Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Gwilitsilani Nchito Mau a Mulungu​—Ndi Amoyo

Gwilitsilani Nchito Mau a Mulungu​—Ndi Amoyo

“Mau a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”—AHEB. 4:12.

1, 2. Ndi nchito yotani imene Yehova anapatsa Mose? Nanga anam’tsimikizila za ciani?

TIYELEKEZELE kuti mufunikila kukakamba ndi wolamulila wamphamvu padziko lonse lapansi, moimilako anthu a Mulungu. Kodi mungamve bwanji? Mwacionekele, mungakhale ndi nkhawa, mungacite mantha, ndipo mungadzione kuti ndinu wosayenelela. Kodi mungakonzekele bwanji mau amene mudzakamba? Nanga mungacitenji kuti mukakambe mwamphamvu monga woimilako Mulungu wamphamvuyonse?

2 Izi n’zimene zinacitikila Mose. Iye anali “munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” Yehova anamuuza kuti apite kwa Farao kuti akapulumutse anthu a Mulungu opondelezedwa, amene anali akapolo ku Iguputo. (Num. 12:3) Zimene zinacitika zinaonetsa kuti Farao anali munthu woipa mtima ndi wodzikuza. (Eks. 5:1, 2). Ngakhale n’conco, Yehova anauza Mose kuti apite akalamule Farao, kuti amasule anthu a Mulungu pafupifupi 3 miliyoni amene anali mu ukapolo. N’zomveka kuti Mose anafunsa Yehova kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?” Mose ayenela kuti anadziona kuti ndi wosayenelela ndipo sangakwanitse. Koma Yehova anam’tsimikizila kuti sadzakhala yekha pamene anamuuza kuti: “Ndidzakhala nawe.”—Eks. 3:9-12.

3, 4. (a) N’cifukwa ciani Mose anacita mantha? (b) Ndi pa cocitika citi pamene mungamve monga mmene Mose anamvelela?

 3 N’cifukwa ciani Mose anacita mantha? Mwacionekele, anali kuopa kuti Farao sadzam’landila ndi kumumvela monga woimilako Yehova Mulungu. Mose anali kuopanso kuti anthu a mtundu wake sadzakhulupilila kuti Yehova anam’sankha kuwatsogolela kutuluka mu Iguputo. Conco, Mose anauza Yehova kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupilila ndi kumvela mau anga? Cifukwatu adzanena kuti, ‘Yehova sanaonekele kwa iwe.’”—Eks. 3:15-18; 4:1.

4 Nanga bwanji inu? Mwina simungafunikile kupita kukakamba ndi wolamulila wamphamvu. Koma bwanji ngati mumalephela kukamba ndi anthu a m’gawo lanu za Yehova ndi Ufumu wake? Ngati n’conco, onani zimene tingaphunzile pa nkhani ya Mose.

‘N’CIANI ICO CILI M’DZANJA LAKO?’

5. Kodi Yehova anaika ciani m’dzanja la Mose? Nanga zimenezo zinathetsa bwanji mantha ake? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

5 Pamene Mose anauza Yehova kuti anali kuopa kuti anthu sadzam’khulupilila, Mulungu anam’konzekeletsa ndi zimene zinali kubwela. Nkhani ya pa Ekisodo imati: “Yehova anamufunsa [Mose] kuti: ‘Cili m’dzanja lakoco n’ciani?’ ndipo Mose anayankha kuti: ‘Ndodo.’ Kenako iye anati: ‘Iponye pansi.’ Anaiponya pansi ndipo inasanduka njoka. Pamenepo Mose anayamba kuthaŵa. Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Igwile kumcila.’ Conco Mose anaigwila, ndipo inasandukanso ndodo m’dzanja lake. Popitiliza Mulungu anati: ‘Ukacite zimenezi kuti akakhulupilile kuti Yehova . . . anaonekela kwa iwe.’” (Eks. 4:2-5) Motelo, Mulungu anaika m’dzanja la Mose umboni woonetsa kuti uthenga wake unali wocokela kwa Yehova. Cimene cinali kuoneka ngati ndodo wamba cinasanduka njoka cifukwa ca mphamvu ya Mulungu. Cozizwitsa cimeneci cikanaonetsa kuti Mose anatumidwadi ndi Mulungu ndi kuti iye anali naye. Conco, Yehova anauza Mose kuti: “Ndodo iyi izikakhala m’dzanja lako kuti ukaigwilitse nchito pocita zizindikilo.” (Eks. 4:17) Ndi umboni umenewu, Mose anali ndi cidalilo cakuti angapite kukakamba ndi Farao ndiponso ndi anthu a Mulungu.—Eks. 4:29-31; 7:8-13.

6. (a) Polalikila tiyenela kukhala ndi ciani m’dzanja lathu? N’cifukwa ninji? (b) Kodi “mau a Mulungu ndi amoyo” motani? Ndipo “ndi amphamvu” motani?

6 Funso limeneli lakuti: “Cili m’dzanja lakoco n’ciani”? lingafunsidwenso kwa ife tikapita kukalalikila uthenga wa m’Baibulo kwa ena. Nthawi zambili, timakhala ndi Baibulo m’dzanja lathu kuti tiligwilitsile nchito. Ena amaona Baibulo ngati buku wamba, koma Yehova amalankhula nafe kupyolela m’Mau ake ouzilidwa olembedwa mmenemo. (2 Pet. 1:21) Baibulo lili ndi malonjezo a Mulungu amene adzakwanilitsidwa mu Ufumu wake. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo analemba kuti: “Mau a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Ŵelengani Aheberi 4:12.) Malonjezo onse a Yehova amakwanilitsidwa cifukwa iye akupitilizabe kugwila nchito kuti awakwanilitse. (Yes. 46:10; 55:11) Munthu akadziŵa mfundo zopezeka m’Mau a Yehova, zimene amaŵelenga m’Baibulo zimakhudza kwambili umoyo wake.

7. Tingacitenji kuti ‘tizifotokoza bwino mau a coonadi’?

7 Yehova waika m’dzanja lathu Mau ake amoyo amene aonetsa kuti uthenga wathu ndi wodalilika, ndipo umacokeladi kwa iye. Ndiye cifukwa cake, pamene Paulo anali kuphunzitsa Timoteyo, anam’limbikitsa kuti ‘azifotokoza bwino mau a coonadi.’ (2 Tim. 2:15) Nanga ifenso tingatsatile motani malangizo a Paulo? Tingacite zimenezi mwa kuŵelengela anthu malemba oyenelela amene angawafike pamtima. Tumapepala twa uthenga tumene tunatuluka mu 2013, tunakonzedwa kuti tutithandize kucita zimenezi.

 ŴELENGANI LEMBA LOYENELELA

8. Woyang’anila nchito wina anati ciani ponena za tumapepala twauthenga?

8 Tumapepala tonse twatsopano twauthenga tunalembedwa mofanana. Conco, tikadziŵa mmene tingagwilitsile nchito kapepala kamodzi, ndiye kuti tadziŵa tonse. Tumapepalatu ndi tosavuta kutugwilitsila nchito. Woyang’anila nchito wina wa ku Hawaii, U.S.A., analemba kuti: “Sitinadziŵe kuti tumapepala tumenetu tudzakhala tothandiza mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, ndi wa mu mseu.” Iye waona kuti mmene tumapepala tumenetu anatulembela, tumacititsa anthu kukhala ofunitsitsa kukambitsilana. Ndipo zimenezi zimathandiza kukhala ndi makambilano ogwila mtima. Iye waona kuti funso ndi mayankho patsamba loyamba zimathandizanso eninyumba kumasuka poyankha.

9, 10. (a) Tumapepala twauthenga tumatilimbikitsa motani kugwilitsila nchito Baibulo? (b) Ndi tumapepala tuti tumene mwaona kuti ndi tothandiza? Ndipo n’cifukwa ninji?

9 Kapepala kalikonse kamatilimbikitsa kuŵelenga lemba loyenelela. Mwacitsanzo, onani kapepala kakuti Kodi Mavuto Adzathadi? Kaya mwininyumba ayankhe kuti “inde,” “iyai,” kapena “kaya,” tembenukilani patsamba la mkati popanda kufotokoza ciliconse ndipo kambani kuti, “Onani zimene Baibulo limanena.” Kenako ŵelengani Chivumbulutso 21:3, 4.

10 N’cimodzimodzi ndi kapepala kakuti Kodi Baibo Mumaiona Bwanji? Yankho lililonse limene mwininyumba angapeleke pa mayankho atatuwo, tembenukilani patsamba la mkati ndi kukamba kuti, “Baibulo limanena kuti ‘Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.’” Mwina mungakambenso kuti, “Lembali lili ndi zambili.” Ndiyeno tsegulani lemba la 2 Timoteyo 3:16, 17.

11, 12. (a) Tumapepala twauthenga tungathandize motani kuti ulaliki wanu ukhale wokondweletsa? (b) Nanga tungakuthandizeni bwanji kukonzekela maulendo obwelelako?

11 Zimene mwininyumba angayankhe zidzakuthandizani kudziŵa zimene mungaŵelenge ndi kukambilana m’kapepalako. Mulimonse mmene zingakhalile, m’malo mongopatsa anthu tumapepala, ndi bwino kuŵelenga nao Baibulo. Pa ulendo woyamba mungaŵelenge lemba limodzi kapena aŵili. Paulendo wotsatila mungakambilane zoonjezeleka.

12 Pa tsamba lothela lililonse pali kamutu kakuti “Ganizilani Funso Ili.” Pansi pa kamutu kameneka pali funso ndi malemba  amene tingakambilane paulendo wobwelelako. Tikagaŵila kapepala kakuti Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, paulendo wobwelelako tingafunse kuti: “Kodi Mulungu adzasintha bwanji dziko lathu kuti likhale labwino?” Aikapo Mateyu 6:9, 10 ndi Danieli 2:44. Ngati ndi kapepala kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?, tingafunse kuti: “N’cifukwa ciani timakalamba ndi kufa?” Aikapo Genesis 3:17-19 ndi Aroma 5:12.

13. Fotokozani mmene tingagwilitsile nchito tumapepala twauthenga kuti tiyambitse maphunzilo a Baibulo.

13 Tumapepala twauthenga tungatithandize kuyambitsa maphunzilo a Baibulo. Munthu akagwilitsila nchito kacidindo kamene kali patsamba lothela, kadzamtsogolela pa Webusaiti yathu. Ndipo iyo idzam’limbikitsa kuti ayambe kuphunzila Baibulo. Tumapepala tumenetu tumaonetsanso kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wocokela Kwa Mulungu, ndi kusonyeza phunzilo logwilizana ndi nkhani ya m’kapepala kalikonse. Mwacitsanzo, kapepala kakuti, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, kamatsogolela m’phunzilo 5 la m’kabuku kauthenga. Ndipo kapepala kakuti, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, kamatsogolela m’phunzilo 9. Tumapepala tumenetu tunakonzedwa kuti tutithandize kugwilitsila nchito Baibulo paulendo woyamba ndi paulendo wobwelelako. Zimenezi zidzatithandiza kuyambitsa maphunzilo ambili. N’ciani cina cimene tingacite kuti tizigwilitsila nchito bwino Mau a Mulungu mu ulaliki?

KAMBILANANI NDI ANTHU NKHANI IMENE AKUGANIZAPO

14, 15. Citsanzo ca Paulo cingatithandize bwanji pokonzekela ulaliki?

14 Paulo anali wofunitsitsa kudziŵa zimene “anthu oculuka” anali kuganiza mu ulaliki. (Ŵelengani 1 Akorinto 9:19-23.) N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cakuti anali kufuna kuthandiza “anthu onse,” Ayuda ndi anthu ena, kuphunzila coonadi kuti akapulumuke. (Mac. 20:21) Citsanzo ca Paulo cingatithandize bwanji pamene tikonzekela kukalalikila anthu onse a m’gawo lathu?—1 Tim. 2:3, 4.

15 Mwezi uliwonse, maulaliki a citsanzo amapezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Yesani kuwagwilitsila nchito. Koma ngati pali nkhani zina zimene zafala m’gawo lanu, konzani ulaliki wogwila mtima wogwilizana ndi zimene anthu akuganiza. Ganizilani kudela kumene mumakhala, anthu a kumeneko, ndi zimene zimawadetsa nkhawa kwambili. Ndiyeno, sankhani lemba loyenelela. Woyang’anila dela wina anafotokoza kuti iye ndi mkazi wake amagwilitsila nchito Baibulo kwambili. Iye anati: “Anthu ambili m’gawo lathu amatilola kuŵelenga nao lemba limodzi ngati tidzakamba mwacidule ndi mosapita m’mbali. Timatsegulilatu Baibulo lathu, ndiyeno tikapatsana moni timaŵelenga lemba.” M’ndime zotsatila, onani nkhani, mafunso, ndi malemba amene mungagwilitsile nchito m’gawo lanu.

Kodi mumagwilitsila nchito bwino Baibulo ndi tumapepala twauthenga mu ulaliki? (Onani ndime 8-13)

16. Fotokozani mmene tingagwilitsile nchito Yesaya 14:7 mu ulaliki.

16 Ngati mumakhala kudela kumene kaŵilikaŵili kumacitika zinthu zosoŵetsa mtendele, mungafunse munthu kuti: “Mungamve bwanji ngati lelo pa nyuzipepala pali nkhani yaikulu yakuti: ‘Tsopano dziko lonse lili pamtendele, ndipo palibenso msokonezo. Anthu ndi okondwela kwambili.’ Izi ndi zimene Baibulo limakamba pa Yesaya 14:7. Ndipo m’Baibulo muli malonjezo ambili a Mulungu onena za nthawi ya mtsogolo imene padziko padzakhala mtendele.” Ndiyeno m’pempheni kuti muŵelenge naye limodzi la malonjezo amenewo m’Baibulo.

17. Pokambilana ndi anthu, tingaloŵetsemo bwanji lemba la Mateyu 5:3?

17 Kodi amuna ambili a m’gawo lanu amavutika kuti apeze zinthu zofunika paumoyo? Ngati n’conco, mungayambe makambilano  anu mwa kufunsa kuti: “Ndi ndalama zingati zimene mwamuna ayenela kukhala nazo kuti banja lake likhale lacimwemwe?” Munthuyo akayankha mungakambe kuti: “Amuna ambili amapeza ndalama zoposa zimenezo, koma mabanja ao sakhutila nazo. Nanga cofunika makamaka n’ciani?” Ndiyeno ŵelengani Mateyu 5:3 ndi kuyambitsa phunzilo.

18. Potonthoza ena, tingagwilitsile nchito bwanji Yeremiya 29:11?

18 Ngati anthu a m’gawo lanu akuvutika cifukwa ca tsoka lacilengedwe limene linacitika posacedwapa, mungayambe ulaliki wanu mwa kunena kuti: “Nabwela pano kuti titonthozane. (Ŵelengani Yeremiya 29:11.) Kodi mwaziona zinthu zitatu zimene Mulungu afuna kuti tikhale nazo? Iye afuna kuti tikhale ndi ‘mtendele,’ ‘tsogolo labwino,’ ndi ‘ciyembekezo.’ Kodi sizokondweletsa kudziŵa kuti Mulungu afuna kuti tikhale ndi umoyo wabwino? Nanga zimenezo zingatheke bwanji?” Ndiyeno muonetseni phunzilo logwilizana ndi nkhaniyo m’kabuku ka Uthenga Wabwino.

19. Fotokozani mmene tingagwilitsile nchito Chivumbulutso 14:6, 7 pokambilana ndi anthu okonda zacipembedzo.

19 Ngati mumakhala kudela kumene anthu amakonda zacipembedzo, mungayambe makambilano anu mwa kufunsa kuti: “Ngati mngelo akamba ndi inu, kodi mungamvetsele zimene akukuuzani? (Ŵelengani Chivumbulutso 14:6, 7.) Popeza mngelo ameneyu akamba kuti ‘opani Mulungu,’ kodi muganiza kuti akamba za Mulungu uti? Mngelo ameneyu anali kukamba za ‘amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.’ Nanga ndani ameneyu?” Ndiyeno, ŵelengani Salimo 124:8, limene limati: “Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova, Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.” Kenako, m’pempheni kuti mukabwelenso kudzakambilana zoonjezeleka ponena za Yehova Mulungu.

20. (a) Tingagwilitsile nchito motani lemba la Miyambo 30:4 kuphunzitsa munthu za dzina la Mulungu? (b) Kodi pali lemba limene mumagwilitsila nchito limene lakhala ndi zotsatilapo zabwino?

20 Ngati mukambilana ndi wacinyamata, mungayambe makambilano anu mwa njila iyi: “Ndifuna kukuŵelengela lemba limene lili ndi funso lofunika kwambili. (Ŵelengani Miyambo 30:4.) Popeza kuti palibe munthu amene angacite zimenezi, n’zoonekelatu kuti lembali likamba za Mlengi wathu. Kodi dzina lake tingalidziŵe bwanji? Ndingakonde kukuonetsa dzinalo m’Baibulo.”

MUZIGWILITSILA NCHITO KWAMBILI MAU A MULUNGU MU ULALIKI

21, 22. (a) Kodi lemba loyenelela lingasinthe motani umoyo wa munthu? (b) Nanga mwatsimikiza mtima kucita ciani pamene muli mu ulaliki?

21 Simungadziŵe mmene lemba loyenelela lingakhudzile anthu. Mwacitsanzo, Mboni ziŵili za ku Australia zinafika pakhomo la mtsikana wina. Mmodzi wa io anafunsa mtsikanayo kuti, “Kodi dzina la Mulungu ulidziŵa?” Ndiyeno anaŵelenga lemba limodzi la Salimo 83:18. Mtsikanayo anati: “Ndinadabwa kwambili! Mbonizo zitacoka, ndinayendetsa galimoto pa mtunda wa makilomita 56 kupita ku sitolo kogulitsa mabuku acikristu. Ndinali kufuna kuona zimene Mabaibulo ena amakamba pa lembali. Ndinayang’ananso dzina la Mulungu mu dikishonale. Pamene ndinatsimikiza kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndinayamba kuona kuti payenela kuti palinso zinthu zina zimene sindinali kudziŵa.” Patapita nthawi yocepa, iye ndi mwamuna amene anali kudzakwatilana naye anayamba kuphunzila Baibulo. Ndiyeno anabatizika.

22 Mau a Mulungu amasintha anthu amene amawaŵelenga ndi kukhulupilila malonjezo amoyo a Yehova. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.) Uthenga wa m’Baibulo uli ndi mphamvu kuposa ciliconse cimene tingakambe kuti tifike munthu pamtima. Ndiye cifukwa cake, nthawi zonse tiyenela kugwilitsila nchito Mau a Mulungu cifukwa ndi amoyo.