Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acimwemwe ni Anthu Amene Amatumikila “Mulungu Wacimwemwe”

Acimwemwe ni Anthu Amene Amatumikila “Mulungu Wacimwemwe”

“Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—SAL. 144:15.

NYIMBO: 44, 125

1. N’cifukwa ciani atumiki a Yehova ni anthu acimwemwe? (Onani pikica pamwambapa.)

MBONI ZA YEHOVA ni anthu acimwemwe kwambili. Pa misonkhano yawo ya mpingo, yadela, komanso pa zocitika zina pamakhala maceza acisangalalo na kuseka. N’cifukwa ciani timakhala acimwemwe kwambili? Cifukwa cacikulu n’cakuti timam’dziŵa bwino Yehova, “Mulungu wacimwemwe,” ndipo timam’tumikila, na kuyesetsa kutengela citsanzo cake. (1 Tim. 1:11; Sal. 16:11) Popeza Mulungu ni Gwelo la cimwemwe, amafunanso kuti ise tizikhala acimwemwe. Conco watipatsa zifukwa zambili zokhalila acimwemwe.—Deut. 12:7; Mlal. 3:12, 13.

2, 3. (a) Kodi cimwemwe n’ciani? (b) N’cifukwa ciani cingakhale covuta kukhala acimwemwe masiku ano?

2 Nanga bwanji imwe? Kodi ndimwe acimwemwe? Kodi mungathe kuwonjezela cimwemwe cimene muli naco? Cimwemwe cingatanthauze ‘kumvela bwino mu mtima, kumene kumaphatikizapo kukhala wokhazikika maganizo,wokhutila, ngakhalenso wosangalala kwambili.’ Baibo imaonetsa kuti anthu okhawo amene ali pa ubwenzi wabwino na Yehova ndiwo angakhale na cimwemwe ceni-ceni. Koma masiku yano, n’zovuta munthu kukhala wacimwemwe. Cifukwa ciani?

3 Pali mavuto ambili amene angatilepheletse kukhala acimwemwe. Mwacitsanzo, munthu amene tinali kum’konda angamwalile kapena kucotsedwa mu mpingo. Palinso mavuto ena monga kutha kwa cikwati kapena nchito, mikangano ya m’banja, kapena kusakambitsana bwino. Ena amakumana na mavuto monga kusekewa na anzawo ku sukulu kapena kunchito, kuzunzidwa kapena kuikidwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. Timakumananso na mavuto monga kufooka kwa thanzi, matenda osathelapo, komanso kuvutika maganizo. Zonsezi zingatilepheletse kukhala acimwemwe. Ngakhale zili conco, Yesu Khristu, Mfumu ‘yacimwemwe ndi yamphamvu yokhayo,’ ni wokonzeka kutitonthoza na kutithandiza kukhala acimwemwe. (1 Tim. 6:15; Mat. 11:28-30) Mu ulaliki wake wa pa phili, Yesu anachula makhalidwe osiyana-siyana amene angatithandize kukhala acimwemwe, olo pamene tikumana na mavuto aakulu m’dziko la Satanali.

KUKHALA MUNTHU WAUZIMU N’KOFUNIKA KWAMBILI KUTI TIKHALE ACIMWEMWE

4, 5. Tingacite ciani kuti tikhale na cimwemwe cokhalitsa?

4 Cinthu coyamba cimene Yesu anachula n’cofunika kwambili. Iye anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosowa zawo zauzimu, cifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Tingaonetse bwanji kuti timazindikila zosoŵa zathu zauzimu? Tingacite izi mwa kuphunzila Mau a Mulungu wathu wacimwemwe, kutsatila miyezo yake, na kuika patsogolo zinthu zokhudza kulambila. Tikatelo, tidzakhala na cimwemwe coculuka, ndipo tidzalimbitsa cikhulupililo cathu m’malonjezo a Mulungu. Komanso tidzalimbikitsidwa na “ciyembekezo cosangalatsa,” cimene Mau a Mulungu amapeleka kwa olambila oona.—Tito 2:13.

5 Kupanga ubwenzi wolimba na Yehova n’kofunika kwambili kuti tikhale na cimwemwe cokhalitsa. Mouzilidwa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse kondwelani mwa Ambuye [Yehova]. Ndibwelezanso, kondwelani.” (Afil. 4:4) Kuti tikhale pa ubwenzi na Mulungu, tifunika kupeza nzelu zocokela kwa iye. Mau a Mulungu amati: “Wodala ndi munthu amene wapeza nzelu, ndiponso munthu amene wapeza kuzindikila. Munthu akagwilitsitsa nzelu, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwilitsitsa adzachedwa odala,” kapena kuti acimwemwe.—Miy. 3:13, 18.

6. N’ciani cina cimene tifunika kucita kuti tikhale na cimwemwe cokhalitsa?

6 Komabe, kuti tikhaledi na cimwemwe cokhalitsa, tifunika kumaseŵenzetsa zimene timaŵelenga m’Mau a Mulungu. Pogogomeza kufunika kocita zimene timaphunzila, Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazicita.” (Yoh. 13:17; ŵelengani Yakobo 1:25.) Kuseŵenzetsa zimene timaphunzila n’kumene kungatithandize kupeza zosoŵa zathu zauzimu, komanso kukhala na cimwemwe cokhalitsa. Koma kodi zingatheke bwanji kukhalabe acimwemwe popeza kuti pali mavuto ambili amene angatilande cimwemwe? Cabwino, tiyeni tikambilane mau otsatila amene Yesu anakamba mu ulaliki wake wa pa phili.

MAKHALIDWE AMENE AMATITHANDIZA KUKHALA ACIMWEMWE

7. Kodi zingatheke bwanji anthu amene akumva cisoni kukhala acimwemwe?

7 “Odala ndi anthu amene akumva cisoni, cifukwa adzasangalatsidwa.” (Mat. 5:4) Ena angafunse kuti, ‘Zingatheke bwanji anthu amene akumva cisoni kukhala osangalala?’ Apa Yesu sanali kukamba za anthu onse amene akumva cisoni. Olo anthu oipa amamva cisoni akaona mavuto amene afala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta’ ino. (2 Tim. 3:1) Koma iwo sakhala acimwemwe cifukwa cisoni cawo siciwasonkhezela kuyandikila Yehova. Pa lembali, Yesu ayenela kuti anali kukamba za anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu. Anthu amenewa amamva cisoni cifukwa coona kuti anthu ambili akana Mulungu, komanso sakutsatila mfundo zake za makhalidwe abwino. Anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu amadziŵa kuti ni ocimwa, ndiponso amaona mavuto aakulu amene abwela cifukwa ca kucimwa kwa anthu. Yehova amawaona anthu amenewa, ndipo amawatonthoza poseŵenzetsa Mau ake, na kuwathandiza kukhala na umoyo wacimwemwe.—Ŵelengani Ezekieli 5:11; 9:4.

8. Kodi kukhala wofatsa kumathandiza bwanji munthu kukhala wacimwemwe?

8 “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi.” (Mat. 5:5) Kodi kukhala ofatsa kungatithandize bwanji kukhala acimwemwe? Anthu akaphunzila coonadi amasintha umoyo wawo. Mwina poyamba iwo anali ankhanza, okonda mikangano, kapena aukali. Koma popeza anavala “umunthu watsopano,” lomba ni ‘acifundo cacikulu, okoma mtima, odzicepetsa, ofatsa, ndi oleza mtima.’ (Akol. 3:9-12) Zotulukapo zake n’zakuti amakhala na umoyo wamtendele ndi wacimwemwe, ndiponso amakhala na mabwenzi abwino. Kuwonjezela apo, Baibo inalonjeza kuti anthu aconco ‘adzalandila dziko lapansi.’—Sal. 37:8-10, 29.

9. (a) Kodi ofatsa “adzalandila dziko lapansi” m’njila yotani? (b) N’cifukwa ciani “anthu amene akumva njala ndi ludzu la cilungamo” angakhale acimwemwe?

9 Kodi “ofatsa . . . adzalandila dziko lapansi” m’njila yotani? Ophunzila a Yesu odzozedwa na mzimu adzalandila dziko lapansi m’lingalilo lakuti adzayamba kulamulila dzikoli monga mafumu na ansembe. (Chiv. 20:6) Koma anthu mamiliyoni ambili amene alibe ciyembekezo copita kumwamba, adzalandila dziko lapansi m’njila yakuti adzapatsidwa mwayi wokhala na moyo wamuyaya padzikoli mwamtendele komanso mosangalala. Odzozedwa komanso a nkhosa zina ni anthu amene ali acimwemwe cifukwa ca ‘kumva njala ndi ludzu la cilungamo.’ (Mat. 5:6) Njala na ludzu lawo la cilungamo zidzathelatu m’dziko lapansi latsopano. (2 Pet. 3:13) Mulungu akadzacotsa zoipa zonse padzikoli, anthu olungama adzakhala na cimwemwe nthawi zonse, cifukwa sikudzakhala zilizonse zowasokoneza.—Sal. 37:17.

10. Kodi kukhala wacifundo kumatanthauzanji?

10 “Odala ndi anthu acifundo, cifukwa adzacitilidwa cifundo.” (Mat. 5:7) Liu la Ciheberi lomasulidwa kuti cifundo limatanthauza “kukhudzika mtima mwaubwenzi,” kapena kuti “kumvela ena cisoni.” Nalonso liu la Cigiriki lomasulidwa kuti cifundo limatanthauza kumvela munthu wina cisoni. Komabe, m’Baibo, cifundo cimaphatikizapo zambili osati kungomvela wina cisoni. Cimaphatikizaponso kucitapo kanthu poonetsa kuti munthu tikumumvela cisoni.

11. Pa nkhani ya kukhala acifundo, kodi tiphunzila ciani m’fanizo la Msamariya wacifundo?

11 Ŵelengani Luka 10:30-37. Fanizo la Yesu la Msamariya wacifundo lingatithandize kumvetsa bwino tanthauzo la cifundo. Cifukwa ca cifundo, Msamariya uja anacitapo kanthu kuti athandize munthu uja amene anavulazidwa na acifwamba. Atatsiliza fanizoli, Yesu anauza munthu amene anali kukamba naye kuti: “Pita, iwenso uzikacita zomwezo.” Conco, mungacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimacita zinthu monga mmene Msamariya wacifundo anacitila? Kodi ningawonjezele zimene nimacita poonetsa cifundo mwa kuyesetsa kuthandiza anthu amene akuvutika? Mwacitsanzo, kodi mungathandizeko Akhristu okalamba, alongo amasiye, ndi ana amene makolo awo si Mboni? Komanso bwanji osacitapo kanthu kuti ‘mulimbikitse amtima wacisoni?’—1 Ates. 5:14; Yak. 1:27.

Muzionetsa cifundo kwa ena, ndipo mudzakhala na cimwemwe coculuka (Onani palagilafu 12)

12. Kodi kukhala acifundo kumatithandiza bwanji kukhala acimwemwe?

12 Koma kodi kukhala acifundo kumatithandiza bwanji kukhala acimwemwe? Kuonetsa ena cifundo ni mbali imodzi ya kupatsa, ndipo kupatsa kumabweletsa cimwemwe. Komanso, tikakhala acifundo timakhala acimwemwe cifukwa timadziŵa kuti tikucita zinthu zokondweletsa Yehova. (Mac. 20:35; ŵelengani Aheberi 13:16.) Mfumu Davide pokamba za munthu amene amacita zinthu moganizila ena, anati: “Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo. Adzachedwa wodala padziko lapansi.” (Sal. 41:1, 2) Tikakhala acifundo, Yehova nayenso amaticitila cifundo. Ndipo izi zingapangitse kuti tikakhale na moyo wacimwemwe kwamuyaya.—Yak. 2:13.

CIFUKWA CAKE “ANTHU OYELA MTIMA” AMAKHALA ACIMWEMWE

13, 14. Kodi kukhala oyela mtima kumatithandiza bwanji kukhala acimwemwe?

13 Yesu anati: “Odala ndi anthu oyela mtima, cifukwa adzaona Mulungu.” (Mat. 5:8) Kuti tikhale oyela mtima, maganizo athu na zolakalaka zathu ziyenela kukhala zoyela. Kukhala na maganizo oyela nthawi zonse n’kofunika ngako kuti kulambila kwathu kukhalebe kovomelezeka.—Ŵelengani 2 Akorinto 4:2; 1 Tim. 1:5.

14 Anthu oyela mtima amakhala pa ubwenzi wabwino na Yehova, cifukwa iye anati: “Odala ndiwo amene acapa mikanjo yawo.” (Chiv. 22:14) Kodi ‘amacapa mikanjo yawo’ m’lingalilo lotani? Akhristu odzozedwa ‘amacapa mikanjo yawo’ m’lingalilo lakuti iwo ni oyela pamaso pa Yehova, moti adzapatsiwa moyo wosafa, komanso adzasangalala kwamuyaya kumwamba. Nawonso a khamu lalikulu, amene ali na ciyembekezo cokakhala pano pa dziko lapansi, ali na mwayi wokhala mabwenzi a Mulungu. Ndipo pali pano, iwo anayamba kale ‘kucapa mikanjo yawo ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa.”—Chiv. 7:9, 13, 14.

15, 16. Kodi anthu oyela mtima ‘amamuona Mulungu’ m’njila yotani?

15 Koma kodi anthu oyela mtima amamuona bwanji Mulungu popeza kuti ‘palibe munthu angaone [Mulungu] n’kukhalabe ndi moyo’? (Eks. 33:20) Liu la Cigiriki lomasulidwa kuti ‘kuona’ lingatanthauze “kuona m’maganizo, kuzindikila, kapena kudziŵa.” Anthu amene amaona Mulungu ndi ‘maso a mtima wawo’ ndi aja amene amamudziŵa bwino na kukonda makhalidwe ake. (Aef. 1:18) Yesu anatengela kwambili khalidwe la Mulungu. Ndiye cifukwa cake anati: “Amene waona ine waonanso Atate.”—Yoh. 14:7-9.

16 Kuwonjezela pa kudziŵa makhalidwe a Mulungu, olambila oona ‘angaone Mulungu’ mwa kuganizila zimene iye amawacitila. (Yobu 42:5) Komanso, angaone Mulungu mwa kuyang’anitsitsa ndi ‘maso a mtima wawo,’ pa madalitso osaneneka amene iye walonjeza kwa anthu amene amam’tumikila mokhulupilika na kuyesetsa kukhalabe oyela. Ndipo odzozedwa adzamuona zeni-zeni Yehova akadzaukitsidwa na kulandila mphoto yawo ya kumwamba.—1 Yoh. 3:2.

TINGAKHALE ACIMWEMWE OLO TIKUMANE NA MAVUTO

17. Kodi kukhala anthu okhazikitsa mtendele kumatithandiza bwanji kukhala acimwemwe?

17 Yesu anakambanso kuti: “Odala ndi anthu amene amabweletsa mtendele.” (Mat. 5:9) Anthu amene amayesetsa kukhazikitsa mtendele, amakhala acimwemwe. Yakobo analemba kuti: “Cilungamo ndico cipatso ca mbewu zimene anthu odzetsa mtendele amafesa mu mtendele.” (Yak. 3:18) Ngati tasemphana maganizo na winawake mu mpingo kapena m’banja, tingapemphe Mulungu kuti atithandize kukhazikitsa mtendele. Tikatelo, Yehova adzatipatsa mzimu wake woyela, umene udzatithandiza kuonetsa khalidwe labwino. Ndipo zotulukapo zake, tidzakhala acimwemwe. Yesu anagogomeza kufunika kocitapo kanthu kuti tikhazikitse mtendele ngati tasemphana maganizo na munthu wina. Iye anati: “Conco ngati wabweletsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba, ndipo ukabwelako, peleka mphatso yako.”—Mat. 5:23, 24.

18, 19. N’cifukwa ciani Akhristu angakhale acimwemwe olo pamene akuzunzidwa?

18 “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizilani zoipa zilizonse cifukwa ca ine.” Kodi pamenepa Yesu anatanthauzanji? Iye anapitiliza kuti: “Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:11, 12) Atumwi atakwapulidwa na kuuziwa kuti aleke kulalikila, “anacoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala.” Sikuti anasangalala cifukwa cokwapulidwa. Koma “cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu.”—Mac. 5:41.

19 Masiku anonso, anthu a Yehova amapilila mwacimwemwe pamene akuvutika cifukwa ca dzina la Yesu, kapena pamene akukumana na mayeselo aakulu. (Ŵelengani Yakobo 1:2-4.) Molingana na atumwi, sitikondwela cifukwa covutika. Koma tikakhalabe okhulupilika kwa Yehova pamene tikumana na mayeselo, iye amatithandiza kupilila molimba mtima komanso mwacimwemwe. Mwacitsanzo, mu August 1944, akulu-akulu a boma lina lankhanza anaika Henryk Dornik na m’bale wake m’ndende yozunzilako anthu. Pokamba za abalewo, anthu amene anali kuwazunza anati: “N’zosatheka kuwanyengelela kucita zimene safuna. Iwo amasangalala kufela cikhulupililo cawo.” M’bale Dornik anafotokoza kuti: “Sin’nali kufuna kufela cikhulupililo canga. Koma kupilila cizunzo molimba mtima ndi mwacimwemwe cifukwa cofuna kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova, kunanithandiza kukhala wokondwela. . . . Kupemphela na mtima wonse kunanithandiza kuyandikila kwambili Yehova, ndipo iye anakhala Mthandizi wanga wodalilika.”

20. N’cifukwa ciani ndise okondwa kutumikila “Mulungu wacimwemwe”?

20 Ngati tili pa ubwenzi wabwino na “Mulungu wacimwemwe,” tingakhalebe osangalala olo pamene tikuzunzidwa cifukwa ca cikhulupililo cathu, kutsutsidwa na acibululu, kudwala, kapena kuvutika cifukwa ca ukalamba. (1 Tim. 1:11) Timakhalanso acimwemwe podziŵa kuti Mulungu wathu, “amene sanganame,” adzakwanilitsa zinthu zonse zokondweletsa zimene watilonjeza. (Tito 1:2) Yehova akadzakwanilitsa malonjezo ake, tidzakhala na cimwemwe cacikulu, moti tidzafika poiŵalilatu mavuto na mayeselo onse amene tikukumana nawo masiku yano. Madalitso amene tidzalandila m’Paradaiso adzakhala oculuka kwambili kuposa mmene timaganizila. Ndipo kudzakhala cisangalalo cosaneneka. Ndithudi, ‘tidzasangalala ndi mtendele woculuka.’—Sal. 37:11.