Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tizikamba Zoona

Tizikamba Zoona

“Muzilankhulana zoona zokhazokha.”—ZEK. 8:16.

NYIMBO: 56, 124

1, 2. Ni cida citi cimene cabweletsa mavuto osaneneka kwa anthu? Nanga n’ndani anayamba kuciseŵenzetsa?

FONI, babu, motoka, na filiji ni zina mwa zipangizo zamakono zimene zathandiza anthu kukhala na umoyo wabwinopo. Koma zinthu zina zimene anthu apanga zabweletsa mavuto. Zinthu monga mfuti, mabomba ochela m’nthaka, ndudu, mabomba a nyukiliya, na zina zambili-mbili. Koma pali cida cina cakale kwambili, cimene cabweletsa mavuto osaneneka kwa anthu. Kodi n’ciani cimeneco? Bodza! Kutanthauza kukamba mau amene si oona, pofuna kupusitsa kapena kusoceletsa munthu wina. Kodi n’ndani anayamba kukamba bodza? Yesu Khristu anakamba kuti “Mdyelekezi” ndiye “tate wake wa bodza.” (Ŵelengani Yohane 8:44.) N’liti pamene Mdyelekezi anakamba bodza loyamba?

2 Zinacitika zaka masauzande apitawo m’munda wa Edeni. Mwamuna na mkazi woyambilila, Adamu na Hava, anali kukhala mosangalala m’Paradaiso mmene Mlengi wawo anawaikamo. Kenako, Mdyelekezi anabwela. Iye anali kudziŵa kuti Mulungu analamula anthu aŵiliwo kuti asadye zipatso za “mtengo wodziwitsa cabwino ndi coipa,” kuti angafe . Ngakhale zinali conco, kupitila mwa njoka, Satana anauza Hava kuti: “Kufa simudzafa ayi [bodza loyamba limeneli]. Mulungutu akudziŵa kuti tsiku limene mudzadye cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.”—Gen. 2:15-17; 3:1-5.

3. N’cifukwa ciani tingakambe kuti Satana anakamba bodza cifukwa ca mtima wake waciwembu? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

3 Satana anakamba bodza limeneli cifukwa ca mtima wake waciwembu. Iye anali kudziŵa bwino kuti Hava akakhulupilila bodza lake n’kudya cipatsoco, adzafa. Adamu na Hava anakhulupililadi bodzalo, ndipo anaphwanya lamulo la Yehova. Zotulukapo zake, m’kupita kwa nthawi, iwo anafa. (Gen. 3:6; 5:5) Coipa kwambili kuposa pamenepo, kudzela mwa ucimo umenewo, ‘imfa inafalikila kwa anthu onse.’ Ndipo “imfa inalamulila monga mfumu . . . , ngakhalenso kwa anthu amene sanacimwe monga mmene anacimwila Adamu.” (Aroma 5:12, 14) Conco, m’malo mosangalala na moyo wangwilo komanso wosatha, monga mmene Mulungu anafunila pa ciyambi, anthu amangokhala na moyo “zaka 70. Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadela. . . zaka 80.” Olo zili conco, umoyo ni ‘wodzala ndi mavuto ndi zopweteka.’ (Sal. 90:10) N’zomvetsa cisoni kwambili! Koma zonsezi zinacitika cifukwa ca bodza la Satana.

4. (a) Kodi tidzakambilana mafunso ati? (b) Malinga na Salimo 15:1, 2, ni munthu wotani amene angakhale bwenzi la Yehova?

4 Pofotokoza zocita za Mdyelekezi, Yesu anati: “Sanakhazikike m’coonadi, cifukwa mwa iye mulibe coonadi.” Mpaka pano, kwa Satana kulibe coonadi, cifukwa iye akupitiliza ‘kusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu’ poseŵenzetsa mabodza ake. (Chiv. 12:9) Ise sitifuna kusoceletsedwa na Mdyelekezi. Conco, tiyeni tikambilane mafunso atatu aya: Kodi Satana akusoceletsa bwanji anthu? N’cifukwa ciani anthu amakonda kunama? Komanso, kuti tisawononge ubwenzi wathu na Yehova monga anacitila Adamu na Hava, tingaonetse bwanji kuti ‘timalankhula zoona’ nthawi zonse?—Ŵelengani Salimo 15:1, 2.

MMENE SATANA AKUSOCELETSELA ANTHU

5. Kodi Satana akusoceletsa bwanji anthu masiku yano?

5 Mtumwi Paulo anadziŵa kuti n’zotheka kupewa kusoceletsedwa na Satana, cifukwa “tikudziŵa bwino ziwembu zake.” (2 Akor. 2:11) Koma dziko lonse lili m’manja mwa Mdyelekezi. Izi ziphatikizapo zipembedzo zonse zonama, magulu a ndale acinyengo, komanso amalonda adyela. (1 Yoh. 5:19) Conco, n’zosadabwitsa kuti Satana na viŵanda vake amasonkhezela anthu amene ali na maudindo apamwamba kuti ‘azilankhula mabodza.’ (1 Tim. 4:1, 2) Mwacitsanzo, anthu ena a mabizinesi akulu-akulu amakamba mabodza pofuna kulimbikitsa anthu kugula zinthu zimene zingawaononge, kapena pofuna kuwadyela masuku pamutu.

6, 7. (a) N’cifukwa ciani atsogoleli onama acipembedzo ndiwo ali na mlandu waukulu kwambili? (b) Ni mabodza ati amene atsogoleli acipembedzo amafalitsa amene imwe munamvelako?

6 Atsogoleli onama acipembedzo ndiwo ali na mlandu waukulu kwambili cifukwa ca mabodza amene amaphunzitsa. Zili conco cifukwa ngati munthu wakhulupilila ciphunzitso cabodza na kucita zinthu zimene Mulungu amazonda, angataye mwayi wokapeza moyo wosatha. (Hos. 4:9) Yesu anadziŵa kuti atsogoleli acipembedzo a m’nthawi yake anali na mlandu wosoceletsa anthu. Iye anawadzudzula mosapita m’mbali. Anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenela kuponyedwa m’Gehena [ciwonongeko cothelatu] kuposa inuyo.” (Mat. 23:15, ftn.) Yesu anawadzudzula mwamphamvu atsogoleli onama amenewo. Iwo analidi ‘ocokela kwa atate wawo Mdyerekezi.’—Yoh. 8:44.

7 Masiku anonso, kuli atsogoleli ambili acipembedzo. Ena amachedwa na maina monga akuti a pasta, ansembe, abusa, arabi, ndi maina ena ambili. Mofanana ndi atsogoleli acipembedzo a m’nthawi ya Yesu, anthu amenewa “akupondeleza coonadi” ca Mawu a Mulungu, ndipo ‘asinthanitsa coonadi ca Mulungu ndi bodza.’ (Aroma 1:18, 25) Iwo amafalitsa ziphunzitso zabodza, monga cakuti munthu ali na mzimu wosafa, ca Helo wa moto, komanso cakuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Amafalitsanso ciphunzitso copusa cakuti Mulungu amavomeleza mathanyula (kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha), komanso vikwati va amuna kapena akazi okha-okha.

8. Ni bodza lanji limene atsogoleli andale adzakamba posacedwapa? Nanga zimenezo ziyenela kutikhudza bwanji?

8 Atsogoleli andale nawonso asoceletsa anthu na mabodza awo. Posacedwa, tidzamvela bodza lam’kunkhuniza, pamene anthu adzalengeza kuti akwanitsa kukhazikitsa “bata ndi mtendele” pa dziko lapansi. Koma “ciwonongeko codzidzimutsa cidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Tiyenela kusamala kuti tisakasoceletsedwe na bodza lawo lakuti pa dziko pali mtendele, koma pamene m’ceni-ceni pali mavuto ambili. Ise Akhristu ‘tikudziwa bwino kuti tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku.’—1 Ates. 5:1-4.

CIFUKWA CAKE ANTHU AMAKONDA KUNAMA

9, 10. (a) N’cifukwa ciani anthu amanama? (b) N’ciani cimene tiyenela kukumbukila ponena za Yehova?

9 Ngati anthu apanga cinthu catsopano, ndipo ambili acikonda, m’kupita kwa nthawi opanga zinthuzo amapanga zambili. Ni mmenenso zakhalila na bodza. Masiku ano, anthu ambili amakonda kukamba mabodza, ndipo si olamulila okha kapena atsogoleli cabe amene amanamiza anzawo. Nkhani yakuti “Cifukwa Cake Timanama,” ya m’magazini yochedwa National Geographic inati: “Kunama kwakhala khalidwe lozika mizu kwambili pakati pa anthu.” Anthu amakonda kunama kuti adziteteze kapena kuti adzichukitse. Ena amanama kuti abise zolakwa zawo, kapena kuti apeze ndalama, nchito, kapena zinthu zina zimene afuna. Malinga n’zimene nkhaniyo inakamba, anthu “amakonda kunama pa zinthu zazing’ono kapena zazikulu, kwa anthu osawadziŵa, kapena kwa anzawo a ku nchito, kwa mabwenzi, kapena kwa okondedwa awo.”

10 Kodi khalidwe la kunama labweletsa mavuto anji? Anthu amayamba kukayikilana, ndipo ubwenzi umasokonezeka. Mwacitsanzo, ganizilani cabe mmene cimaŵaŵila mu mtima ngati mkazi wacita cigololo, koma n’kunama mwamuna wake wokhulupilikayo pofuna kubisa colakwaco. Cimaŵaŵanso kwambili ngati mwamuna amazunza mkazi ndi ana ake kunyumba, koma akakhala pa gulu n’kumadzionetsa monga tate wabwino. Tiyenela kukumbukila kuti anthu acinyengo amenewa sangabise zolakwa zawo pa maso pa Yehova, cifukwa kwa iye “zinthu zonse zili poonekela ndipo amatha kuziona bwinobwino.”—Aheb. 4:13.

11. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo coipa ca Hananiya na Safira? (Onani pikica kuciyambi.)

11 Mwacitsanzo, Baibo imafotokoza mmene ‘Satana analimbitsila mtima’ banja lina lacikhristu kunamiza Mulungu m’nthawi ya atumwi. Hananiya na Safira anapangana kuti anamize atumwi. Atagulitsa munda wawo, anatenga ndalama zina n’kukapeleka kwa atumwi, zina n’kubisa. Iwo anacita izi kuti aoneke monga anthu owolowa manja kwambili mu mpingo. Koma Yehova anaona cinyengo cawo, ndipo anawalanga.—Mac. 5:1-10.

12. N’ciani cidzacitikila anthu onama amene salapa? Ndipo n’cifukwa ciani?

12 Kodi Yehova amawaona bwanji anthu onama? Satana komanso anthu onse onama amene salapa, adzaponyewa “m’nyanja yamoto.” (Chiv. 20:10; 21:8; Sal. 5:6) Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova amaona anthu onama mofanana na anthu amene amacita zinthu monga “agalu,” kutanthauza anthu amene khalidwe lawo n’lonyansa pa maso pa Mulungu.—Chiv. 22:15.

13. Kodi Yehova ni Mulungu wotani? Nanga kudziŵa zimenezi kumatilimbikitsa kucita ciani?

13 Tidziŵa kuti Yehova “si munthu, woti anganene mabodza.” Komanso “n’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Num. 23:19; Aheb. 6:18) Ndipo ‘Yehova amadana ndi . . . lilime lonama.’ (Miy. 6:16, 17) Conco, kuti tim’kondweletse, tifunika kumakamba zoona nthawi zonse. N’cifukwa cake timapewa ‘kunamizana.’—Akol. 3:9.

ISE ‘TIMALANKHULA ZOONA’

14. (a) N’ciani cimene cimatisiyanitsa na anthu a m’zipembedzo zonama? (b) Fotokozani mfundo ya pa Luka 6:45.

14 Kodi Akhristu oona amasiyana bwanji na anthu a m’zipembedzo zonama? Iwo ‘amalankhula zoona.’ (Ŵelengani Zekariya 8:16, 17.) Mtumwi Paulo anati: “Tikusonyeza . . . kuti ndife atumiki” mwa ‘kulankhula zoona.’ (2 Akor. 6:4, 7) Yesu anati: “Pakamwa [pa munthu] pamalankhula zosefukila mumtima.” (Luka 6:45) Izi zitanthauza kuti munthu woona mtima, amakamba zoona nthawi zonse. Amakamba zoona, kaya pa nkhani yaikulu kapena yaing’ono, kwa anthu osawadziŵa, anzake a ku nchito, mabwenzi ake, ndi kwa okondedwa ake. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndise oona mtima pa zinthu zonse? Onani zitsanzo zotsatilazi.

Kodi mwaona vuto limene mlongo wacitsikana uyu ali nalo? (Onani palagilafu 15, 16)

15. (a) N’cifukwa ciani kukhala umoyo waciphamaso si cinthu canzelu? (b) N’ciani cingathandize acicepele kupewa kutengela zocita za anzawo? (Onani mau a munsi.)

15 Bwanji ngati ndimwe wacicepele, ndipo simufuna kutsalila pa zimene anzanu amacita? Musalole kuti mtima wofuna kulingana na anzanu ukupangitseni kukhala na umoyo wapaŵili, monga mmene acicepele ena amacitila. Iwo amaoneka monga a khalidwe labwino akakhala pa nyumba kapena ku misonkhano. Koma amasinthilatu akakhala na acicepele a kudziko, kapena akakhala pa malo ocezela pa intaneti. Amakamba kapena kulemba mau oipa, kuvala mosayenelela, kumvetsela nyimbo zoipa, kumwa kwambili kapena kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo, kucita zibwenzi mwakabisila, na zinthu zina zoipa kwambili. Iwo amakhala umoyo waciphamaso. Amanama kwa makolo awo, Akhristu anzawo, komanso kwa Mulungu. (Sal. 26:4, 5) Komabe, Yehova amadziŵa ngati ‘timam’lemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yathu ili kutali ndi iye.’ (Maliko 7:6) Conco, n’cinthu canzelu kumvela malangizo a m’Baibo akuti: “Mtima wako usamasilile anthu ocimwa, koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.”—Miy. 23:17. *

16. Tingaonetse bwanji kuti timakamba zoona pamene tifunsila utumiki winawake wapadela?

16 Mwina mumafuna kutumikila monga mpainiya, kapena kukatumikila mu utumiki winawake wapadela, monga pa Beteli. Pofunsila mautumiki amenewa, mufunika kuyankha moona mtima komanso mosabisa mfundo zina, pa mafunso onse amene amafunsidwa ponena za thanzi lanu, khalidwe, komanso zosangalatsa zimene mumakonda. (Aheb. 13:18) Bwanji ngati munacita khalidwe linalake lodetsa kapena losayenelela ndipo nkhaniyo ikalibe kusamalidwa na akulu? Muyenela kupempha akulu kuti akuthandizeni. Mukatelo, mudzatumikila muli na cikumbumtima coyela.—Aroma 9:1; Agal. 6:1.

17. Tiyenela kucita ciani ngati adani atifunsa zokhudza abale athu?

17 Nanga bwanji ngati m’dziko limene mukhala muli ciletso ca boma, ndipo mwaitanidwa kuti akakufunseni mafunso ponena za abale anu? Kodi muyenela kucita ciani? Kodi muyenela kuwauza zonse zimene mudziŵa? Kodi Yesu anacita ciani pamene anali kufunsidwa mafunso na bwanamkubwa waciroma? Potsatila mfundo ya m’Malemba yakuti pali “nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula,” nthawi zina Yesu sanali kuyankha ciliconse. (Mlal. 3:1, 7; Mat. 27:11-14) Zikakhala conco, tifunika kucita zinthu mozindikila, kuti tisaike moyo wa abale athu pa ciopsezo.—Miy. 10:19; 11:12.

Mungadziŵe bwanji nthawi yofunika kukhala cete komanso nthawi yofunika kukamba zonse zoona? (Onani palagilafu 17, 18)

18. Ni udindo wanji umene timakhala nawo pamene tikamba na akulu zokhudza abale athu?

18 Koma bwanji ngati wina mu mpingo wacita chimo lalikulu, ndipo imwe mudziŵa bwino zimene zinacitika? Akulu ali na udindo woonetsetsa kuti mpingo ni woyela. Conco, iwo angakufikileni nokufunsani kuti muwafotokozele zimene mudziŵa pa nkhaniyo. Kodi mudzacita ciani, maka-maka ngati amene anacita chimolo ni mnzanu wapamtima kapena m’bululu wanu? Baibo imati: “Wotulutsa mawu okhulupilika amanena zolungama,” kapena kuti zoona. (Miy. 12:17; 21:28) Conco, muli na udindo wouza akulu zoona, osabisako mbali ina kapena kusintha mfundo zina. Iwo amafunika kudziŵa bwino zeni-zeni zimene zinacitika kuti apeze njila yabwino yothandizila wocimwayo kukonzanso ubwenzi wake na Yehova.—Yak. 5:14, 15.

19. Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

19 Popemphela kwa Yehova, wamasalimo Davide anati: “Mumakondwela ndi coonadi cocokela pansi pa mtima.” (Sal. 51:6) Davide anadziŵa kuti kukamba zoona kumadalila zimene zili mu mtima mwa munthu. Ndipo Akhristu oona, pa mbali iliyonse ya umoyo wawo, ‘amalankhulana zoona zokhazokha.’ Njila ina imene ise atumiki a Mulungu tingaonetsele kuti ndise osiyana ndi anthu a m’dzikoli ni mwa kuphunzitsa anthu coonadi mu ulaliki. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene tingacitile zimenezi.

^ par. 15 Onani mutu 15, wakuti “Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?,” ndi mutu 16, wakuti “N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?,” m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri.