Onani zimene zilipo

Akazi, N’cifukwa Ciani Muyenela Kugonjela Amuna Monga Mutu?

Akazi, N’cifukwa Ciani Muyenela Kugonjela Amuna Monga Mutu?

Akazi, N’cifukwa Ciani Muyenela Kugonjela Amuna Monga Mutu?

“Mutu wa mkazi ndi mwamuna.”—1 AKOR. 11:3.

1, 2. (a) Kodi mtumwi Paulo analemba zotani pa nkhani yokhudza dongosolo la Yehova la umutu ndiponso kugonjela? (b) Kodi tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

 YEHOVA anakhazikitsa dongosolo labwino limene mtumwi Paulo anachula pamene analemba kuti: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna” ndipo “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akor. 11:3) Nkhani yapitayi inanena kuti Yesu anali kuona kuti ni mwayi kugonjela Mutu wake, Yehova Mulungu, ndipo anali kusangalala kucita zimenezi. Inanenanso kuti mutu wa amuna acikhristu ni Khristu. Khristu anali wokoma mtima, wodekha, wacifundo ndiponso wopanda dyela pocita zinthu na anthu. Amuna mumpingo ayenelanso kusonyeza makhalidwe amenewa pocita zinthu na anthu ena maka-maka akazi awo.

2 Nanga bwanji akazi? Kodi mutu wawo ni ndani? Paulo analemba kuti: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna.” Kodi akazi ayenela kuona bwanji mawu ouzilidwa amenewa? Kodi mfundo imeneyi imagwilanso nchito ngati mwamuna ali wosakhulupilila? Kodi kugonjela mwamuna monga mutu kumatanthauza kuti mkazi azingokhala cete osanena maganizo ake pamene zisankho zikupangidwa m’banja? Nanga mkazi angatani kuti azitamandidwa?

“Nidzam’pangila Wom’thangatila”

3, 4. N’cifukwa ciani dongosolo la umutu n’lothandiza m’banja?

3 Mulungu ni amene anakhazikitsa dongosolo la umutu. Adamu atalengedwa, Yehova Mulungu anati: “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; nidzam’pangila wom’thangatila iye.” Hava atalengedwa, Adamu anasangalala kwambili kuona kuti ali na mnzake woti azimuthandiza moti ananena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Gen. 2:18-24) Adamu na Hava anali na mwayi wapadela wokhala atate ni amayi a anthu angwilo omwe akanakhala mosangalala m’paradaiso kosatha padziko lonse.

4 Cifukwa ca kupanduka kwa makolo athu oyambilila, anthu sanalinso angwilo ngati mmene zinalili poyamba m’munda wa Edene. (Ŵelengani Aroma 5:12.) Koma dongosolo la umutu silinasinthe. Mwamuna na mkazi akamatsatila dongosolo limeneli amapindula kwambili ndipo banja lawo limakhala losangalala. Zotsatila zake zimakhala zofanana ni mmene Yesu anali kumvela pa nkhani yogonjela Yehova monga mutu wake. Asanakhale munthu, Yesu ‘anali kukondwela pamaso pa Yehova nthawi zonse.’ (Miy. 8:30) Cifukwa ca kupanda ungwilo amuna amavutika kukhala mutu wabwino ndipo akazi zimawavutanso kugonjela bwino-bwino. Koma amuna na akazi akamayesetsa kucita zonse zimene angathe, dongosolo la umutu limeneli limathandiza kuti akhale na banja losangalatsa.

5. N’cifukwa ciani anthu okwatilana ayenela kutsatila malangizo opezeka pa Aroma 12:10?

5 Cofunika kwambili kuti banja likhale losangalala ni kutsatila malangizo a m’Malemba opita kwa Akhristu onse akuti: “Posonyezana cikondi caubale khalani ndi cikondi ceniceni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Mwamuna na mkazi ayenelanso kuyesetsa ‘kukhala okomelana mtima wina ndi mnzake, a cifundo cacikulu, okhululukilana ndi mtima wonse.’—Aef. 4:32.

Ngati Mwamuna Wanu Ali Wosakhulupilila

6, 7. Kodi cingacitike n’ciani ngati mkazi wacikhristu akhalabe wogonjela mwamuna wake wosakhulupilila?

6 Bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu satumikila Yehova? Nthawi zambili amuna ni amene amakhala osakhulupilila. Zikatele, kodi mkazi ayenela kuona bwanji mwamuna wake? Baibo imayankha kuti “Inu akazi, muzigonjela amuna anu, kuti ngati ali osamvela mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyela ndi ulemu wanu waukulu.”—1 Pet. 3:1, 2.

7 Mawu a Mulungu amalimbikitsa akazi kukhalabe ogonjela amuna awo osakhulupilila. Khalidwe labwino la mkazi lingacititse mwamuna kuti aganizile za zimene zimapangitsa mkazi kukhala na khalidwe labwinolo. Zotsatila zake n’zakuti mwamunayo angayambe kukhala ni cidwi na zimene mkazi wake yemwe ni Mkhristu amakhulupilila, ndipo m’kupita kwanthawi angaphunzile coonadi.

8, 9. Kodi mkazi wacikhristu angacite ciani ngati mwamuna wake wosakhulupilila sakulabadila khalidwe lake labwino?

8 Bwanji ngati mwamuna wosakhulupililayo salabadila zimene mkazi wake amacita? Malemba amalimbikitsa mkazi wokhulupililayo kusonyeza makhalidwe acikhristu nthawi zonse ngakhale kuti zimenezi zingakhale zovuta. Mwacitsanzo, lemba la 1 Akorinto 13:4 limati: “Cikondi n’coleza mtima.” Conco mkazi wacikhristu ayenela kupitilizabe kucita zinthu “modzicepetsa kothelatu ndi mofatsa, moleza mtima” ndipo azilolela mwacikondi zimene zikumucitikila. (Aef. 4:2) Mzimu woyela, womwe ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito, ungakuthandizeni kukhalabe na makhalidwe abwino ngakhale pamene zinthu zili zovuta.

9 Paulo analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Mzimu wa Mulungu umathandiza mwamuna kapena mkazi wacikhristu kucita zinthu zambili zomwe sakanazikwanitsa payekha. Mwacitsanzo, munthu akamacitilidwa nkhanza na mwamuna kapena mkazi wake angakhale na maganizo ofuna kubwezela. Koma Baibo imalangiza Akhristu onse kuti: “Musabwezele coipa pa coipa; . . . pakuti Malemba amati: ‘Kubwezela ndi kwanga; ndidzawabwezela ndine, atelo Yehova.’” (Aroma 12:17-19) Nalonso lemba la 1 Atesalonika 5:15 limatilangiza kuti: “Onetsetsani kuti wina asabwezele coipa pa coipa kwa wina aliyense, koma nthawi zonse yesetsani kucita cabwino kwa wina ndi mnzake ndi kwa ena onse.” Mothandizidwa na mzimu woyela wa Yehova tingakwanitse kucita zinthu zimene sizingatheke mwa mphamvu yathu. Conco ni bwino kupempha mzimu woyela wa Mulungu kuti utithandize pa zimene tikulephela kucita.

10. Kodi Yesu anali kucita ciani anthu ena akamunenela kapena kumucitila zinthu zoipa?

10 Yesu anapeleka citsanzo cabwino pa zimene tiyenela kucita anthu akamatinenela kapena kuticitila zinthu zoipa. Lemba la 1 Petulo 2:23 limati: “Pamene anali kunenedwa zacipongwe, sanabwezele zacipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipeleka kwa iye amene amaweluza molungama.” Tikulimbikitsidwa kutengela citsanzo cake cabwino. Musamakhumudwe cifukwa ca khalidwe loipa la anthu ena. Monga mmene Akhristu onse akulangizidwila, muzikhala “a cifundo cacikulu, a maganizo odzicepetsa. Osabwezela coipa pa coipa kapena cipongwe pa cipongwe.”—1 Pet. 3:8, 9.

Kodi Akazi Ayenela Kungokhala Cete?

11. Kodi ni mwayi wapadela uti umene akazi ena acikhristu apatsidwa?

11 Kodi kugonjela amuna monga mutu kumatanthauza kuti akazi safunika kulankhula ciliconse pa nkhani za m’banja kapena nkhani zina? Ayi si conco. Yehova wapatsa akazi na amuna zinthu zambili zoti acite. Tangoganizani za mwayi wapadela umene anthu a 144,000 ali nawo wokhala mafumu komanso ansembe kumwamba motsogoleledwa na Khristu pamene azidzalamulila dziko lapansi. M’gulu limeneli mulinso akazi. (Agal. 3:26-29) Apatu n’zoonekelatu kuti Yehova wapatsa akazi nchito yaikulu m’gulu lake.

12, 13. Pelekani citsanzo cosonyeza kuti akazi anali kunenela.

12 Mwacitsanzo, m’nthawi za Baibo akazi ena anali kunenela. Pa lemba la Yoweli 2:28, 29 pali ulosi wakuti: “Ndidzatsanulila mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenela, . . . ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulila mzimu wanga masiku awo.”

13 Ophunzila a Yesu okwana 120 amene anasonkhana m’cipinda capamwamba ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E. anali akazi na amuna. Mzimu wa Mulungu unatsanulidwa pa anthu onsewo. Conco Petulo anagwila mawu a ulosi wa mneneli Yoweli ndipo anasonyeza kuti zimene anali kucita amuna na akazi amenewa, kunali kukwanilitsidwa kwa ulosiwo. Iye anati: “Izi ndi zimene zinanenedwa kudzela mwa mneneli Yoweli kuti: ‘Ndipo m’masiku otsiliza,’ akutelo Mulungu, ‘ndidzatsanulila mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyana-siyana. Pamenepo ana anu aamuna ndi aakazi adzanenela. . . . Ndidzatsanulilanso mbali ya mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi adzakazi anga m’masiku amenewo, ndipo iwo adzanenela.’”—Mac. 2:16-18.

14. Kodi akazi anacita zotani pothandiza kuti Cikhristu coyambilila cifalikile?

14 M’nthawi ya atumwi akazi anathandiza kwambili kufalitsa Cikhristu. Iwo anali kulalikila za Ufumu wa Mulungu ndipo anacita zinthu zina zothandiza pa nchito yolalikila. (Luka 8:1-3) Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anachula za Febe ‘amene anali kutumikila mumpingo wa ku Kenkereya.’ Popeleka moni kwa anchito anzake, Paulo anachula akazi okhulupilika angapo kuphatikizapo “Turufena ndi Turufosa, akazi ogwila nchito mwakhama potumikila Ambuye.” Iye ananenanso kuti, ‘Peresida, wokondedwa wathu anacita nchito zambili potumikila Ambuye.’—Aroma 16:1, 12.

15. Masiku ano, kodi akazi amacita zotani pothandiza kuti Cikhristu cifalikile?

15 Masiku ano, ambili mwa anthu oposa 7 miliyoni amene akulalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse, ni akazi a misinkhu yonse. (Mat. 24:14) Ambili mwa akazi amenewa akucita utumiki wanthawi zonse. Ena ni amishonale pomwe ena akutumikila pa Beteli. Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Ambuye anapatsa mawu: Akazi akulalikila uthengawo ndiwo khamu lalikulu.” (Sal. 68:11) Mawu amenewa akukwanilitsidwa masiku ano. Yehova amayamikila kwambili nchito imene akazi amagwila polengeza uthenga wabwino ndiponso pokwanilitsa zolinga zake. Conco mfundo yakuti akazi acikhristu azigonjela siitanthauza kuti azingokhala cete.

Akazi Aŵili Amene Sanangokhala Cete

16, 17. Kodi citsanzo ca Sara cikusonyeza bwanji kuti akazi sayenela kungokhala cete m’banja?

16 Ngati Yehova wapatsa akazi zinthu zambili zoti acite, ndiye kuti amuna ayenela kufunsila maganizo kwa akazi awo asanapange zisankho zikulu-zikulu. Akamacita zimenezi ndiye kuti akusonyeza nzelu. Malemba amachula zocitika zingapo pamene akazi analankhula kapena kucita zinthu ngakhale kuti amuna awo sanalabadile zonena kapena zocita zawo. Taganizilani zitsanzo ziŵili izi.

17 Sara anali kuuza mobweleza-bweleza mwamuna wake Abulahamu kuti acotse mkazi wake waciŵili limodzi na mwana wake cifukwa cakuti sanali kusonyeza ulemu. “Mawuwo anaipila Abulahamu,” koma osati Mulungu. Ndipo Yehova anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe nawo, cifukwa ca mnyamatayo, ndi cifukwa ca mdzakazi wako; momwe monse akunenela iwe Sara umvele iwe mawu ake.” (Gen. 21:8-12) Abulahamu anamvela Yehova ndipo anacita zimene Sara ananena.

18. Kodi Abigayeli anacita ciani?

18 Taganizilaninso za Abigayeli, mkazi wa Nabala. Pamene Davide anali kuthaŵa mfumu ya nsanje, Sauli, anakakhala pafupi na ziweto za Nabala. Davide na anyamata ake sanatenge ciliconse pa katundu woculuka wa Nabala yemwe anali wolemela koma m’malo mwake iwo anali kuteteza katundu wakeyu. Koma Nabala “anali waphunzo ndi woipa macitidwe ake,” ndipo ‘anakalipila’ anyamata a Davide. Nabala anali ‘munthu woipa’ ndiponso ‘wopusa.’ Pamene anyamata a Davide mwaulemu anam’pempha Nabala kuti awapatseko zinthu, iye anakana. Kodi Abigayeli anatani atamva zimene zinacitikazi? Popanda kuuza Nabala iye “anafulumila, natenga mikate mazana aŵili, ndi zikopa ziŵili za vinyo, nkhosa zisanu zowochawocha, ndi miyeso isanu ya tiligu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana aŵili,” ndipo anazipeleka kwa Davide na anyamata ake. Kodi pamenepa, Abigayeli anacita zolondola? Inde, cifukwa cakuti Baibo imati: “Yehova anam’kantha Nabala, nafa.” Ndipo kenako Davide anakwatila Abigayeli.—1 Sam. 25:3, 14-19, 23-25, 38-42.

‘Mkazi Amene Amatamandidwa’

19, 20. Kodi n’ciani cimacititsa kuti mkazi azitamandidwa?

19 Malemba amayamikila akazi okwatiwa amene amacita zinthu mmene Yehova amafunila. Buku la Miyambo limatamanda “mkazi wangwilo,” ndipo limati: “Mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake um’khulupilila, sadzasowa phindu. Mkaziyo am’citila zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.” Limatinso, “Atsegula pakamwa pake ndi nzelu, ndipo cilangizo ca cifundo cili pa lilime lake. Ayang’anila mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. Ana ake adzanyamuka, nadzamucha wodala; mwamuna wake nam’tama.”—Miy. 31:10-12, 26-28.

20 Kodi n’ciyani cimacititsa kuti mkazi azitamandidwa? Lemba la Miyambo 31:30 limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi cabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Kuopa Yehova kumaphatikizapo kugonjela mofunitsitsa dongosolo la umutu limene Mulungu anakhazikitsa. Baibo imati: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna,” monga zililinso kuti “mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu” ndipo “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”—1 Akor. 11:3.

Yamikilani Mulungu Cifukwa ca Mphatso Imene Anakupatsani

21, 22. (a) Kodi Akhristu okwatilana ali na zifukwa zotani zoyamikila Mulungu cifukwa ca mphatso ya ukwati? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza dongosolo la Yehova la ulamulilo ndiponso umutu? (Onani bokosi pa tsamba 17.)

21 Akhristu okwatilana ali na zifukwa zambili zoyamikila Mulungu. Iwo angamayende mosangalala atagwilana manja. Iwo maka-maka ayenela kuthokoza Mulungu cifukwa ca mphatso ya ukwati. Ndipo ukwati umawapatsa mwayi wocitila limodzi zinthu ndiponso kuyenda na Yehova. (Rute 1:9; Mika 6:8) Popeza Mulungu ni amene anayambitsa ukwati, amadziŵa bwino zimene zimafunika kuti okwatilana akhale osangalala. Nthawi zonse, citani zinthu mogwilizana na zimene amafuna, ndipo ngakhale kuti tili m’dziko la mavuto ‘cimwemwe ca Yehova cidzakhala mphamvu yanu.’—Neh. 8:10.

22 Mwamuna wacikhristu amene amakonda mkazi wake ngati mmene amadzikondela, amacita umutu wake mwacikondi ndiponso mwacifundo. Amakonda kwambili mkazi wake woopa Mulungu popeza mkaziyo amam’thandiza ndiponso amam’lemekeza kwambili. Ndipo cofunika kwambili n’cakuti, ukwati wawo wacitsanzo cabwino umalemekeza Yehova Mulungu wathu yemwe ni woyenela kutamandidwa

Kodi Mukukumbukila?

• Kodi dongosolo la Yehova ni lotani pa nkhani ya umutu na kugonjela?

• N’cifukwa ciani anthu okwatilana ayenela kulemekezana?

• Kodi mkazi yemwe ni Mkhristu ayenela kucita zinthu motani na mwamuna wake wosakhulupilila?

• N’cifukwa ciani amuna ayenela ufunsa akazi awo asanapange zisankho pa nkhani zikulu-zikulu?

[Mafunso Ophunzilila]

[Bokosi]

N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kugonjela Ulamulilo?

Yehova wakhazikitsa dongosolo la ulamulilo ndiponso umutu pakati pa angelo ake komanso anthu. Wacita zimenezi n’colinga cakuti zinthu ziziyenda bwino pakati pa zolengedwa zake zauzimu ndiponso anthu. Dongosolo limeneli limathandiza angelo ake ndiponso anthu kuti azigwilitsa nchito ufulu wawo wosankha polemekeza Mulungu komanso kum’tumikila mogwilizana.—Sal. 133:1.

Mpingo wa Akhristu odzozedwa umazindikila ulamulilo umene Yesu Khristu ali nawo ndiponso kuti iye ni mutu. (Aef. 1:22,23) Popeza amazindikila ulamulilo wa Yehova, “Mwanayonso adzadziika pansi pa Uyo amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:27, 28) Ndiyetu, mpake kuti atumiki a Mulungu odzipeleka ayenela kugonjela dongosolo la umutu mumpingo ndiponso m’banja. (1 Akor. 11:3; Aheb. 13:17) Tikamacita zimenezi timapindula cifukwa Yehova amatiyanja ndiponso amatidalitsa.—Yes. 48:17.

[Cithunzi]

Pemphelo lingathandize mkazi wacikhristu wokwatiwa kusonyeza makhalidwe abwino

[Zithunzi]

Yehova amayamikila nchito imene akazi amagwila popititsa patsogolo zinthu za Ufumu