Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzimvetsela Mau a Yehova Kulikonse Kumene Mungakhale

Muzimvetsela Mau a Yehova Kulikonse Kumene Mungakhale

“Makutu ako adzamva mau kumbuyo kwako, akuti: ‘Njila ndi iyi.’”—YES. 30:21.

1, 2. Kodi Yehova amapeleka motani malangizo kwa atumiki ake?

M’NTHAWI za m’Baibulo, anthu anali kulandila malangizo a Yehova m’njila zosiyanasiyana. Kuti Mulungu avumbulile anthu zimene zinali kudzacitika mtsogolo, anagwilitsila nchito angelo, masomphenya kapena maloto. Yehova anawapatsanso zocita. (Num. 7:89; Ezek. 1:1; Dan. 2:19) Ena analandila malangizo kupyolela mwa anthu oimilako Yehova, amene anali mbali ya gulu lake la padziko lapansi. Anthu a Yehova amene anatsatila malangizo ake anadalitsidwa, mosasamala kanthu za njila imene anawalandilila.

2 Masiku ano, Yehova amapeleka malangizo kwa anthu ake mwa kugwilitsila nchito Baibulo, mzimu woyela, ndi mpingo. (Mac. 9:31; 15:28; 2 Tim. 3:16, 17) Malangizo ocokela kwa iye ndi osavuta kumva cakuti zimakhala ngati ‘makutu athu akumva mau kumbuyo kwathu, akuti: “Njila ndi iyi. Yendani mmenemu.”’ (Yes. 30:21) Tinganene kuti Yesu nayenso amatiuza mau a Yehova potsogolela mpingo kupyolela mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Tiyenela kutsatila kwambili malangizo amenewa cifukwa cakuti moyo wathu wosatha umadalila pa kumvela.—Aheb. 5:9.

3. N’ciani cingatilepheletse kutsatila malangizo a Yehova? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

 3 Satana amadziŵa kuti malangizo a Yehova adzatipulumutsa. Iye amayesetsa kutisokoneza kuti tisawatsatile. Ndiponso, ‘mtima wathu wonyenga’ ungatilepheletse kutsatila malangizo a Yehova. (Yer. 17:9) Conco, tiyeni tikambilane mmene tingakanizile zopinga zimene zingatilepheletse kumvela mau a Mulungu. Tidzakambilananso mmene pemphelo lingatetezele ubale wathu ndi Yehova, mosasamala kanthu za mmene zinthu zili paumoyo wathu.

KANIZANI MACENJELA A SATANA

4. Satana angasokoneze motani maganizo a anthu?

4 Satana amafuna kusokoneza maganizo a anthu mwa kufalitsa mabodza. (Ŵelengani 1 Yohane 5:19.) Mabodza amenewa amafalitsidwa padziko lonse lapansi kupitila m’manyuzipepala, m’mabuku, m’magazini, pa wailesi, pa TV, ndi pa Intaneti. Zinthu zimenezi zingakhale ndi nkhani zothandiza, koma nthawi zambili zimalimbikitsa makhalidwe osemphana ndi miyezo ya Yehova. (Yer. 2:13) Mwacitsanzo, nyuzi ndi mafilimu kapena mapulogalamu a pa TV, zingalimbikitse kukwatilana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Ndipo zimenezi zacititsa anthu ambili kuona kuti Baibulo limakhwimitsa zinthu pankhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.—1 Akor. 6:9, 10.

5. Tingapewe bwanji kusoceletsedwa ndi mabodza a Satana?

5 Kodi anthu okonda miyezo ya Mulungu angapewe bwanji kusoceletsedwa ndi mabodza a Satana? Nanga angasiyanitse bwanji cabwino ndi coipa? Baibulo limayankha kuti: ndi kokha “Mwa kudziyang’anila ndi kucita zinthu mogwilizana ndi mau [a Mulungu].” (Sal. 119:9) Mau a Mulungu ali ndi malangizo ofunika amene angatithandize kusiyanitsa nkhani zoona ndi zabodza. (Miy. 23:23) Yesu anakamba kuti timafunikila “mau onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Tiyenela kuphunzila mmene tingatsatilile mfundo za m’Baibulo paumoyo wathu. Mwacitsanzo, kale kwambili Mose asanalembe lamulo la Yehova loletsa cigololo, Yosefe wacinyamata anadziŵa kuti khalidwe limeneli linali chimo kwa Mulungu. Pamene mkazi wa Potifala anam’nyengelela kuti acite coipa, iye sanafune ngakhale pang’ono kucimwila Yehova. (Ŵelengani Genesis 39:7-9.) Ngakhale kuti mkazi wa Potifala anam’kakamiza kwa nthawi yaitali, Yosefe anasankha kumvela Mau a Yehova osati a mkaziyo. Masiku ano, nafenso tiyenela kumvela Mau a Yehova osati mabodza a Satana.

6, 7. Tingacitenji kuti tipewe malangizo oipa a Satana?

6 Dzikoli ladzala ndi ziphunzitso ndi zikhulupililo zacipembedzo zosokoneza. Zimenezi zacititsa anthu ambili kuganiza kuti kufunafuna cipembedzo coona n’kopanda phindu. Koma ngati tifunitsitsa kumvela Yehova, iye adzatithandiza kupeza coonadi  mosavuta. Motelo, tiyenela kusankha amene tidzamvela. Popeza n’zosatheka kumvetsela mau ocokela kumbali ziŵili panthawi imodzi, tiyenela ‘kudziŵa mau’ a Yesu ndi kumumvela. Iye anasankhidwa ndi Yehova kuti aziyang’anila nkhosa zake.—Ŵelengani Yohane 10:3-5.

7 Yesu anati: “Samalani zimene mukumvazi.” (Maliko 4:24) Malangizo a Yehova ndi osavuta kumva ndipo ndi oyenela. Koma tiyenela kusamala ndi kukonzekeletsa mtima wathu kuti tiziwamvela. Ngati sitisamala tingayambe kumvetsela malangizo oipa a Satana, m’malo momvetsela malangizo acikondi a Mulungu. Tisalole nyimbo za kudziko, mavidiyo, mapulogalamu a pa TV, mabuku, anzathu, aphunzitsi, kapena anthu odzicha akatswili kutsogolela umoyo wathu.—Akol. 2:8.

8. (a) Kodi Satana angagwilitsile nchito bwanji mtima wathu kuti atisoceletse? (b) N’ciani cingaticitikile ngati tinyalanyaza macenjezo?

8 Satana amadziŵa kuti ndi cibadwa cathu kufuna kucita zinthu zoipa, ndipo amafuna kuti tizicita zimenezo. Satana akatilefula zimavuta kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu. (Yoh. 8:44-47) Nanga tingacitenji kuti tisagonje? Ganizilani munthu amene zokhumba zake zim’pangitsa kucita cinthu coipa cimene anali kuona kuti sangacite. (Aroma 7:15) N’ciani cacititsa kuti zinthu zifike pamenepo? Mwacionekele, munthuyo pang’onopang’ono anayamba kunyalanyaza mau a Yehova. Mwina iye analephela kuzindikila macenjezo osonyeza kuti mtima wake wayamba kutengeka, kapena anali kungowanyalanyaza. Mwacitsanzo, zingakhale kuti iye analeka kupemphela, kulalikila, ndi kusonkhana. Ndiyeno, anagonja ku cilakolako ca uchimo ndi kucita cinthu cimene anali kudziŵa kuti n’coipa. Tingapewe kugonjela ku zilakolako zathu ngati nthawi zonse tikhala chelu kuzindikila macenjezo alionse, ndi kucitapo kanthu mwamsanga kuti tiongolele. Ndipo ngati timamvela mau a Yehova, tidzapewa kumvetsela ampatuko.—Miy. 11:9.

9. N’cifukwa ciani kudziŵa mwamsanga zilakolako za uchimo n’kofunika?

9 Munthu akadziŵa mwamsanga matenda amene adwala, zingapulumutse moyo wake. Mofananamo, tingapewe ngozi ngati mwamsanga tadziŵa zilakolako zoipa zimene zingatiloŵetse m’macimo. Tikangodziŵa zilakolako zimenezo, ndi bwino kucitapo kanthu kuti ‘tisagwidwe amoyo ndi [Satana] pofuna kukwanilitsa colinga cake.’ (2 Tim. 2:26) Nanga tingacitenji tikadziŵa kuti talola maganizo athu ndi zokhumba zathu kutengeka ndi kusiyana ndi zimene  Yehova afuna kuti ticite? Tiyenela kubwelela kwa iye mofulumila, kufunafuna citsogozo cake, ndi kucitsatila ndi mtima wonse. (Yes. 44:22) Tisaiŵale kuti kupanga cosankha coipa kungavutitse cikumbumtima cathu kwambili, ngakhale pambuyo pakuti tabwelela kwa Yehova. Conco, ndi bwino kupewa kupatuka kwa Mulungu, mwa kucitapo kanthu mwamsanga kuti tipewe kucita chimo.

Kodi kucita zinthu za kuuzimu nthawi zonse kungatiteteze bwanji ku macenjela a Satana? (Onani ndime 4-9)

PEWANI KUNYADA NDI UMBOMBO

10, 11. (a) Kunyada kumaonekela bwanji? (b) Tiphunzilapo ciani pa citsanzo coipa ca Kora, Datani, ndi Abiramu?

10 Tisaiŵale kuti mtima wathu ungatisoceletse. Zilakolako zathu za ucimo zingakhale zamphamvu kwambili. Mwacitsanzo, kunyada kapena umbombo, zingaticititse kuti ticite chimo lalikulu. Munthu wonyada amadziona kuti ndi wofunika kwambili, ndi kuti angacite ciliconse cimene afuna. Iye amaona kuti palibe aliyense angamuuze zocita, kuphatikizapo Akristu anzake, akulu, ngakhale gulu la Mulungu. Kwa munthu wotelo, mau a Yehova amveka pang’ono.

11 Paulendo wa Aisiraeli wa m’cipululu, Kora, Datani, ndi Abiramu, anapandukila ulamulilo wa Mose ndi Aroni. Cifukwa ca kunyada, apandu amenewo anadzipangila makonzedwe ao olambilila Yehova. Nanga Yehova anacitanji? Iye anawapha onse. (Num. 26:8-10) Nkhani imeneyi ili ndi phunzilo lalikulu kwa ife. Kupandukila Yehova kumatsogolela ku imfa, ndipo tizikumbukilanso kuti “kunyada kumafikitsa munthu ku cionongeko.”—Miy. 16:18; Yes. 13:11.

12, 13. (a) Pelekani citsanzo coonetsa mmene umbombo ungatitsogolele ku ngozi. (b) Fotokozani mmene umbombo ungakulile mofulumila ngati siticitapo kanthu.

12 Umbombo naonso ndi woipa. Munthu waumbombo amacita zinthu mopitilila malile, ndipo amacita kunyanya ndi khalidwe lake. Pambuyo pakuti Namani mkulu wa asilikali wacilitsidwa matenda ake akhate, iye anafuna kupatsa mphatso mneneli Elisa, koma mneneliyo anakana. Komabe, Gehazi, mtumiki wa Elisa, anakhumbila mphatso zimenezi. Mumtima mwake Gehazi anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, ndim’thamangila [Namani] kuti ndikatengeko zinthu zina kwa iye.” Ndiyeno, Gehazi anathamangila Namani mwakabisila, ndi kukamba zabodza kuti apemphe “talente imodzi ya siliva ndi zovala ziŵili.” N’ciani cinacitikila Gehazi cifukwa ca zimene anacita ndi kunama bodza kwa Elisa mneneli wa Yehova? Gehazi waumbombo anakanthidwa ndi khate la Namani.—2 Maf. 5:20-27.

13 Umbombo umayamba pang’onopang’ono, koma ngati siticitapo kanthu, ungakule ndi kuononga moyo wathu. Nkhani ya m’Baibulo ya Akani ionetsa mmene umbombo ungakhalile wamphamvu. Onani mmene umbombo wa Akani unakulila msinkhu. Iye anati: “Nditaona covala camtengo wapatali ca ku Sinara, pakati pa katundu wotsalayo, cokongola m’maonekedwe, komanso masekeli a siliva 200, ndi mtanda umodzi wa golide wolemela masekeli 50, ndinazikhumba zinthuzo, ndipo ndinazitenga.” M’malo mokaniza cikhumbo coipa cimeneco, Akani anaba katunduwo cifukwa ca umbombo ndi kukaubisa m’hema wake. Chimo la Akani litaululika, Yoswa anamuuza kuti Yehova adzam’bweletsela tsoka. Tsiku limenelo Akani ndi banja lake anaponyedwa miyala ndipo anafa. (Yos. 7:11, 21, 24, 25) Umbombo wafala ndipo ungasoceletse aliyense. Ndiye cifukwa cake tiyenela “kukhala maso ndi kucenjela ndi kusilila kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) Ngakhale kuti nthawi zina tingaganizile zinthu zoipa, tiyenela kuongolela maganizo athu kuti zikhumbo zoipa zisatiloŵetse m’chimo.—Ŵelengani Yakobo 1:14, 15.

14. Tingacitenji tikaona kuti tayamba kucita zinthu mosonkhezeledwa ndi kunyada kapena umbombo?

 14 Kunyada ndi umbombo zimatsogolela ku ngozi. Kuganizila zotsatilapo za makhalidwe oipa kudzatithandiza kuti tisalole zilakolako zoipa kutilepheletsa kumva mau a Yehova. (Deut. 32:29) Kupyolela m’Baibulo, Mulungu woona amatiuza za njila yabwino. Amatiuzanso mapindu amene timapeza tikatsatila njilayo, ndi zotsatilapo zake tikatenga njila yoipa. Ngati mtima wathu utilimbikitsa kucita zinthu mosonkhezeledwa ndi kunyada kapena umbombo, n’kwanzelu kuganizila zotsatilapo zake. Tiziganizila mmene colakwaco cidzakhudzila umoyo wathu, okondedwa athu, ndipo makamaka ubale wathu ndi Yehova.

PITILIZANI KULANKHULA NDI YEHOVA

15. Tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Yesu?

15 Yehova amatifunila zabwino. (Sal. 1:1-3) Amapeleka citsogozo pa nthawi imene tikucifuna. (Ŵelengani Aheberi 4:16.) Ngakhale kuti Yesu anali wangwilo, iye nthawi zonse anali kulankhula ndi Yehova m’pemphelo. Yehova anathandiza Yesu ndi kum’tsogolela m’njila zodabwitsa. Anam’tumizila angelo kuti am’tumikile, anapeleka mzimu Woyela kuti um’thandize, ndipo anam’tsogolela posankha atumwi 12. Mau a Yehova anamveka kucokela kumwamba, kuonetsa kuti iye anali kucilikiza Yesu ndi kukondwela naye. (Mat. 3:17; 17:5; Maliko 1:12, 13; Luka 6:12, 13; Yoh. 12:28) Mofanana ndi Yesu, ifenso tiyenela kukhutula mtima wathu kwa Mulungu m’pemphelo. (Sal. 62:7,  8; Aheb. 5:7) Kupyolela m’pemphelo, tingapitilizebe kulankhula ndi Yehova ndi kucita zinthu zom’lemekeza.

16. Kodi Yehova watithandiza bwanji kumvela mau ake?

16 Ngakhale kuti Yehova amapeleka malangizo ake kwa onse, iye sakakamiza munthu kuwatsatila. Tikapempha mzimu wake woyela, ndipo iye adzatipatsa moolowa manja. (Ŵelengani Luka 11:10-13.) Komabe, n’kofunika kuti ‘tizimvetsela mwachelu kwambili.’ (Luka 8:18) Mwacitsanzo, ndi kupanda nzelu kupempha Yehova kuti atithandize kukaniza cilakolako ca ciwelewele, koma kwinaku tikupenyelela zamalisece kapena mafilimu a ciwelewele. Kuti Yehova atithandize, tiyenela kukhala pamalo pamene mzimu wake umapezeka, monga pamisonkhano ya mpingo. Atumiki ambili a Yehova apewa mavuto mwa kumvetsela kwa Yehova pamisonkhano. Izi zawathandiza kuzindikila zilakolako zoipa zimene zingayambe m’mitima yao, ndi kuongolela maganizo amenewo.—Sal. 73:12-17; 143:10.

MUZIMVELA MAU A YEHOVA NTHAWI ZONSE

17. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kudzidalila?

17 Citsanzo ca Davide, Mfumu ya Isiraeli wakale, cili ndi phunzilo lofunika. Iye ali mnyamata, anagonjetsa Goliyati, cimphona cacifilisiti. Davide anadzakhala msilikali ndiyeno pambuyo pake mfumu. Nchito yake inali kuteteza Aisiraeli ndi kuwapangila zosankha zabwino. Koma pamene anadzidalila, mtima wake unam’nyenga ndipo anacita chimo lalikulu ndi Batiseba. Iye anakonzanso ciwembu cakuti Uriya, mwamuna wa Batiseba, aphedwe. Davide atalangidwa, anavomeleza zolakwa zake, ndipo anakhalanso paubale wabwino ndi Yehova.—Sal. 51:4, 6, 10, 11.

18. N’ciani cingatithandize kuti tipitilize kumvetsela mau a Yehova?

18 Tiyenela kutsatila uphungu wa pa 1 Akorinto 10:12 kuti tipewe kudzidalila kwambili. Popeza ‘sitingaongolele mapazi athu,’ tingayambe kutsogoleledwa ndi mau a Yehova kapena mau a Mdani wake. (Yer. 10:23) Conco, ndi bwino nthawi zonse kupemphela, kutsatila citsogozo ca mzimu woyela, ndi kumvela mau a Yehova.