Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tizidalila Mtsogoleli Wathu—Khristu

Tizidalila Mtsogoleli Wathu—Khristu

“Mtsogoleli wanu ndi mmodzi, Khristu.”—MAT. 23:10.

NYIMBO: 16, 14

1, 2. Kodi Yoswa anali na nkhawa yanji Mose atamwalila?

YOSWA anali kukumbukilabe mawu amene Yehova anamuuza, akuti: “Mose mtumiki wanga wamwalila. Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu ndi kulowa m’dziko limene ndikulipeleka kwa ana a Isiraeli.” (Yos. 1:1, 2) Uku kunali kusintha kwakukulu cotani nanga mu umoyo wa Yoswa, amene kwa zaka pafupi-fupi 40, anali cabe mtumiki wa Mose!

2 Popeza Mose anali mtsogoleli wa Aisiraeli kwa zaka zambili, Yoswa ayenela kuti anali na nkhawa yakuti kaya anthu a Mulungu adzamugonjela monga mtsogoleli wawo watsopano kapena ayi. (Deut. 34:8, 10-12) Pokamba za Yoswa 1:1, 2, buku lina lofotokoza Baibo limati: “M’masiku akale komanso masiku ano, nthawi yosintha mtsogoleli m’dziko ni nthawi imene citetezo ca dziko cimakhala pa ciopsezo kwambili.”

3, 4. Tidziŵa bwanji kuti Mulungu anadalitsa Yoswa cifukwa com’dalila? Nanga ni funso lotani limene tingadzifunse?

3 M’pomveka kuti Yoswa anali na nkhawa. Komabe, patapita cabe masiku angapo, iye anacita zimene Mulungu anam’lamula. (Yos. 1:9-11) Yoswa anadalila Yehova, ndipo anadalitsidwa. Baibo imaonetsa kuti Yehova anatsogolela Yoswa na Aisiraeli poseŵenzetsa mngelo. Mngelo ameneyo ayenela kuti anali Mawu, Mwana wa Mulungu woyamba kubadwa.—Eks. 23:20-23; Yoh. 1:1.

4 Ndi thandizo la Yehova, Aisiraeli anapitilizabe kugonjela mtsogoleli wawo watsopano, Yoswa, amene analoŵa m’malo mwa Mose. Na ise tikukhala m’nthawi imene zinthu zambili zikusintha m’gulu la Mulungu. Conco tingadzifunse kuti, ‘Pamene gulu la Mulungu likupita patsogolo mofulumila kwambili, kodi tili na zifukwa zomveka zotipangitsa kudalila Yesu, mtsogoleli wathu wosankhidwa na Mulungu?’ (Ŵelengani Mateyu 23:10.) Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambilane mmene Yehova anatsogolela anthu ake m’nthawi yakale, pamene zinthu zinasintha.

ANATSOGOLELA ANTHU A MULUNGU KULOŴA M’DZIKO LA KANANI

5. Kodi Yoswa anakumana na munthu wotani pamene anali pafupi kufika ku Yeriko? (Onani pikica kuciyambi.)

5 Aisiraeli atangowoloka Yorodano, Yoswa anakumana na munthu wacilendo. Ali pafupi kufika ku Yeriko, anakumana na munthu ali na lupanga m’dzanja lake. Popeza kuti sanamudziŵe munthuyo, Yoswa anamufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” Yoswa anadabwa pamene munthuyo anamuuza kuti ni “kalonga wa gulu lankhondo la Yehova,” amene anabwela kudzateteza anthu a Mulungu. (Ŵelengani Yoswa 5:13-15.) Malemba ena ofotokoza za cocitikaci amaonetsa ngati kuti Yehova anali kukamba na Yoswa mwacindunji. Koma n’zoonekelatu kuti Mulungu anali kukamba naye kupitila mwa mngelo, monga mmene anali kucitila nthawi zambili m’mbuyomo.—Eks. 3:2-4; Yos. 4:1, 15; 5:2, 9; Mac. 7:38; Agal. 3:19.

6-8. (a) N’cifukwa ciani malangizo ena amene Yehova anapeleka kwa Aisiraeli anaoneka monga osathandiza? (b) Nanga n’ciani cionetsa kuti malangizowo anali anzelu komanso a pa nthawi yake? (Onani mawu a munsi.)

6 Kupitila mwa mkulu wa angeloyo, Yehova anapatsa Yoswa malangizo omveka bwino a zimene anayenela kucita kuti awononge mzinda wa Yeriko. Poyamba, ena mwa malangizowo sanali kuoneka monga othandiza kweni-kweni. Mwacitsanzo, Yehova analamula kuti amuna onse a Isiraeli adulidwe. Izi zikanacititsa kuti anthuwo asathe kumenya nkhondo kwa masiku angapo cifukwa ca ululu. Mwina tingafunse kuti, ‘Kodi imeneyi inalidi nthawi yabwino yocita mdulidwe?’—Gen. 34:24, 25; Yos. 5:2, 8.

7 Mwacidziŵikile, asilikali a Isiraeli odulidwawo anali kudela nkhawa kuti adzateteza bwanji mabanja awo ngati adani atawaukila. Koma posapita nthawi, iwo anamvela kuti amuna a mu Yeriko ali na mantha kwambili, cakuti mzindawo “unatsekedwa mwamphamvu cifukwa ca ana a Isiraeli.” (Yos. 6:1) Mwacionekele, izi zinalimbikitsa Aisiraeli kudalila kwambili malangizo a Mulungu.

8 Cinanso, Aisiraeli analamulidwa kuti asauthile nkhondo mzinda wa Yeriko, koma kuti auzungulile kamodzi pa tsiku kwa masiku 6, ndiponso kuti pa tsiku la 7, akauzungulile maulendo 7. N’kutheka kuti ena mwa asilikali a Isiraeli, mu mtima mwawo anali kukamba kuti, ‘Tikungotaya nthawi cabe na kuwononga mphamvu!’ Koma M’tsogoleli wosaoneka wa Aisiraeli anali kudziŵa zimene anali kucita. Mapulani a mtsogoleliyu anathandiza kuti cikhulupililo ca Aisiraeli cilimbe kwambili. Komanso anathandiza kuti Aisiraeli asagwebane mwacindunji na asilikali amphamvu a mu Yeriko.—Yos. 6:2-5; Aheb. 11:30. *

9. N’cifukwa ciani tiyenela kumatsatila malangizo amene timalandila m’gulu la Mulungu? Fotokozani citsanzo.

9 Tiphunzilapo ciani pa nkhaniyi? Nthawi zina sitingamvetsetse zifukwa zimene gulu la Mulungu lapangila masinthidwe ena ake. Mwacitsanzo, mwina poyamba sitinamvetsetse cifukwa cake gulu la Mulungu linali kutilimbikitsa kuseŵenzetsa mafoni na matabuleti mu ulaliki, pa misonkhano, kapena pa phunzilo laumwini. Koma mwacidziŵikile, tsopano taona mapindu oseŵenzetsa zida zimenezi ngati n’kotheka. Tikaona ubwino wa masinthidwe amene apangidwa, olo kuti mwina poyamba tinali kukayikila, cikhulupililo na mgwilizano wathu zimalimba.

UTSOGOLELI WA KHRISTU M’NTHAWI YA ATUMWI

10. N’ndani anapangitsa kuti bungwe lolamulila licite miting’i yofunika kwambili ku Yerusalemu?

10 Patapita zaka pafupi-fupi 13 kucokela pamene Koneliyo anakhala Mkhristu, Akhristu ena aciyuda anali kulimbikitsabe mdulidwe. (Mac. 15:1, 2) Pa nthawi ina, ku Antiokeya kunabuka mkangano pa nkhaniyi. Conco, panapangidwa makonzedwe akuti Paulo apite ku Yerusalemu kukafunsa za nkhaniyi ku bungwe lolamulila. Kodi ndani anacititsa kuti papangidwe makonzedwe amenewa? Paulo anati: “N’napita kumeneko cifukwa ca vumbulutso.” Mwacidziŵikile, Khristu ndiye anali kuyendetsa zinthu n’colinga cakuti bungwe lolamulila likathetse nkhaniyo.—Agal. 2:1-3, nwt-E.

Utsogoleli wa Khristu unaonekela bwino m’nthawi ya atumwi (Onani palagilafu 10, 11)

11. (a) Kodi Akhristu ena aciyuda anapitilizabe kukhulupilila ciani pa nkhani ya mdulidwe? (b) Kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kucilikiza akulu ku Yerusalemu modzicepetsa? (Onaninso mawu a munsi.)

11 Motsogoleledwa na Khristu, bungwe lolamulila linagamula kuti kunali kosafunikila kuti Akhristu a mitundu ina azicita mdulidwe. (Mac. 15:19, 20) Koma patapita zaka pambuyo pa cigamulo cimeneci, Akhristu ambili aciyuda anapitiliza kucita mdulidwe ana awo. Conco, pamene akulu ku Yerusalemu anamva mphekesela yakuti Paulo satsatila Cilamulo ca Mose, anam’patsa malangizo amene anamveka acilendo kwa iye. * (Mac. 21:20-26) Anamuuza kuti atenge amuna anayi n’kupita nawo ku kacisi, kuti anthu poona akaganize kuti Paulo ‘amasunga Cilamulo.’ Paulo akanatha kukana malangizo amenewa na kufotokozela akulu kuti Akhristu aciyudawo ndiwo anali na vuto, cifukwa sanali kumvetsetsa nkhani ya mdulidwe. Koma Paulo anali na mtima wofuna kucilikiza akulu pa colinga cawo colimbikitsa mgwilizano mu mpingo wacikhristu. Ndiye cifukwa cake anamvela modzicepetsa malangizo amene anapatsidwa. Mwina tingadzifunse kuti, ‘N’cifukwa ciani Yesu analola kuti nkhani ya mdulidwe itenge nthawi yaitali conco osathetsedwa, pamene imfa yake inali itathetsa kale Cilamulo ca Mose?’—Akol. 2:13, 14.

12. Kodi zioneka kuti n’cifukwa ciani Khristu analolela kuti patenge nthawi yaitali asanathetse nkhani ya mdulidwe?

12 Kwa ena, zimatenga nthawi kuti ayambe kucita zinthu mogwilizana na kamvedwe katsopano ka coonadi. Akhristu aciyuda anafunika nthawi yokwanila kuti asinthe kaonedwe kawo ka zinthu. (Yoh. 16:12) Kwa Akhristu ena, cinakhala covuta kuvomeleza kuti mdulidwe sunalinso cizindikilo cakuti ali pa ubwenzi wapadela na Mulungu. (Gen. 17:9-12) Komanso, Akhristu ena aciyuda anali kucita mdulidwe cifukwa coopa kuzunzidwa na Ayuda anzawo, amene anali kucita mdulidwe. (Agal. 6:12) Olo zinali conco, m’kupita kwa nthawi, Khristu anapeleka malangizo owonjezeleka pa nkhaniyi, kupitila m’makalata ouzilidwa amene Paulo analemba.—Aroma 2:28, 29; Agal. 3:23-25.

KHRISTU AKALI KUTSOGOLELA MPINGO WAKE

13. N’ciani cingatithandize kuti tiziyamikila utsogoleli wa Khristu masiku ano?

13 Ngati sitikumvetsetsa bwino zifukwa zimene gulu lapangila masinthidwe ena ake, tingacite bwino kuganizila mmene Khristu anatsogolela anthu a Mulungu m’nthawi yakale. M’nthawi ya Yoswa komanso m’nthawi ya atumwi, Khristu anali kupeleka malangizo anzelu pofuna kuteteza anthu a Mulungu, kulimbitsa cikhulupililo cawo, na mgwilizano wawo.—Aheb. 13:8.

14-16. Kodi malangizo amene “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” amapeleka amaonetsa bwanji kuti Khristu amadela nkhawa za umoyo wathu wauzimu?

14 Cimene cimaonetsa kuti Yesu amadela nkhawa umoyo wathu wauzimu, ni malangizo a pa nthawi yake amene iye amapeleka kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Mwacitsanzo, Marc, tate wa ana anayi, anati: “Satana amafuna kufooketsa mpingo mwa kusokoneza mabanja. Conco, malangizo akuti tizicita kulambila kwa pabanja tsiku lililonse ni ofunika kwambili kwa mitu ya mabanja. Mfundo ni yakuti, iwo afunika kuteteza mabanja awo.”

15 Tikaganizila malangizo amene Khristu amatipatsa, timazindikila kuti iye amafunitsitsa kutithandiza kupita patsogolo mwauzimu. Patrick, amene ni mkulu, anati: “Poyamba, ena sanakondwele na makonzedwe akuti tizikumana m’tumagulu twa ulaliki kumapeto kwa wiki. Koma makonzedwe amenewa athandiza kuti limodzi mwa makhalidwe a Yesu ofunika kwambili lionekele bwino. Khalidwe limenelo ni la kuganizila anthu ovutika. Kaamba ka makonzedwe amenewa, abale na alongo amene sanali kucita zambili mwauzimu, anayamba kudzimva kuti ni okondedwa komanso ofunika. Ndipo zotulukapo zake n’zakuti iwo apita patsogolo mwauzimu.”

16 Kuwonjezela pa kutisamalila mwauzimu, Khristu amatithandiza kuikabe maganizo athu pa nchito yofunika kwambili imene ikucitika pa dziko lapansi masiku ano. (Ŵelengani Maliko 13:10.) Mkulu wina wacatsopano, dzina lake André, nthawi zonse amayesetsa kutsatila malangizo atsopano amene gulu la Mulungu limapeleka. Iye anati: “Kucepetsedwa kwa ciŵelengelo ca atumiki a pa Beteli kumatikumbutsa kuti mapeto ayandikila, komanso kuti tiyenela kugwila nchito yolalikila mwacangu na modzipeleka.”

MUZIMVELA MOKHULUPILIKA MALANGIZO A KHRISTU

17, 18. Kodi kuganizila mapindu amene tapeza cifukwa ca masinthidwe aposacedwa kuli na ubwino wanji?

17 Malangizo amene Mfumu yathu, Yesu Khristu, amapeleka amaonetsa kuti iye amaganizila za tsogolo lathu. Conco, tiziganizila za madalitso amene tapeza cifukwa cocita zinthu mogwilizana na masinthidwe aposacedwa. Mwacitsanzo, pa kulambila kwanu kwa pabanja, mungakambilane za mmene mwapindulila na masinthidwe okhudza misonkhano kapena ulaliki. Kucita izi kudzakulimbikitsani kwambili.

Kodi mukuthandiza banja lanu ndi anthu ena kuyendela pamodzi na gulu la Yehova? (Onani palagilafu 17, 18)

18 Tikamaganizila ubwino wa malangizo a gulu la Yehova komanso mapindu amene timapeza, tidzalimbikitsidwa kutsatila malangizowo mwacimwemwe. Mwacitsanzo, tsopano taona kuti kucepetsa ciŵelengelo ca mabuku amene timapulinta, kwathandiza kuti tisamaononge ndalama zambili. Komanso, kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, kwapangitsa kuti nchito ya Ufumu ipite patsogolo pa dziko lonse lapansi. Kukumbukila mfundoyi kungatilimbikitse kuti tiziseŵenzetsa kwambili mafoni na matabuleti poŵelenga na kuphunzila zofalitsa zathu, ngati tingakwanitse kutelo. Mwa kucita izi, tidzaonetsa kuti tili na maganizo monga a Khristu ofuna kuseŵenzetsa mwanzelu cuma ca gulu.

19. N’cifukwa ciani tifunika kumvela mokhulupilika malangizo a Khristu?

19 Ngati titsatila malangizo a Khristu mokhulupilika, tidzalimbitsa mgwilizano komanso cikhulupililo ca ena. Pokumbukila za kucepetsedwa kwa ciŵelengelo ca atumiki a pa Beteli pa dziko lonse, André anati: “Khalidwe limene abale na alongo amene anali kutumikila pa Beteli anaonetsa pambuyo pa masinthidwe amenewa, linanilimbikitsa kuti niziwalemekeza, komanso kuti nizidalila kwambili utsogoleli wa Khristu. Iwo akupitiliza kuyendela pamodzi na galeta la Yehova, mwa kutumikila mwacimwemwe pa utumiki uliwonse umene apatsidwa.”

TIKHALE NA CIKHULUPILILO NDIPO TIZIDALILA MTSOGOLELI WATHU

20, 21. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kudalila Khristu, Mtsogoleli wathu? (b) Tidzakambilana funso liti m’nkhani yotsatila?

20 Posacedwa, Mtsogoleli wathu Yesu Khristu, ‘adzapambana pa nkhondo yolimbana’ na adani ake, ndipo adzacita “zinthu zocititsa mantha.” (Chiv. 6:2; Sal. 45:4) Pali pano, iye akukonzekeletsa anthu a Mulungu kaamba ka nchito yaikulu ya m’dziko latsopano. Pa nthawiyo, ise tonse tidzagwila nawo nchito yomanga komanso yophunzitsa anthu, imene idzacitika pa nthawi ya ciukililo.

21 Khristu, Mfumu yathu yodzozedwa adzatiloŵetsa m’dziko latsopano kokha ngati tipitiliza kum’dalila na mtima wonse, mosasamala kanthu za kusintha kwa zinthu. (Ŵelengani Salimo 46:1-3.) Koma nthawi zina, cingativute kupilila ngati zinthu zasintha mosayembekezeleka mu umoyo wathu. Zinthu zikakhala conco, kodi n’ciani cingatithandize kukhalabe na mtendele wa mumtima na kupitiliza kukhulupilila Yehova? Tidzakambilana funso limeneli m’nkhani yotsatila.

^ par. 8 Akatswili ofukula zinthu zakale anapeza zakudya zambili m’matongwe a ku Yeriko. Izi zigwilizana na zimene Baibo imakamba, zakuti Aisiraeli sanazinge mzinda wa Yeriko kwa nthawi yaitali. Olo kuti Aisiraeli sanaloledwe kudya zakudya za mu mzindawo, imeneyi inali nthawi yoyenelela yakuti iwo alande dziko la Kanani cifukwa inali nyengo yokolola, ndipo m’minda munali zakudya zambili.—Yos. 5:10-12.

^ par. 11 Onani bokosi yakuti, “Paulo Anakumana ndi Chiyeso Modzichepetsa,” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2003, peji 24.