Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Akhristu Acikulile—Yehova Amayamikila Kukhulupilika Kwanu

Akhristu Acikulile—Yehova Amayamikila Kukhulupilika Kwanu

AKULU pa dziko lonse, amayamikila kwambili mautumiki amene amacita m’gulu la Mulungu. Ndithudi, iwo ni dalitso kwa ise tonse! Caposacedwapa, panapangidwa masinthidwe ena ake. Akulu okalamba anauzidwa kuti asiyile abale ocepelapo msinkhu ena mwa maudindo aakulu amene anali nawo. Cifukwa ciani?

Makonzedwe atsopano ni akuti atumiki a dela komanso alangizi a masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu, ayenela kusiya mautumiki amenewa akafika zaka 70. Komanso, akulu akafika zaka 80, ayenela kusiyila abale ocepelapo msinkhu maudindo ena, monga wokhala mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi, kapena mgwilizanitsi wa Bungwe la Akulu mu mpingo. Kodi akulu acikulile amenewa anamvela bwanji na kusintha kumeneku? Kukamba zoona, iwo aonetsadi kuti ni atumiki okhulupilika kwa Yehova na ku gulu lake.

M’bale Ken, amene anatumikila monga mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi kwa zaka 49, anati: “Masinthidwe amenewa n’nagwilizana nawo kwambili. Ndipo kuseni pa tsiku limene n’namvela za kusinthaku, n’nali n’tapemphela kale kwa Yehova. N’namupempha kuti ngati n’zotheka papezeke m’bale wacinyamata amene angatumikile monga mgwilizanitsi.” Umu ni mmene abale acikulile ambili okhulupilika pa dziko lonse anamvelela. Koma popeza anali kukonda kutumikila abale awo, poyamba abalewa sanakondwele kweni-kweni na kusinthaku.

M’bale Esperandio, amene anali mgwilizanitsi wa bungwe la akulu, anati: “Cinaniŵaŵako pang’ono.” Koma iye anakambanso kuti: “N’nali kufunikila nthawi yokwanila yosamalila thanzi langa, cifukwa n’nali kudwala-dwala.” Tikamba pano, m’bale Esperandio akutumikilabe Yehova mokhulupilika, ndipo abale na alongo amamuona kuti ni dalitso mu mpingo mwawo.

Nanga bwanji za abale amene anatumikila kwa zaka zambili monga oyang’anila oyendela? Kodi anamvela bwanji atauzidwa kuti asiye utumikiwu na kupatsiwa mautumiki ena? M’bale Allan, amene anatumikila monga woyang’anila woyendela kwa zaka 38, anati: “N’tauzidwa za kusinthaku, n’nakwinyilila.” Komabe, iye anazindikila kufunika kophunzitsa nchito abale acinyamata. Pali pano, m’baleyu akutumikilabe Yehova mokhulupilika.

M’bale Russell anatumikila kwa zaka 40 monga woyang’anila woyendela, komanso monga mlangizi wa masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu. M’baleyu anakamba kuti atamva za kusinthaku, poyamba iye na mkazi wake, sanamvele bwino. Iye anati: “Tinali kuukonda ngako utumiki wathu, ndipo tinali kuona kuti tikali na mphamvu zakuti tingapitilize kutumikila.” M’bale Russell na mkazi wake, tsopano amaseŵenzetsa maluso awo potumikila mu mpingo wa kwawo, ndipo ofalitsa a mu mpingowo amakondwela kutumikila nawo pamodzi.

Olo kuti zimene takambazi sizinakucitikilemponi, nkhani ya m’buku la 2 Samueli ingakuthandizeni kuwamvetsetsa Akhristu amene izi zinawacitikila.

MWAMUNA WODZICEPETSA KOMANSO WOZINDIKILA ZIMENE SANGAKWANITSE

Ganizilani zimene zinacitika pamene mwana wa Mfumu Davide, Abisalomu, anapanduka. Davide anathaŵa ku Yerusalemu n’kupita ku Mahanaimu, kum’maŵa kwa Mtsinje wa Yorodano. Kumeneko, Davide na anthu amene anali nawo anayamba kusoŵa cakudya na zinthu zina zofunikila mu umoyo. Kodi mukumbukila zimene zinacitika?

Amuna atatu anawabweletsela zinthu zambili, monga zogonapo, zakudya zosiyana-siyana, na ziwiya zina zofunikila. Mmodzi wa amunawo anali Barizilai. (2 Sam. 17:27-29) Abisalomu wopandukayo atagonjetsedwa, Davide ananyamuka ulendo wobwelela ku Yerusalemu, ndipo Barizilai anam’pelekeza mpaka kukafika ku mtsinje wa Yorodano. Mfumu Davide inapempha Barizilai kuti apite naye ku Yerusalemu, kukakhala kumeneko, ndipo inamuuza kuti izikam’patsa cakudya. Komabe, Barizilai anali “munthu wolemela kwambili,” ndipo anali kale na cakudya cokwanila. (2 Sam. 19:31-33) Olo zinali conco, Davide ayenela kuti anam’konda Barizilai cifukwa ca khalidwe lake labwino, komanso anali kufuna kuti azikafunsilako malangizo kwa iye. Ndithudi, ukanakhala mwayi wapadela kwa Barizilai kukhala pa nyumba ya mfumu, komanso kugwila nchito kumeneko!

Popeza Barizilai anali munthu wodzicepetsa ndi wozindikila zimene sangakwanitse, anafotokozela Davide kuti anali na zaka 80. Ndiyeno anati: “Kodi ine mtumiki wanu ndingasiyanitse cabwino ndi coipa”? (2 Sam. 19:35) Kodi anatanthauza ciani pamenepa? Barizilai ayenela kuti anaphunzila zambili mu umoyo wake. Ndipo akanatha kupeleka malangizo abwino, monga mmene “akulu” ena anacitila pambuyo pake kwa Mfumu Rehobowamu. (1 Maf. 12:6, 7; Sal. 92:12-14; Miy. 16:31) Conco, pamene Barizilai anakamba kuti sakanakwanitsa kusiyanitsa cabwino na coipa, mwacidziŵikile anali kutanthauza kuti sakanakwanitsa kucita zambili cifukwa ca ukalamba. Anavomeleza kuti cifukwa ca ukalamba, anali kuvutika kumva, komanso sanali kumvela kukoma kwa cakudya. (Mlal. 12:4, 5) Ndiye cifukwa cake Barizilai anauza Davide kuti atenge wacicepele Chimamu, amene ayenela kuti anali mwana wa Barizilaiyo.—2 Sam. 19:35-40.

KUKONZEKELA ZAM’TSOGOLO

Barizilai anakana kukatumikila m’nyumba ya mfumu cifukwa cakuti anali wokalamba. Izi zionetsa kuti anali kudziŵa zimene sakanakwanitsa. Masinthidwe amene takamba kuciyambi kwa nkhani ino, nawonso anapangidwa pa cifukwa cofananaco. Komabe, panali zambili zimene tinaziganizila popanga masinthidwe amenewa. Sitinangoganizila za umoyo wa munthu mmodzi kapena thanzi lake, monga mmene zinalili kwa Barizilai. Tinaganizila zimene zikanakomela akulu okhulupilika pa dziko lonse lapansi.

Abale acikulile komanso odzicepetsa amenewa, anaona kuti gulu la Yehova lingalimbe na kukonzekela bwino zam’tsogolo, ngati abale acinyamata angaphunzitsidwe kusamalila maudindo amene iwo anali kusamalila. Nthawi zambili, abale acikulilewo ndiwo anali kuphunzitsa abale acinyamata kusamalila maudindo, monga mmene Barizilai anaphunzitsila mwana wake, komanso mmene Paulo anaphunzitsila Timoteyo. (1 Akor. 4:17; Afil. 2:20-22) Tsopano, abale acinyamata amenewa aonetsa kuti ni “mphatso za amuna,” zimene zingathe “kumanga thupi la Khristu.”—Aef. 4:8-12; yelekezelani na Numeri 11:16, 17, 29.

MAUTUMIKI ENA AMENE MUNGACITE

Abale ambili m’gulu la Mulungu, amene anasiyila abale ena maudindo awo, ayamba mautumiki ena kapena awonjezela zocita potumikila Yehova.

Mwacitsanzo, m’bale Marco, amene anatumikila monga woyang’anila woyendela kwa zaka 19, anati: “Kusintha kumeneku kwanipatsa mpata woyesetsa kuthandiza amuna osakhulupilila amene akazi awo ni Mboni mu mpingo mwathu.”

Geraldo, amene anatumikila monga woyang’anila woyendela kwa zaka 28, anati: “Zolinga zathu tsopano ziphatikizapo kuthandiza ofalitsa ozilala na kutsogoza maphunzilo ambili a Baibo.” M’baleyo anakamba kuti iye na mkazi wake, pali pano akutsogoza maphunzilo a Baibo 15. Ndipo ofalitsa ambili ndithu amene anali ozilala, lomba amapezeka ku misonkhano.

M’bale Allan, amene tam’gwila mau poyamba paja, anati: “Lomba timakhala na nthawi yambili yolalikila. Tikusangalala na ulaliki wapoyela ndi wa m’malo amalonda. Komanso, timalalikila maneba athu, cakuti aŵili a iwo amabwela ku Nyumba ya Ufumu.”

Ngati ndimwe m’bale wodalilika ndi wokhulupilika, ndipo simukutumikilanso pa udindo umene munali nawo poyamba m’gulu la Mulungu, pali njila ina imene mungathandizile ena mu mpingo. Mungaphunzitseko abale acinyamata zimene mumadziŵa. M’bale Russell, amene tam’chula poyamba paja, anati: “Yehova akuphunzitsa na kuseŵenzetsa abale acinyamata ocita bwino ndi aluso. Abale na alongo m’mipingo akupindula na khama lawo pa kuphunzitsa na kucita ubusa.”—Onani bokosi yakuti, “ Thandizani Abale Acinyamata Kukhala Ofikapo Mwauzimu.”

YEHOVA AMAYAMIKILA KUKHULUPILIKA KWANU

Ngati simukutumikilanso pa udindo umene munali kutumikila poyamba, simuyenela kudziona monga osafunikila. Munathandiza kale anthu ambili-mbili mu utumiki wanu umene munali kuucita na mtima wonse, ndipo mungapitilize kuthandiza ena. Ndimwe okondedwa, ndipo Yehova na ise tonse, tidzapitiliza kukukondani.

Komanso, cofunika kwambili n’cakuti Yehova sadzaiŵala zimene munacita. Baibo imati, iye sadzaiŵala “nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.” (Aheb. 6:10) Lemba limeneli limatitsimikizila ise tonse kuti, Yehova sadzaiŵala ngakhale zimene timacita masiku ano pom’tumikila. Inde, Yehova amakukondani kwambili, cakuti sizingatheke iye kuiŵala zimene munacita m’mbuyomu pom’tumikila, na zimene mukucita popitiliza kum’tumikila!

Nanga bwanji ngati imwe si ndimwe mmodzi wa abale amene anakhudzidwa mwacindunji na masinthidwe amene takamba m’nkhani ino? Kusintha kumeneku kumakukhudzani ndithu. Motani?

Ngati pali m’bale wacikulile wokhulupilika, amene poyamba anali kutumikila pa udindo winawake, ndiye kuti mungaphunzile zambili kwa iye, cifukwa ni wokhwima mwauzimu ndipo amadziŵa zambili. Muzifunsila malangizo kwa iye. Muzim’pempha nzelu. Ndipo muziona mmene akuseŵenzetsela maluso ake mu utumiki umene akucita pali pano.

Mwina ndimwe wacikulile amene simukutumikilanso pa utumiki umene munalipo kale, kapena ndimwe m’bale olo mlongo amene mungalandileko malangizo kwa acikulile amenewa. Mulimonse mmene zilili, kumbukilani kuti Yehova amayamikila atumiki ake amene am’tumikila mokhulupilika kwa zaka zambili, ndipo akupitiliza kum’tumikila.