MBILI YANGA
Kutaikilidwa Atate—Kupeza Atate
ATATE anabadwila ku Graz, m’dziko la Austria mu 1899. Conco, io anali mnyamata pa Nkhondo Yoyamba ya dziko lonse. Mu 1939, nkhondo yaciŵili ya padziko lonse itangoyamba, anawakakamiza kuloŵa usilikali ku German. Mu 1943, anaphedwa pa nkhondo ku Russia. Izi n’zimene zinacitika kuti nditaikilidwe atate. Panthawi imeneyo ndinali ndi zaka pafupifupi ziŵili. Sindinawadziŵepo ndipo ndinali kuyewa kukhala nao, makamaka nditadziŵa kuti anyamata ena kusukulu anali ndi atate ao. Pamene ndinali wacicepele, ndinatonthozedwa kuphunzila za Atate wathu wakumwamba, amene ndi Atate wamkulu wosakhoza kufa.—Hab. 1:12.
KUGWILIZANA NDI BUNGWE LA ANYAMATA
Ndili ndi zaka 7, ndinagwilizana ndi bungwe la anyamata lochedwa Boy Scouts. Bungwe la padziko lonse limeneli linakhazikitsidwa mu 1908 ku Britain, ndi mkulu wa gulu la nkhondo la ku Britain dzina lake Robert Stephenson Smyth Baden-Powell. Mu 1916, iye anakhazikitsanso kabungwe ka anyamata kochedwa Wolf Cubs (kapena Cub Scouts.)
Kumapeto a mlungu, tinali kukonda kupita kukagonela kuthengo m’matenti, titavala mayunifomu, ndiponso tinali kucita pelete motsatila kulila kwa ng’oma. Nthawi imene inali kundikondweletsa kwambili, ndi pamene tinali kuimba titayatsa moto panja m’madzulo ndi kuseŵela m’thengo ndi anyamata ena. Tinaphunzilanso zambili za cilengedwe, ndipo zimenezi zinandithandiza kuyamikila nchito ya Mlengi wathu.
Anyamata a m’kabungwe kameneka, amalimbikitsidwa kucita zabwino tsiku lililonse. Imeneyi ndi mfundo imene amatsatila. Popatsana moni tinali kunena kuti “Okonzeka Nthawi Zonse.” Zimenezi zinandikondweletsa kwambili. Pa kagulu kathu tinali oposa 100, ndipo pafupifupi hafu anali Akatolika, ena anali a Protesitanti, koma mmodzi cabe anali Mbuda.
Kuyambila m’caka ca 1920, misonkhano ya dziko lonse, kapena phwando la bungwe limeneli, lakhala likucitika pambuyo pa zaka zingapo. Ndinapezeka pa msonkhano wa nambala 7 mu August 1951, ku Austria m’tauni ya Bad Ischl. Ndiponso mu August 1957, ndipezekanso pa msonkhano wa bungwe limeneli wa nambala 9 ku Sutton Park, pafupi ndi Birmingham, ku England. Pa msonkhano wa mu 1957, panali anyamata 33 sauzande ocokela m’zigawo zosiyanasiyana za ku England, ndi a ku maiko ena 85. Ndiponso, panali anthu 750 sauzande amene anaticezela kuphatikizapo Mfumukazi Elizabeth wa ku England. Ndinaona kuti umenewu unali ubale wa padziko lonse. Koma nthawi imeneyo sindinadziŵe kuti posacedwa ndidzakhala mbali ya ubale weniweni, umene ndi ubale wa kuuzimu.
KUKUMANA NDI MBONI ZA YEHOVA KWA NTHAWI YOYAMBA
Mu 1958, ca m’ma March kapena April, ndinali pafupi kutsiliza maphunzilo anga monga wopeleka zakudya mu hotelo ina yochedwa Grand Hotel Wiesler, m’tauni ya Graz, ku Austria. Ndili kumeneko, mnzanga wina amene anali kugwilila nchito kophikila makeke, dzina lake Rudolf Tschiggerl, anayamba kuceza nane nkhani za m’Baibulo. Nthawiyo ndinali ndisanamvepo coonadi. Nkhani yoyamba imene tinakambilana ndi ya Utatu, ndipo anandiuza kuti si ciphunzitso ca m’Baibulo. Ndinatsutsa zimene iye anali kundiuza ndipo ndinafuna kumuonetsa kuti akunama. Mnzanga ameneyu ndinali kum’konda kwambili. Conco, ndinafuna kum’nyengelela kuti abwelele ku Katolika.
Rudolf, amene tinali kuitana kuti Rudi, anandipatsa Baibulo. Ndinamuuza kuti ndifuna Baibulo la cikatolika cabe. Atandipatsa ndinayamba kuliŵelenga, ndipo ndinapezamo kapepala ka uthenga kosindikizidwa ndi Mboni za Yehova kamene Rudi anaikamo. Sindinakaŵelenge kapepalako cifukwa ndinali kuona kuti mabuku a conco amaoneka kuti ali ndi coonadi pamene alibe. Komabe, ndinali wofunitsitsa kukambilana naye Baibulo. Rudi anacita zinthu mwanzelu ndipo sanandipatsenso buku lililonse. Kwa miyezi itatu, tinali kukambilana Baibulo mwa apa ndi apo, ndipo makambilano athu anali kufika mpaka usiku.
Nditatsiliza maphunzilo anga a m’hotelo m’tauni ya Graz, amai anandilipilila ndalama zina kuti ndionjezele maphunzilo ena a m’hotelo. Conco, ndinapita ku sukulu ina ya ku Bad Hofgastein, tauni ya m’mbali mwa mapili a Alps. Sukulu imeneyi inali kucitila zinthu zina pamodzi ndi Grand Hotel. Ndipo nthawi zina ndinali kugwilako nchito mu hotelo imeneyi kuti ndizigwilitsila nchito zimene ndinali kuphunzila m’kalasi.
ALONGO AŴILI AMISHONALE ANDICEZELA
Rudi anatumiza adilesi yanga yatsopano ku ofesi ya nthambi ku Vienna, ndipo ofesi ya nthambiyo inatumiza adilesi imeneyo kwa alongo aŵili amishonale, Ilse Unterdörfer ndi Elfriede Löhr. * Tsiku lina, mwamuna wolandila alendo mu hotelo, anandiitana ndi kundiuza kuti kuli azimai aŵili m’galimoto amene anali kufuna kundiona. Ndipo ngakhale kuti sindinali kuwadziŵa, ndinapita kukawaona. M’kupita kwa nthawi, ndinadziŵa kuti io anatumikila monga Mboni zonyamula mabuku mwakabisila, pamene nchito yolalikila inali yoletsedwa ndi cipani ca Nazi ku Germany. Nthawi imeneyi Nkhondo Yaciŵili ya Dziko lonse inali isanayambe. Ndipo ngakhale nkhondoyo isanayambe, io anali atamangidwapo ndi apolisi akabisila a ku Germany (Gestapo), ndi kuwatumiza ku msasa wa cibalo ku Lichtenburg. Ndiyeno nkhondoyo ili mkati, anatumizidwa ku msasa wina ku Ravensbrück pafupi ndi mzinda wa Berlin.
Alongo amenewa ndinawalemekeza cifukwa anali a zaka zofanana ndi amai. Motelo, sindinafune kuwataila nthawi mwa kuyamba kukambitsilana nao, ndiyeno mwina pakapita milungu kapena miyezi ndi kuwauzanso kuti sindifuna. Conco, ndinawapempha kuti akandilembele cabe malemba okhudza ciphunzitso cacikatolika ca kuloŵana m’malo kwa atumwi. Ndinawauza kuti tidzakambilana malembawo ndi wansembe wa ku chalichi cathu. Ndinaganiza kuti mwa kucita zimenezo ndizadziŵa coonadi.
KUPHUNZILA ZA ATATE WOONA WAKUMWAMBA
Ciphunzitso ca Akatolika cimati kuloŵana m’malo kwa atumwi kwapitilizabe kucokela m’nthawi ya mtumwi Petulo kudzafika m’nthawi ya apapa. (Chalichi cimamasulila molakwika mau a Yesu a pa Mateyu 16:18, 19.) Ciphunzitso cimeneci cimakambanso kuti zimene apapa amaphunzitsa n’zodalilika. Ndinakhulupilila zimenezi, ndipo ndinaganiza kuti ngati apapa amene Akatolika amawaitana kuti Atate Woyela, amenenso ziphunzitso zao n’zodalilika, amakamba kuti ciphunzitso ca Utatu n’coona, ndiye kuti n’coonadi. Koma ngati zimene io amanena n’zosadalilika, ndiye kuti ciphunzitsoco n’cabodza. Ndiye cifukwa cake Akatolika ambili amakhulupilila kuti kuloŵana m’malo kwa atumwi ndi ciphunzitso cofunika kwambili. Conco, ziphunzitso zonse za Akatolika, kaya n’zoona kapena ai zimadalila pa ciphunzitso cimeneci.
Pamene ndinapita kukafunsa wansembe, iye analephela kuyankha mafunso anga. M’malo mwake, anapita pa shelufu ndi kutenga buku la cikatolika limene limafotokoza za kuloŵana m’malo kwa atumwi kuti ndikaŵelenge ku nyumba. Nditatsiliza kuŵelenga, ndinabwelelanso kwa wansembeyo ndi mafunso ambili. Conco, atalephela kundiyankha, anati: “Sindingakusinthe maganizo, ndipo iwenso sungandisinthe. . . . Usakabwelenso kwa ine!” Iye sanafunenso kukambilana nane.
Tsopano ndinali wokonzeka kuphunzila Baibulo ndi alongo aŵili aja, Ilse ndi Elfriede. Anandiphunzitsa zambili ponena za Atate Woyela woona wakumwamba, Yehova Mulungu. (Yoh. 17:11) Panthawiyo, kudelalo kunalibe mpingo. Conco, alongo aŵili aja anali kucititsa misonkhano m’nyumba ya banja lina lacidwi, ndipo opezekapo anali ocepa. Popeza kuti kunalibe m’bale wobatizika, alongowo anali kukambilana aŵiliŵili mbali zambili za misonkhano. Nthawi zina, abale ocokela ku mipingo ina anali kubwela kudzapeleka nkhani ya onse, ndipo tinali kufunafuna malo alendi.
KUYAMBA NCHITO YOLALIKILA
Mu October 1958, Ilse ndi Elfriede anayamba kuphunzila nane Baibulo. Ndinabatizika patapita miyezi itatu mu January, 1959. Ndisanabatizike ndinapempha alongo aŵili aja kuti ndipite nao mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, kuti ndidziŵe mmene nchito yolalikila imacitikila. (Mac. 20:20) Nditapita nao kwa nthawi yoyamba, ndinawapempha ngati angandipatse gawo langalanga. Anandigaŵila gawo, ndipo ndinali kulalikila ndekha kunyumba ndi nyumba, ndi kubwelelanso kwa anthu acidwi. M’bale woyamba kulalikila naye kunyumba ndi nyumba anali woyang’anila dela, amene pambuyo pake anadzaticezela.
Mu 1960, nditatsiliza maphunzilo anga a m’hotelo, ndinabwelela kwathu kuti ndikathandizile acibale anga kuphunzila coonadi. Koma mpaka pano, kulibe ngakhale mmodzi anakhala mboni. Komabe, ena amaonetsako cidwi pang’ono.
KUYAMBA UTUMIKI WA NTHAWI ZONSE
Mu 1961, makalata ocokela ku ofesi ya nthambi olimbikitsa kuyamba upainiya anaŵelengedwa m’mipingo. Panthawiyo ndinali wosakwatila, ndipo ndinali ndi thanzi labwino. Conco, ndinaona kuti panalibe condiletsa kuyamba upainiya. Ndinakambilana ndi woyang’anila dela Kurt Kuhn, kuti ndimve maganizo ake cifukwa ndinali kufuna kugwila nchito kwa miyezi ingapo kuti ndigule galimoto yocitila upainiya. Kodi iye anati bwanji? Iye anandifunsa kuti: “Kodi Yesu ndi atumwi ake anafunikila galimoto kuti acite utumiki wa nthawi zonse?” Funso limenelo linandigwila mtima. Motelo, mosataya nthawi ndinaganiza zoyamba upainiya. Koma popeza ndinali kugwila nchito mu hotelo maola 72 mlungu uliwonse, coyamba ndinafunika kusintha zinthu zina.
Ndinapempha abwana anga kuti andilole kugwila nchito maola 60 m’malo mwa maola 72. Anandilola, ndipo anapitiliza kundipatsa malipilo amodzimodzi. M’kupita kwa nthawi, ndinapemphanso kuti ndizigwila nchito maola 48 pa mlungu. Anavomelanso pempho langa, koma sanasinthe malipilo anga. Nthawi ina ndinapempha kuti ndizigwila nchito maola 36 pa mlungu, kutanthauza kugwila nchito maola 6 kwa masiku 6. Abwana anandilolanso, ndipo codabwitsa n’cakuti malipilo anga anali amodzimodzi. Zinaoneka kuti abwana anga sanafune kuti ndileke nchito. Conco, kugwila nchito maola amenewo kunandithandiza kucita upainiya wa nthawi zonse. Panthawiyo, apainiya anali kupeleka maola 100 pa mwezi.
Patapita miyezi inai, ndinaikidwa kukhala mpainiya wapadela ndi mtumiki wa mpingo mu mpingo waung’ono m’cigawo ca Carinthia, m’tauni ya Spittal an der Drau. Nthawiyo, apainiya apadela anali kupeleka maola 150 pa mwezi. Ndinalibe mnzanga wolalikila naye, koma ndinayamikila kwambili thandizo la mlongo wina dzina lake Gertrude Lobner, amene anali kutumikila monga wothandiza mtumiki wampingo. *
MAUTUMIKI ASINTHA MOFULUMILA
Mu 1963, ndinaikidwa kukhala woyang’anila dela. Nthawi zina ndinali kukwela sitima pokacezela mipingo nditanyamula masutukesi olema. Abale ambili analibe magalimoto, conco palibe amene anali kubwela kudzanditenga ku sitesheni ya sitima. Posafuna “kudzionetsela,” ndinali kuyenda pansi kupita ku nyumba imene andikonzela, m’malo mokwela takisi.
Mu 1965, ndisanakwatile, anandiitana kukaloŵa Sukulu ya Gileadi ya nambala 41. Ambili amene tinali nao ku Gileadi analinso osakwatila. Nditatsiliza maphunzilo, cokondweletsa n’cakuti ananditumiza kwathu ku Austria, kuti ndikapitilize kutumikila monga woyang’anila dela. Komabe, ndisanacoke ku United States, anandipempha kugwila nchito ndi woyang’anila dela wina kwa milungu inai. Ndinalimbikitsidwa kwambili kutumikila pamodzi ndi Anthony Conte. Iye anali m’bale wokoma mtima, waluso ndi wokonda utumiki. Tinatumikila pamodzi ku dela la Cornwall, mu mzinda wa New York.
Nditabwelela ku Austria, ndinayamba kutumikila ku dela lina kumene ndinakumana ndi Tove Merete, mlongo wokongola, amene anali mbeta. Iye analeledwa m’coonadi ndi makolo ake kuyambila ali ndi zaka zisanu. Abale akatifunsa mmene tinakumanilana, mwanthabwala timati, “Ofesi ya nthambi ndi imene inakonza kuti tikumane.” Mu April 1967, patapita caka cimodzi tinakwatilana, ndipo anatilola kupitiliza kutumikila m’dela.
Caka cotsatila, ndinazindikila kuti Yehova mwa cisomo cake wandisankha kukhala mwana wake wauzimu. Conco, ndinakhala paubale wapadela ndi Atate wanga wakumwamba, ndi onse amene ‘amafuula kuti: “Abba, Atate!”’ malinga ndi Aroma 8:15.
Ine ndi mkazi wanga, Merete, tinapitiliza kutumikila m’dela ndi m’cigawo mpaka mu 1976. M’nyengo yozizila, nthawi zina tinali kugona m’zipinda zopanda ziwiya zothumitsila, ndipo munali kuzizila kwambili. Tsiku lina titauka m’maŵa, tinapeza kuti zofunda zathu zauma ku mbali ya kumutu, ndipo zinali mbuu cifukwa ca nthunzi zathu. Conco, tinayamba kunyamula ziwiya zothumitsila zamagetsi kuti tizizigwilitsila nchito kukazizila usiku. M’nyumba zina mmene tinali kukhala zimbudzi zinali za panja, ndipo munali kuzizila kwambili. Motelo, popita kumeneko usiku tinali kupita m’cipale cofewa. Popeza tinalibe nyumba yathuyathu, tikatsiliza kucezela mpingo tinali kukhalabe m’nyumba imodzimodziyo mpaka pa Mande. Ndiyeno, pa Ciŵili m’maŵa tinali kupita ku mpingo wina.
Ndine wokondwa kuti mkazi wanga wokondedwa wandicilikiza kwambili kwa zaka zonsezi. Iye amakonda kwambili ulaliki, ndipo sindinali kufunika kumulimbikitsa kupita mu ulaliki. Amakondanso abale ndi alongo, ndipo amadela nkhawa ena. Iye wakhala thandizo lalikulu kwa ine.
Mu 1976, tinaitanidwa kukatumikila ku ofesi ya nthambi ya ku Austria m’tauni ya Vienna. Ndipo ndinaikidwa kukhala m’Komiti ya Nthambi. Nthawiyo, nthambi ya ku Austria inali kuyang’anila nchito ya m’maiko ambili a kum’maŵa kwa Europe. Ndipo inali kutumiza mabuku mwakabisila ku maiko amenewo. M’bale Jürgen Rundel ndiye anali kutsogolela pa nchitoyi, ndipo anali kuigwila m’njila zosiyanasiyana. Ndinali ndi mwai wotumikila naye, ndipo pambuyo pake ndinapatsidwa nchito yoyang’anila dipatimenti yomasulila mabuku a zinenelo 10 za kum’maŵa kwa Europe. M’bale Jürgen ndi mkazi wake, Gertrude, akali kutumikila mokhulupilika monga apainiya apadela ku Germany. Kuyambila m’caka ca 1978, nthambi ya ku Austria inali kukopa ndi kusindikiza magazini m’zinenelo 6 pa makina aang’ono osindikizila. Tinali kutumizanso magazini kwa anthu amene analembetsa magazini m’maiko osiyanasiyana. M’bale Otto Kuglitsch, amene akutumikila ndi mkazi wake, Ingrid, ku ofesi ya nthambi ku Germany, anali katswili pa nchitoyi.
Abale a kum’mawa kwa Europe anali kusindikizanso mabuku m’maiko ao pogwilitsila nchito makina ocitila fotokope. Ngakhale n’conco, anafunikila thandizo locokela ku maiko ena. Yehova anateteza nchito imeneyi. Ndipo ife abale a ku nthambi tinali kuwakonda kwambili abalewo, cifukwa anatumikila movutikila zaka zambili pamene nchito inali yoletsedwa.
ULENDO WAPADELA KU ROMANIA
Mu 1989, ndinali ndi mwai wopita ku Romania ndi M’bale Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulila. Colinga ca ulendowu cinali kukathandiza gulu lalikulu la abale a kumeneko kuti agwilizanenso ndi gulu la Mulungu. Kuyambila m’caka ca 1949, cifukwa ca zifukwa zina, abalewo analeka kugwilizana ndi gulu ndipo anakhazikitsa mipingo yao. Koma io anapitilizabe kulalikila ndi kubatiza ophunzila. Mofanana ndi abale ena amene anali m’gulu lovomelezedwa ndi likulu, naonso anaikidwa m’ndende cifukwa cosatenga mbali m’zandale. Popeza ciletso cinali cikali mkati ku Romania, tinali kukumana mwakabisila m’nyumba ya M’bale Pamfil Albu, pamodzi ndi abale anai audindo ndi oimila Komiti ya Dziko.
Pa tsiku laciŵili la makambilano athu usiku, M’bale Albu anacondelela akulu anai aja kuti agwilizane nafe. Iye anati: “Abale ngati sitigwilizana nao tsopano, mwina sitidzakhalanso ndi mwai wina.” Motelo, abale pafupifupi 5,000 anagwilizananso ndi gulu. Ndithudi, Yehova anapambana koma Satana analephela.
Ca kumapeto kwa 1989, ulamulilo wa cikomunizimu wa kum’maŵa kwa Europe usanagwe, Bungwe Lolamulila linatipempha kuti tisamukile ku likulu ku New York. Sitinayembekezele zimenezo. Tinayamba kutumikila pa nthambi ya ku Brooklyn mu July 1990. Mu 1992, ndinaikidwa kuti ndizithandizila m’Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila. Ndipo kuyambila mu July 1994, ndakhala ndi mwai wotumikila m’Bungwe Lolamulila.
KUKUMBUKILA ZA KUMBUYO NDI KUYANG’ANA MTSOGOLO
Nthawi yogwila nchito monga wopeleka cakudya mu hotelo inapita kale. Tsopano, ndine wokondwa kugaŵanamo pa nchito yokonza cakudya ca kuuzimu ndi kucigaŵila kwa abale padziko lonse. (Mat. 24: 45-47) Ndikayang’ana kumbuyo zaka 50 zimene ndakhala mu utumiki wa nthawi zonse ndimakondwa, ndipo ndimayamikila kwambili kuti Yehova wadalitsa ubale wathu wa padziko lonse. Ndimakondwela kwambili kupezeka pa misonkhano ya maiko kumene timaphunzila zambili za Atate wathu wakumwamba, Yehova, ndi coonadi ca m’Baibulo.
Ndimapemphela kuti anthu mamiliyoni aphunzile Baibulo, alandile coonadi, ndi kutumikila Yehova mogwilizana ndi gulu la abale la padziko lonse. (1 Pet. 2:17) Ndiyang’ananso mtsogolo kudzaona anthu akuukitsidwa padziko ndili kumwamba, ndi kudzaonanso atate wanga a kuthupi. Ndiyembekezela kuti mwina atate, amai, ndi acibale ena okondedwa adzalambila Yehova m’Paladaiso.
Ndiyang’ana mtsogolo kudzaona anthu akuukitsidwa padziko ndili kumwamba, ndi kudzaonanso atate wanga a kuthupi