Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Yesu anauza Asaduki kuti anthu amene adzaukitsidwa “sadzakwatila kapena kukwatiwa.” (Luka 20:34-36) Kodi anali kukamba za ciukililo ca padziko lapansi?

Funso limeneli n’lofunika kwambili, makamaka kwa aja amene anataikilidwa anzao a m’cikwati. Anthu aconco amalakalaka kuti akayanjanenso ndi anzao a m’cikwati akadzaukitsidwa m’dziko latsopano. Mwamuna wina wofedwa anati: “Ine ndi mkazi wanga sitinafune kuti cikwati cathu cithe. Cinali colinga cathu kupitilizabe kulambila Mulungu mogwilizana kwamuyaya, ndipo mpaka pano maganizo anga sanasinthe.” Kodi pali cifukwa cokhalila ndi ciyembekezo cakuti aja amene adzaukitsidwa adzakwatila kapena kukwatiwa? Kunena mwacidule, yankho ndi lakuti sitidziŵa.

Kwa zaka zambili, mabuku athu afotokoza kuti zimene Yesu anakamba ponena za cikwati pambuyo pa ciukililo, zimatanthauza ciukililo ca padziko lapansi. Ndipo kuti aja amene adzaukitsidwa kukhala ndi moyo m’dziko latsopano sadzakwatila kapena kukwatiwa. * (Mat. 22:29, 30; Maliko 12:24, 25; Luka 20:34-36) Ngakhale kuti sitingakambe motsimikiza, kodi n’zotheka kuti Yesu anali kukamba za ciukililo ca kumwamba? Tiyeni tione zimene Yesu anakamba.

Tiyeni tione zimene zinacititsa kuti Yesu akambe mau amenewa. (Ŵelengani Luka 20:27-33.) Asaduki, amene sanali kukhulupilila ciukililo, pofuna kutapa m’kamwa Yesu anam’funsa za ciukililo ndi za cikwati ca pacilamu. * Yesu anawayankha kuti: “Ana a m’nthawi ino amakwatila ndi kukwatiwa. Koma amene ayesedwa oyenelela kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo ndi kudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatila kapena kukwatiwa. Ndiponso io sadzafanso, cifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu mwa kukhala ana a kuuka kwa akufa.”—Luka 20:34-36.

N’cifukwa ninji mabuku athu akhala akufotokoza kuti mwina Yesu anali kukamba za ciukililo ca padziko lapansi? Mfundo imeneyo yazikidwa pa mbali ziŵili. Mbali yoyamba, zioneka kuti Asaduki pom’funsa anali kuganiza za ciukililo ca padziko lapansi, ndi kuti Yesu anawayankha moyenelela. Yaciŵili, popeleka yankho lake, Yesu anachula Abulahamu, Isaki, ndi Yakobo, amene anali makolo okhulupilika amene adzaukitsidwa kudzakhala ndi moyo padziko lapansi.—Luka 20:37, 38.

Komabe, zioneka kuti Yesu anali kukamba za ciukililo ca kumwamba. N’cifukwa ninji tikamba conco? Tiyeni tikambilane mfundo zazikulu ziŵili.

“Amene ayesedwa oyenelela . . . kudzaukitsidwa kwa akufa.” Odzozedwa okhulupilika ndi “oyenelela Ufumu wa Mulungu.” (2 Ates. 1:5, 11) Iwo ayesedwa olungama kuti akhale ndi moyo cifukwa ca dipo. Conco, io sadzafa cifukwa ca uchimo. (Aroma 5:1, 18; 8:1) Amenewa amachedwa ‘odala ndi oyela,’ ndipo ndi oyenelela ciukililo ca kumwamba. (Chiv. 20:5, 6) Komabe, amene adzaukitsidwa kuti adzakhale ndi moyo padziko lapansi adzaphatikizapo “osalungama.” (Mac. 24:15) Kodi tingakambe kuti io “ayesedwa oyenelela” kudzaukitsidwa?

 “Iwo sadzafanso.” Odzozedwa amene amatsiliza moyo wao wa padziko lapansi mokhulupilika, amaukitsidwa kupita kumwamba ndi kupatsidwa moyo wosafa. (1 Akor. 15:53, 54) Imfa sidzakhalanso ndi mphamvu kwa aja amene adzaukitsidwa ku moyo wa kumwamba. *

Malinga ndi zimene tafotokoza, kodi tinganenenji? N’zotheka kuti mau a Yesu onena za cikwati pambuyo pa ciukililo, amakamba za ciukililo ca kumwamba. Ngati n’conco, ndiye kuti mau ake akutiuza zinthu zingapo ponena za amene adzaukitsidwa ku moyo wa kumwamba. Iwo sadzakwatila kapena kukwatiwa, ndipo sadzafa. Ndiyeno mwanjila ina, io adzakhala monga angelo, amene ndi zolengedwa zauzimu zimene zimakhala kumwamba. Komabe, mfundo imeneyi iutsa mafunso ena.

Funso loyamba n’lakuti, n’cifukwa ninji Yesu ananena za ciukililo ca kumwamba poyankha Asaduki, amene mwina anali kuganiza za ciukililo ca padziko lapansi? Nthawi zambili, Yesu sanali kuyankha om’tsutsa malinga ndi zimene io anali kuganiza. Mwacitsanzo, kwa Ayuda amene anali kufuna kuti awaonetse cizindikilo, iye anawauza kuti: “Gwetsani kacisi uyu, ndipo ine ndidzamumanga m’masiku atatu.” Mwacionekele Yesu anadziŵa kuti io anali kuganiza za kacisi weniweni, “komatu iye anali kunena za kacisi wa thupi lake.” (Yoh. 2:18-21) Mwina, Yesu anaona kuti n’kosafunika kuyankha Asadukiwo acinyengo, amene sanali kukhulupilila ciukililo kapena kukhalapo kwa angelo. (Miy. 23:9; Mat. 7:6; Mac. 23:8) M’malo mwake, anachula za ciukililo ca kumwamba kuti ophunzila ake oona mtima apindule. Ophunzila ake amenewa anali kudzalandila ciukililo cimeneci mtsogolo.

Funso laciŵili n’lakuti, n’cifukwa ninji Yesu anatsiliza makambilano ake mwa kuchula Abulahamu, Isaki, ndi Yakobo amene adzaukitsidwa padziko lapansi? (Ŵelengani Mateyu 22:31, 32.) Onani kuti Yesu poyankha anayamba ndi kufotokoza za makolo akale amenewo ndi mau akuti, “kunena za kuuka kwa akufa.” Mau amenewa aonetsa kuti Yesu anasintha nkhani. Ndiyeno, pogwila mau olembedwa ndi Mose, amene Asaduki anali kunena kuti anali kukhulupilila, Yesu anagwilitsila nchito mau amene Yehova anauza Mose pa citsamba coyaka moto. Mau amenewa anapeleka umboni woonjezeleka wakuti ciukililo ca padziko lapansi cidzacitikadi.—Eks. 3:1-6.

Funso lacitatu n’lakuti, ngati mau a Yesu onena za cikwati pambuyo pa ciukililo akamba za ciukililo ca kumwamba, kodi zimenezi zitanthauza kuti aja amene adzaukitsidwa padziko lapansi adzayamba kukwatila? Mau a Mulungu sapeleka yankho lacindunji pa funso limeneli. Ngati Yesu anali kukamba za ciukililo ca kumwamba, ndiye kuti mau ake safotokoza kaya ngati anthu amene adzaukitsidwa padziko lapansi adzayamba kukwatila kapena kukwatiwa m’dziko latsopano.

Pakali pano, zimene tidziŵa n’zakuti Mau a Mulungu amanena kuti imfa ndiyo mapeto a cikwati. Motelo, wofedwa kapena wofeledwa sayenela kudziimba mlandu ngati wasankha kukwatilanso kapena kukwatiwanso. Ici ndi cosankha caumwini, ndipo sitiyenela kuneneza munthu amene wasankha kupezanso mnzake wina wa m’cikwati womuyenelela.—Aroma 7:2, 3; 1 Akor. 7:39.

N’zomveka kuti tingakhale ndi mafunso ambili ponena za moyo m’dziko latsopano. M’malo mongoganizila mayankho a mafunsowo, ndi bwino kuyembekeza kuti tikaone mmene zidzakhalila. Koma ndife otsimikiza kuti: Anthu omvela adzakhala ndi cimwemwe, cifukwa Yehova adzakhutilitsa zosoŵa ndi zokhumba zao zonse m’njila yabwino koposa.—Sal. 145:16.

^ par. 4 Onani Nsanja ya Olonda yacingelezi ya June 1, 1987, masamba 30-31.

^ par. 5 M’nthawi za m’Baibulo, cikwati ca pacilamu, kapena kuloŵa cokolo, unali mwambo wakuti mwamuna akwatile mkazi wa m’bale wake wopanda ana, kuti abeleke ana ndi colinga cakuti dzina la banja la m’bale wake lisafafanizike.—Gen. 38:8; Deut. 25:5, 6.

^ par. 9 Aja amene adzaukitsidwa padziko lapansi, adzakhala ndi ciyembekezo ca moyo wosatha, osati moyo wosafa. Kuti mudziŵe zambili ponena za kusiyana pakati pa moyo wosafa ndi moyo wosatha, onani Nsanja ya Olonda yacingelezi ya April 1, 1984, masamba 30-31..