Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Yehova Amayandikila kwa Ife

Mmene Yehova Amayandikila kwa Ife

Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.—YAK. 4:8.

1. Munthu aliyense amafuna ciani? Nanga ndi anthu ati amene tingakhale nao paubwenzi?

MWACIBADWA munthu aliyense amafuna kukhala paubwenzi ndi ena. Anthu amakhala “paubwenzi ngati amakondana kwambili ndi kudziŵana bwino.” Tonse timamvela bwino kukhala paubwenzi ndi banja lathu ndi anzathu amene amatikonda, amatiyamikila, ndi kutidziŵa bwino. Komabe, Munthu amene tiyenela kukhala naye paubale wolimba kuposa onse ndi Mlengi wathu Wamkulu.—Mlal. 12:1.

2. N’ciani cimene Yehova watilonjeza? Nanga n’cifukwa ciani anthu ambili sakhulupilila lonjezo limeneli?

2 Kupyolela m’Mau ake, Yehova amatilimbikitsa ‘kumuyandikila,’ ndipo amatilonjeza kuti tikatelo, ‘iyenso adzatiyandikila.’ (Yak. 4:8) Zimenezi n’zolimbikitsa kwambili. Koma anthu ena amaona kuti n’zosatheka kuti Mulungu angafune kuti awayandikile. Iwo amaona kuti ndi osayenelela kumuyandikila kapena kuti iye ali kutali kwambili. Kodi n’zothekadi kuyandikila Yehova?

3. Tiyenela kudziŵa ciani ponena za Yehova?

3 Zoona n’zakuti, Yehova “sali kutali ndi aliyense” amene amam’funafuna. Conco, n’zotheka kum’dziŵa. (Machitidwe 17: 26, 27; Salimo 145:18.) Mulungu ndi wokonzeka ndipo ndi wofunitsitsa kutiyanja monga anzake apamtima, ngakhale kuti ndife opanda ungwilo. (Yes. 41:8; 55:6) Cifukwa ca zimene zinam’citikila wamasalimo, iye anati ponena za Yehova: “Inu Wakumva pemphelo, anthu a mitundu yonse adzabwela kwa inu. Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu.” (Sal. 65:2, 4) Tsopano, tiyeni tione nkhani ya m’Baibulo imene ionetsa mmene Mfumu Asa wa ku Yuda anayandikilila Mulungu, ndi mmene Mulungu anamuyandikilila. *

TSATILANI CITSANZO CA MUNTHU WAKALE

4. Ndi citsanzo cotani cimene Asa anapeleka kwa anthu a ku Yuda?

4 Mfumu Asa anaonetsa cangu kwambili pakulambila koona pamene anacotsa mahule a pakacisi. Ndipo anathetsa kulambila mafano kumene kunali kofala m’dzikolo. (1 Maf. 15:9-13) Iye analimbikitsa anthu kuti “afunefune Yehova Mulungu wa makolo ao ndi kutsatila cilamulo.” Yehova anadalitsa zaka 10 zoyambilila za ulamulilo wa Asa mwa kum’patsa mtendele woculuka. Kodi Asa anazindikila kumene mtendele umenewo unacokela? Iye anauza anthu kuti: “Malo m’dzikoli akadalipo cifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu. Tam’funafuna ndipo watipatsa mpumulo pakati pa adani athu onse otizungulila.” (2 Mbiri 14:1-7) Tiyeni tione zimene zinatsatilapo.

5. N’cocitika citi cimene cionetsa kuti Asa anali kudalila Mulungu? Nanga panali zotsatilapo zotani?

5 Yelekezelani kuti ndinu Asa. Ndipo Zera Mwitiyopiya ndi gulu lankhondo la asilikali 1 miliyoni ndi magaleta 300 wabwela kudzamenyana ndi Yuda. (2 Mbiri 14:8-10) Kodi mungacite bwanji mukaona gulu lalikulu limenelo likuloŵa mu ufumu wanu? Ndipo gulu lanu lili cabe ndi asilikali 580 sauzande, kutanthauza kuti ndinu ocepa kuwilikiza kaŵili poyelekezela ndi adani anu. Kodi mungafunse kuti n’cifukwa ciani Mulungu walola zimenezo kucitika? Zotelo zikacitika, kodi mungadalile mphamvu zanu? Zimene Asa anacita zionetsa kuti iye anali paubale wolimba ndi wodalilika ndi Yehova. Iye anapemphela mocokela pansi pamtima kuti: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambili kapena ndi opanda mphamvu. Tithandizeni Yehova Mulungu wathu cifukwa tikudalila inu, ndipo tabwela m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.” Nanga Mulungu analiyankha bwanji pempho la Asa? “Yehova anagonjetsa Aitiyopiyawo.” Palibe mdani aliyense anapulumuka nkhondo imeneyo.—2 Mbiri 14:11-13.

6. Tingatsatile motani citsanzo ca Asa?

6 N’ciani cinathandiza Asa kudalila kwambili citsogozo ndi citetezo ca Mulungu? Baibulo limati, “Asa anacita zabwino pamaso pa Yehova” ndi kuti “anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 15:11, 14) Ifenso, tiyenela kutumikila Mulungu ndi mtima wathunthu kuti tikhale paubale wolimba ndi iye, tsopano ndi mtsogolo. Ndife oyamikila kuti Yehova watikokela kwa iye ndi kutithandiza kupanga ubale wolimba ndi kupitilizabe kukhala paubale umenewo ndi iye. Onani njila ziŵili mmene Yehova wacitila zimenezo.

YEHOVA WATIKOKA KUPYOLELA MU DIPO

7. (a) N’ciani cimene Yehova wacita cimene cimatikokela kwa iye? (b) Ndi njila yaikulu iti imene Yehova amatikokela kwa iye?

7 Yehova anaonetsa kuti amakonda  anthu pamene analenga dziko lathu lapansi lokongola. Iye wapitilizabe kuonetsa kuti amatikonda mwa kutipatsa zinthu zabwino zocilikiza moyo. (Mac. 17:28; Chiv. 4:11) Kuposa zonse, Yehova amatisamalila mwa kuuzimu. (Luka 12:42) Ndiponso, amatitsimikizila kuti amamva pamene tipemphela kwa iye. (1 Yoh. 5:14) Komabe, njila yaikulu imene Mulungu amatikokela kwa iye ndi kupyolela mu dipo. (Ŵelengani 1 Yohane 4:9, 10, 19.) Yehova anatuma “Mwana wake wobadwa yekha” padziko lapansi kudzatimasula ku ucimo ndi imfa.—Yoh. 3:16.

8, 9. Kodi Yesu ali ndi mbali yotani pa kukwanilitsa cifunilo ca Yehova?

8 Yehova afuna kuti anthu onse apindule ndi dipo, kuphatikizapo aja amene anakhala ndi moyo dipo lisanalipilidwe. Kucokela pamene Yehova analosela za Mpulumutsi wa anthu, kwa Mulungu zinali monga kuti dipo limenelo lalipilidwa kale. Mulungu anadziŵa kuti cifunilo cake sicidzalephela. (Gen. 3:15) Patapita zaka zambili, mtumwi Paulo anayamikila Mulungu cifukwa ‘cotimasula ndi dipo lolipilidwa ndi Kristu Yesu.’ Paulo anaonjezela kuti: “Mulungu anacita izi pofuna kuonetsa cilungamo cake pokhululuka macimo amene anacitika kale.” (Aroma 3:21-26) Ndithudi, Yesu wacita mbali yaikulu potithandiza kuyandikila Mulungu.

9 Anthu odzicepetsa angadziŵe Yehova ndi kukhala naye paubale wathithithi kokha kupyolela mwa Yesu. Kodi Malemba amavomeleza motani mfundo imeneyi? Paulo analemba kuti, “Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Kristu anatifela.” (Aroma 5:6-8) Dipo la nsembe ya Yesu linalipilidwa, osati cifukwa cakuti ndife oliyenelela iyai, koma cifukwa cakuti ndife okondedwa. Yesu anati: “Palibe munthu angabwele kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine, ndipo ine ndidzamuukitsa tsiku lomaliza.” Ndipo panthawi ina anati, “Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yoh. 6:44; 14:6) Motelo, Yehova amakoka anthu kupyolela mwa Yesu, ndipo amawathandiza kukhalabe m’cikondi cake kuti akalandile moyo wosatha. Amagwilitsila nchito mzimu wake woyela kucita zimenezi. (Ŵelengani Yuda 20, 21.) Onaninso njila ina imene Yehova amatikokela kwa iye.

YEHOVA WATIKOKA KUPYOLELA M’MAU AKE

10. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kuyandikila Mulungu?

10 Pofika pano, m’nkhani ino tagwilitsila nchito malemba amene agwidwa mau kapena osagwidwa mau ocokela m’mabuku 14 a m’Baibulo. Kodi popanda Baibulo tikanadziŵa bwanji kuti tifunika kuyandikila Mlengi wathu? Nanga tikanadziŵa bwanji za dipo ndi kuti Yehova amatikoka kupyolela mwa Yesu? Mwa kugwilitsila nchito mzimu wake, Yehova analemba Baibulo limene limatiuza makhalidwe ake abwino ndi cifunilo cake. Mwacitsanzo, pa Ekisodo 34:6, 7, Yehova anauza Mose kuti iye ndi “Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo.” Ndani sangafune kuyandikila munthu wotelo? Yehova adziŵa kuti tikapitiliza kuphunzila za iye m’Baibulo, iye adzakhala weniweni kwa ife, ndipo tidzamuyandikila kwambili.

11. N’cifukwa ciani tiyenela kuphunzila makhalidwe a Mulungu ndi njila zake? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 Pofotokoza mmene tingayandikilile Mulungu, mau oyamba m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova amati: “Pa ubwenzi uliwonse umene timapanga, timagwilizana  ndi munthuyo cifukwa cakuti timamudziŵa, ndiponso kuti ali ndi khalidwe lapadela limene timalisilila ndi kuliona kukhala labwino zedi. Motelo makhalidwe a Mulungu ndiponso kacitidwe kake ka zinthu, monga zasonyezedwela m’Baibulo, ndi nkhani yofunika kwambili kuiphunzila.” Conco, ndife oyamikila kwambili kuti Yehova analemba Baibulo mwa njila yosavuta kuimvetsetsa.

12. N’cifukwa ninji Yehova anagwilitsila nchito anthu kulemba Baibulo?

12 Yehova akanagwilitsila nchito angelo kulemba Baibulo. Angelo amenewo amadela nkhawa za ife ndi zocita zathu. (1 Pet. 1:12) N’zoona kuti io akanalemba uthenga wa Mulungu wopita kwa anthu, koma angelowo saona zinthu monga mmene anthu amazionela. Iwo sadziŵa mmene anthu amamvelela, zimene amasoŵa, ndi zofooka zao. Yehova adziŵa kuti angelo ndi osiyana kwambili ndi anthu, motelo anasankha anthu kuti alembe Baibulo. Ife anthu timamvetsetsa mmene olemba Baibulo ndi ena ochulidwa m’Malemba anali kumvelela. Timamvetsetsa mmene anali kumvelela akakhumudwa, akacita mantha ndiponso akalakwitsa zinthu. Ndipo timamvetsetsa cimwemwe cao pamene zinthu zinawayendela bwino. Mofanana ndi Eliya, onse olemba Baibulo anali ‘anthu monga ife.’—Yak. 5:17.

Mmene Yehova anacitila zinthu ndi Yona ndi Petulo zimatithandiza motani kumuyandikila kwambili? (Onani ndime 13, 15)

13. Kodi pemphelo la Yona litiphunzititsa ciani?

13 Mwacitsanzo, kodi mngelo akanalemba bwinobwino mmene Yona anamvelela pamene anathaŵa nchito yake yopatsidwa ndi Mulungu? Conco, ndi bwino kuti Yehova analola Yona kulemba yekha nkhani yake, kuphatikizapo pemphelo lake kwa Mulungu pamene anali pansi pa nyanja. Yona anati: “Pamene ndinalefuka kwambili, ndinakumbukila Yehova.”—Yona 1:3, 10; 2:1-9.

14. N’cifukwa ciani timamvetsetsa zimene Yesaya analemba za iye mwini?

 14 Ganizilani zimene Yehova anauza Yesaya kulemba za iye mwini. Pambuyo poona masomphenya a ulemelelo wa Mulungu, mneneliyu anakamba za kupanda ungwilo kwake kuti: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu. Nditsikila kuli cete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa, ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.” (Yes. 6:5) Sizikanatheka kuti mngelo akambe mau amenewa. Koma zinali zotheka kwa Yesaya ndipo timvetsetsa mmene iye anamvelela.

15, 16. (a) N’cifukwa ciani timamvetsetsa mmene ena amamvelela? Pelekani zitsanzo. (b) N’ciani cingatithandize kumuyandikila Yehova?

15 Kodi angelo akanakamba kuti anali ‘osayenelela’ monga mmene Yakobo anakambila? Kapena kodi akanazimva ‘ocimwa’ monga mmene Petulo anamvelela? (Gen. 32:10; Luka 5:8) Nanga akanacita “mantha” monga mmene ophunzila a Yesu anacitila? Kapena kodi angelo olungama akanafunika ‘kulimba mtima’ polalikila uthenga wabwino uku akutsutsidwa monga mmene Paulo ndi ena anacitila? (Yoh. 6:19; 1 Ates. 2:2) Iyai. Angelo ndi apamwamba kwambili kuposa anthu. Anthu opanda ungwilo akakamba zinthu zotelo, timamvetsetsa mmene amvelela, cifukwa ifenso ndife anthu monga io. Tikamaŵelenga zimene io analemba, ‘timasangalala ndi anthu amene akusangalala, ndipo timalila ndi anthu amene akulila.’—Aroma 12:15.

16 Ngati tisinkhasinkha zimene Baibulo limanena ponena za mmene Yehova anacitila ndi atumiki ake okhulupilika akale, tidzaphunzila zinthu zambili zabwino za Mulungu. Iye moleza mtima ndi mwacikondi, amayandikila anthu opanda ungwilo. Tikam’dziŵa bwino Yehova ndi kum’konda kwambili, tidzayandikila kwa iye.—Ŵelengani Salimo 25:14.

PANGANI UBALE WOSADUKA NDI MULUNGU

17. (a) Ndi uphungu wabwino uti umene Azariya anapatsa Asa? (b) Ndipo Asa anaunyalanyaza motani? Nanga panali zotsatilapo zotani?

17 Pambuyo pakuti Mfumu Asa wagonjetsa gulu la nkhondo la Aitiyopiya, mneneli wa Mulungu, Azariya anapatsa Asa ndi anthu ake uphungu wothandiza. Azariya anati: “Yehova akhala nanu inuyo mukapitiliza kukhala naye. Mukamufunafuna iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.” (2 Mbiri 15:1, 2) Koma patapita zaka, Asa analephela kutsatila uphungu wabwino umenewo. Pamene Asa anaopsezedwa ndi ufumu wa Isiraeli wakumpoto, iye anapempha thandizo kwa a Siriya. M’malo mopemphanso thandizo kwa Yehova, iye anacita pangano ndi mitundu yakunja. Mpake kuti Asa anauzidwa kuti: “Mwacita zopusa pankhani imeneyi, cifukwa kuyambila tsopano anthu azicita nanu nkhondo.” Zaka zothela za ulamulilo wa Asa zinali za nkhondo zokhazokha. (2 Mbiri 16:1-9) Tiphunzilapo ciani pamenepa?

18, 19. (a) Kodi tiyenela kucita ciani tikayamba kutalikilana ndi Mulungu? (b) Nanga tingayandikile bwanji kwa Yehova?

18 Sitiyenela kutalikilana ndi Yehova. Tikayamba kutelo, mwamsanga tiyenela kucita mogwilizana ndi lemba la Hoseya 12:6, limene limati: “Ubwelele kwa Mulungu wako. Usonyeze kukoma mtima kosatha ndi cilungamo ndipo nthawi zonse uziyembekezela Mulungu wako.” Cotelo, tiyeni tiyandikile kwambili Yehova mwa kusinkhasinkha phindu la dipo ndi kuphunzila mwakhama Mau ake, Baibulo.—Ŵelengani Deuteronomo 13:4.

19 Wamasalimo analemba kuti: “Kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.” (Sal. 73:28) Tiyeni tonse tipitilizebe kuphunzila zinthu zatsopano za Yehova. Tikacita zimenezo tidzam’konda kwambili. Ndipo tikayandikila Yehova nayenso adzatiyandikila, tsopano ndi kwamuyaya!

^ par. 3 Onani nkhani ya Asa yamutu wakuti, “Mudzapeza Mphoto Cifukwa ca Nchito Yanu,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2012.