Khalanibe na Mtendele wa mu Mtima Olo Pamene Zinthu Zasintha
“Ine ndadzitonthoza ndipo ndakhazika mtima wanga pansi.”—SAL. 131:2.
1, 2. (a) Kodi Mkhristu angakhudzidwe bwanji zinthu zikasintha mosayembekezeleka mu umoyo wake? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Malinga ndi Salimo 131, ni maganizo otani amene angatithandize kukhalabe na cimwemwe ca mu mtima?
LLOYD na Alexandra atauzidwa kuti acoke pa Beteli na kupita kukatumikila ku mpingo, poyamba anadandaula. Iwo anali atatumikila pa Beteli kwa zaka zopitilila 25. Lloyd anati: “N’nali kuukonda ngako utumiki wanga, ndipo Beteli inangokhala ngati ndiye kwathu. N’nali kumvetsa cifukwa cake panakhala masinthidwe amenewa. Koma kwa mawiki na miyezi ingapo izi zitacitika, n’nali kudzimva ngati munthu wokanidwa.” Nthawi zina, Lloyd anali kuona kuti kusintha kumeneku kunali cabe bwino, koma nthawi zinanso anali kukhala na nkhawa kwambili.
2 Zinthu zikasintha mosayembekezeleka mu umoyo wathu, tingakhale na nkhawa yaikulu. (Miy. 12:25) Ngati zinthu zasintha mu umoyo wathu, ndipo zikutivuta kupilila, kodi tingacite ciani kuti ‘tidzitonthoze ndi kukhazika mtima wathu pansi’? (Ŵelengani Salimo 131:1-3.) Tiyeni tikambilane zimene zinathandiza atumiki ena a Yehova akale komanso amakono kukhalabe na mtendele wa mu mtima pamene zinthu zinasintha mu umoyo wawo.
PEZANI “MTENDELE WA MULUNGU”
3. Kodi Yosefe anakumana na mavuto anji?
3 Yosefe anali na zaka pafupi-fupi 17 pamene abululu ake anam’gulitsa ku ukapolo cifukwa ca nsanje. Anam’citila nsanje cifukwa atate awo anali kum’konda kwambili. (Gen. 37:2-4, 23-28) Kwa zaka pafupi-fupi 13, Yosefe anavutika monga kapolo ku Iguputo, komanso anaikidwa m’ndende. Iye anali kutali na kumene kunali Yakobo, atate wake wokondedwa. N’ciani cinam’thandiza kuti asataye mtima kapena kukhumudwa na mavutowa?
4. (a) Kodi Yosefe anali kusumika maganizo ake pa ciani pamene anali m’ndende? (b) Nanga Yehova anayankha bwanji mapemphelo ake?
4 Pamene anali kuvutika m’ndende, Yosefe ayenela kuti anali kusumika maganizo ake pa umboni woonetsa kuti Yehova anali kum’dalitsa. (Gen. 39:21; Sal. 105:17-19) Mwacionekele, maloto aulosi amene iye analota pamene anali wacicepele, nawonso anamuthandiza kukhulupilila kuti Yehova anali kum’konda. (Gen. 37:5-11) N’zoonekelatu kuti Yosefe anali kukhutulila Yehova nkhawa zake m’pemphelo. (Sal. 145:18) Poyankha mapemphelo ake, Yehova anam’thandiza kukhulupilila na mtima wonse kuti iye adzakhala naye m’mayeselo ake onse.—Mac. 7:9, 10. *
5. Kodi “mtendele wa Mulungu” ungatithandize bwanji kukwanilitsa zolinga zauzimu?
5 Ngakhale titakumana na mavuto aakulu, na ise tingatonthozedwe na “mtendele wa Mulungu,” umene umateteza maganizo athu. (Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.) Conco, tikakhala na nkhawa yaikulu, tiyenela kupemphela kwa Yehova. Tikatelo, mtendele wa Mulungu ungatilimbikitse kukwanilitsa zolinga zathu zauzimu na kutipatsa mphamvu kuti tisafooke. Tsopano tiyeni tikambilane zitsanzo zamakono zotsimikizila mfundo imeneyi.
MUZIPEMPHELA KWA YEHOVA KUTI MUKHALENSO NA MTENDELELE WA MU MTIMA
6, 7. Kodi kupeleka mapemphelo acindunji kungatithandize bwanji kukhalanso na mtendele wa mu mtima? Fotokozani citsanzo.
6 Ryan na mkazi wake Juliette atauzidwa kuti utumiki wawo monga apainiya apadela akanthawi watha, anakhala na nkhawa kwambili. Ryan anati: “Titangouzidwa, tinaipemphelela nkhaniyi kwa Yehova. Tinaona kuti umenewo unali mwayi wapadela woonetsa kuti timam’dalila. Ambili mu mpingo mwathu anali acatsopano. Conco, tinapemphela kwa Yehova kuti atithandize kuonetsa citsanzo cabwino pa nkhani ya kukhala na cikhulupililo.”
7 Kodi Yehova anayankha bwanji pemphelo lawo? Ryan anati: “Titangopemphela, maganizo ofooketsa komanso nkhawa zonse zimene tinali nazo zinathelatu. Mtendele wa Mulungu unateteza mitima yathu na maganizo athu. Ndipo tinazindikila kuti Yehova angapitilize kutiseŵenzetsa ngati tiikabe zinthu zauzimu patsogolo.”
8-10. (a) Kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize bwanji kuthetsa nkhawa? (b) Kodi Yehova angatidalitse bwanji ngati tiyesetsa kuika zinthu zauzimu patsogolo?
8 Kuwonjezela pa kutikhazika mtima pansi, mzimu wa Mulungu ungatikumbutsenso malemba olimbikitsa amene angatithandize kuikabe zinthu zauzimu patsogolo. (Ŵelengani Yohane 14:26, 27.) Ganizilani za Philip na mkazi wake Mary, amene anatumikila pa Beteli kwa zaka pafupi-fupi 25. Patapita cabe miyezi inayi kucokela pamene anacoka pa Beteli, onse aŵili anataikilidwa amayi awo. Komanso, Philip anataikilidwa mbululu wake wina. Ndiyeno, iwo anayamba kusamalila atate ake a Mary, amene ali na matenda aakulu a m’maganizo.
9 Philip anati: “N’nali kudziona monga munthu wopilila, koma panali cinacake cimene cinali kusoŵeka. N’taŵelenga Akolose 1:11 m’nkhani inayake yophunzila ya mu Nsanja ya Mlonda, n’nazindikila kuti olo kuti n’nali kupilila, kupilila kwanga sikunali kokwanila. N’nafunika ‘kupilila zinthu zonse ndi kukhala woleza mtima ndiponso wacimwemwe.’ Lembali linanikumbutsa kuti cimwemwe canga sicidalila mmene zinthu zilili mu umoyo wanga, koma cimadalila mmene mzimu wa Mulungu ukugwilila nchito mu umoyo wanga.”
10 Cifukwa cakuti Philip na Mary anaikabe mtima wawo pa zinthu zauzimu olo pamene anakumana na mavuto, Yehova anawadalitsa m’njila zambili. Mwacitsanzo, atangocoka pa Beteli, onse aŵili anapeza maphunzilo a Baibo ocita bwino, amene anali kufuna kuti aziphunzila nawo maulendo angapo pa wiki. Pokumbukila nthawiyo, Mary anati, “Tikaganizila za iwo, tinali kukhala acimwemwe. Zinali monga Yehova akutiuza kuti, ‘Musadele nkhawa, zonse zidzakhala bwino.’”
CITANI MBALI YANU, NDIPO YEHOVA ADZAKUDALITSANI
11, 12. (a) Kodi Yosefe anacita ciani cimene cinapangitsa kuti Yehova am’dalitse? (b) Nanga anadalitsidwa bwanji cifukwa ca kupilila kwake?
11 Zinthu zikasintha mosayembekezeleka mu umoyo wathu, n’zosavuta kukhwethemuka maganizo cifuwa ca nkhawa. Zaconco zikanamucitikilanso Yosefe. Koma iye sanalole nkhawa kumufooketsa. M’malomwake, anacita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zinalili mu umoyo wake, ndipo Yehova anam’dalitsa. Olo pamene anali m’ndende, Yosefe anali kugwila mwakhama nchito imene mkulu wa ndende anam’patsa, monga mmene anali kucitila potumikila Potifara.—Gen. 39:21-23.
12 Nthawi ina, Yosefe anapatsidwa udindo woyang’anila amuna aŵili, amene poyamba anali na maudindo aakulu m’nyumba yacifumu ya Farao. Poona khalidwe la Yosefe la kukoma mtima, tsiku lina amunawo anam’fotokozela mavuto awo, komanso maloto odabwitsa amene analota usiku wa tsikulo. (Gen. 40:5-8) Yosefe sanadziŵe kuti zimene iye anakambilana na amunawo, m’kupita kwa nthawi, zidzakhala na zotulukapo zabwino. N’zoona kuti anakhalabe m’ndende kwa zaka zina ziŵili. Koma pambuyo pake anatulutsidwa, ndipo tsiku lomwelo, anaikidwa kukhala waciŵili kwa mfumu Farao.—Gen. 41:1, 14-16, 39-41.
13. Mosasamala kanthu mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, kodi tingacite ciani kuti Yehova atidalitse?
13 Mofanana na Yosefe, na ise nthawi zina tingakumane na zinthu zothetsa nzelu. Komabe, ngati tikhalabe oleza mtima na kucita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zilili, Yehova adzatidalitsa. (Sal. 37:5) N’zoona kuti nthawi zina ‘tingathedwe nzelu.’ Koma monga mmene mtumwi Paulo anakambila, sitidzathedwa nzelu mpaka “kusowelatu pothawila.” (2 Akor. 4:8) Mau a Paulo amenewa adzakwanilitsidwa pa ise, maka-maka ngati tiikabe mtima wathu pa nchito yolalikila.
IKANIBE MTIMA WANU PA NCHITO YOLALIKILA
14-16. N’ciani cionetsa kuti mlaliki Filipo anaikabe mtima wake pa nchito yolalikila olo pamene zinthu zinasintha mu umoyo wake?
14 Mlaliki Filipo ni citsanzo cabwino cifukwa * Pa nthawiyo, Filipo anali atangopatsidwa kumene utumiki watsopano. (Mac. 6:1-6) Koma pamene ophunzila a Khristu anamwazikana cifukwa ca cizunzo, Filipo sanangokhala phee n’kumaonelela zimene zikucitika. Iye anapita kukalalikila ku Samariya. Pa nthawiyo, anthu ambili a kumeneko anali asanamveleko uthenga wabwino.—Mat. 10:5; Mac. 8:1, 5.
anaikabe mtima wake pa nchito yolalikila, ngakhale pamene zinthu zinasintha. Sitefano ataphedwa cifukwa ca cikhulupililo cake, mu Yerusalemu munabuka cizunzo cacikulu.15 Filipo anali wokonzeka kupita kulikonse kumene mzimu wa Mulungu unam’tsogolela. Ndiye cifukwa cake Yehova anam’tumiza kukalalikila ku gawo latsopano. Iye anali munthu wopanda tsankho. Koma Ayuda ambili anali kuona Asamariya monga anthu otsika. Conco, pamene Filipo anapita kukalalikila ku Samariya, Asamariya ambili ayenela kuti anatsitsimulidwa na uthenga wake. Baibo imakamba kuti makamu a anthu anali “kutchela khutu ndi mtima umodzi.”—Mac. 8:6-8.
16 Kenako, mzimu wa Mulungu unatsogolela Filipo kupita ku Asidodi na ku Kaisareya, mizinda iŵili imene munali anthu ambili amene sanali Ayuda. (Mac. 8:39, 40) Patapita zaka 20 kucokela pamene Filipo anayamba kulalikila ku Samariya, zinthu zinali zitasinthanso mu umoyo wake. Pa nthawiyi, anali na banja, ndipo anali kukhala ku dela limene anali kulalikilako. Olo kuti zinthu zinasintha mu umoyo wake, Filipo anaikabe mtima wake pa nchito yolalikila. Mwa ici, Yehova anam’dalitsa kwambili pamodzi na banja lake.—Mac. 21:8, 9.
17, 18. Kodi kuikabe mtima wathu pa nchito yolalikila kungatithandize bwanji kukhalabe olimba pamene zinthu zasintha?
17 Atumiki ambili a nthawi zonse angavomeleze kuti kuikabe mtima wawo pa nchito yolalikila kwawathandiza kukhalabe olimba ngakhale pamene zinthu zasintha mu umoyo wawo. Mwacitsanzo, ganizilani za Osborne na mkazi wake Polite, amene amakhala ku South Africa. Iwo atacoka pa Beteli, anali kuganiza kuti posapita nthawi adzapeza nyumba yokhalamo, komanso nchito ya maola ocepa. Osborne anati: “Mwatsoka lanji, nchito sitinaipeze mwamsanga.” Mkazi wake Polite anati: “Panapita miyezi itatu nchito osaipeza, ndipo tinalibenso ndalama ku banki. Linali vuto lalikulu.”
18 N’ciani cinawathandiza kupilila vuto limeneli? Osborne anati: “Kulalikila na mpingo kunatithandiza kwambili kuti tisataye mtima komanso kuti tiikebe maganizo athu pa zinthu zauzimu. Tinaganiza zowonjezela zocita pa nchito yolalikila, m’malo mongokhala n’kumadandaula za mavuto
athu. Ndipo kucita zimenezo kunatibweletsela cimwemwe coculuka. Tinayesetsa kusakila nchito, ndipo pamapeto pake tinaipeza.”MUZIYEMBEKEZELA YEHOVA MOLEZA MTIMA
19-21. (a) N’ciani cingatithandize kukhalabe na cimwemwe ca mu mtima? (b) Ni mapindu ati amene tingapeze ngati tiikabe zauzimu patsogolo zinthu zikasintha?
19 Monga taonela m’zitsanzo zimenezi, ngati ticita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, komanso ngati tiyembekezela Yehova mwacidalilo, tidzakhalabe na mtendele wa mu mtima. (Ŵelengani Mika 7:7.) Ndipo ngati tiikabe zauzimu patsogolo pamene zinthu zasintha mu umoyo wathu, ubwenzi wathu na Yehova ungalimbileko. Pokumbukila zimene zinawacitikila, Polite, amene tam’chula m’ndime zapitazi, anati: “Kusintha kwa utumiki kwaniphunzitsa kudalila Yehova ngakhale pamene zinthu zioneka zovuta kwambili. Ndipo ubwenzi wanga na iye walimba maning’i.”
20 Mary, amene tam’chulapo kale m’nkhani ino, akali kusamalila atate ake okalamba kwinaku akucita upainiya. Iye anati: “Tsopano n’nadziŵa kuti ngati nili na nkhawa, nifunika kupemphela, na kukhazika mtima pansi. Cacikulu cimene naphunzilapo n’cakuti, nifunika kumatulila Yehova nkhawa zanga zonse. Ndipo zimene naphunzilazi zidzanithandiza kwambili m’tsogolo.”
21 Lloyd na Alexandra, amene tawachula kuciyambi, anavomeleza kuti kusintha kwa utumiki wawo kunayesa cikhulupililo cawo m’njila imene sanali kuyembekezela. Koma iwo anati: “Cikhulupililo cikayesedwa m’pamene cimaoneka kuti n’ceni-ceni, komanso kuti cingatithandize na kutilimbikitsa pa nthawi ya mavuto. Ndipo pamapeto pake, cimalimba kwambili.”
22. Kodi sitiyenela kukayikila ciani ngati tiyesetsa kucita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wathu?
22 Nthawi zina, zinthu mu umoyo zingasinthe mosayembekezeleka, mwina cifukwa ca kusintha kwa utumiki, matenda, kapena maudindo atsopano a m’banja. Zikakhala conco, musakayikile kuti Yehova amakukondani, ndipo adzakuthandizani pamene mufunika thandizo. (Aheb. 4:16; 1 Pet. 5:6, 7) Conco pali pano, muzicita zonse zimene mungathe malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wanu. Komanso muziyandikila Atate wanu wakumwamba m’pemphelo, ndipo phunzilani kum’dalila na mtima wonse cifukwa iye amakukondani. Mukatelo, mudzakhalabe na mtendele wa mu mtima olo pamene zinthu zasintha mu umoyo wanu.
^ par. 4 Pa nthawi ina atatulutsidwa m’ndende, Yosefe anakamba kuti Yehova anamutonthoza pa mavuto ake mwa kum’patsa mwana wamwamuna. Iye anacha mwana wake woyamba dzina lakuti Manase, cifukwa anati: “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse.”—Gen. 41:51, ftn.
^ par. 14 Onani nkhani yakuti “Kodi Mudziŵa?,” imene ili m’magazini ino.