Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

George Rollston ndi Arthur Willis amene ni apainiya aima pang’ono kuti athile madzi mu injini ya motoka.—Ku Northern Territory, 1933

ZA M’NKHOKWE YATHU

“Kulibe Mseu Woipa Kwambili Kapena Wautali Kwambili”

“Kulibe Mseu Woipa Kwambili Kapena Wautali Kwambili”

PA 26 MARCH, 1937, amuna aŵili olema kwambili a paulendo, anali kuyendetsa thilaki lakuda ndi fumbi pang’ono-pang’ono kuloŵa mumzinda wa Sydney, ku Australia. Iwo anali atacoka mumzindawo kwa caka cimodzi, ndipo anayenda ulendo wa makilomita oposa 19,300, kudutsa m’madela ena akutali kwambili a miyala m’dzikolo. Amuna amenewo sanapite kukayendela dziko kapena kukafufuza zinazake. Arthur Willis ndi Bill Newlands anali aŵili mwa apainiya akhama ofunitsitsa kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu kumadela ambili akutali m’dziko la Australia.

Pofika cakumapeto kwa zaka za m’ma 1920, kagulu kocepa ka Ophunzila Baibo * ku Australia kanali katalalikila kwambili m’mizinda ya m’mbali mwa nyanja, m’matauni, ndi m’madela ena ozungulila. Mkati mwa dzikolo muli cipululu cacikulu kupitilila hafu ya dziko la America, ndipo munali kukhala anthu ocepa. Komabe, abale anali kudziŵa bwino kuti otsatila a Yesu ayenela kucitila umboni za iye “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi,” kuphatikizapo kumadela akutali kwambili m’dziko la Australia. (Mac. 1:8) Koma kodi akanaikwanitsa bwanji nchito yaikulu imeneyo? Pokhala na cikhulupililo conse kuti Yehova adzadalitsa khama lawo, iwo anali ofunitsitsa kucita zonse zimene akanakwanitsa.

APAINIYA AYAMBA NCHITO YOLALIKILA

Mu 1929, mipingo ya ku Queensland ndi ku Western Australia inakonza makalavani kuti ikwanitse kulalikila kumadela akutali. Makalavaniwo anali kugwilitsidwa nchito ndi apainiya amphamvu amene akanakwanitsa kuthana ndi zovuta ndi kuwakonza akawonongeka. Apainiyawa anafikila madela ambili amene anali asanalalikidwepo.

Apainiya amene analibe makalavani anali kugwilitsila nchito njinga kukalalikila m’madela akutali. Mwacitsanzo, mu 1932, Bennett Brickell wa zaka 23, anacoka ku tauni ya Rockhampton mumzinda wa Queensland ndi kupita kumpoto kwa mzindawo kukalalikila kwa miyezi isanu. Pa njinga yake ananyamula mabulangeti, zovala, zakudya, ndiponso mabuku ambili. Mathayela a njinga yake atawonongeka, anapitilizabe ulendo wake ali n’cidalilo cakuti Yehova adzamutsogolela. Anakankha njinga yake pa mtunda wa makilomita 320 kudutsa m’madela amene anthu ena kumbuyoku anafa cifukwa ca ludzu. Kwa zaka zoposa 30 zotsatila, m’bale Brickell anayenda mtunda wa makilomita ambili-mbili kuzungulila Australia. Anali kuseŵenzetsa njinga, honda, ndiponso motoka. Anayamba kulalikila anthu aciabolijini ndi kukhazikitsa mipingo yatsopano. M’baleyu anadziŵika kwambili ndipo anthu anali kum’lemekeza kumadela onse akutali.

KUTHANA NDI MAVUTO

Dziko la Australia ndi limodzi mwa maiko amene ali ndi anthu ocepa kwambili padziko lonse, maka-maka kumadela akutali. Komabe, anthu a Yehova aonetsa khama pofuna kupeza anthu acidwi kumadela akutali m’dzikolo.

Apainiya aŵili, Stuart Keltie ndi William Torrington, anaonetsa khama limenelo. Mu 1933, anadutsa cipululu ca mcenga cochedwa Simpson kuti akalalikile m’tawuni yochedwa Alice Springs, m’kati mweni-mweni mwa dzikolo. Pambuyo pakuti motoka yawo yawonongeka, M’bale Keltie, amene anali na mwendo wopanga, anapitiliza ulendo wolalikila umenewo poseŵenzetsa ngamila. Apainiyawo anadalitsidwa cifukwa ca khama lawo pamene anakumana ndi maneja wa hotela ina m’tauni yochedwa William Creek, ku sitesheni ya sitima. M’kupita kwa nthawi, maneja wa pa hotelayo, dzina lake Charles Bernhardt, analandila coonadi, kugulitsa hotela yake, ndi kuyamba upainiya. Anacita upainiyawu yekha-yekha kwa zaka 15 m’madela ena akutali ndi ouma kwambili m’dziko la Australia.

Arthur Willis akukonzekela ulendo wokalalikila ku dela lakutali m’dziko la Australia.—Ku Perth, Western Australia, 1936

Kukamba zoona, apainiya oyambilila anayenela kulimba mtima ndi kuyesetsa kulimbana ndi mavuto amene anakumana nawo. Pa ulendo wawo wolalikila m’madela akutali m’dziko la Australia, Arthur Willis ndi Bill Newlands, amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino, anavutika kwambili kwa mawiki aŵili pa ulendo wawo wa makilomita 32, cifukwa mvula yamphamvu inacititsa kuti m’cipululu mukhale matope okha-okha. Nthawi zina, anali kuyenda mzigwa za miyala ndi m’tunjila toyendamo madzi kuli kotentha kwambili uku thukuta ili paka-paka, cifukwa coyendetsa thilaki kudutsa m’mcenga wounjikana. Nthawi zambili thilaki yawo ikawonongeka, anali kuyenda wapansi kapena kucova njinga kupita m’tauni yapafupi. Ndiyeno, anali kuyembekezela kwa mawiki ambili kuti zitsulo zagalimoto yowonongekayo zibwele. Ngakhale kuti anali kukumana ndi mavuto ambili conci, anapitiliza kukhala ndi maganizo olimbikitsana. Pogwilako mau a m’magazini yochedwa The Golden Age, m’bale Arthur Willis anati: “Khote-khote ngwanjila, palinga mtima mpomwepo.”

Charles Harris, amene anakhala mpainiya kwa zaka zambili anafotokoza kuti mavuto amene anakumana nawo polalikila kumadela akutali anam’cititsa kuyandikila kwambili kwa Yehova. Anakambanso kuti: “Kukhala ndi katundu wocepa mu umoyo n’kwabwino kwambili. Ngati Yesu nthawi zina anali kugona panja kukakhala kofunikila kutelo, ndiye kuti nafenso tiyenela kucita cimodzi-modzi mwacimwemwe ngati utumiki umene tapatsidwa ufuna zimenezo.” Ndipo n’zimene apainiya ambili anacita. Cifukwa ca khama lawo, uthenga wabwino unafalikila m’dziko lonse la Australia, ndipo unathandiza anthu ambili kuima kumbali ya Ufumu wa Mulungu.

^ par. 4 Ophunzila Baibo anayamba kudziŵika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova mu 1931.—Yes. 43:10.