Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

 ZA M’NKHOKWE YATHU

“Seŵelo la Eureka” Linathandiza Ambili Kuphunzila Coonadi

“Seŵelo la Eureka” Linathandiza Ambili Kuphunzila Coonadi

LIU lakuti “Eureka,” limatanthauza “Ndacipeza!” Liu limeneli linali kumveka m’zaka za m’ma 1800 ku California, U.S.A., munthu wogwila nchito ku migodi akapeza golide. Komabe, Charles Taze Russell ndi Ophunzila Baibulo anzake, anapeza cinthu camtengo wapatali kwambili, cimene ndi coonadi ca m’Baibulo. Ndipo io anali ofunitsitsa kuuzako ena coonadi cimeneci.

Pofika m’cilimwe ca mu 1914, anthu mamiliyoni a m’mizinda ikuluikulu anasonkhana kuti apenyelele “Seŵelo la Cilengedwe.” Filimu ya maola 8 imeneyi yofotokoza zinthu zakale, inakonzedwa ndi Ophunzila Baibulo. Ndipo, filimu yozikidwa pa Baibulo inali ndi zithunzi zokongola za mitundumitundu, osimba ogwila mtima, ndi tunyimbo twabwino. Ndipo openyelela anaphunzila zinthu zokhudza cilengedwe, mbili ya anthu, mpaka kudzafika ku mapeto a Ulamulilo wa Yesu Kristu wa Zaka 1000.—Chiv. 20:4. *

Nanga bwanji aja amene anali kukhala m’matauni aang’ono ndi kumidzi? Kuti anthu onse a njala ya coonadi apindule, mu August 1914, Ophunzila Baibulo anatulutsa “Seŵelo la Eureka,” kucokela ku “Seŵelo la Cilengedwe.” Ziwiya za seŵelo limeneli zinali zonyamula m’manja, ndipo linali lopanda zithunzi. Seŵelo limeneli linali ndi mbali zitatu, ndipo mbali iliyonse inali m’zinenelo zingapo. Seŵelo la “Eureka X” linali ndi mau onse a wosimba ndi tunyimbo twabwino. Koma seŵelo la “Eureka Y” linali ndi nkhani zonse zojambula ndi zithunzi zokongola. Ndipo “Seŵelo la Eureka la Banja,” lopenyelela ku nyumba, linali ndi mau ocepa a wosimba ndi tunyimbo. Ziwiya zoonetsela mafilimu zochipa zinali kupezeka ndi Ophunzila Baibulo.

Anali kugwilitsila nchito pulojekita poonetsa zithunzi za mitundumitundu

Popanda pulojekita yoonetsela filimu kapena cinsalu cacikulu ca pacipupa, Ophunzila Baibulo anali kugwilitsila nchito seŵelo la mau okha limeneli kwaulele kuti afalitse uthenga wa Ufumu m’midzi ndi m’magawo atsopano. Seŵelo la “Eureka X” la mau okha linali kuulutsidwa masana kapena usiku. Ndipo pulojekita ya seŵelo la “Eureka Y” sinali kugwilitsila nchito malaiti, koma toci. Lipoti lina la mu Nsanja ya Mlonda ya ku Finland inati: “Timaonetsa zithunzi zimenezi kulikonse.” Zimenezo zinali zoona!

M’malo mocita lendi maholo aakulu, nthawi zambili Ophunzila Baibulo anali kupeza malo aulele monga makalasi a pa sukulu, maholo a kumakhoti, masitesheni a sitima, ndi zipinda zocitilamo maseŵela za m’ma nyumba aakulu. Nthawi zambili filimu imeneyi anali  kuionetsela panja, pa cinsalu cacikulu coyela cokoloŵeka pa nkhokwe. Anthony Hambuch analemba kuti: “Alimi anakonza bwalo m’munda wa zipatso ndi kupanga mabenchi a mitengo kuti anthu azisangalala ndi filimuyo.” Pa maulendo ao, a gulu loonetsa seŵelo la “Eureka,” anali kugwilitsila nchito ngolo yokokedwa ndi mahosi yonyamulila katundu wao wonse.

Openyelela seŵelo la “Eureka” anali kuyambila pa anthu ocepa mpaka m’mahandiledi. M’tauni ina ya anthu 150, ku United States, anthu 400 anapenyelela seŵelo pasukulu ina panthawi zosiyanasiyana. Kumalo ena, anthu ena anayenda mtunda wa makilomita 8 kuti akapenyelele “Seŵelo la Eureka.” Ku Sweden, aneba a mlongo Charlotte Ahlberg amene anasonkhana m’nyumba yake yaing’ono “anakhudzika mtima kwambili” atamva seŵelo la mau limeneli. M’tauni ina ya kumigodi ku Australia, anthu 1,500 anapenyelela filimu imeneyi. Lipoti lina mu Nsanja ya Mlonda linati, m’masukulu a sekondale ndi m’makoleji, “aphunzitsi ndi ana a sukulu anacita cidwi ndi zithunzithunzi ndi malekodi puleya athu okondweletsa. “Seŵelo la Eureka” linafala ngakhale m’nyumba zoonetsela mafilimu.

KULIMILILA MBEU ZA COONADI

“Seŵelo la Eureka,” linakhala ciwiya cothandiza kwambili cimene Ophunzila Baibulo anali kugwilitsila nchito pophunzitsa anthu kuti anthuwo akaphunzitsenso ena atsopano. Sitingachule kuti ndi anthu angati amene anapenyelela “Seŵelo la Eureka.” Ndipo maseŵelo amenewa anali kuonetsedwa mobwelezabweleza. Komabe, mu 1915 pa magulu 86 amene anakhazikitsidwa, magulu 14 ndi amene anali kuonetsa seŵelo limeneli nthawi zonse. Ngakhale kuti ciŵelengelo ca anthu amene anapenyelela seŵeloli sicidziŵika bwinobwino, lipoti la kumapeto kwa cakaco linaonetsa kuti anthu oposa 1 miliyoni analipenyelela. Ndipo anthu 30 sauzande anapempha mabuku ofotokoza Baibulo.

Ngakhale kuti mwina “Seŵelo la Eureka” silikumbukika kwambili, anthu mamiliyoni analipenyelela kuyambila ku Australia mpaka ku Argentina, ku South Africa mpaka ku zilumba za ku Britain, ku India, ndi ku Caribbean. Pakati pa anthu amenewa, ambili anaphunzila coonadi, cimene ndi camtengo wapatali kwambili kuposa golide, cakuti anali kufuula kuti “Eureka!”

^ par. 4 Onani nkhani yakuti, “Kale Lathu—Padutsa Zaka 100 Tsopano” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2014, masamba 30-32.