Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumalandila “Cakudya pa Nthawi Yoyenela”?

Kodi Mumalandila “Cakudya pa Nthawi Yoyenela”?

TIKUKHALA m’nthawi yovuta kwambili m’mbili yonse ya anthu. (2 Tim. 3:1-5) Cikondi cathu pa Yehova ndi kufunitsitsa kwathu kutsatila miyezo yake, zimayesedwa tsiku lililonse. Yesu anakambilatu za nthawi yovuta imeneyi, ndipo anatsimikizila otsatila ake kuti adzalandila cilimbikitso kuti akapilile mpaka mapeto. (Mat. 24:3,13; 28:20) Kuti awalimbikitse, iye anaika kapolo wokhulupilika kuti aziwapatsa ‘cakudya ca kuuzimu pa nthawi yoyenela.’—Mat. 24:45, 46.

Kuyambila pamene kapolo wokhulupilika anaikidwa mu 1919, mamiliyoni a “anchito apakhomo” ocokela m’zinenelo zonse abwela m’gulu la Mulungu, ndipo akudyetsedwa mwa kuuzimu. (Mat. 24:14; Chiv. 22:17) Komabe, mabuku athu ena sapezeka m’zinenelo zina, ndipo anthu ena alibe kompyuta kapena intaneti kuti apeze mabuku athu. Mwacitsanzo, ambili alibe mavidiyo ndi nkhani zina zimene zimapezeka cabe pa jw.org. Kodi izi zitanthauza kuti io amamanidwa cakudya copatsa thanzi labwino la kuuzimu? Kuti timvetsetse mfundo imeneyi, tiyeni tiyankhe mafunso anai ofunika kwambili.

 1. Kodi mbali yaikulu ya cakudya cimene Yehova amatipatsa ndi iti?

Pamene Satana anayesa Yesu kuti asandutse miyala kukhala mikate, Yesu anayankha kuti: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mau onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:3, 4) Mau a Yehova ndi olembedwa m’Baibulo. (2 Pet. 1:20, 21) Conco, Baibulo ndilo mbali yaikulu ya cakudya ca kuuzimu.—2 Tim. 3:16, 17.

Gulu la Yehova latulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lathunthu kapena mbali yake m’zinenelo zoposa 120. Ndipo caka ciliconse amalitulutsanso m’zinenelo zina. Mosiyana ndi Baibulo limeneli, palinso mabiliyoni a Mabaibulo ena athunthu kapena mbali yake m’zinenelo zina masauzande. Kupita patsogolo kocititsa cidwi kumeneku ndi kogwilizana ndi cifuno ca Yehova cakuti “anthu kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Popeza “palibe colengedwa cimene [Yehova] sangathe kuciona,” ndife otsimikiza mtima kuti adzakokela ku gulu lake anthu amene “amazindikila zosoŵa zao zauzimu,” ndi kuwapatsa cakudya ca kuuzimu.—Aheb. 4:13; Mat. 5:3, 6; Yoh. 6:44; 10:14.

2. Nanga mabuku athu amatithandiza bwanji kuti tilandile cakudya ca kuuzimu?

Kuti munthu akhale ndi cikhulupililo colimba, ayenela kucita zambili osati kuŵelenga cabe Baibulo. Ayenela kumvetsetsa zimene amaŵelenga ndi kuzigwilitsila nchito. (Yak. 1:22-25) Nduna ya ku Itiyopiya ya m’nthawi ya atumwi inamvetsetsa mfundo imeneyi. Iyo inali kuŵelenga Mau a Mulungu pamene mlaliki Filipo anaifunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuŵelengazo?” Ndunayo inayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulila?” (Mac. 8:26-31) Filipo anacitapo kanthu mwa kuthandiza ndunayo kudziŵa coonadi molondola. Zimene ndunayo inaphunzila zinaifika pamtima cakuti inabatizika. (Mac. 8:32-38) Mofananamo, mabuku athu ofotokoza Baibulo amatithandiza kudziŵa coonadi molondola. Amatifika pamtima ndi kutilimbikitsa kugwilitsila nchito zimene timaphunzila.—Akol. 1:9,10.

Kupitila m’mabuku athu, atumiki a Yehova amalandila zakudya ndi zakumwa za kuuzimu zoculuka. (Yes. 65:13) Mwacitsanzo, Nsanja ya Mlonda yofalitsidwa m’zinenelo zoposa 210, imafotokoza maulosi a m’Baibulo. Imatithandiza kumvetsetsa zinthu zozama za kuuzimu ndi kutithandiza kutsatila mfundo za m’Baibulo paumoyo wathu. Magazini a Galamukani! ofalitsidwa m’zinenelo 100, amatithandiza kudziŵa zambili zokhudza cilengedwe ca Yehova. Amationetsanso mmene tingatsatilile uphungu wothandiza wa m’Baibulo. (Miy. 3:21-23; Aroma 1:20) Kapolo wokhulupilika amafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenelo zoposa 680. Kodi mumapatula nthawi yoŵelenga Baibulo tsiku lililonse? Nanga mumaŵelenga magazini atsopano ndi mabuku onse atsopano amene amafalitsidwa m’cinenelo canu caka ciliconse?

Kuonjezela pa mabuku, gulu la Yehova limakonzanso maautilaini a nkhani ogwilitsila nchito pamisonkhano ya mpingo, yadela, ndi yacigawo. Kodi mumakonda kumvetsela nkhani, maseŵelo, zitsanzo, ndi mbali zofunsa mafunso pamisonkhano imeneyi? Ndithudi, Yehova amatikonzela phwando la kuuzimu.—Yes. 25:6.

 3. Ngati mabuku ena m’cinenelo canu mulibe, kodi zitanthauza kuti muli ndi njala ya kuuzimu?

Yankho ndi lakuti iyai. Ndipo sitiyenela kudabwa kuti nthawi zina atumiki ena a Yehova angakhale ndi cakudya ca kuuzimu coculuka kuposa ena. N’cifukwa ciani zili conco? Ganizilani za atumwi. Iwo analandila malangizo oculuka kuposa ophunzila ambili a m’nthawi ya atumwi. (Maliko 4:10; 9:35-37) Ngakhale n’conco, ophunzila amenewo sanali ndi njala ya kuuzimu. Iwo anapatsidwa zimene anali kufunikila.—Aef. 4:20-24; 1 Pet. 1:8.

Ndi bwino kudziŵanso kuti zinthu zambili zimene Yesu anakamba ndi kucita ali padziko lapansi sizinalembedwe m’ma Uthenga abwino. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Pali zinthu zinanso zambili zimene Yesu anacita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana m’dzikoli.” (Yoh. 21:25) Ngakhale kuti otsatila a Yesu a m’nthawi ya atumwi anali kudziŵa zambili za Yesu, munthu wangwilo kuposa zimene ife tidziŵa, sitili osoŵa kuuzimu. Yehova watiphunzitsa zambili zokhudza Yesu kuti titsatile bwino mapazi ake.—1 Pet. 2:21.

Ganizilaninso za makalata amene atumwi anatumiza ku mipingo m’nthawi ya atumwi. Kalata imodzi yolembedwa ndi Paulo sinalembedwe m’Baibulo. (Akol. 4:16) Kodi tingakambe kuti cakudya cathu ca kuuzimu n’cosakwanila, cabe cifukwa cakuti tilibe kalatayo? Iyai. Yehova adziŵa zimene tifunikila, ndipo watipatsa cakudya cokwanila kuti tikhale olimba kuuzimu.—Mat. 6:8.

Yehova amadziŵa zimene tifunikila, ndipo watipatsa cakudya cokwanila kuti tikhale olimba kuuzimu

Masiku ano, atumiki ena a Yehova ali ndi cakudya ca kuuzimu coculuka kuposa ena. Kodi m’cinenelo canu muli mabuku ocepa cabe? Ngati n’conco, dziŵani kuti Yehova amakudelani nkhawa. Muzigwilitsila nchito mabuku amene alipo m’cinenelo canu, ndipo ngati n’zotheka, muzisonkhana ndi mpingo wa cinenelo cimene mumamvetsetsa. Ndipo khalani ndi cidalilo cakuti Yehova adzakuthandizani kukhala olimba kuuzimu.—Sal. 1:2; Aheb. 10:24, 25.

4. Ngati mulibe intaneti kuti muŵelenge mabuku pa webusaiti ya jw.org, kodi mudzakhala ofooka kuuzimu?

Pa webusaiti yathu, pali magazini ndi mabuku ena ophunzilila Baibulo. Palinso nkhani zothandiza kwa anthu okwatilana, acinyamata, ndi aja ali ndi ana aang’ono. Mabanja amapindula kuphunzila nkhani zimenezi pa Kulambila kwao kwa Pabanja. Ndiponso, amaikapo malipoti a mapulogalamu apadela, monga mwambo wotsiliza maphunzilo a Gileadi ndi miting’i ya pacaka. Kupyolela pa Webusaiti yathu, abale ambili amadziŵa za masoka acilengedwe ndi milandu imene imakhudza anthu Yehova. (1 Pet. 5:8, 9) Webusaiti yathu imathandizanso kwambili kufalitsa uthenga wabwino ngakhale m’maiko mmene nchito yathu ndi yoletsedwa.

Motelo, mungakhalebe olimba kuuzimu kaya muli ndi Intaneti kapena ai. Kapolo wagwila nchito mwakhama kusindikiza mabuku okwanila kuti wanchito wapakhomo aliyense azidya bwino mwa kuuzimu. Conco, simufunika kucita kudzipha kuti mpaka mugule ciwiya coloŵela pa jw.org. Ena angapulinteko nkhani zina pa Webusaiti yathu ndi kupatsako ena amene alibe intaneti, koma mipingo siyenela kucita zimenezi.

Tiyamikila kwambili kuti Yesu wasunga lonjezo lake lakuti adzasamalila zosoŵa zathu za kuuzimu. Pamene masiku otsiliza awa ovuta ali pafupi kutha, tili ndi cidalilo cakuti Yehova adzapitilizabe kutipatsa ‘cakudya ca kuuzimu pa nthawi yoyenela.’