Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Malo a Akazi m’Kakonzedwe ka Yehova

Malo a Akazi m’Kakonzedwe ka Yehova

“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—SAL. 68:11.

1, 2. (a) Ndi mphatso zotani zimene Mulungu anapatsa Adamu? (b) N’cifukwa ciani Mulungu anapangila Adamu mkazi? (Onani cithunzi pamwamba.)

YEHOVA anali ndi colinga polenga dziko lapansi. Iye “analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yes. 45:18) Munthu woyamba kulengedwa Adamu anali wangwilo, ndipo Mulungu anam’patsa malo okhalamo okongola, amene ndi munda wa Edeni. Adamu anali kukondwela kwambili kuyang’ana mitengo yocititsa cidwi, tumadzi tukutsetseleka m’tumitsinje, ndi nyama zikuseŵela. Koma anasoŵeka cinthu cofunika kwambili. Yehova anaonetsa cimene cinasoŵekaco pamene anakamba kuti: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangila womuthandiza, monga mnzake womuyenelela.” Ndiyeno, Mulungu anagoneka Adamu tulo tofa nato, anam’cotsa nthiti imodzi, ndipo ‘anapanga mkazi kucokela kunthiti” imeneyo. Pamene Adamu anauka, anakondwela kwambili ndipo anati, “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga. Ameneyutu adzachedwa Mkazi.”—Gen. 2:18-23.

2 Mkazi anali mphatso ya Adamu yocokela kwa Mulungu, ndipo anali mthandizi wabwino. Mkaziyo anali ndi mphatso yapadela yodzabeleka ana. Ndipo “Adamu anacha mkazi wake dzina lakuti Hava, cifukwa anali kudzakhala mai wa munthu aliyense  wamoyo.” (Gen. 3:20) Mulungu anapatsa anthu aŵili oyamba mphatso yamtengo wapatali. Iwo anali ndi mwai wodzaza dziko lapansi ndi anthu ena angwilo. Mwa kubeleka ana, dziko lapansi linali kudzakhala paladaiso wodzala ndi anthu angwilo, ndipo anali kudzayang’anila zamoyo zonse.—Gen. 1:27, 28.

3. (a) Kuti Adamu ndi Hava adalitsidwe ndi Mulungu, anayenela kucitanji? Nanga n’ciani cinacitika? (b) Tikambilana mafunso ati?

3 Kuti Adamu ndi Hava alandile madalitso amene anawakonzela, anayenela kumvela Yehova ndi kuvomeleza ulamulilo wake. (Gen. 2:15-17) Mwa kucita zimenezi, io akanacita zonse zimene Mulungu anafuna kuti io acite. Komabe, n’zacisoni kuti io anasankha kumvela Satana, “njoka yakale ija,” ndi kucimwila Mulungu. (Chiv. 12:9; Gen. 3:1-6) Kodi kupanduka kumeneku kumawakhudza bwanji akazi? Nanga ndi zinthu ziti zimene akazi okhulupilika akale anacita? N’cifukwa ninji akazi Acikristu amakono anganenedwe kuti ndi “khamu lalikulu”?—Sal. 68:11.

ZOTSATILAPO ZA KUPANDUKA

4. Ndani anaimbidwa mlandu cifukwa ca kucimwa kwa anthu aŵili oyamba?

4 Adamu atafunsidwa cifukwa cimene iye anapandukila anapeleka cifukwa cosamveka, amvekele: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa cipatso ca mtengowo, ndipo ine ndadya.” (Gen. 3:12) Adamu sanavomeleze kucimwa kwake. M’malo mwake, anaimba mlandu mkazi wake ndi Mulungu, Mpatsi wacikondi. Onse aŵili Adamu ndi Hava anacimwa, koma Adamu ndiye anaimbidwa mlandu pa ucimo wao. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo analemba kuti, “ucimo unaloŵela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu].”—Aroma 5:12.

5. N’ciani catsatilapo pamene Mulungu walola kuti anthu adzilamulile kwa kanthawi?

5 Satana ananamiza anthu aŵili oyamba kuti Yehova sanafunikile kuwalamulila. Zimenezi zinadzutsa funso lonena za ulamulilo lakuti: Ndani woyenelela kulamulila? Kuti apeleke yankho, Mulungu walola kuti anthu adzilamulile kwa kanthawi. Iye anadziŵa kuti zocita za anthu zidzaonetsa kuti io alephela kudzilamulila. Kwa zaka zambili, ulamulilo umenewu wabweletsa mavuto adzaoneni kwa anthu. M’zaka za m’ma 1900 zokha, anthu pafupifupi 100 biliyoni anafa pa nkhondo. Ndipo pakati pa anthu amenewa pali amuna, akazi, ndi ana opanda mlandu. Umenewu ndi umboni wokwanila wakuti, “munthu amene akuyenda alibe ulamulilo woongolela mapazi ake.” (Yer. 10:23) Kudziŵa mfundo imeneyi, kudzatithandiza kuvomeleza kuti Yehova ndiye wolamulila wathu.—Ŵelengani Miyambo 3:5, 6.

6. M’maiko ambili, kodi ana aakazi amaonedwa bwanji?

6 M’dziko lino lolamulidwa ndi Satana, amuna ndi akazi akumana ndi mavuto adzaoneni. (Mlal. 8:9; 1 Yoh. 5:19) Nkhanza zoopsa kwambili zacitilidwa makamaka kwa akazi. Padziko lonse lapansi, pafupifupi 30 pelesenti ya akazi amamenyedwa ndi amuna ao, kapena zisumbali zao. M’madela ambili anthu amaikila kumbuyo ana acimuna. Iwo amacita zimenezi cifukwa coganiza kuti anawo akadzakula adzapitiliza ndi dzina la banja, ndi kusamalila makolo okalamba ndi ambuye ao. M’maiko ena, ana aakazi amaonedwa kukhala osafunika, cakuti makolo amataya pathupi pa ana ambili aakazi.

7. Ndi ciyambi cotani cimene Mulungu anapeleka kwa amuna ndi akazi?

7 Ndithudi, Mulungu sakondwela ndi kucitila akazi nkhanza. Iye amacitila akazi mwacilungamo ndipo amawalemekeza. Mmene Yehova amaonela akazi zinaonekela bwino pamene analenga Hava wangwilo. Iye anamulenganso kukhala mthandizi  wabwino wa Adamu osati kapolo. Ndiye cifukwa cake kumapeto kwa tsiku la 6 la kulenga, Mulungu “anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambili.” (Gen. 1:31) Inde, “zonse” zimene Yehova anapanga zinali “zabwino kwambili.” Onse amuna ndi akazi anali ndi ciyambi cabwino.

AKAZI AMENE ANATHANDIZIDWA NDI YEHOVA

8. (a) Fotokozani khalidwe la anthu ambili masiku ano. (b) M’mbili yonse ya anthu, ndani amene Mulungu wathandiza?

8 Pambuyo pa kupanduka kwa mu Edeni, anthu apitilizabe kusamvela Mulungu. M’zaka zaposacedwapa, makhalidwe a anthu aipa kwambili kuposa kale. Baibulo linanenelatu kuti ‘m’masiku otsiliza’ khalidwe la anthu lidzaipa. Makhalidwe oipa afala kwambili, ndipo izi zikuonetsatu kuti ino ndi “nthawi . . . yovuta.” (2 Tim. 3:1-5) M’mbili yonse ya anthu, “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,” wathandiza amuna ndi akazi okhulupilika kwa iye, omvela malamulo ake, ndi amene amagonjela ulamulilo wake.—Ŵelengani Salimo 71:5.

9. Ndi angati amene anapulumuka Cigumula? Nanga n’cifukwa ninji?

9 Pamene Mulungu anaononga dziko la kale la ciwawa m’nthawi ya Nowa mwa kubweletsa Cigumula, ndi anthu ocepa cabe amene anapulumuka. Ngati panthawiyo acibale a Nowa anali ndi moyo, ndiye kuti naonso anaonongeka pa cigumula. (Gen. 5:30) Ciŵelengelo ca akazi amene anapulumuka Cigumula cinali cofanana ndi ca amuna. Amene anapulumuka ndi Nowa, mkazi wake, ana ake atatu, ndi azikazi ao. Iwo anapulumuka cifukwa anali kuopa Mulungu ndipo anacita cifunilo cake. Mabiliyoni a anthu amene alipo ndi moyo masiku ano, ndi mbadwa za anthu 8 aja amene anayanjidwa ndi Yehova.—Gen. 7:7; 1 Pet. 3:20.

10. N’cifukwa ninji Mulungu anathandiza akazi a makolo akale okhulupilika amene anali kuopa Yehova?

10 Papita zaka, Mulungu anathandizanso akazi a makolo akale okhulupilika amene anali kuopa Yehova. Iwo sanadandaule ponena za umoyo wao ndipo Yehova anawadalitsa. (Yuda 16) Mmodzi wa akazi amenewo ndi Sara. Iye sanadandaule pamene io anasiya nyumba yao yabwino ndi kukakhala alendo m’matenti ku dziko lina. M’malo mwake, ‘Sara anali womvela kwa Abulahamu, ndipo anamucha kuti “mbuyanga.”’ (1 Pet. 3:6) Ganizilaninso Rabeka, amene anali mphatso yocokela kwa Yehova ndipo anakhala mkazi wabwino. N’zosadabwitsa kuti mwamuna wake, Isaki, “anam’konda kwambili, ndipo anatonthozedwa pambuyo pa imfa ya mai ake.” (Gen. 24:67) Masiku ano, timayamikila kwambili kukhala ndi akazi oopa Mulungu pakati pathu, amene ali ngati Sara ndi Rabeka!

11. Kodi anamwino aŵili aciheberi anaonetsa bwanji kulimba mtima?

11 Panthawi imene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo, io anaculuka kwambili. Conco, Farao analamula kuti ana onse acimuna aciheberi ayenela kuphedwa akabadwa. Komabe, ganizilani anamwino kapena kuti azamba aciheberi Sifira ndi Puwa, amene mwina anali kutsogolela pa nchito ya unamwino. Cifukwa coopa Yehova, io molimba mtima anakana kupha anawo. Conco, Mulungu anawadalitsa ndipo anakhala ndi mabanja aoao.—Eks. 1:15-21.

12. N’ciani cimene cinali capadela kwa Debora ndi Yaeli?

12 M’nthawi ya oweluza aciisiraeli, mneneli wamkazi Debora anathandizidwa ndi Mulungu. Iye analimbikitsa oweluza Baraki, ndipo anacita mbali yaikulu pothandiza Aisiraeli kuti amasuke kwa adani ao amene anali kuwapondeleza. Debora ananenelatu kuti mkazi osati Baraki, ndiye adzalandila  ulemelelo, cifukwa cogonjetsa Akanani. Adani amenewa anagonjetsedwa pamene Yaeli, mkazi amene sanali waciisiraeli anapha Sisera, mkulu wa gulu la nkhondo la Akanani.—Ower. 4:4-9, 17-22.

13. Baibulo limakamba ciani ponena za Abigayeli?

13 Abigayeli anali mkazi wokhulupilika amene anakhalako m’zaka za m’ma 1000 B.C.E. Iye anali wanzelu, koma mwamuna wake Nabala anali woipa mtima, wacabecabe, ndi wopanda nzelu. (1 Sam. 25:2, 3, 25) Kwa kanthawi Davide ndi anthu ake anateteza katundu wa Nabala. Koma pamene Davide ndi anchito ake anapempha cakudya kwa Nabala, iye ‘anaŵalalatila’ ndipo sanawapatse kalikonse. Zimenezi zinakwiitsa Davide, cakuti anaganiza zokapha Nabala ndi anthu ake. Abigayeli atamva zimenezi, anatenga zakudya ndi zakumwa ndi kupelekela Davide ndi anthu ake. Anacita zimenezi kuti Davide asakhetse magazi. (1 Sam. 25:8-18) Pambuyo pake Davide anauza Abigayeli kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana nane lelo.” (1 Sam. 25:32) Nabala atafa Davide anakwatila Abigayeli.—1 Sam. 25:37-42.

14. Ana aakazi a Salumu anathandiza pa nchito iti? Nanga alongo masiku ano amathandiza pa nchito yofananako iti?

14 Pamene Ababulo anaononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., amuna, akazi, ndi ana ambili anaphedwa. Mpanda wa Yerusalemu unamangidwanso mu 455 B.C.E., motsogozedwa ndi Nehemiya. Ndipo pakati pa anthu amene anathandiza kumanganso mpandawo panali ana a Salumu, kalonga wa hafu ya cigawo ca Yerusalemu. (Neh. 3:12) Iwo anagwila nchito ya pansi imeneyi ndi mtima wonse ngakhale kuti anali ana a kalonga. Masiku ano, timayamikila kwambili alongo ambili amene amadzipeleka ndi mtima wonse kuthandiza pa nchito yomanga yosiyanasiyana.

AKAZI OOPA MULUNGU M’NTHAWI YA YESU

15. Ndi udindo wotani umene Mulungu anapatsa Mariya?

15 N’kutheka kuti Yesu asanabadwe ndiponso m’nthawi yake, Yehova anadalitsa akazi angapo ndi maudindo apadela. Mmodzi wa io anali namwali Mariya. Ali wotomeledwa ndi Yosefe, anapezeka kuti ali ndi pakati mwa mzimu woyela. N’cifukwa ciani Mulungu anam’sankha kukhala mai wa Yesu? Mwacionekele, iye anali ndi makhalidwe a kuuzimu amene akanam’thandiza kulela mwana wake wangwilo kuti akule. Ndithudi, unali mwai waukulu kukhala mai wa munthu wa mkulu amene anakhalapo padziko lapansi.—Mat. 1:18-25.

16. Pelekani citsanzo cimene cionetsa mmene Yesu anali kuonela akazi.

16 Yesu anali wokoma mtima kwa akazi. Mwacitsanzo, ganizilani mkazi amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12. Iye analoŵa m’khamu la anthu, kudzela kumbuyo kwa Yesu ndi kumugwila malaya. M’malo mom’dzudzula, Yesu mokoma mtima anati: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, matenda ako aakuluwo atheletu.”—Maliko 5:25-34.

17. N’cozizwitsa citi cimene cinacitika pa Pentekosite wa mu 33 C.E.?

17 Akazi ena amene anali ophunzila a Yesu anali kutumikila iye ndi atumwi ake. (Luka 8:1-3) Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., amuna ndi akazi pafupifupi 120 analandila mzimu wa Mulungu mwanjila yapadela. (Ŵelengani Machitidwe 2:1-4.) Kutsanulila kwa mzimu kumeneku kunanenedwelatu ndi Yehova m’mau awa: “Ndidzatsanulila mzimu wanga pa camoyo ciliconse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenela. . . . Ndidzatsanulilanso mzimu wanga pa anchito anu aamuna ndi aakazi.” (Yow. 2:28, 29) Cozizwitsa cimeneci ca pa Pentekosite cinaonetsa kuti Mulungu anayanja amuna ndi akazi amenewa, amene anakhala “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 3:28; 6:15, 16)  Pakati pa akazi Acikristu amene anali kulalikila m’nthawi ya atumwi, panali ana aakazi anai a mlaliki Filipo.—Mac. 21:8, 9.

AKAZI NDI “KHAMU LALIKULU”

18, 19. (a) Ponena za kulambila koona, ndi mwai wotani umene Mulungu wapeleka kwa amuna ndi akazi? (b) Nanga wamasalimo amawacha bwanji akazi amene amalengeza uthenga wabwino?

18 Kucokela ca m’ma 1875, amuna ndi akazi ocepa anali ndi cidwi pa kulambila koona. Iwo anali oyamba pa anthu amene anayamba kulengeza mbili yabwino, ndipo anali mbali ya kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Yesu wakuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14.

19 Masiku ano, kagulu kocepa ka Ophunzila Baibulo kakula ndi kukhala Mboni za Yehova zokwanila 8 miliyoni. Mu 2013, anthu oposa 11 miliyoni anaonetsa cidwi mwa kupezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Yesu. M’maiko ambili ciŵelengelo cacikulu ca amenewa ndi akazi. Ndiponso, pa alaliki a Ufumu a nthawi zonse oposa 1 miliyoni padziko lonse ambili ndi akazi. Ndithudi, Mulungu wapeleka mwai kwa akazi okhulupilika wokwanilitsa mau a wamasalimo akuti: “Yehova wapeleka lamulo, ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—Sal. 68:11.

Zoonadi, akazi amene amalengeza uthenga wabwino ndi “khamu lalikulu” (Onani ndime 18, 19)

AKAZI OOPA MULUNGU ADZALANDILA MADALITSO OCULUKA MTSOGOLO

20. Ndi nkhani zotani zimene tingaphunzile?

20 M’nkhani ino, n’zosatheka kukambilana za akazi onse okhulupilika ochulidwa m’Baibulo. Komabe, tonsefe tingaphunzile za io m’Mau a Mulungu ndi m’nkhani zopezeka m’mabuku athu. Mwacitsanzo, tingasinkhesinkhe kukhulupilika kwa Rute. (Rute 1:16, 17) Kuŵelenga buku la m’Baibulo lochedwa ndi dzina la Mfumukazi Esitere ndi nkhani zina za iye, kudzalimbitsa cikhulupililo cathu. Tidzapindula ngati tiphunzila nkhani za conco pa Kulambila kwa Pabanja. Ngati timakhala tokha, tingaphunzile nkhani za conco pa phunzilo laumwini.

21. Kodi akazi okhulupilika aonetsa bwanji kukhulupilika kwao kwa Yehova pa nthawi yovuta?

21 Ndithudi, Yehova amadalitsa nchito yolalikila imene akazi acikristu amacita, ndipo amawathandiza pa nthawi yovuta. Mwacitsanzo, panthawi ya ulamulilo wopondeleza wa Nazi ndi wa cikomyunizimu, Yehova anathandiza akazi okhulupilika kukhalabe okhulupilika kwa iye. Ambili anavutika ndipo ena anaphedwa cifukwa ca kukhulupilika kwao. (Mac. 5:29) Monga kale, masiku ano alongo athu pamodzi ndi alambili onse amacilikiza ulamulilo wa Yehova. Mofanana ndi zimene Yehova anauza Aisiraeli akale, iye awagwila dzanja lamanja ndi kuwauza kuti: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe.”—Yes. 41:10-13.

22. Ndi madalitso otani amene tiyembekezela mtsogolo?

22 Posacedwapa, amuna ndi akazi oopa Mulungu adzasandutsa dziko lapansi kukhala paladaiso. Ndipo adzathandiza anthu mamiliyoni amene adzaukitsidwa kuphunzila za cifunilo ca Yehova. Mpaka nthawi imeneyo, kaya ndife amuna kapena akazi, tiyeni tiziyamikila mwai wathu wotumikila Mulungu “mogwilizana.”—Zef. 3:9.