Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Wamphamvuzonse Koma Woganizila Ena

Wamphamvuzonse Koma Woganizila Ena

“[Yehova] akudziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndife fumbi.”—SAL. 103:14.

NYIMBO: 30, 10

1, 2. (a) Mosiyana na anthu amphamvu, kodi Yehova amacita nawo zinthu motani anthu? (b) Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

ANTHU amphamvu komanso olemekezeka, nthawi zambili “amapondeleza” anzawo. (Mat. 20:25; Mlal. 8:9) Koma Yehova ni wosiyana ngako na anthu amenewa. Olo kuti ni Wamphamvuzonse, iye amatiganizila kwambili ise anthu opanda ungwilo. Ndipo amacita nase zinthu mokoma mtima. Amaona nkhawa zathu na kutithandiza pa zosoŵa zathu. Komanso, popeza “amakumbukila kuti ndife fumbi,” satilamula kucita zinthu zimene sitingakwanitse.—Sal. 103:13, 14.

2 M’Baibo muli zitsanzo zambili zoonetsa kuti Yehova amacita zinthu moganizila atumiki ake. Tiyeni tikambilaneko zitsanzo zitatu. Coyamba ni ca mmene Mulungu anathandizila Samueli wacicepele kupeleka uthenga waciweluzo kwa Mkulu wa Ansembe Eli. Caciŵili, mmene Yehova anacitila zinthu moleza mtima na Mose, pamene anali kukana kutumikila monga mtsogoleli wa Aisiraeli. Ndipo cacitatu, mmene Mulungu anatsogolelela Aisiraeli potuluka mu Iguputo. Pamene tikambilana zimenezi, onani zimene tiphunzilapo ponena za Yehova, komanso zimene ise tingacite potengela citsanzo cake.

ANACITA ZINTHU MOGANIZILA WACICEPELE

3. N’ciani cimene cinacitikila Samueli tsiku lina usiku? Nanga izi zibweletsa funso labwanji? (Onani pikica kuciyambi.)

3 Samueli anayamba “kutumikila Yehova” pa cihema ali wamng’ono kwambili. (1 Sam. 3:1) Tsiku lina usiku, iye atagona, panacitika zinthu zina zimene sizinali kucitika kaŵili-kaŵili. * (Ŵelengani 1 Samueli 3:2-10.) Anamva winawake akumuitana. Poganiza kuti Mkulu wa Ansembe Eli ndiye anali kumuitana, Samueli anathamangila kumene kunali iye nokamba kuti: “Ndabwela mbuyanga, ndamva kuitana.” Eli anakamba kuti sindiye anali kumuitana. Zaconco zitacitikanso kaŵili, Eli anazindikila kuti Mulungu ndiye anali kuitana Samueli. Conco anauza mnyamatayo mmene angayankhile akamvanso kuitana, ndipo Samueli anamvela. N’cifukwa ciani Yehova, kupitila mwa mngelo, sanadziulule kuti ndiye anali kuitana Samueli? Baibo siikamba cifukwa cake. Koma tikaganizila mmene zinthu zinayendela pambuyo pake, timatha kuona kuti Yehova anacita izi cifukwa comuganizila Samueli wacicepeleyo. Kodi anaonetsa bwanji kumuganizila?

4, 5. (a) Kodi Samueli anamvela bwanji Mulungu atam’tuma kuti akapeleke uthenga waciweluzo kwa Eli? Nanga zinthu zinayenda bwanji m’maŵa mwake? (b) Kodi nkhani imeneyi itiphunzitsa ciani za Yehova?

4 Ŵelengani 1 Samueli 3:11-18. M’Cilamulo ca Yehova, munali lamulo lakuti ana afunika kumalemekeza acikulile, maka-maka atsogoleli. (Eks. 22:28; Lev. 19:32) Kodi muganiza kuti Samueli akanalimba mtima kupita kwa Eli m’maŵa kukamuuza uthenga woŵaŵa waciweluzo wocokela kwa Mulungu? Mwacionekele, yankho ni yakuti iyai. Ndipo Baibo imakamba kuti Samueli “anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.” Komabe, Mulungu anapangitsa Eli kuzindikila kuti Iye ndiye anali kuitana Samueli. Izi zinasonkhezela Eli kulamula Samueli kuti amufotokozele za masomphenyawo. Anati: “Usandibisile . . . ngakhale mau amodzi pa mau onse amene iye wakuuza.” Samueli anamvela, ndipo “anamuuza mau onse.”

5 N’zoonekelatu kuti Eli sanadabwe kwambili na uthenga umene Samueli anamuuza. Unali wogwilizana na uthenga wa “munthu wa Mulungu,” amene anacenjeza mkulu wa ansembeyo m’mbuyomo. (1 Sam. 2:27-36) Nkhani imeneyi ya Samueli na Eli ionetsa kuti Yehova ni wanzelu komanso woganizila ena kwambili.

6. Tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Mulungu anacitila zinthu na Samueli wacicepele?

6 Kodi ndimwe wacicepele? Ngati n’conco, dziŵani kuti nkhani ya Samueli ni umboni wakuti Yehova amamvetsa mavuto amene mumakumana nawo komanso mmene mumamvelela. Mwina ndimwe wamanyazi, ndipo mumayopa kulalikila uthenga wa Ufumu kwa acikulile, kapena mumayopa kuoneka wosiyana na anzanu. Koma dziŵani kuti Yehova amafuna kukuthandizani. Conco, mukhuthulileni nkhawa zanu m’pemphelo. (Sal. 62:8) Muzisinkha-sinkha pa zitsanzo za acicepele ochulidwa m’Baibo, monga Samueli. Cinanso, muzikambilana na Akhristu anzanu, kaya acicepele kapena acikulile, amene anakumanapo na mavuto ngati amene imwe mukukumana nawo. Iwo angakuuzeni mmene Yehova anawathandizila, mwina m’njila imene iwo sanali kuyembekezela.

ANACITA ZINTHU MOGANIZILA MOSE

7, 8. Kodi Yehova anaonetsa bwanji mtima wom’ganizila kwambili Mose?

7 Pamene Mose anali na zaka 80, Yehova anam’patsa nchito yaikulu komanso yovuta. Anam’lamula kuti akatulutse Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo. (Eks. 3:10) Pambuyo pogwila nchito yoŵeta nkhosa kwa zaka 40 ku Midiyani, Mose ayenela kuti anayopa atapatsidwa nchito imeneyi. Iye anati: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?” Koma Mulungu anam’limbikitsa. Anati: “Ndidzakhala nawe.” (Eks. 3:11, 12) Anamuuzanso kuti: Akulu a Isiraeli “adzamvela mau ako.” Komabe, Mose anayankha kuti: ‘Bwanji ngati sakamvela mau anga?’ (Eks. 3:18; 4:1) Apa Mose anakamba monga akutsutsa Mulungu. Koma Yehova anaonetsabe kuleza mtima. Ndipo anapitiliza kum’limbikitsa. Anam’patsa mphamvu yocita zozizwitsa, cakuti anakhala munthu woyamba m’mbili yonse ya anthu kulandilapo mphamvu zaconco.—Eks. 4:2-9, 21.

8 Koma Mose anapitilizabe kukana. Ananena kuti anali na vuto lokamba movutikila. Poyankha, Mulungu anati: “Ine ndidzakhala nawe polankhula ndipo ndidzakuuza zonena.” Kodi apa lomba Mose anavomela? Sanavomele, moti anapempha Mulungu modzicepetsa kuti atumize munthu wina. M’pomveka kuti Yehova anamukwiyila Mose. Koma anapitiliza kucita zinthu mom’ganizila. Anasankha Aroni kuti akhale wom’lankhulila.—Eks. 4:10-16.

9. Yehova anacita zinthu moleza mtima komanso mom’ganizila Mose. Kodi izi zinam’thandiza bwanji pa utumiki wake?

9 Kodi pa nkhaniyi tiphunzilapo ciani ponena za Yehova? Monga Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova akanafuna, sembe anangom’kakamiza Mose kucita zimene anam’lamula. Koma anacita zinthu moleza mtima ndi mokoma mtima. Anayesetsa kum’limbikitsa mtumiki wake wodzicepetsa ameneyo. Kodi izi zinam’thandiza Mose? Inde, cakuti iye anakhala mtsogoleli wabwino, amene anali kuyesetsa kucita zinthu modekha ndi anthu komanso mowaganizila, monga mmene Yehova anacitila kwa iye.—Num. 12:3.

Kodi mumatengela citsanzo ca Yehova pocita zinthu ndi ena? (Onani palagilafu 10)

10. Timapindula bwanji tikatengela citsanzo ca Yehova ca kuganizila ena?

10 Kodi tiphunzilapo ciani? Kodi ndimwe mwamuna, kholo, kapena mkulu mu mpingo? Ngati n’conco, ndiye kuti muli na mphamvu ya ulamulilo. Mwa ici, n’kofunika kwambili kuti muzitengela citsanzo ca Yehova mwa kukhala woganizila ena, wokoma mtima, ndi woleza mtima pocita zinthu ndi amene mukuwayang’anila. (Akol. 3:19-21; 1 Pet. 5:1-3) Ngati muyesetsa kutengela citsanzo ca Yehova na Mose Wamkulu, Yesu Khristu, mudzakhala wofikilika komanso wotsitsimula kwa ena. (Mat. 11:28, 29) Mudzakhalanso citsanzo cabwino cimene ena angatengele.—Aheb. 13:7.

MPULUMUTSI WOCITITSA MANTHA KOMA WOGANIZILA ENA

11, 12. N’ciani cimene Yehova anacita kuti athandize Aisiraeli kudzimva kukhala otetezeka pamene anali kuwatulutsa mu Iguputo?

11 Pamene Aisiraeli anali kutuluka mu Iguputo mu 1513 B.C.E., mwina ciŵelengelo cawo cinali kupitilila 3 miliyoni. Pa khamulo, panali anthu a mibadwo yosiyana-siyana. Panali ana, okalamba, komanso odwala kapena olemala. Panali kufunikadi Mtsogoleli woganizila ena kuti akwanitse kutsogolela bwino khamu limenelo potuluka mu Iguputo. Ndipo Yehova, kupitila mwa Mose, anaonetsadi kuti anali Mtsogoleli woyenelela. Ndiye cifukwa cake Aisiraeli anali kudzimva otetezeka pamene anali kutuluka mu Iguputo, dziko limene linali ngati ndiye kwawo.—Sal. 78:52, 53.

12 Kodi Yehova anacita ciani kuti anthuwo aone kuti ni otetezeka? Powatulutsa mu Iguputo, anaonetsetsa kuti akuyenda mwadongosolo. Baibo imati anayenda “mwa dongosolo lomenyela nkhondo.” (Eks. 13:18) Dongosolo limenelo linathandiza Aisiraeli kutsimikizila kuti Mulungu wawo anali kuwatsogolela. Cinanso, Yehova anaika zizindikilo zoonetsa kuti anali nawo. Anaika “mtambo masana” na “kuwala kwa moto” usiku. (Sal. 78:14) Zinali monga Yehova akuwauza kuti: “Musaope. Nili na imwe. Nidzakutsogolelani na kukutetezani.” Kaamba ka zimene zinali kudzacitika pambuyo pake, Aisiraeli anafunikadi kukhala na cidalilo colimba mwa Yehova.

Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuwaganizila Aisiraeli pa Nyanja Yofiila? (Onani palagilafu 13)

13, 14. (a) N’zinthu ziti zimene Yehova anacitila Aisiraeli pa Nyanja Yofiira zoonetsa kuwaganizila? (b) Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti ni wamphamvu kwambili kuposa Aiguputo?

13 Ŵelengani Ekisodo 14:19-22. Yelekezelani kuti muli m’khamu la Aisiraeli. Asilikali a Farao akubwela ku mbali imodzi, ndipo ku mbali ina kuli Nyanja Yofiila. Ndiyeno Mulungu akucitapo kanthu kuti akupulumutseni. Akucititsa mtambo woima njo ngati cipilala kucoka kutsogolo kwanu n’kukaima kumbuyo kwanu, kuchinga Aiguputo na kuwacititsa kukhala mu mdima. Koma mukuona kuti khamu lonse la Aisiraeli likuunikilidwa na kuwala kwa mtambowo. Kenako mukuona Mose akutambasula dzanja lake kulata panyanja, ndipo cimphepo camphamvu ca kum’maŵa cikugaŵa nyanjayo n’kupanga cinjila cacikulu. Tsopano imwe, abululu anu, ziŵeto zanu, ndi anthu ena mukuyamba kuyenda pansi pakati pa nyanjayo. Ndipo mukudabwa kuona kuti pansipo palibe matika kapena cinyontho. M’polimba komanso pouma bwino, cakuti mukwanitsa kuyenda mosavutikila. Conco, aliyense, ngakhale okalamba akuyenda bwino-bwino mpaka kukafika ku tsidya lina la nyanjayo.

14 Ŵelengani Ekisodo 14:23, 26-30. Tsopano, Farao wopusa ndi wonyadayo akuloŵa pa nyanjapo kukuthamangitsani. Koma Mose akutambasulanso dzanja lake kulata pa nyanjapo. Atatelo, makoma aŵili a madzi oundana a nyanjayo akukhamuka, ndipo madziwo akuyamba kubwelela mbali zonse ziŵili. Farao na gulu lake lankhondo akuwonongedwa kothelatu!—Eks. 15:8-10.

15. Kodi nkhani ya kupulumutsidwa kwa Aisiraeli itiphunzitsa ciani za Yehova?

15 Pa nkhaniyi tiphunzilapo kuti Yehova ni Mulungu wadongosolo. Khalidwe limeneli la Mulungu limatithandiza kudzimva kuti ndise otetezeka. (1 Akor. 14:33) Cinanso, Yehova ni m’busa wacikondi amene amasamalila anthu ake m’njila zambili. Amawakonda na kuwateteza kwa adani awo. Izi n’zolimbikitsa ngako, maka-maka masiku yano pamene tikuyandikila mapeto a dziko loipali.—Miy. 1:33.

16. Kodi kukambilana mmene Yehova anapulumutsila Aisiraeli kwatipindulitsa bwanji?

16 Masiku anonso, Yehova amasamalila anthu ake mwauzimu ndi mwakuthupi monga gulu. Ndipo adzapitiliza kutisamalila ngakhale pa cisautso cacikulu, cimene cayandikila kwambili. (Chiv. 7:9, 10) Conco, pa cisautso cacikulu, anthu onse a Mulungu, kaya acicepele kapena okalamba, athanzi kapena olemala, sadzacita mantha kapena kutaya mtima. * Koma adzacita zimene Yesu Khristu anakamba, zakuti: “Mudzaimilile cilili ndi kutukula mitu yanu, cifukwa cipulumutso canu cikuyandikila.” (Luka 21:28) Iwo sadzagwedezeka ngakhale poukilidwa na Gogi, amene adzakhala woopsa kwambili kuposa magulu a nkhondo a Farao. Gogi akutanthauza mgwilizano wa mitundu. (Ezek. 38:2, 14-16) N’cifukwa ciani anthu a Mulungu sadzaopa? Cifukwa cakuti adziŵa kuti Yehova sasintha. Monga mmene anacitila m’nthawi ya Aisiraeli, iye adzawapulumutsa na kuwasamalila mwacikondi.—Yes. 26:3, 20.

17. (a) Kodi tiyenela kucita ciani kuti tipindule na nkhani za m’Baibo zofotokoza mmene Yehova amasamalila anthu ake? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Zitsanzo zimene takambilanazi n’zocepa cabe pa zitsanzo zambili-mbili zoonetsa kuti Yehova amasamalila, kupulumutsa, na kutsogolela anthu ake mokoma mtima komanso mowaganizila. Posinkha-sinkha nkhani ngati zimenezi, yesetsani kumvetsetsa mfundo zina za m’nkhaniyo, zimene zingakuthandizeni kudziŵa zambili zokhudza makhalidwe abwino a Yehova. Kumvetsetsa makhalidwe abwino a Mulungu kudzakuthandizani kukulitsa cikhulupililo canu na cikondi canu pa iye. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene tingaonetsele kuti timatengela citsanzo ca Yehova coganizila ena. Tidzaphunzila mmene tingacitile zimenezi m’banja, mu mpingo, na mu ulaliki.

^ par. 3 Katswili wolemba mbili ya Ayuda, dzina lake Josephus, anakamba kuti Samueli anali na zaka 12 pa nthawiyo.

^ par. 16 N’zoonekelatu kuti pa anthu amene adzapulumuka Aramagedo, ena adzakhala olemala. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anacilitsa anthu okhala na “zofooka zilizonse.” Izi zinacitila cithunzi zimene iye adzacita kwa opulumuka Aramagedo, osati kwa oukitsidwa. (Mat. 9:35) Mwacidziŵikile, akufa adzaukitsidwa ali na mathupi athanzi, opanda cilema ciliconse.