Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuphunzitsa Coonadi

Kuphunzitsa Coonadi

“Inu Yehova, . . . mawu anu onse ndi coonadi cokhacokha.”—SAL. 119:159, 160.

NYIMBO: 29, 53

1, 2. (a) Ni nchito yanji imene Yesu anaiika patsogolo mu umoyo wake? Nanga n’cifukwa ciani? (b) Tingacite ciani kuti tizilalikila mogwila mtima monga “anchito anzake a Mulungu”?

YESU KHRISTU anali kalipentala komanso mtumiki. (Maliko 6:3; Aroma 15:8) Iye anafika pokhala katswili pa nchito zimenezi. Pamene anali kalipentala, anaphunzila kuseŵenzetsa mwaluso zida za nchito imeneyi popanga zipangizo zosiyana-siyana zamapulanga. Pamene anali mphunzitsi wa uthenga wabwino, anaseŵenzetsa mwaluso cidziŵitso cake ca m’Malemba pothandiza anthu kumvetsetsa coonadi ca m’Mau a Mulungu. (Mat. 7:28; Luka 24:32, 45) Atafika zaka 30, Yesu analeka kugwila nchito ya ukalipentala, cifukwa anadziŵa kuti kutumikila Mulungu ndiyo nchito yofunika kwambili. Iye anakamba kuti cimodzi mwa zifukwa zimene Mulungu anam’tumila pa dziko lapansi, cinali cakuti adzalalikile uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 20:28; Luka 3:23; 4:43) Yesu anali kuika nchito yolalikila patsogolo mu umoyo wake, ndipo anali kufuna kuti anthu ena azigwila naye nchito imeneyi.—Mat. 9:35-38.

2 Ambili a ise sindise akalipentala. Koma mwacionekele, ndise alaliki a uthenga wabwino. Nchito imeneyi ni yofunika kwambili, cifukwa Mulungu ndiye mwini wake, ndipo ise ndise “anchito anzake.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 6:4) Timakhulupilila kuti “mau onse [a Yehova] ndi coonadi cokhacokha.” (Sal. 119:159, 160) Ndiye cifukwa cake timafuna ‘kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mau a coonadi’ mu ulaliki. (Ŵelengani 2 Timoteyo 2:15.) Kuti tikwanitse kucita izi, tifunika kupitiliza kukulitsa luso loseŵenzetsa Baibo, imene ni cida cacikulu cimene timagwilitsila nchito pophunzitsa anthu coonadi ponena za Yehova, Yesu, komanso Ufumu wa Mulungu. Pofuna kutithandiza kuti tizilalikila mogwila mtima, gulu la Yehova linapanga zida zophunzitsila zimene tifunika kudziŵa bwino moziseŵenzetsela. Timakamba kuti zida zimenezi zili mu Thuboksi yathu ya Zida Zophunzitsila.

3. Popeza tatsala na nthawi yocepa yocitila umboni, kodi colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala ciani? Nanga mfundo ya pa Machitidwe 13:48 ingatithandize bwanji kucita zimenezo?

3 Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’cifukwa ciani timaicha Thuboksi ya Zida Zophunzitsila, osati Thuboksi ya Zida Zolalikilila?’ “Kulalikila” kumatanthauza kulengeza uthenga. Koma “kuphunzitsa” kumatanthauza kukhomeleza uthengawo mu mtima mwa munthu, pofuna kumusonkhezela kucitapo kanthu pa zimene waphunzila. Cifukwa cakuti tatsala na nthawi yocepa yocitila umboni, colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala kuyambitsa maphunzilo a Baibo na kuphunzitsa anthu coonadi. Izi zitanthauza kuti tiyenela kuyesetsa kusakila anthu ‘amene ali ndi maganizo abwino’ amene angawathandize kukhala okhulupilila kuti akapeza moyo wosatha.—Ŵelengani Machitidwe 13:44-48.

4. Tingawapeze bwanji anthu amene ali na ‘maganizo amene angawathandize kukapeza moyo wosatha’?

4 Kodi tingawapeze bwanji anthu amene ali na ‘maganizo amene angawathandize kukapeza moyo wosatha’? Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, anthu amenewa tingawapeze kokha mwa kugwila nchito yolalikila. Tifunika kutsatila malangizo amene Yesu anapeleka. Iye anati: “Mukaloŵa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenelela.” (Mat. 10:11) Timadziŵa kuti pali anthu odzikuza, osaona mtima, kapena opanda cidwi na zinthu zauzimu, amene sangalabadile uthenga wabwino. Conco, timasakila anthu amene ni oona mtima, odzicepetsa, komanso amene ali na njala ya coonadi. Tingayelekezele nchito imeneyi na zimene Yesu anali kucita pogwila nchito yake ya ukalipentala. Iye anali kusakila mapulanga abwino amene angawaseŵenzetse popanga mipando, mathebo, zitseko, majoko, na zinthu zina. Akapeza pulanga yabwino, anali kutenga zida zake na kupanga cinthu cimene akufuna. Na ise tiyenela kuyesetsa kusakila anthu oona mtima na kuwapanga kukhala ophunzila a Khristu.—Mat. 28:19, 20.

5. Kodi tiyenela kudziŵa ciani cokhudza zida zathu zophunzitsila? Fotokozani fanizo. (Onani pikica kuciyambi.)

5 Cida ciliconse ca mu Thuboksi cimakhala na nchito yake. Mwacitsanzo, ganizilani zida za ukalipentala zimene Yesu ayenela kuti anali kuseŵenzetsa. * Iye anali na zida zopimila mapulanga, zodulila, zoboolela, zogobela, zopalila, zolumikizila, na zokhomela. Mofananamo, cida ciliconse cimene cili mu Thuboksi yathu ya Zida Zophunzitsila cili na nchito yake. Zida zimenezi n’zofunika kwambili. Tsopano tiyeni tikambilane zokhudza zida zimenezi, komanso mmene tingaziseŵenzetsele.

ZIDA ZOTHANDIZA ANTHU KUTI ATIDZIŴE

6, 7. (a) Kodi tumakadi tongenela pa webusaiti yathu mwakhala mukutuseŵenzetsa motani? (b) Kodi tumapepa toitanila anthu ku misonkhano tunapangiwa na zolinga ziŵili ziti?

6 Tumakadi tongenela pa webusaiti yathu. Tumakhadi tumenetu n’tothandiza kwambili. Timatuseŵenzetsa pothandiza anthu kuti atidziŵe, komanso kuti adziŵe za webusaiti yathu. Akangena pa webusaiti yathu, angadziŵe zambili zokhudza ise, ndiponso angapemphe phunzilo la Baibo. Kufika pano, talandilapo mapempho oposa 400,000 a phunzilo la Baibo kupitila pa jw.org. Ndipo timalandila mapempho mahandiledi angapo tsiku lililonse! Mungacite bwino kumanyamulako tumakadi tumenetu pa zocita zanu za tsiku na tsiku, kuti muzituseŵenzetsa nthawi iliyonse mukapeza mpata wocitila umboni.

7 Tumapepa twa ciitanilo. Kapepa kamene nthawi zambili timakachula kuti kapepa koitanila anthu ku misonkhano, kanapangiwa na zolinga ziŵili. Kapepaka kamati: “Tikupemphani kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova.” Ndiyeno kamaonetsa kuti munthu angaphunzile Baibo, kaya ku “misonkhano yathu” kapena ‘ndi munthu wom’phunzitsa Baibo.’ Conco, kuwonjezela pa kutidziŵikitsa, kapepa kameneka kamalimbikitsanso anthu amene “amazindikila zosoŵa zawo zauzimu,” kuti ayambe kuphunzila nase Baibo. (Mat. 5:3) Komabe, anthu angabwele ku misonkhano yathu, kaya amaphunzila nase Baibo kapena ayi. Akapezekapo, adzazindikila kuti angaphunzile mfundo zambili za coonadi ca m’Baibo.

8. N’cifukwa ciani tifunika kulimbikitsa anthu kuti akapezekeko ku misonkhano yathu ngakhale kamodzi cabe? Fotokozani citsanzo.

8 Tifunika kupitiliza kuitanila anthu ku misonkhano yathu kuti akapezekeko ngakhale kamodzi cabe. Cifukwa ciani? Cifukwa akapezekapo, adzazindikila kuti mosiyana na Babulo Wamkulu, Mboni za Yehova zimaphunzitsa coonadi ca m’Baibo na kuthandiza anthu kudziŵa Mulungu. (Yes. 65:13) Ray na mkazi wake Linda, amene akhala ku America, anazindikila zimenezi zaka zingapo m’mbuyomo. Iwo anaona kuti afunika kuyamba kupita ku chechi. Anali kukhulupilila kuti Mulungu alipo, ndipo anafuna kuphunzila zambili zokhudza iye. Conco, anayamba kupita ku machechi osiyana-siyana amene anali m’tauni yawo. M’tauniyo munali machechi ambili-mbili. Asanayambe kupita kumachechiwo, anaikilatu ziyenelezo ziŵili zimene chechi inayenela kukwanilitsa kuti akhale mamembala ake. Coyamba, inafunika kukhala chechi yakuti akapitako kukapemphela, akaphunzileko kenakake. Ndipo caciŵili, mamembala a chechiyo anafunika kuvala moonetsa kuti ni anthudi a Mulungu. Patapita zaka zingapo, anatsiliza kupita ku machechi onse a m’tauniyo. Koma sanapeze chechi yoyenelela. Ku machechiko sanaphunzileko ciliconse, ndipo kavalidwe ka anthu kumeneko sikanali kaulemu ngakhale pang’ono. Atatuluka m’chechi yotsilizila, Linda anapita ku nchito kwake, ndipo Ray anayamba kubwelela ku nyumba. Ali m’njila, Ray anaona Nyumba ya Ufumu, ndipo anayamba kudzikambila mu mtima kuti, ‘Kodi mmenemu mumacitika zotani? Lekani nikaloŵemo kuti nikaone.’ Iye anacita cidwi ngako na zimene anaona! Aliyense m’Nyumba ya Ufumuyo anali wokoma mtima, waubwenzi, komanso anavala mwaulemu kwambili. Ray anakhala pa mpando wa kutsogolo, ndipo anakondwela na zimene anaphunzila. Izi zitikumbutsa zimene mtumwi Paulo anakamba ponena za munthu amene wabwela ku misonkhano yacikhristu kwa nthawi yoyamba. Mtumwiyo anakamba kuti munthuyo angakambe kuti: “Zoonadi, Mulungu ali pakati panu.” (1 Akor. 14:23-25) Kucokela nthawiyo, Ray anayamba kupezeka pa misonkhano yonse ya pa Sondo. Ndipo patapita nthawi anayambanso kupezeka pa misonkhano yonse ya mkati mwa wiki. Linda nayenso anayamba kusonkhana. Olo anali na zaka za m’ma 70, iwo anavomela phunzilo la Baibo ndipo anabatizika.

ZIDA ZOYAMBITSILA MAKAMBILANO

9, 10. (a) N’cifukwa ciani tumapepa twauthenga n’tosavuta kuseŵenzetsa mu ulaliki? (b) Fotokozani mmene tingaseŵenzetsele kapepa kakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani?

9 Tumapepa twa uthenga. Tili na tumapepa 8 tosavuta kuseŵenzetsa, tumene ni zida zothandiza kwambili zoyambitsila makambilano. Kucokela pamene tumapepa tumenetu tunatulutsidwa mu 2013, tumapepa toposa 5 biliyoni twapulintiwa. Ubwino wa tumapepa tumenetu ni wakuti, mukaphunzila kugaŵila kapepa kamodzi, ndiye kuti mungakwanitse kugaŵila tumapepa tonse cifukwa tunapangiwa molingana. Kodi mungaseŵenzetse bwanji kapepa kauthenga poyambitsa makambilano?

10 Tinene kuti mwasankha kapepa kakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Ciani? Onetsani munthu funso imene ili patsogolo pa kapepaka na kum’funsa kuti, “Kodi mumaganiza kuti Ufumu wa Mulungu n’ciani? Kodi mungayankhe kuti ndi . . . ?” Ndiyeno m’pempheni kuti asankhepo yankho limene aona kuti n’lolondola. Popanda kukamba kuti wayankha bwino kapena ayi, muonetseni pa kamutu kakuti “Zimene Baibulo Limanena,” kamene kali mkati. Kenako, ŵelengani naye malemba amene ali pamenepo, Danieli 2:44 na Yesaya 9:6. Ngati n’zotheka, pitilizani kukamba naye. Cotsiliza, m’funseni funso la ulendo wobwelelako, limene lili kumbuyo kwa kapepako, pa kamutu kakuti, “Ganizilani Funso Ili.” Funso lake n’lakuti: “Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu?” Mukatelo, ndiye kuti mwayala maziko a ulendo wobwelelako. Pa ulendo wobwelelako, mukawauze za phunzilo 7 la m’kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. Kabuku kameneka ni kamodzi mwa zida zathu zoyambitsila maphunzilo a Baibo.

ZIDA ZOKOPELA CIDWI CA ANTHU MU ULALIKI

11. Kodi magazini athu amapangiwa kuti azitithandiza kucita ciani? Nanga tiyenela kudziŵa ciani cokhudza magazini amenewa?

11 Magazini. Nsanja ya Mlonda na Galamuka! ni magazini amene amafalitsidwa kwambili na kumasulidwa m’zitundu zambili kuposa magazini aliwonse padziko lonse lapansi. Popeza magaziniwa amafalitsidwa padziko lonse, nkhani zake za pacikuto zimakonzewa m’njla yakuti zizikhala zokopa cidwi kwa anthu kulikonse pa dziko. Tiyenela kuseŵenzetsa zida zimenezi kuti tiutse cidwi ca anthu pa nkhani zofunika kwambili mu umoyo. Komabe, tifunika kudziŵa bwino kuti magazini iliyonse anaikonzela ndani maka-maka. Izi zidzatithandiza kuti tizigaŵila magaziniwa kwa anthu oyenelela.

12. (a) Kodi magazini ya Galamuka! anaikonzela ndani maka-maka? Nanga colinga ca magaziniyi n’ciani? (b) Fotokozani zotulukapo zabwino zimene zinakhalapo posacedwapa, pamene munaseŵenzetsa cida cimeneci mu ulaliki.

12 Galamuka! inakonzedwela anthu amene sadziŵa ciliconse cokhudza Baibo, kapena amene amaidziŵako pang’ono. Anthu amenewa angakhale kuti sadziŵa ciliconse cokhudza ziphunzitso zacikhristu, sakhulupilila cipembedzo, komanso sadziŵa kuti Baibo ili na mfundo zothandiza mu umoyo. Colinga cacikulu ca Galamuka! ni kuthandiza woŵelenga kukhulupilila kuti Mulungu aliko. (Aroma 1:20; Aheb. 11:6) Cinanso, magaziniyi inapangiwa kuti izithandiza woŵelenga kukhala na cikhulupililo cakuti Baibo ni “mawu a Mulungu.” (1 Ates. 2:13) Nkhani zitatu za pacikuto za m’magazini a Galamuka! a mu 2018 ni izi: “Njila Yopezela Cimwemwe,” “Zinsinsi 12 za Banja Lacimwemwe” na yakuti “Thandizo kwa Ofedwa.”

13. (a) Kodi Nsanja ya Mlonda yogaŵila inakonzedwela ndani? (b) Fotokozani zotulukapo zabwino zimene zinakhalapo posacedwapa, pamene munaseŵenzetsa cida cimeneci mu ulaliki.

13 Nsanja ya Mlonda yogaŵila, inakonzewa kuti izithandiza anthu amene amalemekeza Mulungu na Mawu ake kumvetsetsa ziphunzitso za m’Baibo. Anthu amenewa akhoza kukhala kuti amadziŵako zina za m’Baibo, koma sadziŵa molondola ziphunzitso zake. (Aroma 10:2; 1 Tim. 2:3, 4) Nkhani zitatu za pa cikuto m’magazini a Nsanja ya Mlonda yogaŵila, a mu 2018, zipeleka mayankho pa mafunso aya: “Kodi Baibo Ikali Yothandiza Masiku Ano?,” “Kodi Kutsogolo Kuli Ciani?,” komanso yakuti, “Kodi Mulungu Amakudelani Nkhawa?”

ZIDA ZOLIMBIKITSA ANTHU KUCITAPO KANTHU

14. (a) Kodi mavidiyo anayi amene ali mu Thuboksi yathu ya Zida Zophunzitsila ali na nchito yanji? (b) Nanga n’zotulukapo zabwino ziti zimene zinakhalapo pamene munaseŵenzetsa mavidiyo amenewa?

14 Mavidiyo. M’nthawi ya Yesu, kalipentala anali kuseŵenzetsa zida za manja cabe. Koma masiku yano, kuwonjezela pa zida zimenezo, akalipentala amaseŵenzetsa zida zamalaiti monga zocekela, zoboolela, zosalazila, zokhomela misomali, na zina zaconco. Mofananamo, kuwonjezela pa zofalitsa zopulintiwa, tilinso na mavidiyo okopa cidwi amene timatambitsa anthu. Anayi mwa mavidiyo amenewa ali mu Thuboksi yathu ya Zida Zophunzitsila. Mavidiyo amenewa ni akuti: N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?, Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji?, N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu?, komanso yakuti Mboni za Yehova—Kodi Ndife Anthu Otani? Mavidiyo a maminetsi osapitilila aŵili ni othandiza ngako pa ulendo woyamba mu ulaliki. Koma otalikilapo mungawaseŵenzetse pa ulendo wobwelelako, kapena kwa anthu amene ali na nthawi yokwanila. Zida zamphamvu zimenezi zimasonkhezela anthu kuyamba kuphunzila Baibo na kupezeka pamisonkhano yathu.

15. Fotokozani zitsanzo zoonetsa mmene anthu amakhudzidwila akatambako imodzi mwa mavidiyo athu m’citundu cawo.

15 Mwacitsanzo, mlongo wina anakumana na mayi wina wocokela ku Micronesia, amene citundu cake ni Ciyapese. Iye anamuonetsa mayiyo vidiyo ya m’citundu cake yakuti, N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? Vidiyo itayamba, mayi uja anati: “Ici n’citundu canga. Sinikukhulupilila! Nadziŵila kakambidwe kake kuti munthu amene akukamba ni wocokela kwathu. Akukamba citundu cathu!” Ndiyeno, mayiyo anakamba kuti adzaŵelenga na kutamba zonse za m’citundu cake zimene zili pa webusaiti yathu. (Yelekezelani na Machitidwe 2:8, 11) Ganizilani citsanzo cina ici: Mlongo wina ku America anatumizila msuweni wake link ya vidiyo imodzi-modziyi m’citundu cake. Ataitamba, munthuyo anatumila mlongoyo meseji yakuti: “Mbali yakuti pali munthu wina woipa amene akulamulila dziko inanicititsa cidwi kwambili, cakuti napempha phunzilo la Baibo pa intaneti.” Munthuyo amakhala m’dziko limene Mboni za Yehova n’zoletsedwa.

ZIDA ZOPHUNZITSILA COONADI

16. Fotokozani colinga ca tumabuku utu: (a) Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. (b) Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. (c) Ndani Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?

16 Tumabuku. Kodi anthu amene sadziŵa kuŵelenga, kapena amene m’citundu cawo mulibe zofalitsa mungawaphunzitse bwanji coonadi? Tili na zida zothandiza kwambili kwa anthu aconco. Tili na kabuku kakuti, Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. * Cida cothandiza ngako coyambitsila phunzilo la Baibo ni kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. Mungaonetse munthu nkhani zokwana 14 zimene zili kumapeto kwa kabukuka, na kum’pempha kuti asankhepo imene wakonda. Ndiyeno, mungayambe kuphunzila naye nkhani imeneyo. Kodi munayesako kucita zimenezi pa ulendo wobwelelako? Kabuku kacitatu mu Thuboksi yathu ni kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? Kabuku aka kanakonzewa kuti kazitithandiza kutsogolela anthu ku gulu la Mulungu. Kuti mudziŵe mmene mungakaseŵenzetsele pambuyo pa phunzilo la Baibo lililonse, onani Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu ka March 2017.

17. (a) Fotokozani colinga ca buku lililonse lophunzilila. (b) Kodi anthu amene apita patsogolo mpaka kubatizika afunika kucita ciani? Nanga cifukwa cake n’ciani?

17 Mabuku. Mukayamba kuphunzila Baibo na munthu poseŵenzetsa kabuku, nthawi iliyonse mungasinthe n’kuyamba kuseŵenzetsa buku lakuti, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. Cida cimeneci cidzathandiza munthuyo kudziŵa bwino ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. Mukatsiliza buku limeneli, ndipo ngati wophunzila akupita patsogolo, mungapitilize kuphunizila naye buku lakuti, Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu. * Buku limeneli limathandiza wophunzila kudziŵa mmene angagwilitsile nchito mfundo za m’Baibo mu umoyo wake. Komanso, kumbukilani kuti ngakhale pambuyo pakuti wophunzila wabatizika, muyenela kupitiliza kuphunzila naye mpaka mutatsiliza mabuku onse aŵili. Izi zidzathandiza wophunzilayo kukhala wozikika mozama m’coonadi.—Ŵelengani Akolose 2:6, 7.

18. (a) Kodi 1 Timoteyo 4:16 imatilimbikitsa kucita ciani monga aphunzitsi a coonadi? Nanga tikacita zimenezo, zotulukapo zake zimakhala zotani? (b) Kodi colinga cathu ciyenela kukhala ciani pamene tiseŵenzetsa Thuboksi yathu ya Zida Zophunzitsila?

18 Pokhala Mboni za Yehova, tinapatsidwa “coonadi ca uthenga wabwino” cimene cingathandize anthu kukapeza moyo wosatha. (Akol. 1:5; ŵelengani 1 Timoteyo 4:16.) Ndiye cifukwa cake tapatsidwa Thuboksi yokhala na zida zoyenelela zimene zingatithandize pophunzitsa anthu coonadi. (Onani “ Thuboksi ya Zida Zophunzitsila.”) Tiyeni tiziyesetsa mmene tingathele kuseŵenzetsa mwaluso zida zimenezi. Wofalitsa aliyense angasankhe yekha cofalitsa ca mu thuboksi yathu cimene afuna kuseŵenzetsa polalikila, komanso nthawi imene afuna kucigwilitsila nchito. Koma colinga cathu cisakhale cabe kugaŵila zofalitsa, ndiponso sitiyenela kugaŵila zofalitsa zathu kwa anthu amene alibe cidwi. Colinga cathu ni kupanga ophunzila kwa anthu amene ni oona mtima, odzicepetsa, komanso a njala ya coonadi, inde, anthu amene ali ‘ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48; Mat. 28:19, 20.

^ par. 5 Onani nkhani yakuti, “Mmisiri wa Matabwa,” na bokosi yakuti “Zipangizo za Mmisiri wa Matabwa,” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2010.

^ par. 16 Ngati munthu sadziŵa kuŵelenga, mungamupemphe kuti azikutsatilani m’kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kamene kali na zithunzi zambili koma mau ocepa.

^ par. 17 Buku lakuti Mmene Mungakhalilebe m’Cikondi ca Mulungu likadzatuluka m’Cinyanja, mukayambe kuseŵenzetsa limenelo.