Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Bwelelani Mukalimbikitse Abale Anu’

‘Bwelelani Mukalimbikitse Abale Anu’

PETULO analila kwambili pambuyo pokana Yesu. Ngakhale kuti mtumwi ameneyu zikanam’vuta kupitilizabe kucita bwino kuuzimu, Yesu anafunabe kum’gwilitsila nchito kuthandiza ena. Conco, Yesu anamuuza kuti: “Ukabwelela, ukalimbikitse abale ako.” (Luka 22:32, 54-62) Petulo anadzakhala mmodzi wa mizati ya mpingo wacikristu m’nthawi ya atumwi. (Agal. 2:9) Mofananamo, mwamuna amene kale anali mkulu angayambenso kutumikila ndi kupezanso cimwemwe polimbikitsa okhulupilila anzake mwa kuuzimu.

Ena amene kale anali oyang’anila anatsitsidwa pa maudindo. Ndipo zimenezo zinawacititsa kudziona monga analephela udindo wao. Julio, * amene anatumikila monga mkulu ku Bolivia kwa zaka zoposa 20, anati: “Kukonzekela nkhani, kucezela abale, ndi kucita maulendo aubusa inali mbali yaikulu ya moyo wanga. Popanda maudindo onse amenewa ndinadzimva monga ndataikilidwa cinthu cacikulu. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambili.” Tsopano Julio atumikilanso monga mkulu.

“SANGALALANI”

Wophunzila Yakobo analemba kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayeselo osiyanasiyana.” (Yak. 1:2) Yakobo anali kukamba za mayeselo obwela cifukwa ca cizunzo ndi kupanda ungwilo kwathu. Iye anachula zinthu monga zilakolako zoipa ndi kukondela ndi zina zotelo. (Yak. 1:14; 2:1; 4:1, 2, 11) Koma tikalakwa Yehova amatipatsa cilango, ndipo cilangoco cimakhala coŵaŵa. (Aheb. 12:11) Conco, mayeselo amenewo sayenela kutilanda cimwemwe.

Ngakhale kuti tinatsitsidwa pa maudindo mu mpingo, tingakhalebe ndi mwai woona ngati cikhulupililo cathu cikali colimba, ndi kuonetsa kuti timakonda Yehova. Zimatipatsanso mpata woganizila cifukwa cake tinali kutumikila pa maudindo amenewo. Kodi  tinakalamila udindo cifukwa cofuna kudzipindulitsa kapena cifukwa cokonda Mulungu? Kapena mwina tinali otsimikiza mtima kuti mpingo ndi wa Mulungu ndipo unafunikila cisamalilo? (Mac. 20:28-30) Aja amene anali akulu kale koma apitiliza kutumikila Mulungu mosangalala monga ofalitsa, amaonetsa kwa onse, kuphatikizapo Satana, kuti cikondi cao pa Yehova ndi ceniceni.

Pamene Mfumu Davide analangidwa cifukwa cocita macimo aakulu, iye anavomeleza cilango ndipo anakhululukidwa. Iye anaimba kuti: “Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene macimo ake aphimbidwa. Wodala ndi munthu amene Yehova sanamusungile colakwa cake, amene alibe mtima wacinyengo.” (Sal. 32:1, 2) Mosakaikila, cilango cinathandiza Davide kukhala m’busa wabwino wa anthu a Mulungu.

Nthawi zambili, aja amene anatsitsidwapo monga akulu, amakhala abusa abwino kwambili kuposa kale. Mkulu wina amene anatsitsidwapo anati: “Tsopano ndadziŵa mocitila ndi aja amene amalakwa.” Winanso anati: “Tsopano udindo wanga wotumikila abale ndimauona kukhala wofunika kwambili.”

KODI MUNGATUMIKILENSO?

Wamasalimo analemba kuti: “[Yehova] sadzakhalila kutiimba mlandu nthawi zonse cifukwa ca zolakwa zathu.” (Sal. 103:9) Cotelo, tisaziganiza kuti Mulungu sangadalilenso munthu amene anacitapo chimo lalikulu. Ricardo, amene anatsitsidwapo pambuyo potumikila monga mkulu kwa zaka zambili, anati: “Ndinakhumudwa kwambili cifukwa ndinaona monga ndalephela. Kwa nthawi yaitali, ndinali kulephela kubwelela kukatumikilanso abale monga woyang’anila cifukwa codziona kukhala wolephela. Ndinalibe cidalilo cakuti ndingakhalenso wodalilika. Koma cifukwa cokonda kuthandiza ena, ndinali kutsogoza maphunzilo, kulimbikitsa abale pa Nyumba ya Ufumu, ndi kulalikila nao. Zimenezo zinandithandiza kukhalanso ndi cidalilo, ndipo tsopano nditumikilanso monga mkulu.”

Yehova wathandiza amuna ambili kupezanso cimwemwe ndi kukhala ofunitsitsa kutsogolela mu mpingo

Kusunga cakukhosi kungalepheletse m’bale kutumikilanso monga mkulu. Ndi bwino kukhala monga mtumiki wa Yehova, Davide, amene anathaŵa cifukwa ca nsanje ya Mfumu Sauli. Davide anakana  kubwezela coipa kwa Sauli ngakhale pamene mpata unapezeka wocita zimenezo. (1 Sam. 24:4-7; 26:8-12) Pamene Sauli anafa pa nkhondo, Davide anamulila. Iye anakamba kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani anali anthu “okondeka ndi osangalatsa.” (2 Sam. 1:21-23) Davide sanasunge cakukhosi.

Ngati muganizila kuti ena sanakumvetsetseni kapena munacitilidwa mopanda cilungamo, musalole mkwiyo kusokoneza maganizo anu. Mwacitsanzo, William wa ku Britain atatsitsidwa pa maudindo pambuyo potumikila monga mkulu kwa zaka 30, anayamba kukwiila akulu ena. Nanga n’ciani cinam’thandiza kuyambanso kuona zinthu moyenela? Iye anati, “Kuŵelenga buku la Yobu kunandilimbikitsa. Ngati Yehova anathandiza Yobu kukhalanso pa mtendele ndi anzake atatu aja, cingam’letse n’ciani kundithandiza kuti ndikhalenso pa mtendele ndi akulu?”—Yobu 42:7-9.

MULUNGU AMADALITSA AMENE AMAYAMBANSO KUTUMIKILA MONGA ABUSA

Ngati munatula udindo wanu wotumikila nkhosa za Mulungu, zingakhale bwino kudzifunsa cifukwa cimene munacitila zimenezo. Kodi n’cifukwa cakuti munakumana ndi mavuto ena ake? Kapena munayamba kuona zinthu zina kukhala zofunika kwambili paumoyo wanu? Kodi munakhumudwa cifukwa ca zophophonya za ena? Mulimonse mmene zingakhalile, dziŵani kuti pamene munali mkulu munali kuthandiza ena m’njila zambili. Nkhani zanu ndi citsanzo canu zinali kulimbikitsa ena, ndipo maulendo anu aubusa anali kuwathandiza kupilila mayeselo ao. Kukhulupilika kwanu monga mkulu kunali kukondweletsa Yehova, monga mmene inunso kunali kukukondweletsani.—Miy. 27:11.

Onetsani kukonda kwanu Yehova mwa kucita utumiki wopatulika mwacimwemwe

Yehova wathandiza amuna ambili kupezanso cimwemwe ndi kukhala ofunitsitsa kutsogolela mu mpingo. Ngati munatula udindo monga mkulu, kapena ngati munatsitsidwa, ‘mungayesetse kuti mukhalenso woyang’anila.’ (1 Tim. 3:1) Paulo ‘sanaleke kupemphelela’ Akristu a ku Kolose kuti akhale odziŵa zinthu za Mulungu molondola, ‘kuti aziyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti azimukondweletsa pa ciliconse.’ (Akol. 1:9, 10) Ngati mwayamikilidwanso monga mkulu, muziyang’ana kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu kuti mukhale odekha ndi acimwemwe. M’masiku ano otsiliza, anthu a Mulungu amafunikila thandizo la kuuzimu la abusa acikondi. Kodi ndinu okonzeka ndi ofunitsitsa kulimbikitsa abale anu?

^ par. 3 Maina ena asinthidwa.