kuti abale oyenelela azingokhala osaikidwa pa udindo. Mwacitsanzo, m’dziko lina mtumiki wothandiza woyenelela anapatsidwa maudindo ambili akulu-akulu. Olo kuti akulu mu mpingo wake anaona kuti m’baleyo akukwanilitsa ziyenelezo za m’Malemba zokhalila mkulu, iwo sanam’muyeneleze kuti aikidwe pa udindowu. Cifukwa ciani? Akulu ena acikulile mu mpingowo anali kuumilila kuti m’baleyo akali wacicepele cakuti sangayenelele kukhala mkulu. N’zomvetsa cisoni kuti m’baleyo sanapatsidwe mwayi wokhala mkulu cabe cifukwa cakuti anali kumuona monga wacicepele kwambili. Ici n’citsanzo cimodzi cabe, koma malipoti aonetsa kuti m’maiko enanso, anthu ali na maganizo otelo. Conco n’kofunika kwambili kuti tizidalila Malemba m’malo modalila nzelu zathu kapena cikhalidwe ca kwathu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti timamvela zimene Yesu anatilamula zakuti sitiyenela kuweluza ena potengela maonekedwe awo akunja.

MUZIWELUZA NDI CIWELUZO COLUNGAMA

18, 19. Tifunika kucita ciani kuti tiziona anthu ena mmene Yehova amawaonela?

18 Olo kuti ndise opanda ungwilo, tingaphunzile kuona ena mmene Yehova, Mulungu wopanda tsankho, amawaonela. (Mac. 10:34, 35) Koma kuti tikwanitse kucita zimenezi, tifunika kupitiliza kucita khama na kutsatila malangizo a m’Baibo. Tikamacita zimenezi, ndiye kuti tikumvela lamulo la Yesu lakuti “lekani kuweluza poona maonekedwe akunja.”—Yoh. 7:24.

19 Posacedwa, Mfumu yathu Yesu Khristu, idzaweluza anthu onse na ciweluzo colungama, osati potengela cabe zimene waona na maso ake kapena zimene wangomva na makutu ake. (Yes. 11:3, 4) Ndithudi, imeneyo idzakhala nthawi yokondweletsa ngako!