Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pitilizani Kuonetsa Cikondi Cifukwa Cimamangilila

Pitilizani Kuonetsa Cikondi Cifukwa Cimamangilila

“Cikondi cimamangilila.”—1 AKOR. 8:1.

NYIMBO: 109, 121

1. Ni nkhani iti yofunika kwambili imene Yesu anakamba kwa ophunzila ake pa usiku wakuti adzaphedwa maŵa?

PAMENE Yesu anali na ophunzila ake, pa usiku wakuti adzaphedwa maŵa, anakamba za khalidwe la cikondi pafupi-fupi ka 30. Iye analamula ophunzila ake kuti ‘azikondana.’ (Yoh. 15:12, 17) Iwo anafunika kukhala na cikondi cacikulu pakati pawo kuti cidzakhale cizindikilo cakuti ni otsatila ake oona. (Yoh. 13:34, 35) Pamenepa, Yesu sanali kukamba za cikondi ca mumtima cabe. Koma anali kukamba za cikondi codzimana, cimene cimaonekela na nchito zake. Iye anati: “Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake. Mupitiliza kukhala mabwenzi anga mukamacita zimene ndikukulamulani.”—Yoh. 15:13, 14.

2. (a) Kodi atumiki a Mulungu amadziŵika na khalidwe lanji? (b) Ni mafunso ati amene tidzakambilana m’nkhani ino?

2 Cikondi codzimana cimene atumiki a Yehova ali naco pakati pawo, komanso mgwilizano wawo wolimba, ni umboni wakuti iwo ni anthu a Mulungu. (1 Yoh. 3:10, 11) N’zokondweletsa ngako kuona kuti pakati pa atumiki a Yehova masiku ano pali cikondi cacikulu, mosasamala kanthu kuti ni osiyana mitundu, maiko, zikhalidwe, na zitundu. Mwina tingafunse kuti: ‘N’cifukwa ciani cikondi n’cofunika kwambili maka-maka masiku ano? Kodi Yehova na Yesu amatilimbikitsa bwanji mwacikondi? Kodi aliyense wa ise angaonetse bwanji cikondi monga ca Khristu cimene “cimamangilila”?’—1 Akor. 8:1.

CIFUKWA CAKE CIKONDI N’COFUNIKA NGAKO MASIKU ANO

3. Kodi anthu amakhudzidwa bwanji na mavuto m’masiku otsiliza ano?

3 Tikukhala m’masiku ‘ovuta’, ndipo umoyo ni ‘wodzala na mavuto na zopweteka.’ Ndiye cifukwa cake anthu oculuka amakhala na nkhawa kwambili. (Sal. 90:10; 2 Tim. 3:1-5) Ndipo anthu ambili amaona kuti cili bwino kungodzipha cabe. Ofufuza amakamba kuti anthu oposa 800,000 amadzipha caka ciliconse. Zimenezi zitanthauza kuti pa masekondi 40 aliwonse, munthu wina amadzipha. N’zomvetsa cisoni kuti ngakhale ena mwa atumiki a Mulungu, amataya mtima kwambili mpaka kufika podzipha.

4. Ni anthu ati ochulidwa m’Baibo amene anali na maganizo ofuna cabe kufa?

4 M’nthawi yakale, atumiki ena okhulupilika a Mulungu anathedwa nzelu cifukwa ca mavuto awo, cakuti anafika polaka-laka kufa cabe. Mwacitsanzo, pamene mavuto ake anafika poipa kwambili, Yobu anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16; 14:13) Komanso Yona, cifukwa cokhumudwa kwambili na mmene zinthu zinayendela pa nchito yake yolalikila, anakamba kuti: “Tsopano inu Yehova, cotsani moyo wanga, pakuti kuli bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.” (Yona 4:3) Pa nthawi ina, nayenso mneneli wokhulupilika Eliya anataya mtima cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo, cakuti anapempha kuti afe. Iye anati: “Basi ndatopa nazo. Tsopano cotsani moyo wanga Yehova.” (1 Maf. 19:4) Koma Yehova anali kuwakonda kwambili atumiki ake odzipeleka amenewo, ndipo anali kufuna kuti akhalebe na moyo. Iye sanawaimbe mlandu cifukwa cokhala na maganizo ofuna kufa. M’malo mwake, anawathandiza kuthetsa maganizo amenewo na kuwalimbikitsa mwacikondi kuti apitilize kum’tumikila mokhulupilika.

5. N’cifukwa ciani kukonda abale na alongo athu n’kofunika kwambili masiku ano?

5 Masiku ano, abale na alongo athu ambili akukumana na mavuto aakulu, ndipo amafunika kulimbikitsidwa mwacikondi. Ena akukumana na cizunzo, komanso ena amanyozewa. Palinso ena amene anzawo ku nchito amawatsutsa na kuwajeda. Ndipo ena amakhala olema kwambili cifukwa cogwila nchito ya ovataimu, kapena cifukwa coseŵenza modzipanikiza kuti atsilize nchito pa nthawi imene apatsidwa. Komanso, ena akukumana na mavuto m’banja mwawo, monga kutsutsidwa na mwamuna kapena mkazi wawo wosakhulupilila. Cifukwa ca mavuto amenewa ndi ena, ambili mu mpingo amakhala olema komanso opanikizika maganizo. Kodi n’ndani angawalimbikitse kuti asalefuke?

TIMALIMBIKITSIDWA NA CIKONDI CA YEHOVA

6. Kodi Yehova amawalimbikitsa bwanji atumiki ake?

6 Yehova amalimbikitsa atumiki ake mwa kuwatsimikizila kuti amawakonda kwambili. Aisiraeli ayenela kuti analimbikitsidwa ngako pamene Yehova anawauza kuti: “Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda. . . . Usacite mantha cifukwa ine ndili nawe.” (Yes. 43:4, 5) Pokhala atumiki a Yehova, sitikayikila kuti iye amatikonda kwambili. * Pokamba za olambila oona, mau a Mulungu amati, Yehova ‘adzawapulumutsa cifukwa ndi wamphamvu. Iye adzakondwela nawo.’—Zef. 3:16, 17.

7. Kodi cikondi ca Yehova kwa atumiki ake cili ngati ca mayi woyamwitsa m’njila yanji? (Onani pikica kuciyambi.)

7 Yehova analonjeza anthu ake kuti adzawasamalila na kuwatonthoza olo atakumana na mavuto otani. Iye anati: ‘Inu mudzayamwadi. Ndidzakunyamulani m’manja ndipo ndidzakusisitani mwacikondi n’takuikani pamwendo. Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.’ (Yes. 66:12, 13) Kodi si mau ocititsa cidwi amenewa? Yehova akudziyelekezela na mayi wacikondi amene wanyamula mwana wake m’manja, kapena amene akusisita mwanayo mwacikondi atamuika pamendo. Pamenepa, Yehova akuonetsa cikondi cacikulu cimene ali naco pa atumiki ake. Conco, tisamakayikile kuti Yehova amatikonda komanso amationa kuti ndise amtengo wapatali.—Yer. 31:3.

8, 9. Kodi cikondi ca Yesu cimatilimbitsa bwanji?

8 Palinso cina cimene cimaonetsa kuti Yehova amatikonda. Iye “anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Nayenso Yesu anaonetsa cikondi cacikulu mwa kupeleka moyo wake kaamba ka ise. Cikondi cimeneci cimatilimbikitsa kwambili. Baibo imakamba kuti ngakhale ‘cisautso, kapena zowawa’ sizingatilekanitse “ndi cikondi ca Khristu.”—Aroma 8:35, 38, 39.

9 Tikakumana na mavuto aakulu amene angatifooketse, cikondi cacikulu cimene Khristu anationetsa cimatilimbikitsa na kutipatsa mphamvu kuti tipilile. (Ŵelengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Cikondi ca Yesu cimatilimbikitsa kupitiliza kutumikila Yehova, olo pamene takumana na mavuto, monga masoka azacilengedwe, cizunzo, zokhumudwitsa, kapena nkhaŵa yaikulu.

ABALE ATHU AMAFUNIKILA CIKONDI CATHU

Kuphunzila citsanzo ca Yesu kungakusonkhezeleni kulimbikitsa ena (Onani palagilafu 10, 11)

10, 11. N’ndani ali na udindo wolimbikitsa abale na alongo mu mpingo? Fotokozani.

10 Yehova amatilimbikitsanso mwacikondi poseŵenzetsa mpingo. Aliyense wa ise angaonetse kuyamikila cikondi ca Yehova mwa kukonda na kulimbikitsa abale na alongo athu mwauzimu komanso kuwatonthoza. (1 Yoh. 4:19-21) Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukucitila.” (1 Ates. 5:11) Aliyense mu mpingo, osati akulu cabe, angatengele citsanzo ca Yehova na Yesu mwa kutonthoza na kulimbikitsa abale na alongo athu.—Ŵelengani Aroma 15:1, 2.

11 Ena mu mpingo angakhale na matenda ovutika maganizo, ndipo angafunike kupeza cithandizo kwa madokota odziŵa za matendawa. (Luka 5:31) Akulu na ofalitsa mumpingo si akatswili a matenda a maganizo. Ngakhale n’conco, iwo angathandize mwa ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wacisoni, kuthandiza ofooka, kukhala oleza mtima kwa onse.’ (1 Ates. 5:14) Tonse tiyenela kuyesetsa kukhala acifundo na oleza mtima, komanso kukamba motonthoza ndi molimbikitsa kwa ofooka. Kodi mumayesetsa kutonthoza na kulimbikitsa ena? Nanga n’ciani cimene mungacite kuti muzilimbikitsa kwambili ena na kuwatonthoza?

12. Fotokozani citsanzo ca mlongo amene analimbikitsidwa na mpingo.

12 Kodi cikondi cathu cingalimbikitse bwanji anthu amene amavutika kwambili maganizo? Mlongo wina wa ku Europe, anati: “Nthawi zina, nimakhala na maganizo odzipha. Komabe pali anthu amene amanicilikiza. Abale na alongo mu mpingo wathu apulumutsa moyo wanga. Nthawi zonse, iwo amanilimbikitsa kwambili na kunionetsa cikondi. Olo kuti ni ocepa amene amadziŵa kuti nili na matenda ovutika maganizo, mpingo wonse umanilimbikitsa nthawi zonse. Mlongo wina na mwamuna wake ali monga makolo anga akuuzimu. Iwo amanilimbikitsa mwacikondi, ndipo amakhala okonzeka kunithandiza nthawi iliyonse, kaya masana kapena usiku.” N’zoona kuti sitingacite zolingana polimbikitsa Akhristu anzathu. Komabe, aliyense wa ise angacite zambili polimbikitsa abale na alongo amene amavutika maganizo. *

MMENE TINGALIMBIKITSILE ENA MWACIKONDI

13. N’ciani cofunika kuti tilimbikitse ena?

13 Muziwamvetsela mokoma mtima. (Yak. 1:19) Kumvetsela mwacifundo pamene munthu wovutika maganizo akutifotokozela nkhawa zake, kumaonetsa kuti tili na cikondi. Mungam’funse mafunso mosamala, oonetsa kuti mumam’dela nkhawa, n’colinga cakuti mudziŵe mmene akumvelela mumtima. Mukacita zimenezi, mudzadziŵa zimene mungacite kuti mum’limbikitse. Nkhope yanu iyenela kuonetsa kuti mukum’dela nkhawa komanso mumam’konda. Ngati akufotokoza vuto lake, mvetselani moleza mtima ndipo pewani kum’dula mau. Kumvetsela moleza mtima kudzakuthandizani kumvetsetsa nkhawa zake. Mukatelo, iye adzayamba kukudalilani ndipo adzakhala wokonzeka kumvetsela zimene mungakambe pom’limbikitsa. Iye akaona kuti mumam’ganiziladi, adzalimbikitsidwa kwambili.

14. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa cizoloŵezi copeza ena zifukwa?

14 Pewani mtima wokonda kupeza ena zifukwa. Pamene tikamba na munthu wovutika maganizo, tiyenela kupewa kukamba monga tikumuimba mlandu. Kucita izi kungapangitse kuti zoyesayesa zathu zofuna kum’limbikitsa mwacikondi zikhale zosaphula kanthu. Baibo imakamba kuti: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.” (Miy. 12:18) N’zoona kuti sitingacitile dala kukamba mau “olasa” amene angakhumudwitse munthu wovutika maganizo. Koma ngakhale sitinacitile dala kukamba mawu aconco, zimakhalabe zopweteka kwambili kwa munthuyo. Conco, kuti tilimbikitse ena mwacikondi, tifunika kukhala acifundo. Tiyenela kuyesetsa kuganizila mmene iwo akumvelela cifukwa ca mavuto awo.—Mat. 7:12.

15. Ni buku liti lokhala na mfundo zothandiza kwambili limene tingaseŵenzetse polimbikitsa ena mwacikondi?

15 Muziseŵenzetsa Mawu a Mulungu potonthoza ena. (Ŵelengani Aroma 15:4, 5.) Baibo ni buku limene lili na mfundo zothandiza kwambili zimene zimatitonthoza. Baibo ni yocokela kwa “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupilila ndiponso amene amatitonthoza.” Kuwonjezela pa malemba otonthoza, tili na mabuku ambili ophunzilila Baibo. Mwacitsanzo, tingaseŵenzetse buku la Watch Tower Publications Index, komanso Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova. Mabuku amenewa angatithandize kupeza mfundo zolimbikitsa za m’Malemba, zimene tingaziseŵenzetse polimbikitsa na kutonthoza abale na alongo athu pa mavuto alionse amene angakhale nawo.

16. Ni makhalidwe ati amene tifunika kuonetsa polimbikitsa Mkhristu wovutika maganizo?

16 Khalani okoma mtima ndi odekha. Tikakhala okoma mtima ndi odekha pamene tilimbikitsa ena, timaonetsa kuti tili na cikondi copanda dyela. Yehova ni “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.” Iye amaonetsa “cifundo cacikulu” kwa atumiki ake. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:3-6; Luka 1:78; Aroma 15:13) Paulo anapeleka citsanzo cabwino pa mbali imeneyi. Iye analemba kuti: “Tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalilila ana ake. Conco popeza timakukondani kwambili, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo, cifukwa tinakukondani kwambili.” (1 Ates. 2:7, 8) Ngati ticita zinthu mokoma mtima kwa ena, Yehova angatiseŵenzetse poyankha mapemphelo a munthu wovutika maganizo.

17. Kodi tifunika kuwaona bwanji abale athu kuti tiwalimbikitse mwacikondi?

17 Musamayembekezele kuti abale anu azicita zinthu popanda kulakwitsa. Muziwaona moyenela abale na alongo anu. Kuyembekezela kuti abale athu nthawi zonse azicita zinthu mosalakwitsa n’kudzinamiza, ndipo kungapangitse kuti tisamakhale acimwemwe. (Mlal. 7:21, 22) Kumbukilani kuti Yehova sayembekezela atumiki ake kucita zinthu mwangwilo. Ngati titengela citsanzo cake, tidzakhala okonzeka kunyalanyaza zophophonya za Akhristu anzathu. (Aef. 4:2, 32) Pewani kukamba monga mukuwaimba mlandu wakuti sacita zambili potumikila Yehova, kapena kuwayelekezela ndi ena. M’malomwake, khalani na cizoloŵezi cowayamikila pa zimene akucita mu utumiki wawo. Kucita izi kungawalimbikitse, ndiponso kungawapatse “cifukwa cosangalalila” mu utumiki wawo.—Agal. 6:4.

18. N’ciani cimatisonkhezela kulimbikitsa ena mwacikondi?

18 Mtumiki aliyense wa Yehova ni wamtengo wapatali kwa iye na kwa mwana wake Yesu, amene anapeleka moyo wake monga nsembe ya dipo. (Agal. 2:20) Timawakonda kwambili abale na alongo athu. Ndipo timafuna kucita nawo zinthu mokoma mtima ndi mwacikondi. Conco, kuti tikhale anthu olimbikitsa, tiyenela ‘kutsatila zinthu zobweletsa mtendele ndiponso zolimbikitsana.’ (Aroma 14:19) Tonse tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene dziko lapansi lidzakhala Paradaiso, mmene simudzakhala zinthu zilizonse zofooketsa. Simudzakhala matenda, nkhondo, imfa, cizunzo, mavuto a m’banja, na zokhumudwitsa. Pofika kumapeto kwa zaka 1000, anthu adzakhala angwilo. Ndipo anthu amene adzapyola ciyeso comaliza adzakhala padziko lapansi monga ana a Yehova Mulungu. Iwo adzakhala na “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Conco, tiyeni tipitilize kuonetsana cikondi cimene cimamangilila, komanso kuthandizana kuti tonse tikalandile mphoto yokondweletsa imeneyo.

^ par. 6 Onani mutu 24 m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova.

^ par. 12 Kuti mudziŵe mmene mungathetsele maganizo ofuna kudzipha, onani nkhani za mu Galamukani zakuti: “Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?” (April 2014); “Kodi Mungatani Mukakhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” (January 2012); ndi yakuti “Moyo N’gokoma” (November 8, 2001).